-
Kodi Mukudziwa?Nsanja ya Olonda—2011 | October 1
-
-
▪ Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anathetsa zinthu zopanda chilungamo zimene zinkachitika m’kachisi. Baibulo limati: ‘Yesu anathamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda. Iye anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,’ koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”’—Mateyu 21:12, 13.
-
-
Kodi Mukudziwa?Nsanja ya Olonda—2011 | October 1
-
-
Popeza Yesu anadzudzula osintha ndalamawa kuti anasandutsa kachisi kukhala “phanga la achifwamba,” ndiye kuti iwo ankabera anthu powalipiritsa ndalama zambiri akafuna kusinthitsa ndalama zawo.
-