Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 3/1 tsamba 18-22
  • Kubala Ana Pakati pa Anthu a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubala Ana Pakati pa Anthu a Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kubala Ana mu Israyeli
  • Nthaŵi Zovuta kwa Ana mu Israyeli
  • Kubala Ana Pakati pa Akristu Oyambirira
  • ‘Chisautso m’Thupi’
  • “Nthaŵi Yotsalako Yafupikitsidwa”
  • Kubala Ana Lerolino
  • Chitsanzo cha Makedzana
  • “Nthaŵi Zovuta”
  • Thayo Lobala Ana mu Nthaŵi Ino ya Mapeto
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Khalani Nacho Chikhulupiriro ndi Chikumbumtima Chabwino
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Tifunika Kukhala Maso Kwambiri Tsopano
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 3/1 tsamba 18-22

Kubala Ana Pakati pa Anthu a Mulungu

“Yehova . . . achulukitsire chiŵerengero chanu cha lero ndi chikwi chimodzi.”​—DEUTERONOMO 1:11.

1. Ndimotani mmene Baibulo limalankhulira ponena za kubala ana?

“TAWONANI! Ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphoto yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake.” Timaŵerenga tero pa Masalmo 127:3-5. Inde, kubala ana uli mwaŵi wosangalatsa womwe Mlengi Yehova anapereka kwa anthu aŵiri oyambirira ndi mbadwa zawo.​—Genesis 1:28.

Kubala Ana mu Israyeli

2. Nchifukwa ninji mabanja a akulu anali okhumbirika pakati pa mbadwa za Abrahamu, Isake ndi Yakobo?

2 Mabanja a akulu anali kulingaliridwa kukhala okhumbika pakati pa mbadwa za Abrahamu kupyolera mwa Isake ndi Yakobo. Ngakhale ana obadwa kwa akazi achiŵiri ndi adzakazi anali kulingaliridwa kukhala alamulo. Umu ndi mmene zinaliri ndi ena a ana amuna a Yakobo, omwe anakhala atate a maziko a mafuko 12 a Israyeli. (Genesis 30:3-12; 49:16-21; yerekezani ndi 2 Mbiri 11:21.) Pamene kuli kwakuti makonzedwe oyambirira a Mulungu kaamba ka ukwati anali a mkazi mmodzi, iye analekerera mitala ndi kukwatira adzakazi pakati pa mbadwa za Abrahamu, ndipo ichi chinagwira ntchito kaamba ka kuwonjezeka kwa mwamsanga m’chiŵerengero cha anthu. Aisrayeli anayenera kukhala “anthu akuchuluka ngati fumbi lapansi.” (2 Mbiri 1:9; Genesis 13:14-16) Mkati mwa mtundu umenewo mukabwera “mbewu” yolonjezedwa kupyolera mwa amene “mitundu yonse yadziko lapansi” ikakhala yokhoza kudzidalitsa.​—Genesis 22:17, 18; 28:14; Deuteronomo 1:10, 11.

3. Nchiyani chimene chinali mkhalidwe mu Israyeli mkati mwa ulamuliro wa Solomo?

3 Mwachiwonekere, mu Israyeli kubala ana kunali kuyang’anidwa monga chizindikiro cha dalitso la Yehova. (Masalmo 128:3, 4) Chiyenera kudziŵidwa, ngakhale kuli tero, kuti mawu otsegulira a nkhaniyi, ogwidwa mawu kuchokera pa Salmo 127, analembedwa ndi Mfumu Solomo, ndipo wochulukira wa ulamuliro wa mfumu imeneyi unali mwapadera nthaŵi ya chiyanjo kwa Israyeli. Za nthaŵi imeneyo Baibulo limanena kuti: “Ayuda ndi Aisrayeli anachuluka ngati mchenga wa ku nyanja, namadya namamwa namakondwera. Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani [kumpoto] mpaka ku Beeriseba [kum’mwera], masiku onse a Solomo.”​—1 Mafumu 4:20, 25.

Nthaŵi Zovuta kwa Ana mu Israyeli

4, 5. (a) Nchifukwa ninji kubala ana nthaŵi zonse sikunali choyambitsa chimwemwe mu Israyeli? (b) Ndi zochitika zachisoni zotani zimene zinachitika pa chifupifupi zochitika ziŵiri mu Yerusalemu?

4 Koma panali nyengo zina m’mbiri ya Israyeli pamene kubala ana sikunali chinachake koma chimwemwe. Panthaŵi ya kuwonongedwa koyamba kwa Yerusalemu, mneneri Yeremiya analemba kuti: “Maso anga alefuka ndi misozi. . . . Chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m’makwalala a mudziwu. . . . Kodi akazi adzadya zipatso zawo, kunena ana amene anawaseweza?” “Manja a akazi achisoni anaphika ana awo awo.”​—Maliro 2:11, 20; 4:10.

5 Mwachiwonekere, zochitika zomvetsa chisoni zofananazo zinawoneka chifupifupi zaka mazana asanu ndi aŵiri pambuyo pake. Katswiri wodziŵa mbiri yakale wa Chiyuda Josephus anasimba kuti mkati mwa kugwidwa kwa Yerusalemu mu 70 C.E., ana analanda chakudya kuchokera pakamwa pa atate awo, ndipo amayi anatenga chakudya kuchokera pakamwa pa makanda awo. Iye akulongosola mmene mkazi wa Chiyuda anaphera mwana wake woyamwa, kuwotcha thupilo, ndi kudya mbali ya ilo. Kubweretsa ana m’dziko la Chiyuda m’zaka zomalizira zotsogolera ku kuperekedwa kwa ziŵeruzo za Yehova motsutsana ndi Yerusalemu mu 607 B.C.E. ndi 70 C.E. sikukanalongosoledwa kukhala thayo lobala ana.

Kubala Ana Pakati pa Akristu Oyambirira

6, 7. (a) Ndi machitachita otani amene Yesu anachotsa kaamba ka Akristu? (b) Ndi kupyolera mwa chiyani mmene Israyeli wauzimu akayenera kukula, ndipo nchiyani chimene chimatsimikizira chimenechi?

6 Ndimotani mmene kubala ana kunawonedwera pakati pa Akristu oyambirira? Choyamba chiyenera kudziŵidwa kuti Yesu anathetsa mitala ndi kukwatira adzakazi pakati pa ophunzira ake. Iye anakhazikitsanso muyezo woyambirira wa Yehova, wotchedwa ukwati wa mkazi mmodzi, kapena ukwati wa mwamuna mmodzi kwa mkazi mmodzi. (Mateyu 19:4-9) Pamene kuli kwakuti Israyeli wakuthupi anakhala wotchuka kupyolera m’kubala ana, Israyeli wauzimu anayenera kukula kupyolera m’kupanga ophunzira.​—Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8.

7 Ngati kufutukuka kwa Chikristu kunafunikira kubwera mokulira chifukwa cha kubala ana, Yesu sakanalimbikitsa ophunzira ake “kupanga malo” kaamba ka umbeta “chifukwa cha ufumu wa kumwamba.” (Mateyu 19:10-12) Mtumwi Paulo sakanalemba kuti: “Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita bwino koposa.”​—1 Akorinto 7:38, NW.

8. Nchiyani chimene chimasonyeza kuti ambiri a Akristu oyambirira anali okwatira ndipo anali ndi ana?

8 Komabe, pamene anali kulimbikitsa umbeta kaamba ka kuchirikiza zikondwerero za Ufumu, osati Yesu kapena Paulo anakakamiza icho. Onse aŵiri anawoneratu kuti Akristu ena adzakwatira. Mwachibadwa, ena a awa adzakhala ndi ana monga chochitika cha nthaŵi zonse. Malemba Achikristu a Chigriki ali ndi ndime zambiri zimene zinapereka kwa Akristu oyambirira uphungu wachindunji pa kulera ana. (Aefeso 6:1-4; Akolose 3:20, 21) Ngati akulu kapena atumiki otumikira ali okwatira, iwo anayenera kukhala makolo opereka chitsanzo.​—1 Timoteo 3:4, 12.

9. Mogwirizana ndi mtumwi Paulo, ndimotani mmene akazi Achikristu ena akachinjirizidwira mwa kubala ana, koma nchiyani chimene iwo akafunikira m’kuwonjezerapo?

9 Mtumwi Paulo anakhoza ngakhale kunena kuti kukhala ndi ana kukakhala chinjirizo kwa akazi ena Achikristu. Ponena za thandizo lakuthupi kwa akazi amasiye osowa, iye analemba kuti: “Koma amasiye ang’ono uwakane. . . . Ndipo aphunziranso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera. Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye ang’ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira. Pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana.” Akazi oterowo akayenera “kupulumutsidwa mwa kubala ana, ngati akhala m’chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.”​—1 Timoteo 5:11-15; 2:15.

‘Chisautso m’Thupi’

10. Ndi uphungu wosiyana wotani kaamba ka akazi amasiye umene Paulo anapereka mu kalata yake yoyamba kwa Akorinto?

10 Chiri chodziŵikiratu, ngakhale kuli tero, kuti m’kalata yake yoyamba kwa Akorinto, mtumwi Paulo mmodzimodziyo analingalira yankho losiyana kwa akazi amasiye. Iye anayeneretsa uphungu wake pa kukwatira, akumanena kuti anachipereka icho “monga mwakulola.” Iye analemba kuti: “Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine. Koma ngati sadziŵa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima. Koma akhala [mkazi wamasiye] wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndiganiza kuti inenso ndiri nawo mzimu wa Mulungu.”​—1 Akorinto 7:6, 8, 9, 40.

11. (a) Nchiyani chimene awo amene ali okwatira angakumane nacho, ndipo ndimotani mmene chilozero cha m’mphepete pa 1 Akorinto 7:28 chimawunikira pa ichi? (b) Nchiyani chimene Paulo anatanthauza pamene iye ananena kuti, “ndipo ndikulekani”?

11 Paulo analongosola kuti: “Ngati namwali akwatiwa, sanachimwa. Koma otere adzakhala nacho chisautso m’thupi, ndipo ndikulekani.” (1 Akorinto 7:28) M’chigwirizano ndi “chisautso m’thupi” chimenecho, zilozero za m’mphepete za New World Translation zimatilozera ife ku Genesis 3:16, kumene timaŵerenga kuti: “Kwa mkaziyo [Yehova] anati: ‘Ndidzachulukitsa kusauka kwako potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.’” M’kuwonjezera ku mavuto a m’banja othekera, “chisautso m’thupi” chimene awo okwatira adzakumana nacho mosakaikira chidzaphatikizapo mavuto ogwirizana ndi kubala ana. Pamene kuli kwakuti Paulo sanaletse ukwati ngakhale kubala ana, iye mwachiwonekere anadzimva wathayo kuchenjeza Akristu anzake kuti zoterozo zikabweretsa mavuto ndi zocheutsa zimene zikawatsekereza iwo mu utumiki wawo kwa Yehova.

“Nthaŵi Yotsalako Yafupikitsidwa”

12. Ndi uphungu wotani umene mtumwi Paulo anapereka kwa Akristu okwatira, ndipo kaamba ka chifukwa chotani?

12 M’zana loyamba C.E., Akristu sanali aufulu kutsogoza miyoyo yawo monga anthu a kudziko. Mkhalidwe wawo ukayambukira ngakhale moyo wawo wa mu ukwati. Paulo analemba kuti: “Koma ichi nditi, abale, yafupika nthaŵi. Tsono akukhala nawo akazi akhalebe monga ngati alibe, . . . ndi iye wakuchita nalo dziko lapansi, monga ngati wosachititsa; pakuti mawonekedwe a dziko iri apita. Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. . . . Koma ichi ndinena mwa kupindula kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye wopanda chochewukitsa.”​—1 Akorinto 7:29-35.

13. Ndi m’lingaliro lotani mmene ‘nthaŵi yotsalako inafupikitsidwira’ kaamba ka Akristu a m’zana loyamba?

13 Wophunzira Baibulo Frédéric Godet analemba kuti: “Pamene kuli kwakuti osakhulupirira amalingalira dziko kukhala lotsimikizirika kukhala ku nthaŵi yosatha, Mkristu nthaŵi zonse wakhala ndi nsonga yaikulu yoyembekezeredwa pamaso pake, Parousia [Kukhalapo].” Kristu anapatsa ophunzira ake chizindikiro cha “kukhalapo” kwake, ndipo anachenjeza iwo kuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.” (Mateyu 24:3, 42) Nthaŵi yotsalako “inafupikitsidwa” m’chakuti Akristu a m’zana loyamba amenewo anayenera kukhala mokhazikika akumayembekezera kudza kwa Kristu. M’kuwonjezerapo, iwo sanadziŵe ndi nthaŵi yochuluka yotani imene inatsala kaamba ka iwo mwaumwini “nthaŵi ndi zochitika zosawonedweratu” zisanabweretse mapeto a moyo wawo, kutsiriza kuthekera kwawo konse kwa ‘kutsimikizira chiitano chawo.’​—Mlaliki 9:11; 2 Petro 1:10.

