Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulira Panopa
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 2. Kodi kuchokera mu 1914, ndi zinthu ziti zomwe zakhala zikuchitika padzikoli, nanga anthu akhala akusonyeza makhalidwe otani?

      Ophunzira a Yesu anafunsa kuti: “Kodi . . . chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mateyu 24:3) Poyankha, Yesu anawafotokozera zinthu zambiri zimene zidzachitike iye akadzayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba. Zina mwa zinthu zimenezi ndi monga nkhondo, njala komanso zivomezi. (Werengani Mateyu 24:7.) Baibulo linaloseranso kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu adzakhala ndi makhalidwe oipa omwe adzachititse kuti moyo ukhale wovuta kwambiri. (2 Timoteyo 3:1-5) Zinthu zimenezi zakhala zikuchitika kwambiri kuyambira mu 1914.

      3. N’chifukwa chiyani padzikoli pakuchitika zinthu zoipa kwambiri kungochokera pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira?

      Yesu atangokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, anapita kukamenyana ndi Satana komanso ziwanda zake. Satana anagonja pa nkhondoyi. Baibulo limanena kuti: “Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.” (Chivumbulutso 12:9, 10, 12) Satana ndi wokwiya kwambiri chifukwa akudziwa kuti awonongedwa posachedwapa. Iye ndi amene akuchititsa kuti padzikoli pakhale mavuto ambiri chonchi. Zimenezi zikutithandiza kumvetsa chifukwa chake zinthu zafika poipa kwambiri padzikoli. Koma chosangalatsa n’chakuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onsewa.

  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulira Panopa
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 5. Dzikoli lasintha kwambiri kuyambira mu 1914

      Onerani VIDIYO.

      VIDIYO: Dzikoli Lasintha Kwambiri Kuyambira mu 1914 (1:10)

      Yesu ananeneratu zinthu zomwe zidzachitike padzikoli akadzangokhala Mfumu. Werengani Luka 21:9-11, kenako mukambirane funso ili:

      • Pa zinthu zimene zatchulidwa palembali, ndi ziti zimene inuyo munaona zikuchitika kapena kumva kuti zachitika?

      Mtumwi Paulo anafotokoza makhalidwe amene anthu adzakhale nawo m’masiku otsiriza. Werengani 2 Timoteyo 3:1-5, kenako mukambirane funso ili:

      • Malinga ndi lembali, ndi makhalidwe ati amene inuyo mukuona kuti anthu akusonyeza kwambiri masiku ano?

      Zithunzi: Zithunzi zosonyeza zomwe zikuchitika padzikoli ndiponso makhalidwe a anthu m’masiku otsiriza. 1. Mkulu wa asilikali akulankhula mofuula ataimika manja m’mwamba. 2. Nyumba zagwa chifukwa cha chivomezi. 3. Ndege za nkhondo. 4. Gulu la anthu likuyenda litavala mamasiki. 5. Nyumba zosanja ziwiri zaphulitsidwa ndi zigawenga ku New York ndipo zikuyaka. 6. Munthu akudzibaya mankhwala osokoneza bongo. 7. Mwamuna wakunga chibakera ndipo akukalipira mkazi wake. 8. Mowa komanso mankhwala osiyanasiyana. 9. Azimayi avala zovala ndi zodzikongoletsera zapamwamba ndipo akudzijambula. 10. DJ akuika nyimbo ku dansi. 11. Munthu yemwe akuchita nawo zionetsero akuponya bomba.
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena