Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 1/1 tsamba 24-26
  • “M’kamwa mwa Makanda”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “M’kamwa mwa Makanda”
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Mayendedwe Abwino Amachitira Umboni
  • Mboni Zachichepere Zogwira Mtima
  • Kulimba Mtima kwa Achichepere Kumapereka Umboni Wabwino Kwambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 1/1 tsamba 24-26

“M’kamwa mwa Makanda”

PAMENE Samueli anali mwana, anachirimika pa malamulo amkhalidwe abwino mosasamala kanthu za kuipa kwa ana aamuna a Mkulu wa Ansembe Eli. (1 Samueli 2:22; 3:1) M’masiku a Elisa, wotengeredwa ku ukapolo wina wamng’ono Wachiisrayeli ku Aramu anapereka umboni molimba mtima kwa mbuyake wamkazi. (2 Mafumu 5:2-4) Pamene Yesu anali ndi zaka 12, analankhula molimba mtima ndi aphunzitsi a Israyeli, akumafunsa mafunso ndi kupereka mayankho amene anadabwitsa omvetsera. (Luka 2:46-48) Mu mbiri yonse Yehova watumikiridwa mokhulupirika ndi olambira ake achichepere.

Kodi lerolino achichepere akusonyeza mzimu wokhulupirika umodzimodziwo? Inde, ndithudi! Malipoti a ku maofesi a nthambi a Watch Tower Society akusonyeza kuti achichepere okhulupirika ambirimbiri ‘akudzipereka eni ake’ mu utumiki wa Yehova. (Salmo 110:3) Zotulukapo zabwino za zoyesayesa zawo zimalimbikitsa Akristu onse, achichepere ndi achikulire, ‘kusalema pakuchita zabwino.’​—Agalatiya 6:9.

Chitsanzo chabwino ndicho cha Ayumi, kamsungwana ka ku Japan kamene kanakhala wofalitsa pamene kanali ndi zaka zisanu ndi chimodzi ndi kupanga chonulirapo chake cha kuchitira umboni kwa aliyense m’kalasi mwake. Anapeza chilolezo cha kuika zofalitsidwa zingapo mu laibulale ya m’kalasiyo, akumakonzekera kuyankha mafunso alionse amene apasukulu anzake angafunse. Pafupifupi a m’kalasi anzake onse ndiponso mphunzitsi anafikira pa kudziŵa za zofalitsidwazo. Mkati mwa zaka zisanu ndi chimodzi za kuimba kwake sukulu ya pulaimale, Ayumi anachititsa maphunziro a Baibulo 13. Iye anabatizidwa pamene anali mu kalasi lachinayi, ndipo mmodzi wa mabwenzi ake amene anali kuphunzira naye anabatizidwa mu kalasi lachisanu ndi chimodzi. Ndiponso, amake ndi akulu ake aŵiri a wophunzira Baibulo ameneyu nawonso anaphunzira ndipo anabatizidwa.

Mayendedwe Abwino Amachitira Umboni

“Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma,” anatero mtumwi Petro, ndipo Akristu achichepere amaona lamulo limeneli mwamphamvu. (1 Petro 2:12) Monga chotulukapo chake, kaŵirikaŵiri mayendedwe awo okoma amapereka umboni wabwino. M’dziko la mu Afirika la Cameroon, mwamuna wina anafika pamsonkhano wampingo wa Mboni za Yehova kwanthaŵi yachiŵiri ndipo anakhala pafupi ndi kamsungwana kena. Pamene wokamba nkhani anapempha omvetsera kuŵerenga vesi m’Baibulo, mwamunayo anaona kuti kamsungwanako kanali kufulumira kupeza vesilo m’Baibulo lake ndi kutsatira mosamalitsa kuŵerengako. Mkhalidwe wake unamchititsa chidwi kwambiri kwakuti pamapeto a msonkhanowo, anamka kwa wokamba nkhaniyo ndi kunena kuti: “Kamsungwana aka kandipangitsa kufuna kuphunzira nanu Baibulo.”

Mu South Africa muli sukulu ina kumene ophunzira 25 ali ana a Mboni za Yehova. Mayendedwe awo abwino adzetsa mbiri yabwino kwa Mboni za Yehova. Mphunzitsi wina anaululira kholo lina la Mboni kuti sanadziŵe bwino kwambiri za mmene Mboni zimaphunzitsira ana awo bwino chotero, makamaka popeza kuti tchalitchi chake chakhala chosakhoza kuthandiza achichepere. Mphunzitsi wina watsopano anafika kudzathandiza pasukulupo ndipo mofulumira anaona khalidwe labwino la ana a Mboni. Mkaziyo anafunsa mmodzi wa anyamata a Mboniwo chimene anayenera kuchita kuti akhale mmodzi wa Mboni za Yehova. Mnyamatayo anafotokoza kuti anayenera kukhala ndi phunziro la Baibulo, nalinganiza kuti makolo ake afikire wokondwererayo.

