Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 9/15 tsamba 4-7
  • Ino Ndiyo Nthaŵi Yabwino Yokhala Tcheru!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ino Ndiyo Nthaŵi Yabwino Yokhala Tcheru!
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zinthu Sizinasinthe?
  • Nkofunikadi Kukhalabe Ogalamuka
  • Kodi Dzikoli Lithadi Posachedwa?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • “Dikirani”!
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Atumwi Anapempha Chizindikiro
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 9/15 tsamba 4-7

Ino Ndiyo Nthaŵi Yabwino Yokhala Tcheru!

“MUSAKHALE ngati osadziŵa nyengo imene tikukhalamo; tsopano ndiyo nthaŵi yabwino yakuuka kutulo tathu.” (Roma 13:11, Knox) Mtumwi Paulo analemba mawu amenewo kwa Akristu a ku Roma zaka 14 mapeto oopsa a dongosolo lachiyuda mu 70 C.E. asanafike. Chifukwa chakuti iwo anali maso mwauzimu, Akristu achiyuda anali atachoka mu Yerusalemu panthaŵi yoopsa imeneyi, chotero anathaŵa imfa kapena ukapolo. Koma kodi iwo anadziŵa motani kuti anayenera kuchokeratu mumzindawo?

Yesu Kristu anali atawachenjeza kuti adani adzazinga Yerusalemu ndipo okhalamo ake adzapasulidwa. (Luka 19:43, 44) Kenaka, Yesu anauza otsatira ake za zinthu zosiyanasiyana zomwe zidzachitika monga chizindikiro chake ndipo zinali zosavuta kuzimvetsetsa. (Luka 21:7-24) Kwa Akristu amene anali kukhala mu Yerusalemu, kuchoka mumzindawo kunaloŵetsapo kusiya nyumba ndi ntchito zawo. Komabe, iwo anapulumutsa miyoyo yawo chifukwa cha kukhala tcheru ndi kuthaŵa kwawo.

Yesu ataneneratu za chiwonongeko cha Yerusalemu, ophunzira ake anamfunsa kuti: “Zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika [“kukhalapo,” NW] kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Poyankha, Yesu anayerekezera kukhalapo kwake kwamtsogolo ndi nthaŵi ya Chigumula chadziko lonse cha m’tsiku la Nowa. Yesu anafotokoza kuti Chigumulacho chinapululutsa anthu onse oipa. (Mateyu 24:21, 37-39) Choncho, iye anasonyeza kuti Mulungu adzaloŵereraponso pazochita za anthu. Kufikira pati? Inde, kufikira pakuchotseratu dziko lonse loipa, kapena kuti dongosolo la zinthu! (Yerekezerani ndi 2 Petro 3:5, 6.) Kodi zimenezo zingachitike m’nthaŵi yathu?

Kodi Zinthu Sizinasinthe?

Anali Ayuda ochepa kwambiri a m’zaka za zana loyamba amene anakhulupirira kuti mzinda wawo woyera, Yerusalemu, ungawonongedwe. Lerolino, anthu ambiri amene akukhala pafupi ndi volokano koma amene sanaionepo itaphulika sakhulupiriranso kuti ingaphulike. “Zimenezo sizidzachitika ine ndili moyo,” ambiri amalingalira motero pamene machenjezo aperekedwa. “Kwenikweni mavolokano amaphulika patapita zaka mazana aŵiri kapena atatu alionse,” anafotokoza motero wodziŵa za mavolokano Lionel Wilson. “Ungadere nkhaŵa ngati makolo ako anasamukapo chifukwa cha kuphulika kwa volokano. Koma ngati linaphulika m’masiku a agogo ako, tsopano imangokhala ngati nthano.”

Komabe, chidziŵitso cholongosoka chingatithandize kudziŵa zizindikiro za ngozi ndi kuchitapo kanthu mosamalitsa. Pakati pa anthu amene anathaŵa Phiri la Pelée, wina anali kuwadziŵa bwino mavolokano ndipo anadziŵa zizindikiro za ngoziyo. Zizindikiro zimenezo zinadziŵikanso bwino lomwe lisanaphulike Phiri la Pinatubo. Wodziŵa za mavolokano amene anali kufufuza za kuwonjezeka kwa mphamvu yosaonekayo mkati mwa phirilo anauza anthu okhala pafupi kuti achoke.

Inde, anthu ena amanyalanyazabe zizindikiro za ngozi ndipo amapitirizabe kunena kuti palibe chilichonse chimene chidzachitika. Iwo anganyozenso anthu amene akuchitapo kanthu kuti apeŵe ngoziyo. Mtumwi Petro analosera kuti ambiri adzakhala ndi khalidwe limeneli m’tsiku lathu. Iye anati: “Ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.”​—2 Petro 3:3, 4.

Kodi mumakhulupirira kuti tili mu “masiku otsiriza”? M’buku lakuti The Columbia History of the World, John A. Garraty ndi Peter Gay anafunsa kuti: “Kodi tikuona kuloŵa pansi kwa chitukuko chathu?” Kenaka, olemba mbiri ameneŵa anafotokoza za mavuto a maboma, kuwonjezereka kwa upandu ndi kusayeruzika padziko lonse, kusokonezeka kwa moyo wa banja, kulephera kwa sayansi ndi tekinoloji pacholinga chawo chothetsa mavuto a anthu, mavuto a ndale, ndiponso kusokonezeka kwa makhalidwe abwino ndi chipembedzo padziko lonse. Pomaliza, iwo anati: “Ngati zimenezi sizili zizindikiro za mapeto enieni, zikuoneka monga kuti nzizindikiro zake.”

Tili ndi chifukwa chomveka bwino chokhulupirira kuti “mapeto” ayandikira. Komabe, sitiyenera kuchita mantha kuti mwina dziko lenileni lapansili lidzatha, chifukwa chakuti Baibulo limati Mulungu “anakhazika dziko lapansi pamaziko ake, silidzagwedezeka kunthaŵi yonse.” (Salmo 104:5) Komabe, tiyenera kuyembekezera mapeto adzidzidzi a dongosolo la zinthuli limene ladzetsa mavuto ochuluka mumtundu wa anthu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tikuona zizindikiro zambiri zosonyeza masiku otsiriza a dongosolo lino, monga momwe anafotokozera Yesu Kristu. (Onani bokosi lakuti “Zina mwa Zizindikiro za Masiku Otsiriza.”) Bwanji osayerekezera mawu a Yesu ndi zochitika za m’dziko lapansili? Kuchita zimenezo kungakuthandizeni kupanga zosankha zanzeru za inu mwini ndi za banja lanu. Koma kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchitapo kanthu moyenerera tsopano lino?

Nkofunikadi Kukhalabe Ogalamuka

Ngakhale kuti asayansi angadziŵe kuti volokano idzaphulika posachedwa, iwo sanganene nthaŵi yeniyeni imene zimenezo zidzachitika. Mofananamo, ponena za mapeto a dongosolo lino la zinthu, Yesu anati: “Za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36) Popeza kuti sitikudziŵa tsiku lenileni pamene dongosolo la zinthu lilipoli lidzatha, Yesu anatipatsa chenjezo ili: “Dziŵani ichi, kuti mwininyumba akadadziŵa nthaŵi iti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe. Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu [Yesu] adzadza.”​—Mateyu 24:43, 44.

Mawu a Yesu ameneŵa akusonyeza kuti mapeto oopsa a dongosolo lino adzafikira dzikoli modzidzimutsa. Ngakhale ngati ifeyo tili otsatira ake, tiyenera ‘kukhala okonzekeratu.’ Tili mumkhalidwe wonga wa mwininyumba amene angadzidzimuke chifukwa chosadziŵa nthaŵi imene mbala idzaloŵa m’nyumba mwake.

Mofananamo, mtumwi Paulo anauza Akristu a ku Tesalonika kuti: “Inu nokha mudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. . . . Abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala.” Paulo anachenjezanso kuti: “Tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.” (1 Atesalonika 5:2, 4, 6) Kodi ‘kudikira ndi kusaledzera’ kumatanthauzanji?

Mosiyana ndi kuthaŵa kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba kuchoka mu Yerusalemu, kuthaŵira kwathu kumalo achisungiko sikudzachitika mwa kuchoka mumzinda winawake ayi. Atauza okhulupirira anzake a ku Roma kuti adzuke kutulo, Paulo anawauzanso kuti ‘avule ntchito zamdima’ ‘navale Ambuye Yesu Kristu.’ (Aroma 13:12, 14) Mwa kutsatira mosamalitsa mapazi a Yesu, tidzasonyeza kuti ndife atcheru ndi zochitika za m’nthaŵi yathu, ndipo kugalamuka kwauzimu kumeneku kudzatipangitsa kukhala m’gulu la anthu otetezeredwa ndi Mulungu pamene dongosolo la zinthu lilipoli lidzafika pamapeto ake.​—1 Petro 2:21.

Anthu amene amatsatira Yesu Kristu amakhala ndi moyo watanthauzo ndiponso wokhutiritsa. Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri zapeza kuti goli la kukhala wophunzira wa Kristu nlofeŵa ndiponso lodzetsa mpumulo. (Mateyu 11:29, 30) Kuti munthu akhale wophunzira, choyamba amafunikira ‘kuloŵetsa chidziŵitso cha Mulungu ndi cha iye amene anamtuma, Yesu Kristu.’ (Yohane 17:3, NW) Mboni zimachezera makomo mamiliyoni ambiri mlungu uliwonse pofuna kuthandiza anthu kuti apeze “chidziŵitso cholongosoka cha choonadi.” (1 Timoteo 2:4, NW) Iwo adzakhala osangalala kudzachititsa maphunziro a Baibulo aulere panyumba panu. Ndipo pamene mupita patsogolo pachidziŵitso cha Mawu a Mulungu, mosakayika konse inunso mudzatsimikiza kuti masiku ano ndi enadi. Ndithudi, ino ndiyo nthaŵi yabwino yogalamuka kutulo!

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 7]

ZINA MWA ZIZINDIKIRO ZA MASIKU OTSIRIZA

“Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina”; ‘mtendere udzachotsedwa padziko lapansi.’ (Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:4)

Nkhondo ziŵiri zadziko za m’zaka za zana lino, kuphatikizapo nkhondo zinanso zambirimbiri, zachotsa mtendere padziko lapansi. “Nkhondo Yadziko Yoyamba ndipo kenaka Yachiŵiri zinasiyana ndi nkhondo zina zonse zomwe zinamenyedwako kumbuyoko,” analemba motero wolemba mbiri John Keegan, “zinali zosiyana pa ukulu wake, katundu wowonongeka ndiponso anthu ophedwa. . . . Nkhondo Zadziko zimenezi zinapha anthu ambiri, zinawononga katundu wambiri ndipo zinadzetsa mavuto aakulu m’dera lalikulu la dziko lapansi kusiyana ndi nkhondo ina iliyonse yomwe inamenyedwako kumbuyoko.” Tsopano nkhondo zimazunza akazi ndi ana ambiri kuposa asilikali. Bungwe la United Nations Children’s Fund linafotokoza kuti pazaka khumi zapitazo, ana okwana mamiliyoni aŵiri anaphedwa m’nkhondo.

“Njala” (Mateyu 24:7; Chivumbulutso 6:5, 6, 8)

Mu 1996, mitengo ya tirigu ndi chimanga inakwera kwambiri. Chifukwa chake? Chakudya chimenechi chinali chochepa kwambiri m’nkhokwe zapadziko lonse kotero kuti chinali choti chingagaŵidwe kwa masiku 50 okha basi, chimene chili chiŵerengero chotsika koposa. Kukwera mtengo kwa zakudya zofunika kwapangitsa anthu osauka mamiliyoni mazana ambiri padziko lonse​—amene ambiri mwa iwo ndi ana​—kuti azigona ndi njala.

“Zivomezi m’malo akutiakuti” (Mateyu 24:7)

Pazaka 2,500 zapitazo, chilichonse mwa zivomezi zisanu ndi zinayi zokha chinapha anthu oposa 100,000. Zinayi mwa zivomezi zimenezi zachitika 1914 itapita.

“Kuchuluka kwa kusayeruzika” (Mateyu 24:12)

Pamene zaka za zana la 20 zikupita kumapeto, kusayeruzika, kapena kuswa malamulo, kwafalikira. Kuchitira chiŵembu anthu wamba, kupha anthu mopanda chisoni, ndiponso kupululutsana ndi zina mwa zochitika zachiwawa za m’masiku otsiriza ano.

“Miliri m’malo akutiakuti” (Luka 21:11)

M’ma 1990, zikuyembekezereka kuti anthu 30 miliyoni adzafa ndi chifuŵa chachikulu. Tizirombo ta bacteria tonyamula matendawa tsopano sitikumvanso mankhwala. Malungo, yomwe ndi nthenda inanso yakupha, akugwira anthu pakati pa 300 miliyoni ndi 500 miliyoni chaka chilichonse ndipo amapha anthu pafupifupi 2 miliyoni. Pomadzafika pamapeto a zaka khumi zino, zikuyembekezereka kuti chiŵerengero cha anthu ophedwa ndi AIDS chidzafika 1.8 miliyoni pachaka. “Lerolino, mtundu wa anthu ukuyang’anizana ndi miliri yochulukitsitsa,” inafotokoza motero State of the World 1996.

“Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi” (Mateyu 24:14)

Mu 1997, Mboni za Yehova zinathera maola oposa 1,000,000,000 m’ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Mboni zoposa mamiliyoni asanu zimalalikira uthenga umenewu nthaŵi zonse kwa anthu m’maiko 232.

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi cha FAO/​B. Imevbore

Chithunzi cha U.S. Coast Guard

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Akristu anathaŵa mu Yerusalemu chifukwa chakuti anali maso mwauzimu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena