Chaputala 14
Pambuyo pa Pangano Latsopano—Ufumu wa Zaka Chikwi
1, 2. (a) Kodi mamiliyoni a opindula ndi kugwira ntchito kwa pangano latsopano lerolino angayerekezeredwe ndi ayani? (b) Kodi zofunika za pangano latsopano zinanenanji?
ANTHU mamiliyoni ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi alandira kale mapindu abwino kuchokera m’kugwira ntchito kwa pangano latsopano, ngakhale kuli kwakuti iwo saali mkati mwakemo. Iwo ali ofanana ndi nzika zosakhala Aisrayeli zimene zinkakhala mu Israyeli m’masiku amene pangano la Chilamulo cha Mose linali kugwira ntchito. (Eksodo 20:10) Kodi zimenezi zakhala choncho motani popeza kuli mamiliyoni owonjezereka otero a opindula amene ali ogwirizana ndi otsalira a Israyeli wauzimu lerolino?
2 Mu ulosi wa Yeremiya 31:31-34, Iye amene amapereka zofunika za pangano latsopano anati: “Ndidzaika chilamulo changa mkati mwawo, ndipo m’mitima mwawo ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, nadzakhala iwo anthu anga.”
3. (a) Kodi chilamulo cha pangano lakale la Mose chinaperekedwa kwa Israyeli mumpangidwe wotani? (b) Malemba Opatulika Achigiriki Achikristu asanayambe kulembedwa, kodi nkuti kumene Mulungu analemba malamulo a pangano latsopano?
3 M’nkhani ya pangano la Chilamulo, Yehova Mulungu, kupyolera mwa mneneri Mose monga mtetezi, anapereka kwa Israyeli wakuthupi “bukhu lolembedwa ndi dzanja . . . , limene linali ndi malamulo.” (Akolose 2:14, NW) Pamenepa, bwanji, ponena za chilamulo cha pangano latsopano? Mtetezi wake sanali kudzachilemba pamwala, kapena kuchilemba m’bukhu la pamanja. Mtetezi wake sanasiye mabukhu alionse a iyemwini. Timatsimikiza chimene chiri chilamulo cha pangano latsopano kuchokera ku Malemba Opatulika Achikristu Achigiriki. (2 Timoteo 3:16) Koma ngakhale Malemba Opatulika Achigiriki amenewo asanayambe kulembedwa, kuyambira pafupifupi 41 C.E., Yehova Mulungu anayamba kulemba chilamulo chake cha pangano latsopano. Liti? Patsiku la Pentekoste, 33 C.E. Kuti? Penipenipo pamene anali atalonjeza kalekale kuchilemba: “Ndzidzapatsa malamulo anga kuwalonga m’nzeru zawo, ndipo pamtima pawo ndidzawalemba iwo.”—Ahebri 8:10.
4. Kodi kulemba kwa Mulungu malamulo ake pamtima ndi kuŵaika m’maganizo a atumiki ake kukakhala ndi ziyambukiro zabwino zotani?
4 Pokhala atalembedwa pamtima, mwachiwonekere kwambiri malamulo amenewo akakondedwa mosalekeza ndi owamverawo. Ngati malamulo amenewo anaikidwa “m’maganizo mwawo,” mwachiwonekere sakaiŵalidwa ndi iwo. Chifukwa chake, osunga malamulo amenewo amanena, mwa mawu a Salmo 119:97 kuti: “Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiliramo ine tsiku lonse.” Kuchokera pansi penieni pa mitima yawo, amakonda malamulo a Yehova monga momwe akuperekedwera ndi Mtetezi wake, Yesu Kristu. Motero, mwachisonkhezero cholungama, iwo amatsimikiza kusunga malamulo a mtengo wapatali amenewo. Zimenezi zikugwira ntchito kwa onse aŵiri “kagulu ka nkhosa” kokhala mu pangano latsopano ndi ku “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” amene, saali m’pangano latsopano, koma pansi pake.—Yerekezerani ndi 1 Yohane 5:3; Yohane 14:15.
Nkhani Yaufumu Patsogolo!
5. Kodi nchiyani chimene Mtetezi wa pangano latsopano adaneneratu pa Mateyu 24:12-14?
5 Osunga chilamulo cha pangano latsopano samalola konse kugonjera ku chimene Mteteziyo, Yesu Kristu, adaneneratu kukhala mbali ya “chizindikiro . . . cha mapeto a dongosolo la zinthu”: “Chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala. Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira ku chimaliziro, yemweyo adzapulumuka. Ndipo uthenga uwu wabwino waufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu amitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:3, NW, 12-14.
6. (a) Kodi Mateyu 24:14 anali kudzakhala ulosi wamba? (b) Kodi ndani amene awona mawuwo kukhala oposa ulosi, ndipo kodi nchiyani chimene chinganenedwe ponena za chipiriro chawo?
6 Mawu otsirizira ameneŵa onena za umboni wa padziko lonse lapansi ku Ufumu sanali kuneneratu wamba. Anali malangizo kwa ophunzira ake okhala ndi moyo m’nthaŵi ya “mapeto a dongosolo iri la zinthu.” Anali chitsogozo cha njira yawo yolungama kufikira mapeto okwanira a dongosolo la zinthu limene liri lopanda chikondi limenenso liri lodzala ndi kusayeruzika, osati kokha kunyozera chilamulo cha Mulungu. Kodi ndani lerolino amene amatsimikiza kukhala Akristu owona, amene amatenga mawu a Yesu Kristu kukhala malangizo kwa iwo? Maumboni a m’mbiri amene awonjezereka chiyambire 1919 akuyankha motsimikizirika kuti, “Mboni za Yehova”! Mkupiti wawo wa kuphunzitsa Baibulo ponena za Ufumu uli waukulu koposa wonse wodziŵika, ndipo asonyeza kupirira mkati mwa zaka 67 zapitazo. Tsopano chaka chirichonse, ukukula m’mliŵiro ndi mphamvu.
7, 8. (a) Mkati mwa Nkhondo Yadziko I, kodi Satana anayesayesa kuchitanji kwa awo a m’pangano latsopano? (b) M’nyengo ya pambuyo pa nkhondo, kodi ndimotani mmene nkhani ya Ufumu inakhalira yaikulu?
7 Satana Mdyerekezi anayesa kuletsa mkupiti wapadera umenewu wophunzitsa Baibulo mwa kuchititsa otsalira ochepekera a Israyeli wauzimu kusesedwa mkati mwa Nkhondo Yadziko I. Iye analephera! Mwamsanga, pambuyo pa kutsitsimuka kwawo kuchokera kumkhalidwe wofanana ndi imfa m’dzinja la 1919, iwo anachita msonkhano wawo woyamba wa pambuyo pa nkhondo, m’Cedar Point, Ohio, m’September wa chaka chimenecho. Pamsonkhano wachiŵiri wa pa Cedar Point m’September 1922, nkhani yaufumu inawonekera. Patsiku lachinayi la msonkhano umenewo, lokhala ndi mutu wakuti “Tsiku,” prezidenti wa Watch Tower Society anafikitsa nkhani yake yochititsa nthumanzi pakaindeinde mwa kulengeza kuti:
8 “Tsopano tiyeni tibwerere kumunda, O ana a Mulungu Wam’mwambamwamba inu! Nyamulani zida zanu! Khalani olama, khalani amphamvu, olimbika, khalani olimba mtima. Khalani Mboni zokhulupirika ndi zowona za Ambuye. Pitani patsogolo m’nkhondoyo kufikira mbali iriyonse ya Babulo iwonongedwa. Lengezani uthenga kulikonse. Dziko liyenera kudziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu ndi kuti Yesu Kristu ndiye Mfumu ya mafumu ndi Ambuye wa ambuye. Lino ndilo tsiku lalikulu kuposa onse. Tawonani, Mfumu ikulamulira! Inu ndinu oimira ake. Chifukwa chake lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi Ufumu wake.”
Kudziŵa Yehova Mwaluntha Lokulirapo
9. (a) Chifukwa cha kuwonjezeka kwa umboni wonena za boma lachilungamo limenelo, kodi anthu ayenera kutenga mkhalidwe wotani? (b) Awo otenga mkhalidwe wolabadira akupatsidwa chidziŵitso chotani?
9 Tsopano zaka zoposa 70 zapita chiyambire pamene Kristu anaikidwa pampando wachifumu m’mphamvu ya Ufumu mu 1914. Kuyambira nthaŵiyo umboni wonena za boma la Mulungu lolungama wawonjezereka kwambiri. Anthu a dziko lokhalamo anthu afunikira kudziŵika mbali imene aimako m’nkhani ya Ufumu, kaya akuchirikiza Ufumuwo kapena kuutsutsa. Ndipo mawu awa ofunika a pangano latsopano akukwaniritsidwa kwa iwo ochirikiza boma laumulungu limenelo: “Sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziŵe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziŵa, kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo.”—Yeremiya 31:34.
10. (a) Motero kodi otsalira a Aisrayeli auzimu anayamba kuchingamira “nkhosa zina” pansi pa dzina lotani? (b) Kodi nchidziŵitso chotani chimene “nkhosa zina” zapeza?
10 Mu 1935 otsalira a Aisrayeli auzimu anayamba kuchingamira “nkhosa zina” za Mbusa Wabwino kuloŵa m’mayanjano enieni ndi iwo monga “gulu limodzi” pansi pa Yesu Kristu, pokhala iwo onse Mboni za Yehova. Pamenepo a “nkhosa zina,” amenewo anayamba kupanga “khamu lalikulu” popanda chiŵerengero chirichonse choikidwiratu, anayamba, limodzi ndi otsalira obadwa ndi mzimu, “kusunga malamulo a Mulungu” ndi kuchita ‘ntchito ya kuchitira umboni wa Yesu.’ (Chivumbulutso 7:9-17; 12:17) Motero kuyambira pachiyambi mu 1935, “nkhosa zina” zimenezi zinadziŵanso Yehova “kuyambira wamg’ono kufikira wamkulu wa iwo.”
11. Kodi chidziŵitso Chachikristu chonena za Yehova chimasiyana ndi kukhala chabwinopo motani kuposa cha Ayuda pansi pa pangano lachilamulo?
11 Komabe, kodi ndimwanjira yotani, mu imene chidziŵitso Chachikristu cha Yehova chimasiyanira ndi chabwinopo kuposa chidziŵitso chimene Ayuda anali nacho m’pangano la Chilamulo cha Mose? Wopanga pangano latsopano wakumwamba akupitirizabe kutiuza kuti: “Ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira tchimo lawo.“ (Yeremiya 31:34; Ahebri 8:12) Zimenezi ziri chifukwa chakuti pangano latsopano lazikidwa pansembe yabwinopo kupyolera mwa Mtetezi wabwinopo. (Ahebri 8:6; 9:11, 12, 22, 23) Nsembe yabwinopo ya Mtetezi wabwinopo simafunikira kubwerezedwabwerezedwa, mofanana ndi pa Tsiku Lachitetezo m’pangano lakale la Chilamulo cha Mose. (Ahebri 10:15-18) Chifukwa cha zonsezi, kudziŵa Yehova kumene okhala m’pangano latsopano ali nako kulidi kwabwinopo, kopindulitsa kwambiri, kosonyeza luntha kwambiri, kokwanira kwambiri kuposa kudziŵa Mulungu kumene Ayuda anali nako m’pangano Lachilamulo.
12. Koposa zonse, kodi ndimalo otani amene Yehova ali nawo kulinga kwa awo oloŵetsedwa m’pangano latsopano ndi olamulidwa nalo?
12 Koposa zonse, Yehova Mulungu, Wopanga Pangano, ndiye Mfumu pa awo amene akuŵaloŵetsa m’pangano latsopano ndi awo amene akulamulidwa nalo. (Mateyu 5:34, 35; Yeremiya 10:7) Zaka 1 850 Yesu asanaikidwe pampando wachifumu kukhala Mfumu kumwamba mu 1914, mtumwi Paulo anatchula ulamuliro wa Yehova pa omvera chilamulo cha pangano latsopano, kumati: “Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosawoneka, Mulungu wayekha ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthaŵi za nthaŵi. Amen.”—1 Timoteo 1:17.
Ufumu wa Zaka Chikwi Pambuyo pa “Chisautso Chachikulu”
13. (a) Kodi ndiliti ndipo ndim’mikhalidwe yotani mmene “khamu lalikulu” lidzaloŵa m’madalitso otsanuliridwa kuchokera m’pangano latsopano pamlingo wokwanira? (b) Kodi nchifuno chachikulu chotani chimene pangano latsopano lidzakhala litakwaniritsa?
13 “Khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” limene siliri m’pangano latsopano koma likulamulidwa nalo, likuyang’ana mtsogolo ku kutuluka mu “chisautso chachikulu” liri lamoyo. Pambuyo pa kuwonongedwa kwa dongosolo lazinthu loweruziridwa ku chiwonongeko liripoli, iwo adzasangalala, chifukwa cha kulamulira kwa Yesu Kristu kwa zaka chikwi, limodzi ndi oloŵa nyumba anzake padziko lapansi loyeretsedwa. (Chivumbulutso 7:9-14) Pamenepo chifuno cha pangano latsopano chidzakhala chitakwaniritsidwa, chija cha kutulutsa “mbadwa yosankhika” kukhala oloŵa nyumba a Ufumu wakumwamba. (1 Petro 2:9; Machitidwe 15:14) Kupyolera mwa Ufumu wa Mulungu, madalitso adzatsanuliridwa pamlingo wokwanira pa “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” lopulumuka. Satana Mdyerekezi ndi gulu lake losawoneka la ziŵanda adzakhala ataikidwa kuphompho ndipo sadzakhoza kudodometsa.—Chivumbulutso 21:1-4; 20:1-3.
14. Kodi ndikukonzekera kwabwino kotani kumene “khamu lalikulu” lopulumukalo lidzakhala litachita?
14 “Khamu lalikulu” la “nkhosa zina” lopulumukalo lidzakhala litakonzekera bwino lomwe kuyamba kukhala ndi moyo m’dongosolo latsopano la zinthu. Mofanana ndi otsalira a Aisrayeli auzimu, adzakhala atadziŵa Mulungu “kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo.” (Yeremiya 31:34) Popemphera kwa Mulungu, Mfumu yolamulirayo nthaŵi ina inati: “Izi zitanthauza moyo wosatha, kulandira kwawo chidziŵitso cha inu, Mulungu wowona yekha, ndi cha iye amene munamtuma, Yesu Kristu.” (Yohane 17:3, NW) Motero chidziŵitso cha chilengedwe chonse cha Yehova Mulungu chimenechi chidzachititsa chipulumutso chosatha. Zimenezi zidzakhala choncho osati kokha kwa ‘anthu’ amene adzapulumuka amoyo kupyola “chisautso chachikulu” komanso kwa anthu akufa mabiliyoni ambiri amene adzamva mawu a Mfumuyo ndi kutuluka m’manda awo a chikumbukiro. Chidziŵitso chonse cha Yehova chofunika chidzaperekedwa kwa oukitsidwa ameneŵa.—Mateyu 24:21, 22, NW; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 20:11-15.
15. Kodi nchifukwa ninji kuchitidwa kwa pangano latsopano sikudzachititsa kutayikiridwa kulikonse kwa “khamu lalikulu” la “nkhosa zina”?
15 Mwachimwemwe, kukwaniritsidwa kwa pangano latsopano la Mulungu kukhala lachipambano chokulira sikudzatulukira m’kutayikiridwa kwa “khamu lalikulu” la onga nkhosa amene apulumuka chiwonongeko cha dongosolo la zinthu loŵeruziridwa ku chiwonongeko limeneli. Mmalo mwake, kudzatsegula njira ya madalitso okulirapodi pano padziko lapansi loyeretsedwa limene adzalilandira ndi limene adzakhala akalambule bwalo m’kulisanduliza kukhala paradaiso wa dziko lonse. (Mateyu 25:34; Luka 23:43) Mwamsanga tsopano, owononga dziko lapansi kudzakhala kulibe, “Koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. . . . Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. (Salmo 37:9-11) Tonsefe titamandetu Ufumu wa Zaka Chikwi wa Yehova Mulungu kupyolera mwa “Kalonga wa Mtendere” umene utsatira kukwaniritsidwa kwa pangano latsopano!
[Chithunzi patsamba 119]
Mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi dongosolo lino lisanathe