14. (a) Ndimotani mmene Mateyu 24:19 ayenera kumvetsetsedwera? (b) Ndimotani mmene chenjezo la Yesu linatengera chisonkhezero chowonjezereka pamene chaka cha 66 C.E. chinali kuyandikira?

14 Kwa Akristu m’Yudeya ndi Yerusalemu, chifuno cha “kudikira” chinali champhamvu mwapadera. Pamene Yesu anapereka chenjezo la kuwonongedwa kwachiŵiri kwa Yerusalemu, iye ananena kuti: “Tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m’masiku amenewo!” (Mateyu 24:19) Zowona, Yesu sanauze Akristu a m’zana loyamba kuti iwo anayenera kuleka kubala ana. Iye anangopanga chabe ndemanga ya nsonga ya ulosi, kusonyeza kuti pamene chizindikiro cha kuyandikira kwa kuwonongedwa kwa Yerusalemu chidzafika, kuthaŵa kofulumira kukakhala kovuta kwambiri kwa akazi apakati kapena awo okhala ndi ana a ang’ono. (Luka 19:41-44; 21:20-23) Mosasamala kanthu za chimenecho, pamene kusakhazikika kunakula pakati pa Ayuda m’Yudeya mkati mwa zaka zotsogolera ku 66 C.E., mosakaikira chenjezo la Yesu linabwera m’maganizo mwa Akristu ndipo linasonkhezera kawonedwe kawo kulinga ku kubweretsa ana m’dziko m’nthaŵi zovuta zimenezo.

Kubala Ana Lerolino

15, 16. (a) Ndimotani mmene ‘nthaŵi yotsalako yafupikitsidwira’ kaamba ka Akristu okhalapo lerolino? (b) Kodi ndi mafunso otani amene Akristu ayenera kudzifunsa iwo eni?

15 Ndimotani mmene Akristu ayenera kuwonera ukwati ndi kubala ana lerolino, “m’nthaŵi ino ya mapeto”? (Danieli 12:4) Chiri chowona kuposa ndi kalelonse kuti “mawonekedwe a dzikoli akusintha,” kapena, monga mmene matembenuzidwe ena amachiikira icho, “makonzedwe a zinthu a nthaŵi ino akupita mofulumira.”​—1 Akorinto 7:31, Phillips.

16 Tsopano, kuposa ndi kalelonse, “nthaŵi yotsalako yafupikitsidwa.” Inde, kokha nthaŵi yochepa ikutsalira kaamba ka anthu a Yehova kumaliza ntchito imene anawapatsa iwo kuichita, yotchedwa: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Ntchito imeneyi iyenera kukwaniritsidwa mapeto asanafike. Chotero, chiri choyenerera kwa Akristu kudzifunsa iwo eni mmene kukwatira kapena, ngati ali okwatira, kukhala ndi ana kudzayambukirira kugawana kwawo m’ntchito yofunika kwambiri imeneyo.

Chitsanzo cha Makedzana

17. (a) Ndi ntchito yotani imene Nowa ndi ana ake a amuna atatu anayenera kumaliza Chigumula chisanafike, ndipo ndi utali wotani umene iyo mwachiwonekere inatenga? (b) Ndi kaamba ka zifukwa zothekera zotani zimene ana a amuna a Nowa ndi akazi awo anapewera kubala ana mkati mwa nyengo ya Chigumula chisanadze?

17 Yesu anayerekeza nthaŵi ya “kukhalapo kwa Mwana wa munthu, NW” ndi “masiku a Nowa.” (Mateyu 24:37) Nowa ndi ana ake a amuna atatu anali ndi ntchito yachindunji yoyenera kuikwaniritsa chisanafike Chigumula. Iyo inaphatikizapo kumanga chingalawa chachikulu ndi kulalikira. (Genesis 6:13-16; 2 Petro 2:5) Pamene Yehova anapereka malangizo onena za kumanga chingalawacho, ana a Nowa mwachiwonekere anali okwatira kale. (Genesis 6:18) Sitikudziŵa mwachindunji ndi utali wotani umene anatenga kumanga chingalawacho, koma chikuwoneka chachiwonekere kuti icho chinatenga zaka makumi ambiri. Mosangalatsa, mkati mwa nyengo iyi ya Chigumula chisanadze, ana a amuna a Nowa ndi akazi awo analibe ana. Mtumwi Petro mwachindunji akunena kuti ‘amoyo asanu ndi atatu anapulumutsidwa mwa madzi,’ kunena kuti, mabanja anayi okwatirana koma opanda ana. (1 Petro 3:20) Kukhala opanda ana kwa ana amunawo mwachiwonekere kunali kaamba ka zifukwa ziŵiri. Choyamba, m’chiyang’aniro cha chiwonongeko chomwe chinkadzacho mwa Chigumula cha madzi, iwo anali ndi ntchito yoikidwa mwaumulungu kuchita yomwe inafunikira chisamaliro chawo chosagawanika. Chachiŵiri, iwo mosakaikira sanadzimve kukhala ndi chikhoterero cha kubweretsa ana m’dziko limene “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha,” dziko “lodzala ndi chiwawa.”​—Genesis 6:5, 13.

18. Ngakhale kuti sanakhazikitse lamulo loyenera kutsatira, ndimotani mmene njira yotengedwa ndi ana a amuna a Nowa ndi akazi awo ingapereke chakudya kaamba ka malingaliro?

18 Uku sindiko kunena kuti njira ya kachitidwe yotengedwa ndi ana a amuna a Nowa ndi akazi awo chisanachitike Chigumula inatanthauzidwa kukhazikitsa lamulo kaamba ka anthu okwatirana okhala m’tsiku lino. Mosasamala kanthu za chimenecho, popeza Yesu anayerekeza tsiku la Nowa ku nyengo imene tikukhalamo tsopano, chitsanzo chawo chingapereke chakudya kaamba ka malingaliro.

“Nthaŵi Zovuta”

19. (a) Ndimotani mmene nthaŵi zathu zimafananira ndi tsiku la Nowa? (b) Nchiyani chimene Paulo ananeneratu ponena za “masiku otsiriza,” ndipo ndimotani mmene ulosi wake ukugwirizanirana ndi kubala ana?

19 Mofanana ndi Nowa ndi banja lake, tikukhalanso mu “dziko la anthu opanda umulungu.” (2 Petro 2:5) Mofanana ndi iwo, tiri mu “masiku otsiriza” a dongosolo iri loipa la kachitidwe ka zinthu lomwe liri pafupi kuwonongedwa. Mtumwi Paulo analosera kuti “masiku otsiriza” a dongosolo la kachitidwe ka zinthu ka Satana akabweretsa “nthaŵi zovuta kuchita nazo.” Kusonyeza kuti kulera ana kukakhala chimodzi cha zinthu zovuta kuchita nazo, iye anawonjezera kuti ana adzakhala “osamvera akuwabala.” Iye ananena kuti anthu mwachisawawa, osachotsapo ana ndi anamwali, adzakhala “osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadidwe.” (2 Timoteo 3:1-3) Pamene Paulo pano anali kulosera za mikhalidwe pakati pa anthu a kudziko, mwachidziŵikire mikhalidwe yofala imeneyo ikapangitsa kulera kwawo ana kukhala kovuta kwambiri kwa Akristu, monga mmene ena akumanira nazo.

20. Nchiyani chimene chidzalingaliridwa m’nkhani yotsatira?

20 Zochitika zonsezi zikusonyeza kuti chiri choyenera kukhala ndi kawonedwe kolinganizika ka kubala ana. Pamene kuli kwakuti kungabweretse chimwemwe chambiri, iko kungabweretsenso kuwaŵidwa mtima kochuluka. Kuli ndi maubwino ake ndi kuipa kwake. Zina za izi zidzalingaliridwa m’nkhani yotsatira.

Nsonga za Kubwereramo

◻ Nchifukwa ninji mabanja a akulu anali okhumbirika mu Israyeli?

◻ Nchiyani chimene chikusonyeza kuti panali nthaŵi pamene kubala ana kunabweretsa kuwaŵidwa mtima kwa Ayuda?

◻ Ndimotani mmene Israyeli wauzimu akakulira m’chiŵerengero?

◻ Ndimotani mmene ‘nthaŵi yotsalako inafupikitsidwira’ kaamba ka Akristu oyambirira?

◻ Ndi zifukwa zothekera zotani zimene ana a amuna a Nowa ndi akazi awo anakhalira opanda ana chisanadze Chigumula, ndipo bwanji ponena za mkhalidwe lerolino?

[Chithunzi patsamba 21]

Kuthaŵa kofulumira kuchoka ku Yerusalemu kukakhala kovuta kwambiri kwa awo okhala ndi ana a ang’ono

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena