Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 2/1 tsamba 8-9
  • Alephera Kumkola Yesu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Alephera Kumkola Yesu
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Alephera Kukola Yesu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yesu Analepheretsa Afarisi Kuti Amugwire
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • “Yang’anirani Mupeŵe Chotupitsa Mkate cha Afarisi ndi Asaduki”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • “Phunzirani kwa Ine”
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 2/1 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Alephera Kumkola Yesu

YESU wakhala akuphunzitsa m’kachisi, ndipo wangowauza kumene adani ake achipembedzo mafanizo atatu ovumbula kuipa kwawo. Afarisiwo akwiyitsidwa ndipo apangana za kumkola iye kuti anene chinachake chimene adzamgwirirapo. Iwo akonza chiwembu ndi kutumiza ophunzira awo, limodzi ndi otsatira achipani cha Herode, kukayesa kumtchera iye.

“Mphunzitsi,” amunaŵa akutero, “tidziŵa kuti muli wowona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu mowona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang’anira pa nkhope ya anthu. Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai?”

Yesu sakupusitsidwa ndi kusyasyalika kwawoko. Iye akuzindikira kuti ngati anena kuti, ‘Ayi, sikololedwa kapena sikolondola kupereka msonkho umenewu,’ adzakhala waliŵongo la kupandukira Roma. Komabe, ngati anena kuti, ‘Inde, muyenera kupereka msonkhowu,’ Ayuda, amene amanyazitsa kugonjera kotereku ku Roma, adzamuda. Chotero iye akuyankha kuti: “Mundiyeseranji ine, onyenga inu? Tandiwonetsani ine ndalama yamsonkho.”

Pamene abweretsa ndalamayo kwa iye, iye akufunsa kuti: “Ncha yani chithunzithunzi ichi, ndi kulemba kwake?”

“Cha Kaisara,” iwo akuyankha tero.

“Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”

Pamene amuna ameneŵa amva yankho laukatswiri limeneli, azizwa. Ndipo achoka namusiya yekha.

Powona kulephera kwa Afarisi kupeza chinachake chotsutsana ndi Yesu, Asaduki, amene amanena kuti kulibe chiukiriro, akumfikira ndi kufunsa kuti: “Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbewu. Tsono panali ndi ife abale asanu ndi aŵiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbewu, nasiyira mphwake mkazi wake; chimodzimodzi wachiŵiri, ndi wachitatu, kufikira wachisanu ndi chiŵiri. Ndipo pomalizira anamwaliranso mkaziyo. Chifukwa chake m’kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi aŵiriwo? Pakuti onse anakhala naye.”

Poyankha Yesu akuti: “Simusochera nanga mwa ichi, popeza mulibe kudziŵa malembo, kapena mphamvu yake ya Mulungu? Pakuti pamene adzauka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa; koma akhala ngati angelo a kumwamba. Koma za akufa, kuti akaukitsidwa; simunaŵerenga m’kalata wa Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo? Sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: musochera inu ndithu.”

Kachiŵirinso makamuwo azizwa ndi yankho la Yesu. Ndipodi ena a alembi akuvomereza kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino.”

Pamene Afarisi awona kuti Yesu wakhalitsa chete Asaduki, iwo akudza kwa iye m’gulu limodzi. Kuti amuyese iye mowonjezereka, mmodzi wa iwo akufunsa kuti: “Mphunzitsi, lamulo lalikulu ndi liti la m’chilamulo?”

Yesu akuyankha kuti: “La mtsogolo ndili, Mvera, Israyeli; [Yehova] Mulungu wathu, [Yehova] ndiye mmodzi; ndipo udzikonda [Yehova] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse. Lachiŵiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.” Kwenikwenidi, Yesu akuwonjezera kuti: “Pa malamulo awa aŵiri mpokolowekapo chilamulo chonse ndi aneneri.”

“Mphunzitsi, mwanena zowona,” akuvomereza tero mlembi. “Kuti ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye; ndipo, kumkonda Iye, ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzake monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsyereza zamphumphu zonse.”

Powona kuti mlembiyo wayankha mwanzeru, Yesu akumuuza kuti: “Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.”

Kwa masiku atatu tsopano​—Sande, Lolemba, ndi Lachiŵiri​—Yesu wakhala akuphunzitsa m’kachisi. Anthu amvetsera kwa iye ndi chisangalalo, komabe atsogoleri achipembedzo okhumudwitsidwawo akufuna kumupha iye. Mateyu 22:15-40; Marko 12:13-34; Luka 20:20-40.

◆ Kodi ndi chiwembu chotani chimene Afarisi akupanga kuti amkole Yesu, ndipo kodi chingatulukepo nchiyani ngati angapereke yankho la inde kapena ayi?

◆ Kodi ndimotani mmene Yesu akuthetseranso zoyesayesa za Asaduki za kumkolera iye?

◆ Kodi ndi zoyesayesa zowonjezereka zotani zimene Afarisi akupanga za kuyesa Yesu, ndipo kodi chotulukapo nchotani?

◆ Mkati mwa uminisitala wake womalizira m’Yerusalemu, kodi ndi masiku angati amene Yesu akuphunzitsa m’kachisi, ndipo ndi chotulukapo chotani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena