Kuthaŵira Kopulumukira “Chisautso Chachikulu” Chisanadze
“Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, . . . iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri.”—LUKA 21:20, 21.
1. Kodi nchifukwa ninji aja amene akali mbali ya dzikoli afunikira kufulumira kuthaŵa?
ONSE amene ali a dziko la Satana afunikira kufulumira kuthaŵa. Ngati akufuna kupulumuka pamene dongosolo lilipoli la zinthu lichotsedwa padziko lapansi, ayenera kupereka umboni wokhutiritsa wakuti aimadi mosagwedera kumbali ya Yehova ndi kuti salinso a dziko limene Satana akulamulira.—Yakobo 4:4; 1 Yohane 2:17.
2, 3. Kodi ndi mafunso ati okhudza mawu a Yesu olembedwa pa Mateyu 24:15-22 amene tidzakambitsirana?
2 Mu ulosi wake waukulu wonena za mapeto a dongosolo la zinthu, Yesu anagogomezera kufunika kwake kwa kuthaŵako. Kaŵirikaŵiri timakambitsirana zolembedwa pa Mateyu 24:4-14; komanso, zimene zimatsatirapo nzofunikabe. Tikukulimbikitsani kutsegula Baibulo lanu tsopano ndi kuŵerenga mavesi 15 mpaka 22.
3 Kodi ulosi umenewo umatanthauzanji? M’zaka za zana loyamba, kodi “chonyansa cha kupululutsa” chinali chiyani? Kodi kuima kwake “m’malo oyera” kunatanthauzanji? Kodi chochitikacho chili ndi tanthauzo lanji kwa ife?
‘Iye Amene Aŵerenga Azindikire’
4. (a) Kodi nchiyani chimene Danieli 9:27 anati chidzachitika chifukwa cha kukana Mesiya kwa Ayuda? (b) Potchula zimenezo, nchifukwa ninji Yesu mwachionekere anati, ‘Iye amene aŵerenga azindikire’?
4 Onani kuti pa Mateyu 24:15 Yesu anatchula zimene zinalembedwa m’buku la Danieli. M’chaputala 9 cha bukulo muli ulosi umene unalosera za kudza kwa Mesiya ndi chiweruzo chimene anati chidzaperekedwa pa mtundu wachiyuda chifukwa cha kumkana iye. Mbali yothera ya Danieli chaputala 9 vesi 27 imati: ‘Ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula.’ Ayuda oyambirira anakhulupirira kuti mbali imeneyo ya ulosi wa Danieli inakwaniritsidwa m’zaka za zana lachiŵiri B.C.E., pamene Antiochus IV anaipitsa kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Koma Yesu anachenjeza kuti: ‘Iye amene aŵerenga azindikire.’ Kuipitsa kachisi kumene Antiochus IV anachita, ngakhale kuti kunalidi konyansa, sikunachititse chipasuko—cha Yerusalemu, kachisi wake, kapena mtundu wachiyuda. Chotero Yesu mwachionekere anali kuchenjeza omvetsera ake kuti kukwaniritsidwa kwa zimenezo sikunachitike kale koma kuti kunali mtsogolo.
5. (a) Kodi kuyerekezera nkhani za m’Mauthenga Abwino kumatithandiza motani kudziŵa “chonyansa” cha m’zaka za zana loyamba? (b) Kodi nchifukwa ninji Cestius Gallus anafulumira kupititsa asilikali a Roma ku Yerusalemu mu 66 C.E.?
5 Kodi “chonyansa” chimene iwo anayenera kukhala nacho maso nchiyani? Ndi bwino kudziŵa kuti nkhani ya Mateyu imati: ‘Mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, . . . chitaima m’malo oyera.’ Komabe, nkhani imodzimodziyo pa Luka 21:20 imati: ‘Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira.’ Mu 66 C.E., Akristu okhala m’Yerusalemu anazionadi zimene Yesu analosera. Kulimbana kotsatizanatsatizana kwa Ayuda ndi akulu a boma la Roma kunachititsa Yerusalemu kukhala chimake cha chipanduko chotsutsa Roma. Chifukwa chake, m’Yudeya yense, Samariya, Galileya, Dekapoli, ndi Foinike, mpaka kumpoto ku Suriya, ndi kummwera ku Igupto, kunabuka chiwawa. Kuti akhazikitsenso mtendere kudera limenelo la Ufumu wa Roma, Cestius Gallus anafulumira kuchotsa magulu a nkhondo ku Suriya kuwapititsa ku Yerusalemu, amene Ayuda ankatcha “mudzi wopatulika.”—Nehemiya 11:1; Yesaya 52:1.
6. Kodi zinachitikadi motani kuti “chonyansa” chopululutsa ‘chinaima m’malo oyera’?
6 Unali mwambo wa magulu a nkhondo a Roma kunyamula zizindikiro zimene iwo anaziyesa zopatulika koma zimene Ayuda anaziyesa mafano. Ndipotu, liwu lachihebri lotembenuzidwa “chonyansa” m’buku la Danieli limagwiritsiridwa ntchito makamaka pa mafano ndi kupembedza mafano.a (Deuteronomo 29:17) Ngakhale kuti Ayuda analimba, magulu a nkhondo a Roma onyamula zizindikiro zawo zamafano analoŵa m’Yerusalemu m’November wa 66 C.E. ndiyeno anayamba kukumba khoma lakumpoto la kachisi. Panalibe kukayika konse—“chonyansa” chimene chikanapululusa Yerusalemu kotheratu chinali ‘kuima m’malo oyera’! Koma kodi munthu akanathaŵa bwanji?
Kuthaŵa Kunafunika Mwamsanga!
7. Kodi gulu la nkhondo la Roma linachitanji mosayembekezereka?
7 Mwadzidzidzi ndipo pachifukwa chosadziŵika konse malinga ndi kuganiza kwa munthu, pamene Yerusalemu anaoneka kuti adzalandidwa mosavuta, magulu a nkhondo a Roma anachoka. Ayuda opanduka analondola magulu a nkhondo a Roma omabwererawo koma anangofika nawo ku Antipatri, pamtunda wa makilomita 50 kuchokera ku Yerusalemu. Ndiyeno anabwerako. Atafika m’Yerusalemu, anasonkhana m’kachisi kupangana za mmene adzamenyeranso nkhondo. Anamema anyamata kulimbitsa malinga ndi kutumikira m’gulu la nkhondo. Kodi Akristu akanatengeka ndi zimenezo? Ngakhale ngati akanapeŵa, kodi akanakhalabe m’malo angoziwo pamene magulu a nkhondo a Roma anabweranso?
8. Kodi Akristu anachitanji mofulumira kutsatira mawu aulosi wa Yesu?
8 Mwamsanga Akristu m’Yerusalemu ndi m’Yudeya monse anatsatira chenjezo la ulosi wa Yesu Kristu nathaŵa kutuluka m’malo angoziwo. Kuthaŵa kunafunika mwamsanga! M’kupita kwa nthaŵi iwo anafika kumapiri, mwinamwake ena akumakhala ku Pella, m’chigawo cha Perea. Amene analabadira chenjezo la Yesu sanabwerere mopanda nzeru kukayesa kupulumutsa chuma chawo. (Yerekezerani ndi Luka 14:33.) Pothaŵa pansi pa mikhalidwe yotero, akazi apakati ndi amayi olera ana anavutikadi ndi ulendo wa pansi umenewo. Ziletso za tsiku la Sabata sizinalepheretse kuthaŵa kwawo, ndipo ngakhale kuti chisanu chinali pafupi, chinali chisanafikebe. Posapita nthaŵi aja amene analabadira chenjezo la Yesu la kuthaŵa mwamsanga anatuluka bwinobwino kunja kwa Yerusalemu ndi Yudeya. Miyoyo yawo inadalira pa zimenezi.—Yerekezerani ndi Yakobo 3:17.
9. Kodi panapita nthaŵi yotani kufikira pamene magulu a nkhondo a Roma anabweranso, ndipo ndi zotulukapo zotani?
9 Chaka chotsatira, mu 67 C.E., Aroma anayambanso nkhondo yawo kumenyana ndi Ayuda. Choyamba, anagonjetsa Galileya. Chaka chotsatira, anapululutsa Yudeya. Podzafika mu 70 C.E., magulu a nkhondo a Roma anazinga Yerusalemu. (Luka 19:43) Njala inakula kwambiri. Aja otsekeredwa mumzindawo anayamba kuukirana. Aliyense amene anayesa kuthaŵa anaphedwa. Chimene anaona, malinga ndi kunena kwa Yesu, chinali “chisautso chachikulu.”—Mateyu 24:21, NW.
10. Ngati tiŵerenga ndi kuzindikira, kodi nchiyaninso chimene tidzaona?
10 Kodi zimenezo zinakwaniritsa zonse zimene Yesu analosera? Ayi, zina zinali kudza. Ngati, malinga ndi uphungu wa Yesu, tiŵerenga Malemba ndi kuzindikira, sitingalephere kuona zimene zikali kutsogolo. Tingalingalirenso mwamphamvu za tanthauzo lake m’moyo wathu.
“Chonyansa” Chamakono
11. Kodi ndi pamavesi ena aŵiri ati pamene Danieli akutchula “chonyansa,” ndipo ndi nthaŵi iti imene ikufotokozedwa pamenepo?
11 Dziŵani kuti, kuwonjezera pa zimene taona kale pa Danieli 9:27, palinso mawu pa Danieli 11:31 ndi 12:11 onena za “chonyansa chopululutsa.” Mavesi enawa sakulankhula za chiwonongeko cha Yerusalemu. Kwenikweni, zimene zatchulidwa pa Danieli 12:11 zikupezeka pa vesi lachiŵiri kuchokera pa limene latchula “nthaŵi ya chitsiriziro.” (Danieli 12:9) Tikukhala m’nthaŵi imeneyo kuyambira 1914. Chotero tiyenera kukhala maso kuti tidziŵe “chonyansa chopululutsa” chamakono ndiyeno kutsimikiza kuti tachoka m’malo angozi.
12, 13. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kunena kuti League of Nations ndiyo “chonyansa” chamakono?
12 Kodi “chonyansa” chamakono nchiyani? Umboni umasonyeza kuti ndi League of Nations, imene inayamba kugwira ntchito mu 1920, nthaŵi pang’ono kuchokera pamene dziko linaloŵa m’nthaŵi yake yamapeto. Koma kodi inakhala bwanji “chonyansa cha kupululutsa”?
13 Kumbukirani, liwu lachihebri la “chonyansa” limagwiritsiridwa ntchito m’Baibulo makamaka potchula mafano ndi machitachita akupembedza mafano. Kodi League imeneyo inayesedwa fano? Indedi! Atsogoleri achipembedzo anaiika “m’malo oyera,” ndipo otsatira awo anadzipereka kwa iyo ndi mtima wonse. Federal Council of the Churches of Christ (Bungwe la Matchalitchi a Kristu) ku America linalengeza kuti League imeneyo idzakhala “chizindikiro chandale cha Ufumu wa Mulungu padziko lapansi.” Nyumba ya Malamulo ya United States inalandira mulu wa makalata kuchokera ku magulu achipembedzo oilimbikitsa kuvomereza Pangano la League of Nations. Gulu la a Baptist, Congregationalist, ndi a Presbyterian ku Britain linaiyamikira kukhala “njira yokha yomwe ilipo yopezera [mtendere padziko lapansi].”—Onani Chivumbulutso 13:14, 15.
14, 15. Kodi League imeneyo ndipo pambuyo pake United Nations inakhala motani “m’malo oyera”?
14 Ufumu Waumesiya wa Mulungu unali utakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, koma mitundu inamenyera nkhondo ufulu wakudzilamulira. (Salmo 2:1-6) Pamene anati kukhale League of Nations, mitundu imene inali itangomenyako nkhondo yoyamba yadziko, limodzi ndi atsogoleri achipembedzo amene anadalitsa magulu awo a nkhondo, anali atasonyeza kale kuti anaswa lamulo la Mulungu. Sanali kuyang’ana kwa Kristu monga Mfumu. Motero anapatsa gulu laumunthulo malo a Ufumu wa Mulungu; anaika League of Nations “m’malo oyera,” malo amene sanali ake.
15 Monga yoloŵa m’malo League imeneyo, United Nations inayamba kukhalako pa October 24, 1945. Pambuyo pake, apapa a Roma anati United Nations ndiyo “chiyembekezo chokha cha umodzi ndi mtendere” ndikuti ndiyo “njira yopambana ya mtendere ndi chilungamo.” Inde, League of Nations, limodzi ndi United Nations imene inatenga malo ake, zinakhaladi fano, “chonyansa” kwa Mulungu ndi kwa anthu ake.
Kuthaŵa Chiyani?
16. Kodi okonda chilungamo afunikira kuthaŵa kutuluka m’chiyani lerolino?
16 ‘Ataona’ zimenezi, atazindikira gulu la mitundu yonse limenelo ndi mmene likupembedzedwera ngati fano, okonda chilungamo afunikira kuthaŵira kopulumukira. Kuthaŵa kutuluka muti? Kutuluka m’chimene Yerusalemu wosakhulupirikayo amaphiphiritsira m’tsiku lathu, ndiko kuti, Dziko Lachikristu, ndi m’Babulo Wamkulu yense, dongosolo lapadziko lonse la chipembedzo chonyenga.—Chivumbulutso 18:4.
17, 18. Kodi ndi chipululutso chotani chimene “chonyansa” chamakono chidzachita?
17 Kumbukiraninso kuti m’zaka za zana loyamba, pamene magulu a nkhondo a Roma ndi zizindikiro zawo zamafano analoŵa m’mzinda woyera wa Ayuda, cholinga chawo chinali kupasula Yerusalemu ndi kalambiridwe kake konse. M’tsiku lathu chipasuko sichidzangogwera mudzi umodzi, kapena Dziko Lachikristu lokha, komanso dongosolo lonse lapadziko lapansi la chipembedzo chonyenga.—Chivumbulutso 18:5-8.
18 Pa Chivumbulutso 17:16, ulosiwo umati chilombo chofiira chophiphiritsira, chimene chili United Nations, chidzatembenukira Babulo Wamkulu wonga mkazi wachigololo ndi kumuwononga moipa. Ukumagwiritsira ntchito mawu ofotokoza bwino, ulosiwo umati: “Nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiŵa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto.” Tanthauzo la zimenezi nlowopsa kulilingalira. Amenewo adzakhala mapeto a chipembedzo chonyenga cha mtundu uliwonse kumbali zonse za dziko lapansi. Zimenezi zidzasonyezadi kuti chisautso chachikulu chayamba.
19. Kodi ndi magulu otani amene akhala mbali ya United Nations kuyambira pa kupangidwa kwake, ndipo nchifukwa ninji zimenezi zachitika motero?
19 Ndi bwino kudziŵa kuti kuyambira pamene United Nations inayamba kugwira ntchito mu 1945, magulu okana Mulungu, ndi otsutsa chipembedzo akhala omveka pakati pa mamembala ake. Panthaŵi zosiyanasiyana padziko lonse lapansi, magulu otero ofuna kusintha zinthu athandiza kwambiri kuletsa pamlingo wakutiwakuti kapena kuletseratu zochita za zipembedzo. Komabe, pazaka zingapo zapitazo, maboma achepetsako ziletso zawo pa zipembedzo. Anthu ena angaganize kuti ngozi iliyonse imene chipembedzo chinalipo yatha.
20. Kodi zipembedzo za dziko zadzipangira mbiri yotani?
20 Komabe, zipembedzo za Babulo Wamkulu zikupitirizabe monga mphamvu yosokoneza dziko kwambiri. Nthaŵi zambiri mitu ya nkhani imatchula magulu othirana nkhondo ndiponso azigaŵenga mwa kugwiritsira ntchito maina a zipembedzo zawo. Apolisi oletsa chipolowe ndi asilikali aloŵa mu akachisi kukaletsa chiwawa pakati pa magulu achipembedzo omalimbana. Timabungwe tachipembedzo tapereka ndalama kuchirikiza chipanduko cha ndale. Kudana kwa zipembedzo kwalepheretsa United Nations pa kuyesayesa kwake kusungitsa chimvano pakati pa mafuko. Polondola cholinga cha mtendere ndi chisungiko, magulu ena mkati mwa United Nations akufuna kuona kuti chisonkhezero chilichonse cha chipembedzo chimene chimawapinga chatha.
21. (a) Kodi ndani adzasankha nthaŵi pamene Babulo Wamkulu adzawonongedwa? (b) Kodi chofunika kuchita mwamsanga nchiyani nthaŵiyo isanafike?
21 Palinso mbali ina yofunika kwambiri yoyenera kuilingalira. Ngakhale kuti nyanga za nkhondo za United Nations zidzagwiritsiridwa ntchito kuwononga Babulo Wamkulu, chiwonongekocho chidzakhala chiweruzo choperekedwa ndi Mulungu. Chiweruzocho chidzaperekedwa panthaŵi yoikika ya Mulungu. (Chivumbulutso 17:17) Kodi pakali pano tiyenera kuchitanji? “Tulukani mmenemo”—tulukani m’Babulo Wamkulu—likuyankha Baibulo.—Chivumbulutso 18:4.
22, 23. Kodi kuthaŵa kumeneko kumaphatikizapo chiyani?
22 Kuthaŵira kopulumukira kumeneku sindiko kuchoka kumalo enieni, monga momwe anachitira Akristu achiyuda pamene anachoka m’Yerusalemu. Ndiko kuthaŵa kuchoka m’zipembedzo za Dziko Lachikristu, inde, kuchoka m’mbali iliyonse ya Babulo Wamkulu. Sikumangotanthauza kudzilekanitsa kotheratu ndi magulu a zipembedzo zonyenga komanso ndi miyambo yake ndi mzimu umene zimachirikiza. Ndiko kuthaŵira kumalo opulumukira m’gulu lateokrase la Yehova.—Aefeso 5:7-11.
23 Nthaŵi yoyamba pamene atumiki odzozedwa a Yehova anadziŵa chonyansa chamakono, League of Nations, pambuyo pa Nkhondo Yadziko I, kodi Mboni zinatani? Zinali zitathetsa kale kugwirizana kwawo ndi matchalitchi a Dziko Lachikristu. Koma pang’ono ndi pang’ono anazindikira kuti anali kutsatirabe miyambo ina ndi machitachita a Dziko Lachikristu, monga kugwiritsira ntchito mtanda ndi kukondwerera Krisimasi ndi maholide ena akunja. Atadziŵa choonadi ponena za zinthu zimenezi, anachitapo kanthu mwamsanga. Analabadira uphungu wa pa Yesaya 52:11: “Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.”
24. Makamaka kuyambira 1935, ndaninso amene akuthaŵa?
24 Makamaka kuyambira 1935 ndi mtsogolo mwake, khamu lomakula la ena, anthu amene analandira chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso, anayamba kuchita momwemo. Iwonso ‘aona chonyansa chitaima m’malo oyera,’ ndipo akuzindikira tanthauzo lake. Atagamulapo kuthaŵa, apempha kuti maina awo afafanizidwe m’mabuku a mamembala a magulu amene ali mbali ya Babulo Wamkulu.—2 Akorinto 6:14-17.
25. Kodi chofunika nchiyani kuwonjezera pa kuthetsa unansi uliwonse umene munthu angakhale nawo ndi chipembedzo chonyenga?
25 Komabe, kuthaŵa kutuluka m’Babulo Wamkulu kumafuna zambiri osati chabe kungosiya chipembedzo chonyenga. Kumafuna zambiri osati kungopezeka chabe pamisonkhano ingapo pa Nyumba ya Ufumu kapena kupita kukalalikira uthenga wabwino mu utumiki wakumunda kamodzi kapena kaŵiri pamwezi. Mwakuthupi munthu angakhale kunja kwa Babulo Wamkulu, koma kodi wamsiyadi? Kodi wadzilekanitsa ndi dziko limene Babulo Wamkulu ali mbali yake yaikulu? Kodi amaumirirabe pa zinthu zimene zimasonyeza mzimu wake—mzimu wakunyalanyaza dala miyezo yolungama ya Mulungu? Kodi amapeputsa makhalidwe abwino ponena za kugonana ndi kukhulupirika muukwati? Kodi amakonda zinthu zaumwini ndi chuma kuposa zinthu zauzimu? Sayenera kulola kuti afanizidwe ndi dongosolo ili la zinthu.—Mateyu 6:24; 1 Petro 4:3, 4.
Musalole Chilichonse Kukupingani Pothaŵa!
26. Kodi nchiyani chidzatithandiza kusangoyamba komanso kumaliza kuthaŵa mwachipambano?
26 Pakuthaŵa kwathu kupita kopulumukira, sitiyenera kukhumbira zinthu zili kumbuyo. (Luka 9:62) Tiyenera kusumika kwambiri maganizo athu ndi mitima pa Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake. Kodi ndife otsimikiza mtima kusonyeza chikhulupiriro chathu mwa kufunafuna zimenezi choyamba, ndi chidaliro chakuti Yehova adzadalitsa njira imeneyo yakukhulupirika? (Mateyu 6:31-33) Zikhulupiriro zathu zozikidwa pa Malemba ziyenera kutisonkhezera kuchita zimenezo pamene tikuyembekezera mwachidwi kuvumbuluka kwa zochitika zazikulu padziko lapansi.
27. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kulingalirapo kwambiri pa mafunso ofunsidwa panopa?
27 Kuperekedwa kwa chiweruzo chaumulungu kudzayamba ndi chiwonongeko cha Babulo Wamkulu. Ufumu wa chipembedzo chonyenga umenewo wonga mkazi wachigololo udzachotsedwa kosatha. Nthaŵi imeneyo ili pafupi kwambiri! Kodi ife tidzaima pati monga munthu payekha pamene nthaŵi yowopsa imeneyo idzafika? Ndipo pachimake pa chisautso chachikulu, pamene mbali yotsala ya dongosolo loipa la Satana idzawonongedwa, kodi tidzapezeka kumbali iti? Ngati tichita zofunikira tsopano, chipulumutso chathu nchotsimikizirika. Yehova akutiuza kuti: “Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka.” (Miyambo 1:33) Mwa kupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ndi mwachimwemwe mkati mwa mapeto a dongosolo ili, tingayenerere kutumikira Yehova kosatha.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Insight on the Scriptures, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., Voliyumu 1, masamba 634-5.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi “chonyansa” chamakono nchiyani?
◻ Kodi ndi m’lingaliro lotani limene ‘chonyansa . . . chaima m’malo oyera’?
◻ Kodi kuthaŵira kopulumukira kumaphatikizapo chiyani lerolino?
◻ Nchifukwa ninji kuchita zimenezo kuli kofunika mwamsanga?
[Chithunzi patsamba 16]
Kuti apulumuke, otsatira a Yesu anafunikira kuthaŵa popanda kuzengereza