-
Kodi Mumathetsa Motani Mikangano?Nsanja ya Olonda—1994 | July 15
-
-
“Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako. Koma ngati samvera, wonjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena aŵiri, kuti atsimikizidwe mawu onse pakamwa pa mboni ziŵiri kapena zitatu. Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.”—Mateyu 18:15-17.
-
-
Kodi Mumathetsa Motani Mikangano?Nsanja ya Olonda—1994 | July 15
-
-
Ngati nkhaniyo siinathetsedwe, inafunikira kuperekedwa ku mpingo. Poyamba, zimenezi zinatanthauza kwa akulu a Ayuda koma pambuyo pake, kwa akulu a mpingo Wachikristu. Wochimwa wosalapayo angafunikire kuchotsedwa mumpingo. Zimenezo ndizo zikutanthauzidwa ndi kumuona “monga wakunja ndi wamsonkho,” anthu amene Ayuda anatalikirana nawo. Sitepe lalikulu limeneli silinatengedwe ndi Mkristu aliyense payekha. Akulu oikidwa, amene amaimira mpingo, ndiwo okha amene ali ndi ukumu wa kuchitapo kanthu motero.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 5:13.
Kuthekera kwakuti wochimwa wosalapayo angachotsedwe kumasonyeza kuti Mateyu 18:15-17 samakhudza mikangano yaing’ono. Yesu anali kunena za zolakwa zazikulu, komabe zokhoza kuthetsedwa pakati pa anthu aŵiri oloŵetsedwamo. Mwachitsanzo, cholakwacho chingakhale kunamizira, kumene kungayambukire moipa mbiri ya wochimwiridwayo. Kapena chingakhudze nkhani zandalama, pakuti mavesi otsatira ali ndi fanizo la Yesu lonena za kapolo wopanda chifundo amene anakhululukidwa mangawa aakulu. (Mateyu 18:23-35) Ngongole yosalipiriridwa panthaŵi yoikika ingangokhala vuto lakanthaŵi limene lingathetsedwe mosavuta ndi anthu aŵiriwo. Koma lingakhale tchimo lalikulu, kutanthauza, kuba, ngati wokongolayo mouma khosi akana kulipirira zimene anakongolazo.
Machimo ena sangathe kuthetsedwa ndi Akristu aŵiri okha. Pansi pa Chilamulo cha Mose, machimo aakulu anafunikira kuululidwa. (Levitiko 5:1; Miyambo 29:24) Mofananamo, machimo aakulu oloŵetsamo chiyero cha mpingo ayenera kuululidwa kwa akulu ampingo.
Komabe, nkhani zochuluka za kusamvana pakati pa Akristu siziyenera kutsatira njira imeneyi.
-