Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kukhulupirira Ulosi wa M’Baibulo Kumapulumutsa
    Nsanja ya Olonda—2007 | April 1
    • Patangotha miyezi itatu, kazembe wachiroma wa ku Suriya, dzina lake Seshasi Galasi, akulowera kum’mwera ndi asilikali okwana 30,000 kuti akathetse kugalukirako. Gulu lakeli likufika ku Yerusalemu pa Madyerero a Misasa ndipo mwamsanga likulowerera m’madera ozungulira mzindawo. Ayuda ogalukirawo alipo ochepa motero akuthawira mu mpanda wa kachisi uja. Posakhalitsa asilikali achiroma akuyamba kugumula mpandawo. Zimenezi zikuwanyansa kwambiri Ayudawo. Akuipidwa kwambiri kuona asilikali achikunja akuipitsa malo opatulika kwambiri a chipembedzo cha Chiyuda. Koma Akhristu a mumzindawu akukumbukira mawu a Yesu akuti: ‘Mukadzaona chonyansa chosakaza chitaimirira m’malo oyera, pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira ku mapiri.’ (Mateyo 24:15, 16) Kodi Akhristuwa akhulupirira mawu a Yesu amenewa n’kuwamveradi? Zimene zichitike patsogolo pake zisonyeza kuti ayenera kumvera mawuwo kuti apulumuke. Koma kodi athawa bwanji?

      Mosayembekezereka ndiponso pachifukwa chosadziwika bwino, Seshasi Galasi anabwerera ndi asilikali ake n’kuthawira cha kunyanja, Ayudawo ali pambuyo kum’thamangitsa. M’njira yodabwitsayi, mzindawu unayamba wapuma kaye pang’ono kumavuto ake. Pokhulupirira chenjezo la ulosi wa Yesu, Akhristu akuthawa ku Yerusalemu n’kupita ku mzinda wa Pela. Mzindawu unali kumapiri a kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano ndipo sunakhudzidwe ndi nkhondoyi. Anathawa pa nthawi yake. Posakhalitsa Ayuda ogalukira aja akubwerera ku Yerusalemu ndipo akuyamba kukakamiza aliyense kulowa gulu lawo logalukiralo.a Apa n’kuti Akhristu ali phee ku Pela kudikirira kuti zinthu zitha bwanji.

  • Kukhulupirira Ulosi wa M’Baibulo Kumapulumutsa
    Nsanja ya Olonda—2007 | April 1
    • a Wolemba mbiri wina wachiyuda, dzina lake Josephus, ananena kuti Ayuda ogalukirawo anathamangitsa Aromawo kwa masiku 7 kenaka anabwerera ku Yerusalemu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena