-
Mfumu Inayenga Anthu Ake MwauzimuUfumu wa Mulungu Ukulamulira
-
-
1-3. Kodi Yesu anatani atapeza anthu akudetsa kachisi?
YESU ankalemekeza kwambiri kachisi wa ku Yerusalemu chifukwa ankadziwa kuti kachisiyo ankaimira kulambira koona padziko lapansi. Komatu kulambira kumeneku kuyenera kukhala koyera chifukwa Mulungu amene timamulambira ndi woyera. Ndiyeno taganizirani mmene Yesu anamvera pa Nisani 10, mu 33 C.E., atafika kukachisi n’kupeza anthu akuchita zinthu zodetsa kachisi. Kodi ankamudetsa bwanji?—Werengani Mateyu 21:12, 13.
2 Yesu atafika m’bwalo la anthu a mitundu ina anapeza amalonda amene ankachita zinthu mwadyera komanso osintha ndalama akubera anthu amene ankabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova.a Yesu ‘anathamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama.’ (Yerekezani ndi Nehemiya 13:7-9.) Kenako anawadzudzula chifukwa chosandutsa nyumba ya Atate ake kukhala “phanga la achifwamba.” Pochita zimenezi Yesu anasonyeza kuti ankalemekeza kwambiri kachisi chifukwa ankadziwa kuti ankaimira kulambira koona. Anaonetsetsa kuti malo amene anthu amalambirirapo Atate ake azikhala oyera.
-
-
Mfumu Inayenga Anthu Ake MwauzimuUfumu wa Mulungu Ukulamulira
-
-
a Ayuda ochokera m’madera ena ankafunika kugwiritsa ntchito ndalama zovomerezeka popereka msonkho wapachaka wapakachisi ndipo anthu osintha ndalama ankawalipiritsa akafuna kusintha ndalama zawo kuti apeze ndalama zovomerezekazo. Anthu a m’madera enawa ankafunikanso kugula nyama zoti apereke nsembe. Yesu anatchula amalondawa kuti ndi “achifwamba,” ndipo n’kutheka kuti anawatchula choncho chifukwa choti ankalipiritsa anthu mitengo yokwera kwambiri.
-