Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb16 tsamba 3
  • Lemba Lachaka cha 2016

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lemba Lachaka cha 2016
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Nkhani Yofanana
  • “Mupitirize Kukonda Abale”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Chikondi Chanu cha pa Abale Chikhalebe!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kupeza Mfungulo ya Chikondi cha pa Abale
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Musalole Kuti Chikondi Chanu Chizirale
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
yb16 tsamba 3
Banja likulandira alendo kunyumba kwawo komanso likupereka mphatso

Lemba Lachaka cha 2016

“Mupitirize kukonda abale.”—Aheberi 13:1

Yesu ananeneratu zimene zinkayenera kuchitika Yerusalemu akadzatsala pang’ono kuwonongedwa mu 70 C.E. Iye anati: ‘Anthu ambiri . . . adzadana. . . . Chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.’ (Mat. 24:10, 12) Koma mosiyana ndi anthu amenewa, otsatira ake akanadziwika chifukwa cha chikondi. (Yoh. 13:35) Patapita nthawi, mtumwi Paulo analembera kalata Akhristu achiheberi omwe ankakhala ku Yerusalemu. M’kalatayi, anawayamikira chifukwa chakuti ankakondana ndipo anawalimbikitsa kuti apitirize kukondana.

Panopa tikuyembekezera kuti dziko loipa la Satanali liwonongedwa posachedwapa. Mofanana ndi mmene zinthu zinali m’nthawi ya atumwi, ifenso timakhala ndi anthu omwe amakonda ndalama, zosangalatsa, ndi odzikonda komanso sakonda Mulungu ndiponso anzawo. (2 Tim. 3:1-4) Ngakhale zili choncho, a Mboni za Yehovafe timakondana kwambiri padziko lonse lapansi. Choncho tiyeni tipitirize kulemekeza Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi, pamene tikuyesetsa kukonda abale athu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena