-
Kodi Baibulo la Dziko Latsopano Linamasuliridwa Molondola?Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
-
-
Kugwiritsira ntchito mawu osiyanasiyana. Nthawi zambiri mavesi a m’Baibulo amene amasuliridwa liwu ndi liwu amakhala osamveka bwino. Mwachitsanzo pomasulira liwu ndi liwu mawu a Yesu a pa Mateyu 5:3, Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu limati: “Odala ali osauka mumzimu.” Anthu ambiri amaona kuti mawu akuti “osauka mumzimu” ndi ovuta kumvetsa ndipo ena amaganiza kuti Yesu ankanena za kufunika kokhala munthu wodzichepetsa kapena wosauka. Komatu apa Yesu ankatanthauza kuti munthu angapeze chimwemwe chenicheni ngati akutsogoleredwa ndi Mulungu. Choncho Baibulo la Dziko Latsopano linamasulira mawu a Yesu amenewa molondola, ponena kuti “anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.c
-
-
Kodi Baibulo la Dziko Latsopano Linamasuliridwa Molondola?Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
-
-
c Mofanana ndi zimenezi, Baibulo la J. B.Phillips linamasulira vesili kuti, “amene amazindikira kuti akufunikira Mulungu,” ndiponso Baibulo la The Translator’s New Testament linamasulira vesili kuti “amene amazindikira kuti akufunikira zinthu zauzimu.”
-