Ku Costa Rica, Rigoberto anazindikira choonadi pamene a m’kalasi anzake aŵiri anagwiritsira ntchito Baibulo kuyankhira mafunso ake onena za Utatu, moyo, ndi moto wa helo. Zimene ananena zinali zanzeru kwa iye osati kokha chifukwa cha luso lawo pa kugwiritsira ntchito Malemba komanso chifukwa chakuti mayendedwe awo abwino kwambiri anali osiyana kwambiri ndi zimene anaona m’matchalitchi a Dziko Lachikristu. Mosasamala kanthu za chitsutso cha m’banja, Rigoberto akupita bwino lomwe patsogolo m’phunziro lake la Baibulo.

Ku Spain Mboni za Yehova ziŵiri​—imodzi ya zaka zisanu ndi zinayi​—zinafikira mwamuna wina wotchedwa Onofre. Pamene kuli kwakuti Mboni yokulirapoyo ndiyo inali kulankhula kwambiri, Mboni yocheperapoyo inali kutsatira poŵerenga Malemba ndipo inagwira mawu mavesi ena a Baibulo pamtima. Onofre anachita chidwi. Iye anati anafuna kuphunzira Baibulo kumalo amodzimodziwo kumene kamnyamatako kanaphunzirako mmene kangasanthulire Malemba bwino chotero. Chotero, mmamaŵa pa Lamulungu lotsatira, iye anapita ku Nyumba Yaufumu. Anayembekezera kunja kufikira dzuŵa lili pamutu, pamene Mboni zinafika kudzaloŵa misonkhano yawo. Kuyambira pamenepo, iye anapita bwino patsogolo ndipo posachedwa wasonyeza kudzipatulira kwake ndi ubatizo wa m’madzi.

Mboni Zachichepere Zogwira Mtima

Inde, Yehova amagwiritsira ntchito achichepere ndiponso achikulire kufikira anthu ofatsa. Zimenezo zinaonedwa m’chochitika cha ku Hungary. Kumeneko, nesi wina wa pachipatala anaona kuti panthaŵi iliyonse pamene odzazonda wodwala wina wa zaka khumi anafika, ankambweretsera zoŵerenga ndiponso chakudya. Atachita chidwi, anadabwa ponena za zimene kamsungwanako kanali kuŵerenga napeza kuti linali Baibulo. Nesiyo analankhula naye ndipo pambuyo pake anati: “Kuyambira pachiyambi, iye anali kundiphunzitsadi.” Pamene kamsungwanako kanatuluka m’chipatala, iko kanaitanira nesiyo kumsonkhano wachigawo, komano nesiyo anakana pempho lake. Komabe, iye pambuyo pake, anavomera kukafika pa Msonkhano Wachigawo wa “Chinenero Choyera.” Posapita nthaŵi, anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo chaka chimodzi pambuyo pake iye anabatizidwa​—zonsezo monga chotulukapo cha kamsungwana kogwiritsira ntchito nthaŵi yake m’chipatala kuŵerenga mabuku ofotokoza Baibulo.

Ana Ruth, ku El Salvador, anali m’chaka chake chachiŵiri cha sukulu ya sekondale. Anali ndi chizoloŵezi cha kusiya mabuku ofotokoza Baibulo padesiki lake kuti ena aŵerenge ngati anafuna kutero. Ataona mmene mabukuwo anazimiririkira ndi kuonekeranso patapita nthaŵi, Ana Ruth anatulukira kuti wa pasukulu mnzake wina, Evelyn, anali kuwaŵerenga. Patapita kanthaŵi, Evelyn anavomera kukhala ndi phunziro nayamba kufika pamisonkhano ya mpingo. Potsirizira pake, anabatizidwa, ndipo tsopano akutumikira monga mpainiya wothandiza wokhazikika. Ana Ruth ndi mpainiya wokhazikika.

Ku Panama mlongo wina anayamba kuphunzira ndi mkazi wina amene mwamuna wake anayamba kutsutsa choonadi kufikira pamene kuphunzirako kunatsala pang’ono kuimitsidwa. Komabe, pang’ono ndi pang’ono mkhalidwe wamaganizo wa mwamunayo unayamba kufeŵa. Nthaŵi ina pambuyo pake, mkulu wake, Mboni, anampempha kukaika belu la mbala m’nyumba mwake. Pamene anali kuika belulo, mwana wamkazi wa mkulu wake wa zaka zisanu ndi zinayi anafika panyumba ali wosakondwa. Anamfunsa chimene chinachitika, ndipo anati iyeyo ndi mkulu wake anapita kukachititsa phunziro la Baibulo koma munthu wake panalibe panyumba, chotero anali wosakhoza kuchitira Yehova kanthu kalikonse tsiku limenelo. Atate ake aang’onowo anati: “Bwanji osangondilalikira ineyo? Pamenepo udzachitira Yehova kanthu kena.” Mwana wa mkulu wakeyo anathamanga mokondwa kukatenga Baibulo lake, ndipo phunziro linayambidwa.

Amake (mlamu wake wa mwamunayo) anali kumvetsera. Iwo analingalira kuti zonsezo zinangokhala njerengo, komano nthaŵi iliyonse imene mwamunayo anafika panyumbapo, anapempha mwana wa mkulu wakeyo kuphunzira naye Baibulo. Pamene amakewo anaona kuti mlamu wawoyo anali wotsimikiza ndi kuti anali ndi mafunso ena ovuta, iwo anasankha kuchititsa phunzirolo pamodzi ndi mwana wawo wamkaziyo. Iye anayamba kuphunzira kaŵiri pamlungu napita patsogolo mofulumira. Potsirizira pake, anafikiradi pakudzipatulira ndipo anabatizidwa pamsonkhano umodzimodziwo umene mkazi wake anabatizidwapo​—chifukwa cha mkhalidwe wabwino wamaganizo wa mwana wa mkulu wake.

Kulimba Mtima kwa Achichepere Kumapereka Umboni Wabwino Kwambiri

Baibulo limati: “Limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.” (Salmo 27:14) Mawu ameneŵa amagwira ntchito kwa atumiki onse a Mulungu, ndipo achichepere ndiponso achikulire anawagwiritsira ntchito mkati mwa chaka chatha. Ku Australia, pamene msungwana wina wa zaka zisanu anayamba kupita kusukulu yatsopano, amake anamka kwa mphunzitsi wake kukalongosola za chikhulupiriro cha Mboni za Yehova. Mphunzitsiyo anati: “Ndadziŵa kale zimene mumakhulupirira. Mwana wanu wamkazi wandilongosolera zonse.” Kamsungwana kameneka sikanali kamantha kufikira mphunzitsi wake kali kokha kuti kamlongosolere za chikhulupiriro chake.

Andrea wa zaka zisanu wa ku Romania nayenso anasonyeza kulimba mtima. Pamene amake anachoka m’chipembedzo cha Orthodox ndi kukhala Mboni, anansi awo anakana kuwamvetsera. Tsiku lina pa Phunziro Labuku Lampingo, Andrea anamva woyang’anira utumiki akumagogomezera kufunika kwa kulalikira kwa anansi a munthuwe. Analingalira mwamphamvu za zimenezi, ndipo atabwerera kwawo anati kwa amake: “Mutapita kuntchito, ndidzadzuka, kuika mabuku m’chikwama changa monga momwe mumachitira muja Mayi, ndipo ndidzapemphera kwa Yehova kuti andithandize kukalankhula za choonadi ndi anansi.”

Tsiku lotsatira Andrea anachita monga momwe analonjezera. Ndiyeno, molimba mtima, analiza belu la mnansi wina. Pamene mnansiyo anayankha pakhomo, kamsungwana kameneka kanati: “Ndikudziŵa kuti chiyambire pamene amayi anakhala Mboni, simumawakonda. Iwo ayesa kulankhula nanu kangapo, komano simunafune kuwamvetsera. Zimenezi zimawakwiyitsa, koma ndikufuna kuti mudziŵe kuti timakukondani.” Ndiyeno, Andrea anapitiriza kupereka umboni wabwino kwambiri. Patsiku limodzi, anagaŵira mabuku asanu ndi limodzi, magazini asanu ndi amodzi, timabuku tinayi, ndi matrakiti anayi. Kuyambira pamenepo, wakhala akupita muutumiki wakumunda nthaŵi zonse.

Ku Rwanda abale athu akhala akusonyeza kulimba mtima kwakukulu ponena za nkhondo kumeneko. Panthaŵi ina banja lina la Mboni linaikidwa m’chipinda mmene asilikali anakonzekera kuwapha. Banjalo linapempha chilolezo cha kupemphera choyamba. Pempholo linavomerezedwa, ndipo onsewo anapempherera mu mtima, kusiyapo kamwana kakakazi, kotchedwa Deborah. Deborah anapemphera mofuula: “Yehova, mlungu uno ine ndi Atate tagaŵira magazini asanu. Kodi tipitanso bwanji kwa anthu amenewo kuti tikawaphunzitse choonadi ndi kuwathandiza kupeza moyo? Ndiponso, ndidzakhala wofalitsa motani tsopano? Ndikufuna kubatizidwa kuti ndikutumikireni.” Atamva zimenezi, msilikali wina anati: “Sitingakupheni chifukwa cha kamsungwana aka.” Deborah anayankha kuti: “Zikomo.” Banjalo linapulumuka.

Pamene Yesu analoŵa mwachipambano mu Yerusalemu ali pafupi ndi mapeto a moyo wake wa padziko lapansi, analonjeredwa ndi makamu aakulu ofuula mokondwera. Makamuwo anapangidwa ndi ana ndiponso anthu achikulire. Malinga ndi cholembedwacho, ana ‘analinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide!’ Pamene ansembe aakulu ndi alembi anatsutsa zimenezi, Yesu anayankha kuti: “Simunaŵerenga kodi, M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?”​—Mateyu 21:15, 16.

Kodi sikokondweretsa kuona kuti ngakhale lerolino mawu a Yesuwo ngoona? “M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa”​—ndipo, tingawonjezere kuti, mwa achichepere ndi anyamata ndi asungwana osinkhukirapo​—mwatamanda Yehova. Indedi, ponena za nkhani ya kutamanda Yehova, palibe msinkhu wofunika.​—Yoweli 2:28, 29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena