Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 6/1 tsamba 28
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Nthaŵi ya Kudikira
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Opulumuka ku “Mbadwo Woipa”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kodi Kukhalapo kwa Khristu Kumatanthauza Chiyani kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 6/1 tsamba 28

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

“Nsanja ya Olonda” ya November 1, 1995, inafotokoza zimene Yesu ananena pa “mbadwo uwu,” monga momwe timaŵerengera pa Mateyu 24:34. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti pali kukayikira kwina kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914?

Nkhaniyo mu Nsanja ya Olonda sinasinthe kalikonse pachiphunzitso chathu chofunika chonena za 1914. Yesu analongosola chizindikiro chosonyeza kukhalapo kwake m’mphamvu ya Ufumu. Tili ndi umboni wokwana bwino wakuti chizindikiro chimenechi chakhala chikukwaniritsidwa chiyambire 1914. Maumboni onena za nkhondo, njala, miliri, zivomezi, ndi maumboni ena amatitsimikiza kuti chiyambire 1914, Yesu wakhala akugwira ntchito monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Zimenezi zikusonyeza kuti kuchokera pamenepo takhala m’mapeto a dongosolo la zinthu.

Choncho, kodi nchiyani chimene Nsanja ya Olonda inali kumasulira? Eya, mfundo yake inali lingaliro limene Yesu anagwiritsirira ntchito liwu lakuti “mbadwo” pa Mateyu 24:34. Vesilo limati: “Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.” Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anati “mbadwo,” ponse paŵiri m’tsiku lake ndi m’tsiku lathu?

Malemba ambiri amatsimikiza kuti Yesu sanagwiritsire ntchito liwulo “mbadwo” kunena za gulu lina laling’ono kapena gulu lakutilakuti, kutanthauza atsogoleri achiyuda okha kapena ophunzira ake okhulupirika okha. M’malo mwake, anagwiritsira ntchito liwulo “mbadwo” potsutsa makamu a Ayuda amene anamkana. Komabe, mwamwaŵi anthu akanachita zimene mtumwi Petro analimbikitsa patsiku la Pentekoste, kulapa ndi ‘kudzipulumutsa kwa mbadwo uno wokhotakhota.’​—Machitidwe 2:40.

Ndi mawuwo, ndithudi Petro sanali kunena za anthu a msinkhu wakutiwakuti kapena nyengo yakutiyakuti, ndipo sanalinso kugwirizanitsa “mbadwo” ndi deti lina lililonse. Sananene kuti anthu ayenera kupulumutsidwa ku mbadwo umene unabadwa m’chaka chimodzimodzi chimene Yesu anabadwa kapena mbadwo umene unabadwa mu 29 C.E. Petro anali kunena za Ayuda osakhulupirira a nthaŵiyo​—ena mwina anali aang’ono, ena aakulu​—amene anamva ziphunzitso za Yesu, anaona kapena kumva za zozizwitsa zake, ndipo sanamlandire monga Mesiya.

Mwachionekere ndimo mmene Petro anamvera liwulo “mbadwo” malinga ndi mmene Yesu analigwiritsirira ntchito pamene iyeyo ndi atumwi ena atatu anali ndi Yesu pa Phiri la Azitona. Malinga ndi mawu aulosi a Yesu, Ayuda a panthaŵiyo​—makamaka amene analiko panthaŵi ya Yesu​—anali kudzaona kapena kudzamva za nkhondo, zivomezi, njala, ndi maumboni ena akuti mapeto a dongosolo lachiyuda ayandikira. Kwenikweni, mbadwo umenewo sunathe chiwonongeko chisanadze mu 70 C.E.​—Mateyu 24:3-14, 34.

Tiyenera kuvomera kuti si mmene takhala tikuwamvera mawu a Yesu amenewo. Anthu opanda ungwiro amafuna kudziŵa deti lenileni pamene mapeto adzafika. Kumbukirani kuti ngakhale atumwi anafuna kudziŵa nthaŵi yeniyeni, nafunsa kuti: ‘Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?’​—Machitidwe 1:6.

Pokhala ndi zolinga zoona mtima zofananazo, atumiki a Mulungu amakono ayesa, mwa kugwiritsira ntchito zimene Yesu ananena pa “mbadwo,” kupeza nthaŵi yeniyeni mwa kuŵerengera nthaŵi kuyambira 1914. Mwachitsanzo, ankalingalira kuti mbadwo ungakhale zaka 70 kapena 80, wa anthu okalamba ndithu amene akudziŵa bwino tanthauzo la nkhondo ya dziko yoyamba ndi zochitika zina; choncho tikhoza kuŵerengera kuti mapeto ayandikira kufika chapati.

Komabe, ngakhale kuti kulingalira kumeneko kunali ndi zolinga zabwino, kodi kunagwirizana ndi uphungu umene Yesu anapereka pambuyo pake? Yesu anati: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha. . . . Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.”​—Mateyu 24:36-42.

Chotero chidziŵitso chaposachedwapa cha mu Nsanja ya Olonda chonena za “mbadwo uwu” sichinasinthe kamvedwe kathu ka zimene zinachitika mu 1914. Koma chinatipatsa kamvedwe kabwino ka mmene Yesu anagwiritsirira ntchito liwu lakuti “mbadwo,” kutithandiza kuona kuti njira imene analigwiritsirira ntchito si maziko oŵerengera zaka​—kuyambira mu 1914​—pofuna kuona kuti tili pafupi motani ndi mapeto.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena