Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 8/1 tsamba 10-15
  • Pambanani M’kupeŵa Msampha wa Kusirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pambanani M’kupeŵa Msampha wa Kusirira
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amatichenjeza za Upandu Wake
  • Kutcheredwa Msampha ndi Kusirira Chuma Kapena Katundu
  • Kusirira m’Mbali Zina za Moyo
  • Pitirizani Kukhalabe Otsimikiza Kupeŵa Kusirira
  • “Nyengo Yaumbombo”
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Tayerekezerani Dziko Lopanda Umbombo
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Mungathe Kupulumuka ku Misampha ya Satana
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Kodi Ndalama Tingazione Motani M’njira Yoyenera?
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 8/1 tsamba 10-15

Pambanani M’kupeŵa Msampha wa Kusirira

“Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha.”​—1 TIMOTEO 6:9.

1. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulingalira mosamalitsa za misampha?

LIWU lakuti “msampha” lingakuchititseni kulingalira za mlenje akutchera chipangizo chosawonekera kuti agwire nyama yosadziŵa kanthu. Komabe, Mulungu amanena momvekera bwino kuti kwa ifeyo misampha yowopsa kwambiri sindiyo zipangizo zenizeni zimenezo, koma zimene zingatitchere msampha mwauzimu, kapena mwamakhalidwe. Mdyerekezi ndiye katswiri pakutchera misampha yoteroyo.​—2 Akorinto 2:11; 2 Timoteo 2:24-26.

2. (a) Kodi Yehova amatithandiza motani kupeŵa misampha yowopsa? (b) Kodi ndi msampha wotani umene tikulunjikitsapo chidwi tsopano?

2 Yehova amatithandiza mwakutidziŵitsa ina ya misampha yambiri ndi yosiyanasiyana ya Satana. Mwachitsanzo, Mulungu amachenjeza kuti milomo yathu, kapena pakamwa, pangakhale msampha ngati tilankhula mopanda nzeru, mwaukali, kapena za zinthu zimene sitifunikira kunena. (Miyambo 18:7; 20:25) Kunyada kungakhale msampha, monga momwenso kuliri kukhala ndi anthu okonda kukwiya. (Miyambo 22:24, 25; 29:25) Komano tiyeni titembenukire ku msampha wina: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chionongeko ndi chitayiko.” (1 Timoteo 6:9) Chimene chili kumbuyo kwa msampha umenewo kapena maziko ake chinganenedwe m’liwu limodzi lakuti “kusirira.” Ngakhale kuti kaŵirikaŵiri kusirira kumawonekera m’kufunitsitsa kukhala wolemera, kusirira kulidi msampha wokhala ndi mbali zambiri.

Yehova Amatichenjeza za Upandu Wake

3, 4. Kodi mbiri ya anthu amakedzana ili ndi phunziro lotani ponena za kusirira?

3 Kwakukulukulu, kusirira ndiko chikhumbo chosayenerera kapena chopambanitsa cha kukhala ndi zochuluka, kaya zikhale ndalama, chuma, mphamvu, kugonana, kapena zinthu zina. Sindife oyamba kuikidwa paupandu ndi msampha wa kusirira. Kalelo m’munda wa Edeni, kusirira kunatchera msampha Hava ndipo kenaka Adamu. Mwamuna wa Hava, amene anali ndi chidziŵitso chochuluka m’moyo kuposa iye, anali atalangizidwa mwachindunji ndi Yehova. Mulungu anali atawapatsa malo a paradaiso. Iwo anasangalala ndi zakudya zambiri zabwino ndi zosiyanasiyana, zomera panthaka yosaipitsidwa. Iwo anayembekezera kukhala ndi ana angwiro, amene akakhala nawo pamodzi ndi kutumikira Mulungu kosatha. (Genesis 1:27-31; 2:15) Kodi zimenezo sizikuwoneka kukhala zokwanira kukhutiritsa munthu aliyense?

4 Komabe, kukhala ndi zinthu zokwanira sikumaletsa kusirira kukhala msampha. Hava anatcheredwa msampha ndi chiyembekezo cha kukhala wofanana ndi Mulungu, kukhala ndi ufulu wochuluka ndi kudzipangira miyezo yakeyake. Kukuwonekera kuti Adamu anafuna kukhala ndi unansi wosatha ndi mkazi wake wokongola, zivute zitani. Popeza kuti ngakhale anthu angwiro ameneŵa anatcheredwa msampha ndi kusirira, mukhoza kuzindikira chifukwa chake kusirira kungakhale kwaupandu kwa ife.

5. Kodi nkofunika motani kwa ife kupeŵa msampha wa kusirira?

5 Tiyenera kuchenjera ndi kutcheredwa msampha ndi kusirira chifukwa chakuti mtumwi Paulo anatichenjeza kuti: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, . . . sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Paulo anatiuzanso kuti: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu.” (Aefeso 5:3) Chotero chisiriro sichiyenera kukhala konse nkhani yokambitsirana ndi chifuno chokhutiritsa thupi lathu lopanda ungwiro.

6, 7. (a) Kodi nzitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zimasonyeza mmene msampha wa kusirira ungakhalire wamphamvu? (b) Kodi nchifukwa ninji zitsanzo zimenezo ziyenera kukhala chenjezo kwa ife?

6 Yehova analemba zitsanzo zambiri kuti atichenjeze za upandu wa kusirira. Takumbukirani kusirira kwa Akani. Mulungu ananena kuti Yeriko anayenera kuwonongedwa, koma golidi wake, siliva, mkuwa, ndi chitsulo zinali za mosungiramo Mwake. Poyamba Akani angakhale atafuna kutsatira malangizo amenewo, koma kusirira kunamtchera msampha. Pamene analoŵa m’Yeriko, anawona ngati kuti anali paulendo wokagula zinthu kumene anawona zinthu zotchipa zimene sakanatha kukhulupirira, kuphatikizapo malaya okongola amene anali omuyenera. Pamene anali kutola golidi ndi siliva wokwanira madola zikwi zambiri, iye angakhale ataganiza kuti, ‘Ha, simwawi umenewu nanga! Kuchita ngati kuba.’ Kunalidi kuba! Mwakusirira zimene zinayenera kuwonongedwa kapena kuperekedwa, iye anabera Mulungu, ndipo zimenezo zinamchititsa Akani kutaya moyo wake. (Yoswa 6:17-19; 7:20-26) Talingaliraninso zitsanzo za Gehazi ndi Yudasi Isikariote.​—2 Mafumu 5:8-27; Yohane 6:64; 12:2-6.

7 Sitiyenera kunyalanyaza chenicheni chakuti anthu atatu otchulidwa pamwambawa sanali akunja osadziŵa miyezo ya Yehova. M’malomwake, iwo anali ndi unansi wodzipatulira ndi Mulungu. Onsewo anawona zozizwitsa zimene zinayenera kukhomereza mwa iwo mphamvu ya Mulungu ndi kufunika kwa kukhalabe ndi chivomerezo chake. Komabe, msampha wa kusirira ndiwo unawagwetsa. Nafenso tingawononge unansi wathu ndi Mulungu ngati tidzilola kutcheredwa msampha ndi mpangidwe uliwonse wa kusirira. Kodi ndi mitundu kapena mipangidwe iti ya kusirira imene ingakhale yowopsa kwambiri kwa ife?

Kutcheredwa Msampha ndi Kusirira Chuma Kapena Katundu

8. Kodi Baibulo limapereka chenjezo lotani ponena za chuma?

8 Akristu ambiri amva machenjezo omvekera bwino a m’Baibulo onena za kukulitsa kukonda chuma, kulakalaka chuma. Kodi bwanji osapenda ena a ameneŵa, onga amene amapezeka pa Mateyu 6:24-33; Luka 12:13-21; ndi pa 1 Timoteo 6:9, 10? Pamene kuli kwakuti mungaganize kuti mumalandira ndi kulabadira uphungu umenewo, kodi sikotheka kuti Akani, Gehazi, ndi Yudasi angakhale ananena kuti anagwirizana nawonso? Mwachiwonekere, sitiyenera kumangouvomereza m’maganizo. Tiyenera kusamala kuti msampha wa kusirira chuma kapena katundu sukuyambukira moyo wathu watsiku ndi tsiku.

9. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupenda mkhalidwe wathu wamaganizo ponena za kugula zinthu?

9 Kaŵirikaŵiri, tsiku ndi tsiku timafunikira kugula zinthu​—chakudya, zovala, ndi zinthu zina zapanyumba. (Genesis 42:1-3; 2 Mafumu 12:11, 12; Miyambo 31:14, 16; Luka 9:13; 17:28; 22:36) Koma dongosolo lamalonda limasonkhezera chikhumbo cha kufuna zinthu zowonjezereka ndi zatsopano. Kusatsa malonda kwambiri kumene kukudzaza m’manyuzipepala, magazini, ndi pa TV kuli kuyesayesa konyengerera kwakudzutsa chisiriro. Kunyengerera kumeneko kungapezekenso m’masitolo okhala ndi malo okoloweka mabulauzi, makhothi, madilesi, ndi majuzi, ndi mashelufu okhala ndi nsapato zatsopano, ziwiya zamagetsi, ndi makamera. Kungakhale kwanzeru ngati Akristu adzifunsa kuti, ‘Kodi kugula zinthu kwakhala chinthu chofunika kapena chosangalatsa chachikulu m’moyo wanga?’ ‘Kodi ndikufunikiradi zinthu zatsopano zimene ndawona, kapena kodi dongosolo lamalonda likungokulitsa mbewu za chisiriro mwa ine?’​—1 Yohane 2:16.

10. Kodi ndimsampha wa kusirira uti umene ungakhale upandu makamaka kwa amuna?

10 Ngati kugula zinthu kukuwonekera kukhala msampha wofala kwa akazi, kupeza ndalama zochuluka ndimsampha wa amuna osaŵerengeka. Yesu anafanizira msampha umenewu ndi munthu wolemera amene anali ndi chuma chambiri komabe anali wofunitsitsa ‘kupasula nkhokwe zake ndi kumanganso zazikulu ndi kusungiramo dzinthu dzake dzonse ndi chuma chake.’ Yesu sanasiye chikayikiro chilichonse ponena za upanduwo mwakunena kuti: “Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse” kapena umbombo. (Luka 12:15-21) Kaya ndife olemera kapena osauka, tiyenera kulabadira uphungu umenewo.

11. Kodi Mkristu angatcheredwe msampha motani ndi kusirira ndalama zambiri?

11 Kusirira ndalama zochuluka, kapena zinthu zimene tingakhoze kugula, kaŵirikaŵiri kumakhala kobisika. Kungawonekere monga njira yofuna kulemera mwamsanga​—mwinamwake monga mwaŵi wopezeka kamodzikamodzi wa chisungiko cha zachuma mwakusungitsa ndalama m’malonda okhala ndi ngozi yaikulu. Kapena munthu angayesedwe kupeza ndalama ndi machitachita abizinesi okayikitsa kapena osavomerezedwa ndi lamulo. Chikhumbo chosirira chimenechi chingatchere msampha, chingatigonjetse. (Salmo 62:10; Miyambo 11:1; 20:10) Ena ngakhale mumpingo Wachikristu ayamba bizinesi namayembekezera kuti abale awo okhulupirika adzakhala makasitomala enieni. Ngati cholinga chawo sichinali kungopereka zinthu zofunika kapena utumiki mwa ‘kugwiritsa ntchito, kuchita ntchito yokoma ndi manja awo,’ koma kupeza ndalama mofulumira akumavulaza Akristu anzawo, pamenepo akuchita zimenezo chifukwa cha kusirira. (Aefeso 4:28; Miyambo 20:21; 31:17-19, 24; 2 Atesalonika 3:8-12) Kusirira ndalama kwachititsa ena kuloŵa m’kutchova juga mwakubetchera, mpikisano wamwaŵi, kapena malotale. Ena, mwakunyalanyaza chifundo ndi kulingalira kwanzeru, asumirana milandu kukhoti ncholinga choti apatsidwe mfupo yaikulu kapena ndalama zambiri za mlandu.

12. Kodi nchifukwa ninji timadziŵa kuti kusirira chuma kungalakidwe?

12 Zomwe tatchulazi ndi mbali zina zimene tifunikira kudzipenda kotero kuti tiwone mowona mtima ngati kusirira kukuyamba kuzika mizu mwa ife. Ngakhale ngati kwayamba kale kuzika mizu, tikhoza kusintha. Kumbukirani kuti Zakeyu anasintha. (Luka 19:1-10) Ngati aliyense apeza kuti ali ndi vuto lakusirira chuma kapena katundu, ayenera kukhala wotsimikiza mtima monga momwe analiri Zakeyu kotero kuti apeŵe msamphawo.​—Yeremiya 17:9.

Kusirira m’Mbali Zina za Moyo

13. Kodi lemba la Salmo 10:18 limatisonyeza msampha wina wotani wa kusirira?

13 Ena amakupeza kukhala kosavuta kuwona upandu wa kusirira pankhani ya ndalama ndi chuma kuposa mmene kumawonekera m’njira zina. Dikishonale ina Yachigiriki imanena kuti gulu la mawu omasuliridwa “umbombo” kapena “chisiriro” lili ndi tanthauzo la “‘kufuna zowonjezereka,’ mogwirizana ndi mphamvu ndi zina zotero ndiponso chuma.” Inde, tikhoza kutcheredwa msampha ndi kusirira kufuna kukhala ndi ulamuliro pa ena, mwinamwake kuwachititsa kunjenjemera ndi ulamuliro wathu.​—Salmo 10:18.

14. Kodi ndim’mbali ziti zimene chikhumbo cha kukhala ndi ulamuliro chakhala chovulaza?

14 Kuyambira kale kwambiri anthu opanda ungwiro akondwera kulamulira ena. Mulungu anawoneratu kuti chotulukapo chomvetsa chisoni chimene tchimo la anthu likadzetsa chikakhala chakuti amuna okwatira ambiri ‘akalamulira’ akazi awo. (Genesis 3:16) Komabe, chifooko chimenechi chatulukiranso kunja kwa banja. Zaka zikwi zambiri pambuyo pake, wolemba Baibulo ananena kuti “wina apweteka mnzake pomlamulira.” (Mlaliki 8:9) Mosakayikira mumadziŵa mmene zimenezo zakhalira zowona m’nkhani zandale ndi zankhondo, koma kodi zingatheke kuti nafenso patokha, timayesayesa kupeza mphamvu zochuluka kapena ulamuliro pa ena?

15, 16. Kodi ndim’njira zotani mmene Mkristu angatcheredwere msampha ndi chikhumbo cha mphamvu zowonjezereka? (Afilipi 2:3)

15 Tonsefe timachita zinthu ndi anthu ena​—m’mabanja athu, kumalo athu antchito kapena kusukulu, pakati pa mabwenzi, ndi mumpingo. Mwakamodzikamodzi, kapena kaŵirikaŵiri, timakhala ndi mbali yakupanga chosankha pa zimene zidzachitidwa, limodzi ndi njira ndi nthaŵi imene zidzachitidwira. Zimenezo sizolakwa kapena zoipa mwa izo zokha. Komabe, kodi timasangalala mopambanitsa kugwiritsira ntchito ulamuliro uliwonse umene tingakhale nawo? Kodi timakonda kupanga chosankha chomalizira ndi kufuna zowonjezereka? Mamanijala kapena mabwana akudziko kaŵirikaŵiri amasonyeza mkhalidwe wamaganizo umenewu mwakukhala ndi anthu amene amavomereza zonse zimene amanena, popanda kupereka malingaliro osiyana ndi amene samatsutsa kulakalaka (kusirira) mphamvu kwaudziko kwa akuluakulu awo.

16 Umenewu ndimsampha umene tifunikira kupeŵa pochita ndi Akristu anzathu. Yesu anati: “Mudziŵa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye awo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu.” (Mateyu 20:25, 26) Kudzichepetsa kotero kuyenera kuwonekera pamene akulu Achikristu akuchita ndi wina ndi mnzake, ndi atumiki otumikira, ndi gulu lonse la nkhosa. Mwachitsanzo, kodi kulakalaka mphamvu kungawonetsedwe ndi woyang’anira wotsogoza amene amafunsa akulu anzake pankhani zazing’ono zokha koma napanga zosankha zonse zazikulu payekha? Kodi iye ngwofunitsitsadi kugaŵira ena ntchito? Pangabuke mavuto ngati mtumiki wotumikira amene akusamalira msonkhano wa utumiki wakumunda alamula mosayenerera m’makonzedwe ake, kapena ngakhale kupanga malamulo.​—1 Akorinto 4:21; 9:18; 2 Akorinto 10:8; 13:10; 1 Atesalonika 2:6, 7.

17. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kutchula za nkhani ya chakudya pamene tikukambitsirana msampha wa kusirira?

17 Chakudya ndimbali ina imene ambiri amatcheredwa msampha ndi kusirira. Ndithudi, nkwachibadwa kusangalala ndi kudya ndi kumwa; Baibulo limavomereza zimenezo. (Mlaliki 5:18) Komabe, sikwachilendo kukulitsa chikhumbo chimenechi panyengo yaitali ya nthaŵi, chikumapyola pa zimene zili zosangalatsa ndi zokwanira. Ngati imeneyi sinali nkhani yoyenera kudetsa nkhaŵa atumiki a Mulungu, nchifukwa ninji Mawu a Yehova ananena pa Miyambo 23:20 kuti: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka”? Komabe, kodi timapeŵa motani msampha umenewu?

18. Kodi ndikudzipenda kotani kumene tingapange pankhani ya chakudya ndi chakumwa?

18 Mulungu samapereka lingaliro lakuti anthu ake adzidya zakudya zosakondweretsa. (Mlaliki 2:24, 25) Komanso samavomereza kuti tipange chakudya ndi chakumwa kukhala mbali yaikulu ya kukambitsirana ndi kakonzedwe kathu. Tingadzifunse kuti, ‘Kodi kaŵirikaŵiri ndimakhala wotenthedwa maganizo mopambanitsa pamene ndilongosola chakudya chomwe ndinadya kapena ndikukonzekera kukadya?’ ‘Kodi nthaŵi zonse ndimalankhula za chakudya ndi chakumwa pocheza?’ Chisonyezero china chingakhale mmene timachitira pamene tidya chakudya chimene sitinakonze kapena kugula, mwinamwake pamene tili mlendo m’nyumba ya munthu wina kapena pamene chakudya chiperekedwa pamsonkhano Wachikristu. Kodi timadya zambiri kuposa mmene timadyera masiku onse? Tikukumbukira kuti Esau analola chakudya kukhala chofunika koposa, ndipo anadzivulaza kosatha.​—Ahebri 12:16.

19. Kodi ndimotani mmene kusirira kungakhalire vuto pankhani ya chisangalalo cha kugonana?

19 Paulo akutiuza za msampha wina: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima.” (Aefeso 4:17-19; 5:3) Ndithudi, chisiriro cha chisangalalo chakugonana chingakule. Komabe, chisangalalo chimenechi chili ndi malo ake oyenerera mkati mwa zomangira za ukwati. Chikondi chathithithi chogwirizanitsidwa ndi chisangalalo chimenechi chimachita mbali ina m’kuthandiza mwamuna ndi mkazi kukhala odzipereka kwa wina ndi mnzake kwa zaka zambiri za ukwati. Komabe, anthu oŵerengeka angakane kuti dziko lerolino laika chigogomezero chopambanitsa pakugonana, likumasonyeza chisiriro chimene Paulo ananena kukhala chovomerezeka. Lingaliro lolakwa limenelo la chisangalalo cha kugonana limatengeredwa mosavuta makamaka ndi awo amene amadziika pamkhalidwe wa chisembwere ndi umaliseche wosonyezedwa mofala lerolino mu akanema ambiri, mavidiyo, ndi magazini, limodzinso ndi malo a zosangulutsa.

20. Kodi Akristu angasonyeze motani kukhala maso kuupandu wa kusirira pankhani ya kugonana?

20 Nkhani ya tchimo la Davide ndi Batiseba imasonyeza kuti mmodzi wa atumiki a Mulungu angagwidwe ndi msampha wa chisiriro cha kugonana. Ngakhale kuti anali waufulu kusangalala mkati mwa ukwati wake, Davide analola chikhumbo choipa cha kugonana kukula. Powona mmene mkazi wa Uriya analiri wokongola, iye sanaletse malingaliro ake​—ndi zochita zake​—kulinga ku kupeza chisangalalo choipa ndi mkaziyo. (2 Samueli 11:2-4; Yakobo 1:14, 15) Ndithudi tiyenera kupeŵa mtundu umenewu wa chisiriro. Ngakhale mkati mwa ukwati nkoyenera kupeŵa kusirira. Zimenezi zikaphatikizapo kukana machitachita akugonana opambanitsa. Mwamuna wotsimikiza mtima kupeŵa chisiriro m’mbali imeneyi akakhala wokondwera kwenikweni ndi mkazi wake, kotero kuti chosankha chilichonse chimene aŵiriwo akapanga cha kulinganiza banja sichikaika chisangalalo chake kukhala chofunika kwambiri kuposa thanzi la mkazi wake la panthaŵiyo kapena mtsogolo.​—Afilipi 2:4.

Pitirizani Kukhalabe Otsimikiza Kupeŵa Kusirira

21. Kodi nchifukwa ninji kukambitsirana kwathu za kusirira sikuyenera kutilefula?

21 Sikuti Yehova samatikhulupirira pamene apereka machenjezo. Iye amadziŵa kuti atumiki ake odzipereka amafuna kumtumikira mokhulupirika, ndipo ali ndi chidaliro chakuti ambiri adzapitirizabe kuchita zimenezo. Ponena za anthu ake onse pamodzi, iye akhoza kunena zofanana ndi zimene ananena pankhani ya Yobu pamene anali kulankhula ndi Satana kuti: “Kodi wawonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.” (Yobu 1:8) Atate wathu wakumwamba wachikondi, wokhulupirira amatichenjeza za misampha yowopsa, yonga ija yogwirizana ndi mipangidwe ya kusirira, chifukwa chakuti amafuna kuti tipitirize kukhala osadetsedwa ndi okhulupirika kwa iye.

22. Kodi tiyenera kuchitanji ngati phunziro lathuli lavumbula mbali imene ifeyo patokha tili paupandu kapena tili ofooka?

22 Aliyense wa ife ali ndi choloŵa cha chikhoterero chinachake kulinga ku kusirira, ndipo tingakhale titakulitsa chikhoterero chimenecho pansi pa chisonkhezero cha dziko loipali. Bwanji ngati pamene tikuphunzira za kusirira kumeneku​—ponena za chuma, katundu, mphamvu ndi ulamuliro, chakudya, kapena chisangalalo cha kugonana​—mwawona chifooko chinachake? Pamenepo labadirani uphungu wa Yesu wakuti: “Ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kuloŵa m’moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako aŵiri ndi kuloŵa m’gehena.” (Marko 9:43) Pangani kusintha kulikonse kumene kukufunikira m’mkhalidwe wamaganizo kapena zikondwerero. Peŵani msampha wakupha wa kusirira. Motero ndi chithandizo cha Mulungu, mungathe “kuloŵa m’moyo.”

Kodi Ndaphunzira Chiyani?

◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulingalira mosamalitsa za msampha wa kusirira?

◻ Kodi ndimwanjira zotani zimene kusirira chuma kapena katundu kungatitcherere msampha?

◻ Kodi ndimotani mmene kusirira m’mbali zina za moyo kungakhalire upandu weniweni?

◻ Kodi mkhalidwe wathu wamaganizo uyenera kukhala wotani kulinga ku kufooka kulikonse kumene tingakhale nako pankhani ya kusirira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena