Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chizindikiro—Kodi Mukuchilabadira Icho?
    Nsanja ya Olonda—1988 | October 15
    • Pamene nthaŵi yovuta imeneyo ifika, kodi malo anu adzakhala otani? Kodi mudzasiidwa ku chiwonongeko, kapena kodi mudzatengedwa kaamba ka kupulumuka? Kukutsogozani inu m’njira yolondola, lingalirani kachiŵirinso fanizo limene Yesu anapereka: “Pamene pali mtembo, pomweponso [ziwombankhanga, NW] zidzasonkhanidwa konko.”​—Luka 17:34-37; Mateyu 24:28.

      Yesu chotero anali kugogomezera kufunika kwa kukhala ndi kachitidwe kowona patali, kogwirizana. Awo otengedwa kaamba ka chipulumutso ali amene amasonkhana pamodzi mokhazikika ndi kupindula kuchokera ku kuleredwa kwauzimu kumene Mulungu amapereka. Mamiliyoni angapo apeza kuti kudya kwauzimu koteroko kumachokera ku kuyanjana kwathithithi ndi umodzi wa mipingo yoposa 55,000 ya Mboni za Yehova ndi kupyolera m’kuphunzira zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo zonga ngati chimene mukuŵerengachi.

  • Ziwombankhanga Kapena Miimba?
    Nsanja ya Olonda—1988 | October 15
    • Ziwombankhanga Kapena Miimba?

      Chizindikiro

      “KULIKONSE kumene kuli mtembo, kumeneko ziwombankhanga zidzasonkhana.” (Mateyu 24:28, NW) M’mwalo mwa kuphunzira kuchokera ku fanizo limeneli, ena amapeza zophophonya ndi ilo. Iwo amanena kuti ziwombankhanga ziri zosaka zamphamvu zomwe zimadya zinthu zamoyo, osati mitembo. Chotero, maBaibulo ena amagwiritsira ntchito liwu lakuti “miimba.” Koma liwu la Chigriki lomwe liri mu funso a-e-tos’, latembenuzidwa molondola kukhala “chiwombankhanga.”

      Mtundu umodzi wopezedwa mu Israyeli uli chiwombankhanga chofiira modera pang’ono. “Monga mbalame zambiri zakudya nyama,” awona tero John Sinclair ndi John Mendelsohn, “chiwombankhanga chofiira modera pang’ono sichimanyansidwa ndi mtembo ndipo chiri mwa kaŵirikaŵiri pakati pa choyamba kufika pa nyama yophedwa kumene.” Wowona wina anasimba za kusonkhanitsidwa kwa ziwombankhanga zina 60 za mawangamawanga ndi zofiira modera pang’ono mu Kalahari ya Africa. Iye wawonjezera kuti: “Chiwombankhanga Chofiira modera pang’ono chiri cholamulira pamene chifika pa mtembo. M’zochitika zambiri mbalame ziŵririzi, mwinamwake banja, zawonedwa kukhala zikugawana chophedwacho.”

      Ziwombankhanga za m’nyanja (nkhwazi) zirinso zofala m’maiko a ku Mediterranean. M’mazana a kumbuyo, ziwombankhanga za m’nyanja ndi ziwombankhanga za pa mtunda zinadya pa mitembo ya akavalo ophedwa mu nkhondo. “Chadziŵidwa bwino lomwe . . . kuti izo zimatsatria magulu ankhondo kaamba ka chifukwa chimenecho,” yalongosola tero McClintock ndi Strong’s Cyclopædia.

      Pokhala zaliŵiro ndi zowona patali, ziwombankhanga nthaŵi zina zimakhala mbalame zoyamba kufika pa mtembo wakufa. Yesu anali wozoloŵerana ndi kulongosola kumene Yehova Mulungu anafunsa Yobu funso lopyoza iri: “Kodi ndi pa lamulo lako pamene chiwombankhanga chimawuluka m’mwamba ndi pamene chimamanga chisa chake m’mwamba, . . . pamwamba pa mwala ndi pamalo osafikirika? Kuchokera kumeneko ifunikira kufufuza zakudya; kutali maso ake amawona. . . . Kumene kuli mtembo, kumeneko chimakhala.”​—Yobu 39: 27-30.

      Chotero, Yesu anachitira fanizo bwino kuti kokha awo okhala ndi diso lophiphiritsira la chiwombankhanga akakhoza kupindula kuchokera ku chizindikiro.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena