Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 7/15 tsamba 24-25
  • Miyala ya Mtengo Wake Kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Mateyu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Miyala ya Mtengo Wake Kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Mateyu
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kubadwa ndi Utumiki Woyambirira
  • Yesu Mphunzitsi Wokhutiritsa
  • Labadirani Uphungu Wochokera kwa Mwana wa Mulungu
  • Wachitsanzo Wathu Wosunga Umphumphu
  • N’chifukwa Chiyani Ophunzira a Yesu Sankasala Kudya?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Kwenikweni Uthenga Wabwino Nchiyani?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Ngale Kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Luka
    Nsanja ya Olonda—1989
Nsanja ya Olonda—1989
w89 7/15 tsamba 24-25

Miyala ya Mtengo Wake Kuchokera mu Uthenga Wabwino wa Mateyu

YEHOVA MULUNGU anawuzira wosonkhetsa msonkho wakale Mateyu kulemba cholembera chochititsa nthumanzi cha kubadwa, moyo, imfa, ndi chiwukiriro cha Yesu Kristu. Maumboni mu unyinji wa mamanusikripiti a pambuyo pa zana la khumi amanena kuti Uthenga Wabwino umenewu unalembedwa chifupifupi chaka cha chisanu ndi chitatu pambuyo pa kukwera kumwamba kwa Yesu (c. 41 C.E.). Ichi sichimawombana ndi umboni wamkati, popeza kuti cholemberacho chimatha ndi kutumiza kwa Yesu opanga ophunzira mu 33 C.E. ndipo sichimanena chirichonse ponena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu pa manja a Roma mu 70 C.E.

Mu Historia Ecclesiastica yake (Mbiri Yakale ya Zatchalitchi), wolemba mbiri yakale wa zana lachinayi Eusebius akugwira mawu Papias ndi Irenaeus a zana lachiŵiri ndi Origen wa lachitatu, onse omwe amagwirizanitsa Uthenga Wabwino umenewu kwa Mateyu ndi kunena kuti iye anaulemba iwo m’Chihebri. Kodi chimenechi m’chenicheni chinali Chiaramu? Osati mogwirizana ndi makalata otchulidwa ndi George Howard, profesa wa chipembedzo pa Yunivesiti ya Georgia. Iye analemba kuti: “Kulingalira kumeneku kunali poyambirira chifukwa cha chikhulupiriro chakuti Chihebri m’masiku a Yesu sichinali kugwiritsiridwa ntchito nkomwe mu Palestina koma chinaloŵedwa m’malo ndi Chiaramu. Kupeza kotsatira kwa Mipukutu ya mu Dead Sea, yambiri ya yomwe iri zolembedwa za Chihebri, limodzinso ndi makalata ena a Chihebri ochokera ku Palestina kuchokera ku nyengo yachisawawa ya nthawi ya Yesu, tsopano zikusonyeza Chihebri kukhala chinali chamoyo ndipo chabwino m’zana loyamba.” Mwachiwonekere, Mateyu analemba Uthenga Wabwino wake kuti upindulitse Akristu a Chihebri koma angakhale anautembenuzanso m’Chigriki chofala.

Tikukusonkhezerani inu kuŵerenga Uthenga Wabwino wa Mateyu. Pamene tikuyang’ana pa miyala ya mtengo wake yoŵerengeka imene uwo uli nayo, onani nkhani ya kumbuyo imene imamveketsa bwino cholemberachi.

Kubadwa ndi Utumiki Woyambirira

Uthenga Wabwino wa Mateyu umatseguka ndi mpambo wa mibadwo ndi kubadwa kwa Yesu. Pamene Mariya anapezedwa ali ndi pakati, womtomera wake, Yosefe, “anayesa mu mtima kumuleka iye mseri.” (1:19) Koma kodi ndimotani mmene iye akanachitira tero, popeza kuti iwo anali kokha otomerana? Chabwino, kwa Ayuda mkazi wotomeredwa anali ndi mathayo ofanana ndi akazi okwatiwa. Ngati iye anakhala ndi unansi wa kugonana ndi winawake, iye akaponyedwa miyala mofanana ndi mkazi wachigololo. (Deuteronomo 22:23-29) Chotero, chifukwa cha mkhalidwe womangirira wa kutomerana umenewu, Yosefe anakonzekera kusudzula Mariya, ngakhale kuti panalibe kachitidwe ka mwambo kamene kanawagwirizanitsa iwo m’chikwati.

Mitu yoyambirira ya Uthenga Wabwino wa Mateyu iri ndi Ulaliki wa pa Phiri wa Yesu. Mu uwo, Kristu anachenjeza kuti munthu akaŵerengera ku “Khoti Lalikulu” kaamba ka kulankhula kwa mbale wake ndi “mawu osafunika onyoza.” (5:22, NW) Kalankhulidwe koteroko kanafikira ku kuitana mbale wake wa munthu kukhala wopanda pake.

Koma kodi nchiyani chomwe chinali “Khoti Lalikulu”? Linali Bwalo Lamilandu Lalikulu Lachiyuda (Sanhedrin) la ziŵalo 71 la Yerusalemu. Kodi ndi chiyambi chotani chomwe chinafunikira kuyeneretsedwa kukhala chiŵalo mu ilo? Cyclopedia ya McClintock ndi Strong ikunena kuti: “Wofunsirayo anafunikira kukhala wopanda banga mwa makhalidwe ndi kuthupi. Iye anafunikira kukhala wa msinkhu wapakati, wamtali, wa mawonekedwe abwino, wachuma, wophunzira . . . Iye anafunikira kudziŵa zinenero zingapo . . . Anthu okalamba kwambiri, otembenuzidwa, osabala, ndi Anetini anali osayenerera chifukwa cha zifooko zawo; ndipo ofunsira oterowo sakakhoza ngakhale kusankhidwa popeza kuti analibe ana, chifukwa sakakhala achifundo pa mikhalidwe ya panyumba . . . ; osati ngakhale awo omwe sakadzitsimikizira kuti anali ana alamulo a wansembe, Mlevi, kapena m’Israyeli. . . . Wofunsira kukhala wa Sanhedrin Yaikulu anafunikira, choyambirira cha zonse, kukhala anali woweruza m’tauni lakwawo; kukhala anasamutsidwa kuchokera kumeneko kupita ku Sanhedrin Yaing’ono . . . , ndipo kumenekonso kukhala atakwezedwa ku Sanhedrin Yaing’ono yachiŵiri . . . asanalandiridwe monga chiŵalo cha makumi asanu ndi aŵiri mphambu mmodzi.”

Chotero Yesu anatanthauza kuti “aliyense wolankhula kwa mbale wake ndi mawu osayenera onyoza” amakhala ndi liwongo loyerekezedwa ndi lija la munthu wopatsidwa mlandu ndi kuweruzidwa ku imfa ndi Khoti Lalikulu Lachiyuda. Ndi chenjezo lotani nanga kusamanyoza abale athu! Lolani kuti tiletse lirime lathu kotero kuti sitikuyenerera kutsutsidwa mu Khoti Lalikulu Koposa, pamaso pa Yehova, “Woweruza wa dziko lonse lapansi.”​—Genesis 18:25; Yakobo 3:2-12.

Yesu Mphunzitsi Wokhutiritsa

Uthenga Wabwino umenewu umasonyezanso Yesu kukhala mphunzitsi wokhoza kuyankha mafunso mwaluso. Mwachitsanzo, poyankha funso, iye analongosola chifukwa chimene ophunzira ake sanasale kudya. (9:14-17) Iwo analibe chifukwa cha kusala kudya pamene iye anali ndi moyo. Koma monga mmene iye ananeneratu, iwo anasala kudya nalira maliro pamene iye anafa chifukwa sanadziŵe chifukwa chimene imfa yake inaloledwera. Ngakhale kuli tero, pambuyo polandira mzimu woyera pa Pentekoste, iwo anawunikiridwa ndipo sanasalanso kudya m’chisoni.

Akuchitabe ndi nkhani imodzimodziyo, Yesu anawonjezera kuti palibe munthu aphatika chigamba cha nsalu yatsopano pa chovala chakale pakuti mphamvu yake imapangitsa kung’ambikako kuipirako. Iye ananenanso kuti samathira vinyo watsopano m’matumba akale. Thumba la vinyo, kapena mchenje, linali chikopa chopunthidwa cha nyama chosokedwa konse kusiyako mwendo wotseguka. Kuvundika vinyo watsopano kumatulutsa mpweya wa carbon dioxide womwe umakakamiza mphamvu yokwanira kuphulitsa matumba a vinyo akale, owuma. Moyerekeza, chowonadi chimene Kristu anaphunzitsa chinali champhamvu mopambanitsa kaamba ka Chiyuda chakale, chowuma khosi. Kuwonjezerapo, iye sanali kuyesera kuphatika chigamba kapena kupitiriza dongosolo la chipembedzo long’ambika lirilonse ndi miyambo yake yosala kudya ndi ina yake. M’malomwake, Mulungu anagwiritsira ntchito Yesu kuyambitsa dongosolo latsopano la kulambira. Motsimikizirika, kenaka, sitiyenera kuchita chirichonse kuchirikiza mabungwe osakaniza zikhulupiriro kapena kupitiriza chipembedzo chonyenga.

Labadirani Uphungu Wochokera kwa Mwana wa Mulungu

Mogwirizana ndi cholembera cha Mateyu cha kusandulika, Mulungu anatcha Yesu Mwana Wake wovomerezedwa ndi kunena kuti tiyenera kumvetsera kwa iye. (17:5) Chotero tiyenera kulabadira uphungu wonse wa Kristu, wonga ngati chenjezo lake lakuti aliyense wokhumudwitsa munthu woika chikhulupiriro mwa iye chikakhala bwino kumumiza iye m’nyanja ndi mphero yomangiliridwa m’khosi mwake. (18:6) Kodi mwala umenewu unali wa mtundu wanji? Osati waung’ono, popeza kuti Yesu anatanthauza mphero yapamwamba ya mamita 1.2 kufika ku 1.5 modutsa pakati. Kutembenuzira iwo pa mwala waukulu wa m’munsi kunaitanira kaamba ka mphamvu ya nyama. Palibe aliyense akapulumuka m’nyanja ndi kulemera kwakukulu koteroko m’khosi mwake. M’chenicheni, kenaka, Yesu anali kupereka uphungu kwa ife kupeŵa liwongo la kukhumudwitsa aliyense wa atsatiri ake. Ndi cholinga chofananacho, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chirichonse cha kukhumudwitsa mbale wako.”​—Aroma 14:21.

Mwana wa Mulungu anapereka uphungu wosalunjika pamene analengeza tsoka pa alembi ndi Afarisi ndi kunena kuti iwo anafanana ndi manda opaka njereza. (23:27, 28) Chinali cha mwambo kupaka njereza manda ndi mathinda kotero kuti anthu sakawagwira iwo mwangozi ndi kukhala odetsedwa. Mwa kulozera ku kachitidwe kameneka, Yesu anasonyeza kuti alembi ndi Afarisi anawoneka olungama kunja koma anali “odzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika.” Kulabadira uphungu wolozeredwako umenewu kudzatipangitsa ife kuletsa chinyengo ndi kuchita mwa “chikhulupiriro chosanyenga.”​—1 Timoteo 1:5; Miyambo 3:32; 2 Timoteo 1:5.

Wachitsanzo Wathu Wosunga Umphumphu

Pambuyo polemba ulosi wa Yesu wonena za ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake,’ Mateyu akunena za kuperekedwa kwa Kristu, kumangidwa, kuzengedwa mlandu, imfa, ndi chiwukiriro. Pa mtengo, Yesu anakana kumwa vinyo wosanganizidwa ndi ndulu, msanganizo wokhala ndi mphamvu yothetsa kupweteka. (27:34) Akazi mwa mwambo anapereka vinyo woteroyo kwa apandu kuthetsa kupweteka kwa kupachikidwa. Marko 15:23 akunena kuti vinyowo unali “wosanganizidwa ndi mule,” womwe ukawonjezera kukoma. Mwachiwonekere, zonse ziŵiri ndulu ndi mule zinali mu vinyo yemwe Kristu anakana. Pamene iye anafika pa chimake cha moyo wake wa pa dziko lapansi, iye sanafune kumwetsedwa anam’goneka kapena kupusitsidwa. Yesu anakhumba kukhala m’kulamulira kokwanira kwa malingaliro ake kotero kuti akhale wokhulupirika kufikira imfa. Mofanana ndi Wachitsanzo wathu, lolani kuti nthaŵi zonse tikhale odera nkhaŵa ponena za kusunga umphumphu wathu kwa Yehova Mulungu.​—Salmo 26:1, 11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena