Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 24 tsamba 62-tsamba 63 ndime 7
  • Yesu Analalikira M’madera Ambiri a ku Galileya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Analalikira M’madera Ambiri a ku Galileya
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Yesu Anadza Kudziko Lapansi
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • A7-C Zinthu Zikuluzikulu Zimene Yesu Anachita Ali Padziko Lapansi—Utumiki Waukulu wa Yesu MʼGalileya (Gawo 1)
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • Changu cha Kulambira Yehova
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Mesiya Anakwaniritsa Ulosi
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 24 tsamba 62-tsamba 63 ndime 7
Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane apeza Yesu

MUTU 24

Yesu Analalikira M’madera Ambiri a ku Galileya

MATEYU 4:23-25 MALIKO 1:35-39 LUKA 4:42, 43

  • YESU ANALALIKIRA NDI OPHUNZIRA AKE 4 M’MADERA A KU GALILEYA

  • ANTHU AMBIRI ANAMVA ZIMENE YESU ANKACHITA NDIPONSO UTHENGA WAKE

Ali ku Kaperenao Yesu ndi ophunzira ake anatanganidwa kwambiri. Madzulo, anthu a mumzindawo anamubweretsera odwala kuti awachiritse. Chifukwa cha zimenezi Yesu anasowa nthawi yopuma komanso yochita zinthu zina payekha.

Ndiyeno tsiku lotsatira, m’mamawa kwambiri kukadali kamdima Yesu anadzuka n’kupita kumalo a yekha kuti akapemphere kwa Atate wake. Koma pasanapite nthawi yaitali, anthu anazindikira kuti Yesu sakuoneka ndipo “Simoni ndi ena amene anali naye” anayamba kumufunafuna. Zikuoneka kuti Petulo ndi amene ankatsogolera anthuwo chifukwa pa nthawiyi Yesu anali mlendo ku nyumba kwake.—Maliko 1:36; Luka 4:38.

Atamupeza, Petulo anati: “Anthu onse akukufunafunani.” (Maliko 1:37) Anthu a ku Kaperenao sankafuna kuti Yesu achoke. Anthuwa ankasangalala kwambiri ndi zimene Yesu ankachita moti “anayesa kumuletsa kuti asawasiye.” (Luka 4:42) Kodi cholinga chachikulu cha Yesu pobwera padziko lapansi chinali chodzachita zozizwitsa? Kodi anafunika kugwira ntchito yake m’dera lokhali basi? Kodi Yesu anayankha bwanji mafunso amenewa?

Yesu akulankhula ndi Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane ndipo akuloza tauni yapafupi ndi pomwe ali

Yesu anayankha ophunzira ake kuti: “Tiyeni tipite kwina kumidzi yapafupi, kuti ndikalalikire kumenekonso, pakuti ndicho cholinga chimene ndinabwerera.” Ndipotu Yesu anauza anthu amene ankamukakamizawo kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.”—Maliko 1:38; Luka 4:43.

Choncho cholinga chachikulu chimene Yesu anabwerera padziko lapansi chinali kudzalalikira za Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu ndi umene udzayeretse dzina la Atate wake komanso kuthetseratu mavuto onse a anthu. Zimene Yesu anachita pochiritsa anthu mozizwitsa zinatsimikizira kuti anatumidwadi ndi Mulungu. Nayenso Mose anachita zinthu zambiri zodabwitsa kukadali zaka zambiri Yesu asanabwere padziko lapansi. Zimene anachitazi zinkatsimikizira kuti anatumidwa ndi Mulungu.—Ekisodo 4:1-9, 30, 31.

Kenako Yesu ndi ophunzira ake 4 anachoka ku Kaperenao n’kupita kukalalikira ku mizinda ina. Ophunzira amenewa anali Petulo ndi m’bale wake Andireya komanso Yohane ndi m’bale wake Yakobo. Pa nthawi imeneyi panali patangotha mlungu umodzi kuchokera pamene Yesu anawaitana kuti aziyenda naye.

Ntchito yolalikira imene Yesu ndi ophunzira ake anagwira ku Galileya inayenda bwino kwambiri. Moti anthu okhala m’madera akutali anamva za mbiri ya Yesu. “Mbiri yake inafalikira mu Siriya monse,” komanso m’dera la Dekapole lomwe linapangidwa ndi mizinda 10. Mbiriyi inafalikiranso mpaka kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano. (Mateyu 4:24, 25) Gulu la anthu ochokera m’madera amenewa komanso lochokera ku Yudeya linayamba kutsatira Yesu ndi ophunzira ake. Ambiri anabwera ndi anthu odwala kuti adzachiritsidwe. Posafuna kuwakhumudwitsa, Yesu anachiritsa odwalawo komanso kutulutsa mizimu yoipa mwa anthu ena.

  • Kodi Yesu anachita chiyani m’mawa wa tsiku lina?

  • N’chifukwa chiyani Yesu anabwera padziko lapansi, nanga n’chifukwa chiyani anachita zozizwitsa?

  • Kodi Yesu anali ndi ndani pamene ankapita kukalalikira ku Galileya? Kodi anthu anachita chiyani ataona zimene Yesu ankachita?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena