Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuyambika kwa Tsiku Lowopsya
PAMENE Yesu achoka m’Yerusalemu pa Lolemba madzulo, akubwerera ku Betaniya yokhala pa malo otsetsereka a mbali ya kum’mawa ya Phiri la Azitona. Iye wamaliza masiku aŵiri a uminisitala wake womalizira m’Yerusalemu. Yesu mosakaikira akuthanso usiku ndi bwenzi lake Lazaro. Chifikire kuchokera ku Yeriko pa Lachisanu, uwu wakhala usiku wake wachinayi m’Betaniya.
Tsopano, m’mamawa pa Lachiŵiri, Nisani 11, iye ndi ophunzira ake alinso paulendo. Limeneli likutsimikizira kukhala tsiku lowopsya la uminisitala wa Yesu, lotanganitsa koposa. Liri tsiku lake lomalizira kuwonekera m’kachisi. Ndipo liri tsiku lomalizira la uminisitala wake wapoyera asanazengedwe mlandu ndi kuphedwa.
Iwo akupita njira imodzimodziyo yodzera pa Phiri la Azitona kulinga ku Yerusalemu. Panjirapo kuchokera ku Betaniya, Petro akuzindikira mtengo umene Yesu anatemberera dzulo m’mamawa. “Rabi, onani” iye akufuula tero, “wafota mkuyuwo munautemberera.”
Koma kodi nchifukwa ninji Yesu anapha mtengowo? Iye akusonyeza chifukwa chake pamene akupitiriza kunena kuti: “Indedi ndinena kwa inu, ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakaikakaika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale ku phiri ili [pa Phiri la Azitona pamene aimirira], tanyamulidwa, nuponyedwe m’nyanja, chidzachitidwa. Ndipo zinthu zirizonse mukazifunsa m’kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.”
Chotero mwakuchititsa mtengowo kufota, Yesu akupereka phunziro lowoneka kwa ophunzira ake pa kufunika kwawo kwa kukhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. Monga mmene akulongosolera kuti: “Zinthu zirizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.” Ndi phunziro lofunika chotani nanga kwa iwo kuliphunzira, makamaka polingalira za ziyeso zochititsa mantha zimene zayandikira kufika! Komabe, pali kugwirizana kwinanso pakati pa kufota kwa mkuyuwo ndi mtundu wa chikhulupiriro.
Mtundu wa Israyeli, mofanana ndi mkuyuwu, uli ndi mawonekedwe achinyengo. Ngakhale kuti mtunduwo uli mu unansi wapangano ndi Mulungu ndipo mwakunja ungawoneke kukhala ukusunga malamulo ake, iwo watsimikizira kukhala wopanda chikhulupiriro, wosabala zipatso zabwino. Chifukwa chopanda chikhulupiriro, iwo ulidi panjira yokana Mwana wake wa Mulungu! Chotero, mwakuchititsa mkuyu wosabalawo kufota, Yesu akuchitira fanizo mowonekera chimene chidzakhala mapeto otulukapo a mtundu umenewu wosabala, wopanda chikhulupiriro.
Panthaŵi yochepa, Yesu ndi ophunzira ake akuloŵa m’Yerusalemu, ndipo monga mwa chizoloŵezi chawo, iwo apita ku kachisi, kumene Yesu ayamba kuphunzitsa. Ansembe akulu ndi akulu a anthu, mosakaikira posunga m’maganizo kachitidwe ka Yesu tsiku lapita motsutsana ndi osintha ndalama, akumtokosa iye mwakumati: “Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?”
Poyankha Yesu akuti: “Inenso ndikufunsani mawu amodzi, amene ngati mundiwuza, inenso ndikuwuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi: Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu?”
Ansembewo ndi akulu a anthu ayamba kufunsana kuti adzayankha motani. “Tikati, kumwamba, iye adzati kwa ife, munalekeranji kumvera iye? Koma tikati, kwa anthu, tiwopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.”
Atsogoleriwo sakudziŵa choyankha. Chotero akumuwuza Yesu kuti: “Sitidziŵa ife.”
Yesu nayenso, akuti: “Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.” Mateyu 21:19-27; Marko 11:19-33; Luka 20:1-8.
◆ Kodi Lachiŵiri, Nisani 11, liri ndi chiyani?
◆ Kodi ndi maphunziro otani amene Yesu akupereka pamene achititsa mkuyu kufota?
◆ Kodi ndimotani mmene Yesu akuyankhira awo omufunsa za ulamuliro umene iye achitira zinthu?