Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 64 tsamba 152-tsamba 153 ndime 2
  • Anawaphunzitsa Kufunika Kokhululukira Ena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anawaphunzitsa Kufunika Kokhululukira Ena
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Phunziro la Kukhululukira
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Phunziro m’Kukhululukira
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Chifukwa Chake Tiyenera Kukhululukira Ena
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kapolo Wosakhululukira
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 64 tsamba 152-tsamba 153 ndime 2
Kapolo akukanyanga kapolo mnzake pakhosi

MUTU 64

Kufunika Kokhululukira Ena

MATEYU 18:21-35

  • KODI NDIZIKHULULUKA NTHAWI 7 ZOKHA?

  • FANIZO LA WANTCHITO WOPANDA CHIFUNDO

Petulo anamvetsa malangizo amene Yesu anapereka ofotokoza zimene munthu ayenera kuchita ngati wasemphana maganizo ndi m’bale wake. Yesu ananena kuti anthuwo ayenera kuyesetsa kukambirana kaye paokha. Koma zikuoneka kuti Petulo ankafuna kudziwa kuti munthu ayenera kumukhululukira kangati m’bale wake.

Choncho Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, kodi m’bale wanga angandichimwire kangati ndipo ine n’kumukhululukira? Mpaka nthawi 7 kodi?” Atsogoleri ena achipembedzo ankaphunzitsa kuti munthu ankayenera kukhululukira mnzake maulendo atatu okha. Ndiyeno Petulo ayenera kuti ankaona ngati kukhululukira m’bale wake “mpaka nthawi 7” kunali kukoma mtima.—Mateyu 18:21.

Komabe zoti munthu azichita kuwerenga kuti wamukhululukira kangati m’bale wake, sizinkagwirizana ndi zimene Yesu ankaphunzitsa. Choncho pofuna kuthandiza Petulo, Yesu anamuuza kuti: “Ndikukuuza kuti, osati nthawi 7 zokha ayi, koma, Mpaka nthawi 77.” (Mateyu 18:22) Pamenepa Yesu ankatanthauza kuti munthu sayenera kuika malire pa nthawi imene angakhululukire m’bale wake. Choncho Petulo sankafunika kuwerenga nthawi zimene wakhululukira m’bale wake.

Mfumu ikukhululukira kapolo wake ngongole

Kenako Yesu anauza Petulo komanso atumwi enawo fanizo pofuna kuwathandiza kumvetsa kufunika koti azikhululukira anthu ena. Fanizo lake linali lonena za wantchito wina amene analephera kutsanzira bwana wake posonyeza chifundo. Panali mfumu ina imene inkafuna kuti akapolo kapena kuti antchito ake abweze ngongole zomwe anawabwereka. Ndiyeno atumiki a mfumuyi anabweretsa wantchito wina amene anali ndi ngongole yaikulu ya matalente 10,000 [omwe anali madinari 60 miliyoni]. Chifukwa chakuti ngongoleyo inali yaikulu wantchitoyo sakanakwanitsa kuibweza. Choncho mfumuyo inalamula kuti wantchitoyo, mkazi wake komanso ana ake agulitsidwe kuti ndalamazo abwezere ngongoleyo. Nthawi yomweyo wantchitoyo anagwada pamapazi a mfumuyo n’kuichonderera kuti: “Ndilezereniko mtima chonde, ndidzakubwezerani zonse.”—Mateyu 18:26.

Kapolo walamula kuti kapolo mnzake atsekeredwe m’ndende

Mfumuyo inamva chisoni ndipo inamuchitira chifundo moti inamukhululukira ngongoleyo. Munthuyo atachoka kwa mfumuyo anakumana ndi wantchito mnzake amene anamukongoza madinari 100. Anagwira mnzakeyo n’kumukanyanga pakhosi ndipo anamuuza kuti: “Bweza ngongole ija mwamsanga.” Koma mnzakeyo anagwada pamapazi ake n’kumuchonderera kuti: “Mundilezereko mtima chonde, ndidzakubwezerani.” (Mateyu 18:28, 29) Koma wantchito amene anakhululukidwa ngongole uja sanachite zofanana ndi zimene mfumu inamuchitira. Iye anakapereka mnzakeyo kundende kuti akhale kumeneko mpaka atabweza ngongoleyo. Anachita zimenezi ngakhale kuti mnzakeyo anali ndi ngongole yochepa yoti amubwezere.

Mfumu yalamula kuti kapolo wopanda chifundo atsekeredwe m’ndende

Kenako Yesu anafotokoza kuti antchito ena, omwe anaona zinthu zopanda chifundo zimene wantchito uja anachitira mnzakeyo, anakauza mfumu ija za nkhaniyi. Ndiyeno mfumuyo inakwiya kwambiri moti inaitanitsa wantchitoyo n’kumuuza kuti: “Kapolo woipa iwe, ine ndakukhululukira ngongole yonse ija utandidandaulira. Kodi nawenso sukanam’chitira chifundo kapolo mnzako, monga momwe ine ndinakuchitira chifundo?” Zitatero mfumuyo inalamula kuti wantchito wopanda chifundoyo aponyedwe m’ndende mpaka atabweza ngongole yake yonse. Yesu anamaliza fanizoli ponena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba adzathana ndi inu ngati aliyense wa inu sakhululukira m’bale wake ndi mtima wonse.”—Mateyu 18:32-35.

Zimenezitu zikutiphunzitsa kufunika kokhululukira anthu ena. Mulungu anatikhululukira machimo athu amene ali ngati ngongole yaikulu. Choncho zimene m’bale wathu angatilakwire ndi zazing’ono kwambiri poyerekeza ndi zimene Mulungu anatikhululukira. Ndipotu Yehova amatikhululukira maulendo ambirimbiri. Zimenezi ziyenera kutichititsa kuti tizikhululukira m’bale wathu ngakhale atatilakwira kwambiri. Pajatu pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anaphunzitsa kuti Mulungu ‘adzatikhululukira zolakwa zathu’ ngati ‘ifenso timakhululukira amene amatilakwira.’—Mateyu 6:12.

  • N’chiyani chinachititsa Petulo kufunsa nkhani yokhululukira m’bale wake? Nanga n’chiyani chinamuchititsa kuona kuti kunali kukoma mtima kukhululukira munthu wina nthawi 7?

  • Kodi zimene mfumu ija inachitira wantchito wake atamuchonderera zikusiyana bwanji ndi zimene wantchitoyo anachitira wantchito mnzake?

  • Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo limene Yesu ananena?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena