Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 83-tsamba 94
  • Chipembedzo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chipembedzo
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ngati Wina Anena Kuti—
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Cifukwa Cace Muyenera Kuciyesa Cipembedzo Canu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Mmene Mungacidziwire Cipembedzo Coona
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 83-tsamba 94

Chipembedzo

Tanthauzo: Mpangidwe wa kulambira. Chimaloŵetsamo dongosolo la mikhalidwe ya kukhala opembedza, zikhulupiriro, ndi zizoloŵezi zachipembedzo; zimenezi zingakhale za munthu mmodzi; kapena zingachirikizidwe ndi gulu. Kaŵirikaŵiri chipembedzo chimaphatikizapo kukhulupirira Mulungu kapena milungu ingapo; kapena chimachitira anthu, zinthu, zikhumbo, kapena mphamvu kukhala zinthu zolambiridwa. Mbali yaikulu ya chipembedzo yazikidwa pa kupendedwa kwa chilengedwe kochitidwa ndi anthu; palinso chipembedzo chovumbulutsidwa. Pali chipembedzo chowona ndi chonyenga.

Kodi nchifukwa ninji pali zipembedzo zambiri motero?

Kuŵerenga kwaposachedwapa kunasonyeza kuti pali zipembedzo zazikulu 10 ndi mipatuko yokwanira 10 000. Mwa imeneyi, yokwanira 6 000 iri mu Afrika, 1 200 mu United States, ndipo mazana angapo m’maiko ena.

Zoputira zambiri zachititsa kuyambika kwa timagulu tatsopano tachipembedzo. Ena anena kuti zipembedzo zosiyanasiyanazo zimaimira njira zosiyasiyana za kuimira chowonadi cha chipembedzo. Koma mmalo mwake, kuyerekezeredwa kwa ziphunzitso ndi zizoloŵezi zawo ndi Baibulo kumasonyeza kuti, kusiyana kwa zipembedzo kuli chifukwa cha anthu amene afikira kukhala otsatira a anthu mmalo mwa kumvetsera Mulungu. Pamlingo waukulu, nkokondweretsa kuwona kuti, ziphunzitso zimene onse amafanana, koma zimene ziri zosiyana ndi Baibulo, magwero ake ndiwo Babulo wakale. (Wonani tsamba 49, 50, pamutu wakuti “Babulo Wamkulu.”)

Kodi ndani amene ali wosonkhezera chisokonezo cha chipembedzo chotero? Baibulo limatchula Satana Mdyerekezi kukhala “mulungu wa dongosolo iri la zinthu.” (2 Akor. 4:4, NW) Limatichenjeza kuti “zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda, ndipo osati kwa Mulungu.” (1 Akor. 10:20, NW) Pamenepa, nkofunika kwambiri chotani nanga, kutsimikizira kuti tikulambiradi Mulungu wowona, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, ndi kuti kulambira kwathu kuli kokondweretsa kwa iye!

Kodi zipembedzo zonse nzovomerezeka kwa Mulungu?

Ower. 10:6, 7: “Ana a Israyeli anawonjeza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aastaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sidoni, ndi milungu ya Moabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anamleka Yehova osamtumikira. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli.” (Ngati munthu alambira kanthu kalikonse kapena munthu aliyense osati Mulungu wowona, mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kuli kwachiwonekere kuti mpangidwe wake wa kulambira suuli wovomerezeka kwa Yehova.)

Marko 7:6, 7: “Iye [Yesu] ananena nawo [Afarisi Achiyuda ndi alembi], Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza ine ndi milomo yawo, koma mtima wawo ukhala kutali ndi ine. Koma andilambira ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso malangizo a anthu.” (Mosasamala kanthu za amene kaguluko kakudzinenera kukhala kakulambira, ngati iwo amamatira ku ziphunzitso za anthu m’malo mwa Mawu ouziridwa a Mulungu, kulambira kwawo kuli chabe.)

Aroma 10:2, 3, NW: “Ndiwachitira umboni kuti iwo ali ndi changu kwa Mulungu; koma osati chogwirizana ndi chidziŵitso cholongosoka; pakuti, chifukwa cha kusadziŵa chilungamo cha Mulungu koma kufuna kukhazikitsa chawochawo, iwo sanadzigonjetsere ku chilungamo cha Mulungu.” (Anthu angakhale nawo Mawu olembedwa a Mulungu koma nasoŵa chidziŵitso cholongosoka cha zolembedwamo, chifukwa chakuti sanaphunzitsidwe bwino. Iwo angalingalire kuti ngachangu kwa Mulungu, koma angakhale asakuchita zimene iye afuna. Kulambira kwawo sikudzakondweretsa Mulungu, kodi sichoncho?)

Kodi nzowona kuti m’zipembedzo zonse muli abwino?

Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti munthu sayenera kunama kapena kuba ndi zina zotero. Koma kodi zimenezo nzokwanira? Kodi inu mukanakhala wachimwemwe kumwa tambula ya madzi otsiridwa poizoni chifukwa chakuti munthu wina wakutsimikizirani kuti ochuluka a amene mukamwa anali madzi?

2 Akor. 11:14, 15: “Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adziwonetsa monga atumiki achilungamo.” (Panopa tikuchenjezedwa kuti sizonse zimene zimachokera kwa Satana zimene zingawonekere kukhala zonyansa. Imodzi ya njira zake zazikulu zonyengera anthu yakhala chipembedzo chonyenga cha mitundu yonse, chimene kwa ena chiri ndi mawonekedwe olungama.)

2 Tim. 3:2, 5: “Anthu adzakhala . . . akukhala nawo mawonekedwe achipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.” (Mosasamala kanthu za kudzinenera kwawo kwakunja kuti amakonda Mulungu, ngati awo amene mumalambira nawo samagwiritsira ntchito mowona mtima Mawu ake m’miyoyo ya iwo eni, Baibulo limakulimbikitsani kuleka mayanjano otero.)

Kodi kuli koyenera kusiya chipembedzo cha makolo a munthuwe?

Ngati chimene makolo athu anatiphunzitsa chiridi chochokera m’Baibulo, tiyenera kuchigwiritsitsa. Ngakhale ngati timva kuti zizoloŵezi ndi zikhulupiriro za chipembedzo chawo ziri zosagwirizana ndi Mawu a Mulungu, makolo athu ngoyenera ulemu wathu. Koma bwanji ngati munamva kuti chozoloŵezi china cha makolo anu chinali chovulaza kuthanzi ndipo chikafupikitsa moyo wa munthuyo? Kodi mukawatsanzira ndi kulimbikitsa ana anu kuchita motero, kapena kodi mukanagaŵana nawo mwaulemu zimene mwaphunzira? Mofananamo, kuvomereza chowonadi Chabaibulo kumadzetsa thayo. Ngati kuli kotheka, tiyenera kugaŵana ndi mamembala abanja zimene tiphunzira. Tiyenera kupanga chosankha chakuti: Kodi timakondadi Mulungu? Kodi timafunadi kumvera Mwana wa Mulungu? Kuchita kwathu motero kungafunikiritse kuti tisiye chipembedzo cha makolo athu nkuvomereza ndi chipembedzo chowona. Ndithudi sikukakhala koyenerera kulola kudzipereka kwathu kwa makolo athu kukhala kwakukulu kwambiri kuposa kukonda kwathu Mulungu ndi Kristu, kodi sichoncho? Yesu anati: “Iye wa kukonda atate wake, kapena amake koposa ine, sayenera ine.”—Mat. 10:37.

Yoswa 24:14: “Tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi wowona; nimuchotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija lamtsinje, ndi m’Aigupto; nimutumikire Yehova.” (Zimenezo zinatanthauza kusintha kuchoka ku chipembedzo cha makolo awo, kodi sichoncho? Kuti atumikire Yehova movomerezeka, iwo anafunikira kuchotsa mafano alionse ogwiritsiridwa ntchito m’chipembedzo chotero ndi kuyeretsa mitima yawo pa zikhumbo zonse za zinthu zimenezo.)

1 Pet. 1:18, 19: “Podziŵa kuti simunawomboledwa ndi zovunda, golidi ndi siliva, kusiyana nawo makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu; koma ndi mwazi wamtengo wake wapatali monga wa mwana wankhosa wopanda chirema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu.” (Motero, Akristu oyambirira anachoka kumiyambo imeneyo ya makolo awo, miyambo imene sikanawapatsa konse moyo wamuyaya. Kuyamikira nsembe ya Kristu kunawapangitsa kuchotsa chinthu chirichonse chomwe chinachititsa miyoyo yawo kukhala yosakondweretsa, yopanda tanthauzo lenileni chifukwa chakuti sanalemekeze Mulungu. Kodi ife sitiyenera kukhala ndi mkhalidwe umodzimodziwo?)

Kodi nchiyani chimene chiri lingaliro Labaibulo ponena za chikhulupiriro choloŵana?

Kodi Yesu anawawona motani atsogoleri achipembedzo amene anayeserera kukhala olungama koma amene anachitira chipongwe Mulungu? “Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda ine; pakuti ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa ine ndekha, koma iyeyu anandituma ine. . . . Inu muli ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’chowonadi, pakuti mwa iye mulibe chowonadi. Pamene alankhula bodza alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza ndi atate wake wa bodza. Koma ine, chifukwa ndinena chowonadi, simukhulupirira ine. . . . Inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.”—Yoh. 8:42-47.

Kodi kungasonyeze kukhulupirika kwa Mulungu ndi kumiyezo yake yolungama ngati atumiki ake anaphatikizidwa muubale wachipembedzo ndi anthu enieniwo amene amachita zimene Mulungu amatsutsa kapena amene amalekerera zizoloŵezi zotero? “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere iyayi. . . . Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.” (1 Akor. 5:11; 6:9, 10) “Yense . . . wofuna kukhala bwenzi ladziko, akudziika mdani wa Mulungu.” (Yak. 4:4, NW) “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake.”—Sal. 97:10.

2 Akor. 6:14-17: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira? Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? . . . Chifukwa chake, tulukani pakati pawo, ndipo patukani, ati Ambuye, ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo ine ndidzakulandirani inu.”

Chiv. 18:4, 5: “Ndinamva mawu ena ochokera kumwamba, nanena, Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m’mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.” (Kaamba ka maumboni wonani mutu waukulu wakuti “Babulo Wamkulu.”)

Kodi kukhala mbali ya chipembedzo cholinganizidwa nkofunika?

Magulu ambiri azipembedzo zolinganizidwa atulutsa zipatso zoipa. Chimene chiri choipa sindicho chenicheni chakuti maguluwo ali olinganizidwa. Koma ambiri achirikiza mipangidwe ya kulambira imene iri yozikidwa pa ziphunzitso zonyenga ndi imene kwakukulukulu iri yadzoma mmalo mwa kugaŵira chitsogozo chowona chauzimu; iwo agwiritsiridwa ntchito molakwa kulamulira miyoyo ya anthu kaamba ka zolinga zadyera; iwo akhala odera nkhaŵa mopambanitsa ndi zopereka za ndalama ndi kukongoletsa nyumba zolambirira mmalo mwa makhalidwe abwino auzimu; kaŵirikaŵiri mamembala awo ngonyenga. Mwachiwonekere palibe munthu wokonda chilungamo amene akafuna kukhala mbali ya gulu lotero. Koma chipembedzo chowona chiri kusiyana kotsitsimula pa zonsezo. Komabe, kuti chikwaniritse zofunika Zabaibulo, chiyenera kulinganizidwa.

Aheb. 10:24, 25: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muwona tsiku lirikuyandika.” (Kuti lamulo Lamalemba limeneli likwaniritsidwe, payenera kukhala misonkhano Yachikristu imene tingafikepo pamlingo wanthaŵi zonse. Kakonzedwe kotero kamatilimbikitsa kusonyeza chikondi kwa ena, osati kokha kudera nkhaŵa ndi ife eni.)

1 Akor. 1:10, NW: “Tsopano ndikupemphani, abale kupyolera m’dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu kuti muyenera nonse kulankhula mogwirizana, ndi kuti pasakhale magaŵano pakati panu, koma kuti mukakhale ogwirizana bwino lomwe m’maganizo amodzimodzi ndi mu mzera umodzimodzi wa ganizo.” (Chigwirizano chotero sichikapezedwa ngati anthu alionse paokha sanasonkhane pamodzi, kupindula kuprogramu ya chakudya imodzimodzi, ndi kuchitira ulemu gulu limene malangizo otero anaperekedweramo. Wonaninso Yohane 17:20, 21.)

1 Pet. 2:17, NW; “Kondani gulu lonse la abale.” (Kodi amenewa amaphatikizapo kokha amene angasonkhane pamodzi m’nyumba wamba iriyonse? Kutalitali; ndiro gulu lamitundu yonse la abale, monga momwe kwasonyezedwera ndi Agalatiya 2:8, 9 ndi 1 Akorinto 16:19.)

Mat. 24:14: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Kuti mitundu yonse ipatsidwe mwaŵi wakumva uthenga wabwino umenewo, kulalikira kuyenera kuchitidwa mwadongosolo, limodzi ndi uyang’aniro woyenerera. Kukonda Mulungu ndi anthu anzawo kwachititsa anthu kuzungulira dziko lapansi kugwirizanitsa zoyesayesa zawo kuchita ntchito imeneyi.)

Wonaninso mutu waukulu wakuti “Gulu.”

Kodi kukonda munthu mnzanu kulidi nkanthu?

Palibe kukaikira ponena za zimenezi, chikondi chotero nchofunika. (Aroma 13:8-10) Koma kukhala Mkristu kumaloŵetsamo zambiri kuposa kungokhala wokoma mtima kwa anansi athu. Yesu ananena kuti ophunzira ake owona akadziŵika mwapadera ndi chikondano chawo kwa wina ndi mnzake, kwa okhulupirira anzawo. (Yoh. 13:35) Kufunika kwa zimenezo kwagogomezeredwa mobwerezabwereza m’Baibulo. (Agal. 6:10; 1 Pet. 4:8; 1 Yoh. 3:14, 16, 17) Komabe, Yesu anasonyeza kuti chofunikadi kwambiri ndicho kukonda kwathu Mulungu mwiniyo, kumene kumasonyezedwa mwakumvera kwathu malamulo ake. (Mat. 22:35-38; 1 Yoh. 5:3) Kuti tisonyeze chikondi chotero, tifunikira kuphunzira ndi kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu ndi kusonkhana ndi atumiki anzathu a Mulungu m’kulambira.

Kodi kukhala ndi unansi wathu ndi Mulungu kulidi chinthu chofunika?

Nkofunikadi. Kufika chabe pamaulaliki achipembedzo mwanjira yamwambo sikungaloŵe mmalo mwake. Koma tifunikira kukhala osamala. Chifukwa ninji? M’zaka za zana loyamba, panali anthu amene analingalira kuti anali ndi unansi wabwino ndi Mulungu koma amene Yesu anawasonyeza kukhala olakwa kwambiri. (Yoh. 8:41-44) Mtumwi Paulo analemba za ena amene mwachiwonekere anali achangu ponena za chikhulupiriro chawo ndi amene mwachiwonekere analingalira kuti anali ndi unansi wabwino ndi Mulungu koma amene sanazindikire zimene kwenikweni zinali zofunika kuti akhale ndi chiyanjo cha Mulungu.—Aroma 10:2-4.

Kodi ife tingakhale ndi unansi wabwino ndi Mulungu ngati tinaŵerengera malamulo ake kukhala osanunkha kanthu? Limodzi la ameneŵa nlakuti tiyenera kusonkhana nthaŵi zonse ndi okhulupirira anzathu.—Ahebri 10:24, 25.

Ngati ife tiŵerenga Baibulo, kodi zimenezo nzokwanira?

Nzowona kuti anthu ambiri angaphunzire zochuluka mwa kuŵerenga Baibulo iwo eni. Ngati cholinga chawo chiri kuphunzira chowonadi chonena za Mulungu ndi zifuno zake, zimene akuchitazo zikuyamikiridwa kwambiri. (Mac. 17:11) Koma, kunena mosadzinyenga, kodi tikazindikiradi tanthauzo lake lonselo popanda chithandizo? Baibulo limasimba za mwamuna wina amene anali ndi malo antchito apamwamba koma amene anali wodzichepetsa mokwanira kuvomereza kufunikira kwake chithandizo m’kumvetsetsa ulosi wa Baibulo. Chithandizo chimenecho chinaperekedwa ndi chiŵalo cha mpingo Wachikristu.—Mac. 8:26-38; yerekezerani ndi maumboni ena onena za Filipo m’Machitidwe 6:1-6; 8:5-17.

Ndithudi, ngati munthu aŵerenga Baibulo koma sakuligwiritsira ntchito m’moyo wake, kumampindulitsa mochepekera. Ngati iye amalikhulupirira nachita mogwirizana nalo, iye adzagwirizana ndi atumiki a Mulungu m’misonkhano yanthaŵi yonse yampingo. (Aheb. 10:24, 25) Iye adzakhalanso ndi phande mkugaŵana “mbiri yabwino” ndi anthu ena.—1 Akor. 9:16; Marko 13:10; Mat. 28:19, 20.

Kodi munthu angadziŵe motani chimene chiri chipembedzo chowona?

(1) Kodi ziphunzitso zake zazikidwa pachiyani? Kodi zachokera kwa Mulungu, kapena kodi kwakukulukulu nzochokera kwa anthu? (2 Tim. 3:16; Marko 7:7) Mwachitsanzo, funsani kuti: Kodi mpati pamene Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu ali Wautatu? Kodi mpati pamene limanena kuti moyo waumunthu ngwosakhoza kufa?

(2) Pendani kaya ngati chikuzindikiritsa dzina la Mulungu. Yesu anati m’pemphero kwa Mulungu: “Ndaliwonetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa ine m’dziko lapansi.” (Yoh. 17:6) Iye analengeza kuti: “Ndiye Yehova Mulungu wako amene uyenera kumlambira, ndipo ndi kwa iye yekha kumene uyenera kupereka utumiki wopatulika.” (Mat. 4:10, NW) Kodi chipembedzo chanu chakuphunzitsani kuti ‘ali Yehova amene muyenera kulambira’? Kodi mwafikira pakudziŵa Munthuyo wodziŵika ndi dzinalo—zifuno zake, ntchito zake, mikhalidwe yake—kotero kuti mukulingalira kuti mungathe mwachidaliro kuyandikira pafupi naye?

(3) Kodi chikhulupiriro chowona mwa Yesu Kristu chikusonyezedwa? Zimenezi zikuloŵetsamo kuyamikiridwa kwa mtengo wa nsembe ya moyo waumunthu wa Yesu ndi malo ake a ntchito lerolino monga Mfumu yakumwamba. (Yoh. 3:36; Sal. 2:6-8) Chiyamikiro chotero chimasonyezedwa mwakumvera Yesu—kukhala ndi phande inu mwini ndi mwachangu m’ntchito imene iye anagaŵira otsatira ake. Chipembedzo chowona chiri ndi chikhulupiriro chotero chimene chimatsagana ndi ntchito.—Yak. 2:26.

(4) Kodi chiri kwakukulukulu chadzoma, chamwambo, kapena kodi ndicho njira ya moyo? Mulungu amatsutsa mwamphamvu chipembedzo chimene chiri chamwambo chabe. (Yes. 1:15-17) Chipembedzo chowona chimachirikiza muyeso wa Baibulo wa makhalidwe abwino ndi kalankhulidwe koyera mmalo mwa kufooka komkera limodzi ndi zikhoterero zotchuka. (1 Akor. 5:9-13; Aef. 5:3-5) Mamembala ake amasonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu m’miyoyo yawo. (Agal. 5:22, 23) Chotero, awo amene amamamatira kukulambira kowona angadziŵike chifukwa chakuti amayesayesa mowona mtima kugwiritsira ntchito miyezo ya Baibulo m’miyoyo yawo osati kokha pamalo awo osonkhanira koma m’banja mwawo, kuntchito yawo yakuthupi, m’sukulu, ndi m’kusanguluka.

(5) Kodi ziŵalo zake zimakondanadi? Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yoh. 13:35) Chikondi choterocho chimapitirira malire aufuko, amakhalidwe, ndi autundu, kugwirizanitsa anthu pamodzi muubale wowona. Chikondi chimenechi nchamphamvu kwambiri kotero kuti chimaŵalekanitsa kukhaladi osiyana. Pamene mitundu ipita kunkhondo, kodi ndani amene amakonda abale awo Achikristu a m’maiko ena mokwanira kotero kuti amakana kunyamula zida zankhondo ndi kukaŵapha? Ndizo zimene Akristu oyambirira anachita.

(6) Kodi chiridi cholekana ndi dziko? Yesu anati otsatira ake owona akakhala ‘osati ambali yadziko,’ (Yoh. 15:19) Kulambira Mulungu mwanjira imene amavomereza kumafunikiritsa kuti tidzisungire ‘osachitidwa maŵanga ndi dziko.’ (Yak. 1:27) Kodi zimenezo zinganenedwe ponena za awo amene atsogoleri ake achipembedzo ndi mamembala ena amaphatikizidwa m’ndale za dziko, kapena amene miyoyo yawo kwakukulukulu iri yosumikidwa pa kukonda zinthu zakuthupi ndi zilakolako zathupi?—1 Yoh. 2:15-17.

(7) Kodi ziŵalo zake ziri mboni zokangalika za Ufumu wa Mulungu? Yesu ananeneratu kuti: “Uthenga uwu wabwino waufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu amitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mat. 24:14) Kodi nchipembedzo chiti chimene chikulalikiradi Ufumu wa Mulungu kukhala chiyembekezo cha anthu mmalo mwakulimbikitsa anthu kufunafuna ulamuliro wa anthu kuti uthetse mavuto awo? Kodi chipembedzo chanu chakukonzekeretsani kukhala ndi phande m’ntchito imeneyi, ndi kuichita kunyumba ndi nyumba monga momwe Yesu anaphunzitsira atumwi ake kuchita?—Mat. 10:7, 11-13; Mac. 5:42; 20:20.

Kodi Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti chawo ndicho chipembedzo chowona chokha?

Wonani tsamba 275, pamutu wakuti “Mboni za Yehova.”

Kodi nchifukwa ninji anthu ena ali ndi chikhulupiro pamene ena alibe?

Wonani mutu waukulu wakuti “Chikhulupiriro.”

Ngati Wina Anena Kuti—

‘Sindikondwerera m’chipembedzo’

Mungayankhe kuti: ‘Zimenezo sizimandidabwitsa. Anthu ambiri ali ndi lingaliro lanu. Ntakufunsani, Kodi mwalingalira mwanjirayo nthaŵi zonse?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Chimodzi cha zinthu zimene zinandichititsa chidwi chinali kupeza kuti pafupifupi chiphunzitso chachikulu chirichonse chophunzitsidwa m’matchalitchi lerolino sichimapezeka m’Baibulo. (Mwinamwake gwiritsirani ntchito mawu opezeka patsamba 275, pamutu wakuti “Mboni za Yehova,” mukumagogomezera mwapadera pa Ufumu. Mosiyanitsa, sonyezani zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira, monga momwe zandandalikidwira patsamba 270-272.)’

Wonaninso tsamba 16, 17.

‘Muli chinyengo chochulukitsitsa m’chipembedzo’

Mungayankhe kuti: ‘Inde, ndikuvomerezana nanu. Ambiri amalalikira chinthu china ndipo amakhala ndi moyo mwanjira ina. Koma tandiuzani, Kodi mumalingalira motani ponena za Baibulo? (Sal. 19:7-10)’

‘Ndimakhala moyo wabwino. Ndimachitira anansi anga molungama. Zimenezo ziri chipembedzo chokwanira kwa ine’

Mungayankhe kuti: ‘Popeza kuli kwakuti mukunena kuti mumakhala moyo wabwino, mwachiwonekere mukusangalala ndi moyo, kodi sichoncho? . . . Kodi mukakonda motani kukhala m’mikhalidwe yolongosoledwa pano pa Chivumbulutso 21:4? . . . Tawonani chimene Yohane 17:3 amanena kuti nchofunika kuti tigaŵanemo.’

Wonaninso tsamba 88.

‘Sindikondwerera m’chipembedzo cholinganizidwa. Ndimakhulupirira kuti unansi waumwini ndi Mulungu ndiwo womwe ulinkanthu’

Mungayankhe kuti: ‘Zimenezo zandikondweretsa. Kodi mwakhala mukulingalira motero nthaŵi zonse? . . . Kodi munayamba mwagwirizanapo ndi gulu lachipembedzo kale? . . . (Ndiyeno mwinamwake gwiritsirani ntchito mawu a patsamba 87-89.)’

‘Sindimavomerezana ndi zonse zimene tchalitchi changa chimaphunzitsa, koma sindimawona kufunika kwa kusinthira ku china. Ndingakonde kugwirira ntchito kuwongolera mkati mwa changa’

Mungayankhe kuti: ‘Ndikuyamikira kundiuza kwanu zimenezo. Ndiri wotsimikiza kuti mudzavomereza kuti chimene chiridi chofunika kwa ife tonse ndicho kukhala ndi chivomerezo cha Mulungu, kodi sichoncho?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Mulungu amapatsa tonsefe kanthu kena kokalingalira mwamphamvu pano pa Chivumbulutso 18:4, 5 . . . Ngakhale ngati ife monga anthu sitichita zinthu zolakwa, Baibulo limasonyeza kuti tiri ndi liwongo ngati tichirikiza magulu ameneŵa. (Wonaninso mutu waukulu wakuti “Babulo Wamkulu.”)’ (2) (Mwinamwake gwiritsiraninso ntchito mawu a patsamba 89, 90.) (3) ‘Mulungu akufunafuna anthu amene amakonda chowonadi, ndipo akuwasonkhanitsa pamodzi kaamba ka kulambira kogwirizanitsidwa. (Yoh. 4:23, 24)’

‘Zipembedzo zonse nzabwino; inu muli nchanu, ndipo ndiri ndi changa’

Mungayankhe kuti: ‘Mwachiwonekere inu ndinu munthu waluntha. Koma mumazindikiranso kuti tonsefe tifunikira chitsogozo chimene Mawu a Mulungu amapereka, ndicho chifukwa chake inu muli ndi chipembedzo, kodi sizowona?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Pano pa Mateyu 7:13, 14 Baibulo limatipatsa chitsogozo chofunika kwambiri m’mawu a Yesu. (Aŵerengeni.) . . . Kodi nchifukwa ninji zimenezo zingakhale choncho?’

Wonaninso tsamba 83-85.

‘Malinga ngati mukhulupirira Yesu, ziribe kanthu kwenikweni ndi tchalitchi chomwe muli’

Mungayankhe kuti: ‘Palibe kukaikira za ichi, kukhulupirira Yesu nkofunika. Ndipo ndikhulupirira kuti mwamawuwo mukutanthauza kuvomereza chirichonse chomwe anaphunzitsa. Mosakaikira mwawona, monga momwe ndachitira, kuti ambiri amene amanena kuti ali Akristu samakhaliradi moyo chimene dzinalo limaimira.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Tawonani zimene Yesu ananena pano pa Mateyu 7:21-23.’ (2) ‘Pali mtsogolo mwabwino kaamba awo osamala mokwanira kufufuza zimene chifuniro cha Mulungu chiri ndiyeno kuchichita. (Sal. 37:10, 11; Chiv. 21:4)’

‘Kodi nchiyani chomwe chimakupangitsani kuganiza kuti pali chipembedzo chimodzi chokha cholungama?’

Mungayankhe kuti: ‘Mosakaikira, pafupifupi m’chipembedzo chiri chonse, muli anthu owona mtima. Koma chimene chiridi kanthu ndicho chimene Mawu a Mulungu amanena. Kodi ndizikhulupiriro zowona zingati zimene iwo amasonyako? Tawonani zimene zalembedwa pano pa Aefeso 4:4, 5.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Zimenezo zimavomerezana ndi zimene malemba ena amanena. (Mat. 7:13, 14, 21; Yoh. 10:16; 17:20, 21)’ (2) ‘Motero, nkhani imene tiyenera kuyang’anizana nayo ndiyo kudziŵikitsa chipembedzo chimenecho. Kodi tingatero motani? (Mwinamwake gwiritsirani ntchito mawu a patsamba 89, 90.)’ (3) (Wonaninso zimene ziri patsamba 270-272, pamutu wakuti “Mboni za Yehova.”)

‘Ndimangoŵerenga Baibulo langa panyumba ndi kupemphera kwa Mulungu kuti ndizindikire’

Mungayankhe kuti: ‘Kodi munapambana kuŵerenga Baibulo lathunthu?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Pamene mugwiririra ntchito pazimenezo, mudzapeza kanthu kena kokondweretsa kwambiri pa Mateyo 28:19, 20. . . . Zimenezi nzofunika chifukwa chakuti zikusonyeza kuti Kristu amagwiritsira ntchito anthu ena kutithandiza kumvetsetsa zophatikizidwa m’kukhala Mkristu weniweni. Mogwirizana ndi zimenezo, Mboni za Yehova zimadzipereka kuchezera anthu m’nyumba zawo kwa ora limodzi kapena chapompo mlungu uliwonse, kwaulere, kudzakambitsirana Baibulo. Ndiloleni nditenge mphindi zochepa zokha kukusonyezani mmene timachitira?’

Wonaninso tsamba 89.

‘Ndiganiza kuti chipembedzo chiri nkhani yaumwini’

Mungayankhe kuti: ‘Limenelo liri lingaliro lofala masiku ano, ndipo ngati anthu alidi osakondwerera uthenga wa Baibulo, mokondwera timamka kunyumba zina. Koma kodi munazindikira kuti chifukwa chimene ndadzakuwonerani chiri chakuti ichi ndicho chimene Yesu analangiza otsatira ake kuchita? . . . (Mat. 24:14; 28:19, 20; 10:40)’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena