Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 1/15 tsamba 8-9
  • Fanizo la Phwando la Ukwati

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Fanizo la Phwando la Ukwati
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Fanizo la Phwando Laukwati
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la Ukwati
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Asangalatsidwa ndi Mfarisi Wotchuka
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kucherezedwa ndi Mfarisi
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 1/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Fanizo la Phwando la Ukwati

MOGWIRITSIRA ntchito mafanizo aŵiri, Yesu wavumbula alembi ndi akulu ansembe, ndipo iwo akufuna kumupha. Koma Yesu adakali kutali ndi kumaliza nawo. Iye akupitirizabe kuwawuza fanizo linanso, akumati:

“Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wake phwando la ukwati, natumiza akapolo ake kukaitana oitanidwa ku ukwati umene; ndipo iwo sanafuna kudza.”

Yehova Mulungu ndiye Mfumuyo imene ikukonza phwando laukwati kaamba ka Mwana wake, Yesu Kristu. M’kupita kwa nthaŵi, mkwatibwi wake wa atsatiri odzozedwa a 144,000 adzagwirizana naye kumwamba. Nzika za Mfumuyo ali Aisrayeli, amene, pobweretsedwa m’pangano la Chilamulo mu 1513 B.C.E., analandira mwaŵi wa kukhala “ufumu wa ansembe.” Chotero, pa chochitika chimenecho, iwo anakhala oyamba kuitanidwa ku phwando la ukwati.

Komabe, chiitano choyamba kwa oitanidwawo sichinaperekedwe kufikira mu ngululu ya 29 C.E., pamene Yesu ndi ophunzira ake (akapolo a mfumuyo) anayamba ntchito yawo ya kulalikira Ufumu. Koma Aisrayeli akuthupi amene analandira chiitanochi choperekedwa ndi akapolowo kuyambira 29 C.E. mpaka 33 C.E. sanafune kubwera. Chotero Mulungu anapatsa mtundu wa oitanidwawo mwaŵi wina, monga mmene Yesu akulongosolera kuti:

“Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, uzani oitanidwawo, onani, ndakonza phwando langa; ng’ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsya: Idzani ku ukwati.” Chiitano chachiŵiri ndi chomalizira chimenechi cha oitanidwawo chinayamba pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene mzimu woyera unatsanuriridwa pa atsatiri a Yesu. Chiitanochi chinapitirizabe mpaka 36 C.E.

Komabe, unyinji wokulira wa Aisrayeliwo, nawonso anakana chiitanochi. “Ananyalanyaza, nachoka,” Yesu akulongosola kuti, “wina ku munda wake, wina ku malonda ake: ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha.” “Koma,” Yesu akupitiriza tero, “mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wawo.” Izi zinachitika mu 70 C.E., pamene Yerusalemu anapasulidwa mpaka pansi ndi Aroma, ndipo akuphawo anaphedwa.

Yesu kenaka akulongosola chomwe chinachitika m’nthaŵiyo: “Pomwepo [mfumuyo] inanena kwa akapolo ake, za ukwati tsopano zapsya, koma oitanidwawo sanayenera. Chifukwa chake pitani inu ku mphambano za njira, ndipo amene aliyense mukampeze, itanani ku ukwatiku.” Akapolowo anachita zimenezi, ndipo “ukwatiwo unadzala ndi okhala pa chakudya.”

Ntchito imeneyi ya kusonkhanitsa alendo oitanidwawo kuchokera pa mphambano za njira kunja kwa mzinda inayamba mu 36 C.E. Mdindo wankhondo wa ku Roma Korneliyo ndi banja lake anali oyamba a osakhala Ayuda ndi osadulidwa amene anasonkhanitsidwa. Kusonkhanitsidwa kwa osakhala Ayuda amenewa, onse amene ali otenga malo a aja omwe anakana chiitano poyambapo, kwapitirizabe kufikira zaka za zana la 20 zino.

Ndi mkati mwa zaka za zana la 20 mmene chipinda cha phwando la ukwati chidzazidwa. Yesu akusimba chimene tsopano chikuchitika, akumati: “Koma mfumuyo mmene inadza kuwawona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosavala chovala cha ukwati; nanena kwa iye, mnzangawe, unaloŵa muno bwanji wosakhala nacho chovala cha ukwati? Ndipo iye analibe mawu. Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, mumange iye manja ndi miyendo, mumponye ku mdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.”

Mwamunayo wopanda chovala chaukwati akuchitira chithunzi odzitcha kukhala Akristu a Dziko Lachikristu. Mulungu sanawazindikirepo amenewa kukhala ali ndi chizindikiritso choyenera kukhala Aisrayeli auzimu. Mulungu sanawadzoze konse ndi mzimu kukhala oloŵa nyumba a Ufumu. Chotero iwo adzaponyedwa kunja ku mdima kumene adzawonongedwa.

Yesu akumaliza fanizo lake mwa kunena kuti: “Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo oŵerengeka.” Inde, panali ambiri oitanidwa kuchokera mu mtundu wa Israyeli kukhala ziŵalo za mkwatibwi wa Kristu, koma anali Aisrayeli akuthupi oŵerengeka okha amene anasankhidwa. Unyinji wa alendo a 144,000 omwe akulandira mphotho yakumwamba siali aisrayeli akuthupi. Mateyu 22:1-14; Eksodo 19:1-6; Chibvumbulutso 14:1-3.

◆ Kodi ndi ayani oitanidwa poyambirirawo ku phwando la ukwati, ndipo n’liti pamene iwo akupatsidwa chiitanocho?

◆ Kodi n’liti pamene chiitanocho chikuperekedwa kwa nthaŵi yoyamba kwa oitanidwawo, ndipo ndani omwe ali akapolo ogwiritsiridwa ntchito kuchipereka icho?

◆ Kodi n’liti pamene chiitano chachiŵiri chikuperekedwa, ndipo kodi ndani amene akuitanidwa pambuyo pake?

◆ Kodi ndani omwe akuchitiridwa chithunzi ndi mwamunayo wopanda chovala chaukwati?

◆ Kodi ndani omwe ali oitanidwa ambiriwo, ndi osankhidwa oŵerengekawo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena