-
Kodi Ayuda Ndiwo Anthu Osankhidwa a Mulungu?Galamukani!—1990 | July 8
-
-
Kodi Yehova akapitirizabe kuwona Ayuda kukhala anthu ake osankhidwa? Pozindikira kuti ambiri anapatuka ku kulambira kwabwino kwa Yehova, Yesu anati: ‘Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.’ (Mateyu 21:43) Polephera kulabadira chenjezo limenelo, ambiri anapitiriza kupatuka ndi kukana Yesu monga wodzozedwa wa Yehova. Chifukwa chake, sipanapite nthaŵi yaitali kuti Mulungu alole kachisi womangidwansoyo kuwonongedwa mu 70 C.E. (Mateyu 23:37, 38) Kodi ichi chinatanthauza kuti Mulungu tsopano anali kukana Ayuda onse?
-
-
Kodi Ayuda Ndiwo Anthu Osankhidwa a Mulungu?Galamukani!—1990 | July 8
-
-
Motero, onse aŵiri Ayuda ndi osakhala Ayuda akanakhala anthu osankhidwa a Mulungu, ndi chiyembekezo cha kutumikira monga ansembe m’malo mwa mtundu wonse wa anthu. Polankhula za alambiri okhulupirika a chiyambi cha mtundu wosiyana, mtumwi Wachikristu Petro, Myuda wachibadwa, analemba kuti: ‘Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, . . . inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu.’ (1 Petro 2:9, 10) Umenewu ndiwo “mtundu,” anthu okhala ndi mikhalidwe yaumulungu, umene Yesu anati ukabala ‘zipatso za ufumu wa Mulungu’ ndi umene ukasangalala ndi unansi wapadera ndi Yehova.—Mateyu 21:43.
-