Dzina Limene Limapangitsa Kukhala ndi Chikhulupiriro Chenicheni
“SIMUKHULUPIRIRA Yesu ndi mwazi wake wowombolera,” anatero mayi wina kwa wa Mboni za Yehova wina. Bambo wina anati: “Inu mumadzitcha nokha kuti Mboni za Yehova, koma ine ndine mboni ya Yesu.”
Anthu ambiri amaganiza kuti Mboni za Yehova sizikhulupirira Yesu kapena kumlemekeza mokwanira. Koma kodi chenicheni nchiti?
Nzoona kuti Mboni za Yehova zimalemekeza kwambiri dzina la Mulungu, Yehova.a Itamar, Mboni ina ku Brazil, imakumbukira kuti: “Moyo wanga unasintha pamene ndinamva dzina la Mulungu. Pamene ndinaliŵerenga koyamba, ndinachita ngati kuti ndadzuka m’tulo tatikulu. Dzinalo Yehova linandilimbikitsa kwambiri; linandifika pansi pa mtima.” Komabe anawonjezera kuti: “Komanso ndimakonda Yesu kwambiri.”
Chimene Dzina la Yesu Limaimira
Mawu akuti “m’dzina la Yesu” ndi ena ofanana nawo amapezeka m’Malemba onse Achikristu Achigiriki, kapena kuti “Chipangano Chatsopano.” Ndipo mawu akuti “dzina” mogwirizana ndi udindo umene Yesu ali nawo amapezeka nthaŵi 80 m’buku la Machitidwe lokha nthaŵi 30. Akristu a m’zaka za zana loyamba ankabatiza m’dzina la Yesu, ankachiritsa m’dzina lake, ankaphunzitsa m’dzina lake, ankaitana pa dzina lake, anazunzidwa chifukwa cha dzina lake, ndipo analemekeza dzina lake.—Machitidwe 2:38; 3:16; 5:28; 9:14, 16; 19:17.
Malinga ndi dikishonale ina ya Baibulo, mawu a Chigiriki otanthauza “dzina” kaŵirikaŵiri amagwiritsidwa ntchito m’Baibulo “ponena zonse zimene dzinalo limakhudza, za ulamuliro, makhalidwe, udindo, uchifumu, mphamvu, ulemerero, ndi zina zambiri.” Chotero dzina la Yesu limaimira ulamuliro waukulu umene Yehova Mulungu anampatsa. Yesu iye mwini anati: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Pamene Petro ndi Yohane anachiritsa munthu wopunduka, atsogoleri achipembedzo achiyuda anafunsa kuti: “Ndi mphamvu yanji, kapena m’dzina lanji, mwachita ichi inu? “Kenaka Petro ananena mwamphamvu za chikhulupiriro chake mwa ulamuliro ndi mphamvu zimene dzina la Yesu limaimira pamene anawadziŵitsa kuti “m’dzina la Yesu Kristu Mnazarayo . . . mwa iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.”—Machitidwe 3:1-10; 4:5-10.
Kukhulupirira Yesu Kapena Kaisara?
Kunena kuti umakhulupirira dzina la Yesu si chinthu chosavuta. Monga mmene Yesu anali ataneneratu kale, ‘anthu amitundu yonse adzadana ndi ophunzira ake chifukwa cha dzina lake.’ (Mateyu 24:9) Chifukwa chiyani? Chifukwa dzina lake limaimira udindo wake monga Wolamulira wosankhidwa ndi Mulungu, Mfumu ya mafumu, kwa imene mitundu yonse iyenera kudzipereka, koma mitunduyo sinakonzekere ndipo sifuna kutero.—Salmo 2:1-7.
Atsogoleri a chipembedzo a m’tsiku la Yesu nawonso sankafuna kudzipereka kwa Yesu. Iwo anati: “Tiribe Mfumu koma Kaisara,” motero anakana Mwana wa Mulungu. (Yohane 19:13-15) M’malo mwake, iwo anaika chikhulupiriro chawo chonse m’dzina—mu ulamuliro—wa Kaisara ndi boma lake. Iwo analingaliranso kuti Yesu anayenera kufa kuti iwo apitirize ndi maudindo awo.—Yohane 11:47-53.
Patapita zaka mazana mazana kuchokera pamene Yesu anafa, ambiri mwa amene ankadzitcha kuti ndi Akristu anayamba kukhala ndi makhalidwe ofanana ndi a atsogoleri Achiyuda. Otchedwa kuti Akristu amenewa ankakhulupirira amaulamuliro ndi maboma ndipo akhala akuloŵerera m’mikangano yawo. Mwachitsanzo, m’zaka za zana la 11, pamene tchalitchi chinasonkhanitsa anthu wamba kupanga kagulu kotchedwa militia Christi, kapena kuti Ankhondo Achikristu, “udindo womenya nkhondo yachilungamo unachotsedwa m’manja mwa atsogoleri a boma a m’Dziko Lachikristu, ndipo m’malo mwake unatengedwa ndi tchalitchi mwakugwiritsa ntchito gulu lake la Ankhondo Achikristu.” (The Oxford History of Christianity) Nkhaniyo inawonjezera kuti zilengezo zina zoperekedwa ndi papa zinkapangitsa ambiri mwa anthu omenya nkhondowo kukhulupirira kuti mwakumenya nawo nkhondo za mtanda zomwe zinkatchedwa kuti crusades, “ndiye kuti agwirizana ndi Mulungu ndipo motsimikizirika adzakhala ndi malo m’Paradaiso.”
Ena akhoza kulimbikira kunena kuti nzotheka kukhala okhulupirika kwa Yesu ndipo panthaŵi yomweyo nkumapanga nawo ndale, ndiponso kumamenya nawo nkhondo za dziko. Iwo angaone ngati ndi udindo wa Mkristu kulimbana ndi choipa chilichonse chimene chingakhalepo ndipo kuti zimenezi zimaphatikizapo kumenya nkhondo ngati zimenezo zili zoyenera. Koma kodi Akristu oyambirira anali ndi malingaliro otero?
“Akristu oyambirira sankagwira nawo ntchito yausilikali,” imatero nkhani ya mu magazini ya The Christian Century. Inalongosola kuti zisanafike zaka khumi za pakati pa 170 mpaka 180 C.E., palibe umboni uliwonse wakuti Akristu ankagwira ntchito m’gulu lankhondo. Nkhaniyo inawonjezera kuti: “Chabe kuti pang’onopang’ono Akristu anasiya khalidwe lawo lotsutsa ntchito yausilikali.”
Kodi zotsatirapo zake zakhala zotani? Nkhani ya mu The Christian Century inati; “Mwinamwake palibe chinthu chimene chanyozetsa Chikristu kuposa kuloŵerera kwake pazankhondo komwe sikusiyana konse ndi kwa omwe si Akristu. Khalidwe la Akristu loti mbali ina nkumalimbikitsa chikhulupiriro mwa Mpulumutsi wopanda chiwawa pamene kwinaku akulimbikitsa nkhondo zachipembedzo ndi zapakati pamaiko lawononga kwambiri chikhulupiriro.”
Kutsanzira Akristu Oyambirira Lerolino
Kodi nzotheka lerolino kutsanzira chitsanzo cha makhalidwe abwino a Akristu oyambirira? M’zaka za zana lino Mboni za Yehova zasonyeza kuti zimenezo nzotheka. Ponena za izo, mlembi wa magazini a Holocaust Educational Digest anati: “Palibe wa Mboni za Yehova aliyense amene adzapite ku nkhondo. . . . Ngati wolamulira aliyense akanakhala wachipembedzo chimenechi, [Nkhondo Yadziko II] sikanachitika.”
Palinso nkhani yofananayo ponena za kumenyana komwe kwachitika m’madera ena posachedwa, monga komwe kwasakaza Northern Ireland. Zaka zapitazo, wa Mboni za Yehova wina anali kulalikira kunyumba ndi nyumba m’dera la a Pulotesitanti mu mzinda wa Belfast. Mwininyumba wina, atadziŵa kuti Mboniyo poyamba inali m’Katolika, anafunsa kuti: “Pamene unali wachikatolika, kodi unkakonda gulu la IRA [Irish Republican Army]?” Mboniyo inazindikira kuti munthuyo akanayamba chiwawa, chifukwa anali atamangidwapo atapezeka ndi mfuti ali paulendo wake wopita kukapha Mkatolika wina ndipo nkuti atangotulutsidwa kumene. Choncho Mboniyo inayankha kuti: “Sindinenso Mkatolika. Ndine wa Mboni za Yehova. Monga Mkristu weniweni, sindingaphenso wina aliyense chifukwa cha boma lililonse kapena chifukwa cha munthu wina aliyense.” Atamva zimenezo munthuyo anagwirana naye chanza kunena kuti: “Kupha konse nkoipa. Anthu inu mukuchita ntchito yabwino. Pitirizani.”
Chimene Kukhulupirira Dzina la Yesu Kumatanthauza
Komabe, kukhulupirira dzina la Yesu kumatanthauza zambiri kuposa kungoleka kumenya nawo nkhondo. Kumatanthuza kumvera malamulo onse a Kristu. Yesu anati: “Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu,” ndipo limodzi mwa malamulo ake ndi lakuti “mukondane wina ndi mnzake.” (Yohane 15:14, 17) Chikondi chimafuna kuti muzichitira ena zabwino. Chimaletsa tsankho losankhana mitundu, zipembedzo, ndi zachikhalidwe. Yesu anasonyeza mmene zimenezi ziyenera kuchitikira.
Ayuda m’tsiku la Yesu sankakonda Asamariya. Komabe Yesu analankhula kwa mkazi wachisamariya, ndipo zotsatirapo zake, iye pamodzi ndi ena anakhulupirira dzina lake. (Yohane 4:39) Yesu ananenanso kuti ophunzira ake akakhala mboni zake “m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Uthenga wake wopatsa moyo sikuti unali woti uthere kwa Ayuda okha. Pambuyo pake, Petro analangizidwa kukaona Korneliyo, kazembe wankhondo wachiroma. Ngakhale kuti zinali zosaloleka kwa Myuda kukacheza ndi munthu wamtundu wina, Mulungu anamsonyeza Petro kuti ‘asanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa.’—Machitidwe 10:28.
Potsanzira Yesu, Mboni za Yehova zimathandiza anthu onse mofunitsitsa—mosasamala kanthu za mtundu, chipembedzo, kaya zachuma—kuti aphunzire za chipulumutso chimene chikubwera M’dzina la Yesu. Kukhulupirira kwawo dzina la Yesu kumawapangitsa ‘kuvomereza m’kamwa mwawo kuti Yesu ndiye Ambuye.’ (Aroma 10:8, 9) Tikukulimbikitsani kuvomera chithandizo chawo kuti nanunso muphunzire kukhulupirira dzina la Yesu.
Dzina la Yesu liyenera moonadi kukupangitsani kumamlemekeza ndi kumumvera. Mtumwi Paulo anati: “m’dzina la Yesu, bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.” (Afilipi 2:10, 11) Ngakhale kuti anthu ambiri omwe ali padziko lapansi pano safuna kudzipereka ku ulamuliro wa Yesu, Baibulo limasonyeza kuti anthu onse adzayenera kuchita choncho kapena kufa. (2 Atesalonika 1:6-9) Choncho ino ndiyo nthaŵi yokhulupirira dzina la Yesu mwa kusunga malamulo ake onse.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri, onani bolosha lakuti Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, masamba 28-31, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., 1985. Mboni za Yehova zimazindikira kuti, kuti zipeze moyo wosatha ziyenera ‘kukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.’
[Chithunzi patsamba 6]
M’dzina la Yesu, anthu ambirimbiri apha ena ndiponso kuphedwa
[Chithunzi patsamba 7]
Yesu sankasankha anthu a mitundu ina. Kodi inunso mumatero?