-
Fanizo la Anthu Ogwira Ntchito M’munda wa MpesaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
“Pakuti ufumu wakumwamba uli ngati mwinimunda wa mpesa, amene analawirira m’mawa kwambiri kukafuna anthu aganyu kuti akagwire ntchito m’munda wake wa mpesa. Aganyu amenewa atagwirizana nawo kuti aziwapatsa ndalama ya dinari imodzi pa tsiku, anawatumiza kumunda wake wa mpesa. Pafupifupi 9 koloko m’mawa anapitanso kukafuna anthu ena, ndipo anaona ena atangoimaima pamsika alibe chochita. Amenewonso anawauza kuti, ‘Inunso kagwireni ntchito m’munda wa mpesa. Ndidzakupatsani malipiro oyenerera.’ Chotero iwo anapita. Pafupifupi 12 koloko ndi 3 koloko masana, mwinimunda uja anapitanso kukachita chimodzimodzi. Pamapeto pake, pafupifupi 5 koloko madzulo anapitanso ndipo anakapeza ena atangoimaima. Iye anawafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mwangoimaima pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ Iwo anamuyankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba ganyu.’ Iye anawauza kuti, ‘Inunso pitani kumunda wanga wa mpesa.’”—Mateyu 20:1-7.
-
-
Fanizo la Anthu Ogwira Ntchito M’munda wa MpesaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
Ansembe komanso anthu ena omwe anali m’gulu la atsogoleri achipembedzo ankaona kuti Ayuda wamba sankatumikira kwambiri Mulungu ndipo anali ngati aganyu m’munda wa mpesa wa Mulungu. M’fanizo la Yesuli, Ayuda wambawa anali ngati aganyu amene anawalemba ntchito cha m’ma 9 koloko m’mawa kapena amene anayamba cha m’ma 12 koloko, 3 koloko komanso cha m’ma 5 koloko madzulo.
Atsogoleri achipembedzo ankaona kuti amuna ndi akazi amene ankatsatira Yesu anali ngati anthu ‘otembereredwa.’ (Yohane 7:49) Kwa nthawi yaitali anthu amenewa ankagwira ntchito yausodzi komanso ankagwira maganyu osiyanasiyana. Ndiyeno pofika m’mwezi wa July kapena August m’chaka cha 29 C.E., “mwinimunda” anatumiza Yesu kuti akaitane anthu otsikawa kuti adzagwire ntchito ya Mulungu monga ophunzira a Khristu. Anthuwa anali antchito “omalizira” amene Yesu anawatchula, omwe anayamba kugwira ntchito m’munda wa mpesa cha m’ma 5 koloko madzulo.
-