Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 12/15 tsamba 30
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • “Mubwere Nalo Limodzi Limodzi Lonse la Khumi ku Nyumba Yosungiramo”
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yopereka Chakhumi?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • “Tapeza Ife Mesiya”!
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Madalitso a Yehova Alemeretsa
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 12/15 tsamba 30

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwasangalala kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati mwatero, mosakaikira mudzakupeza kukhala kokondweretsa kukumbukira zotsatirazi:

▫ Kodi ndiumboni wokhutiritsa maganizo wotani umene unaperekedwa mwakugwira ntchito kosiyanasiyana kwa mzimu woyera m’zaka za zana loyamba?

Kugwira ntchito kumeneko kunapereka umboni wowoneka wakuti Mulungu sanali kugwiritsiranso ntchito mpingo wa Israyeli wa zaka 1,500 monga anthu ake apadera, koma chivomerezo chake tsopano chinali pa mpingo watsopano Wachikristu, wokhazikitsidwa ndi Mwana wake wobadwa yekha. (Yerekezerani ndi Ahebri 2:2-4.)​—8/15, tsamba 5.

▫ Kodi chachititsa chiwonjezeko chodabwitsa chimene Mboni za Yehova zakhala nacho nchiyani?

Kwakukulukulu, izi ziri chifukwa cha dalitso la Mulungu. Iri ntchito ya Mulungu. Zimene Mboni za Yehova zimaphunzitsa m’ntchito yawo yolalikira zimachokera m’Baibulo. Mfungulo ina yachipambano chawo ndiyo kuvomereza kwawo kotheratu Kristu Yesu monga Mutu woikidwa wa mpingo Wachikristu.​—9/1, tsamba 19.

▫ Kodi nchifukwa ninji Yehova anasonyeza Davide chifundo ponena za tchimo lake lalikulu ndi Batiseba?

Izi zinali kwakukulukulu chifukwa chapangano la Ufumu limene Mulungu anapangana ndi Davide, koma kunalinso chifukwa cha mkhalidwe wa chifundo wa Davide mwiniyo ndi kulapa kwake kowona mtima. (1 Samueli 24:4-7; 2 Samueli 7:12; 12:13; Salmo 51:1, 2, 17)​—9/15, tsamba 10, 11.

▫ Kodi ndimitundu itatu yamaumboni iti imene Malemba Achikristu Achigiriki amapereka kuchirikiza Umesiya wa Yesu?

Umboni woyamba ndiwo mzera wa makolo a Yesu. (Mateyu 1:1-16; Luka 3:23-38) Umboni wina ndiwo maulosi okwaniritsidwa. Pali maulosi ambirimbiri, monga umene umapezeka pa Danieli 9:25, umene umatchula Yesu kukhala Mesiya. Mtundu wachitatu wa umboni ndiwo kuchitira umboni kwa Mulungu mwini; Iye anapereka umenewu panthaŵi zitatu mwa mawu a iye mwini. (Mateyu 17:5; Luka 3:21, 22; Yohane 12:28)​—10/1, tsamba 10, 12.

▫ Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anati, monga momwe kwalembedwera pa Mateyu 24:37: “Monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa mwana wa munthu”?

Nowa anali kumanga chingalawa ndipo anali kuchenjeza oipa kwa nyengo ya zaka makumi angapo Chigumula chisanadze ndi kusesa dongosolo ladziko loipa. Mofananamo, kukhalapo kosawoneka kwa Kristu kumatenga nyengo ya zaka makumi angapo, pamene umboni wadziko lonse ukuperekedwa nakonso kusanathere m’chiwonongeko chachikulu.​—10/1, tsamba 16.

▫ Kodi nzofunika zina ziti za phunziro la Baibulo la banja labwino?

Nthaŵi ifunikira kuomboledwa yakuchita phunziro. Sitikalola kuti nthaŵiyo ilowedwe mmalo ndi zododometsa za TV kapena zocheukitsa zina. Zosoŵa zenizeni za banja ziyenera kulingaliridwa. Gwiritsirani ntchito mafunso alingaliro kutsimikizira kuti anawo akuzindikira zimene akuphunzira. (Mateyu 17:25) Sungani mkhalidwewo uli wabata. Khalani wotenthedwa maganizo, ndipo phatikizani aliyense m’phunzirolo.​—10/15, tsamba 17.

▫ Kodi Akristu ayenera kukhala odera nkhaŵa motani kuti nsanganizo za mwazi zaphatikizidwa kuzakudya?

Akristu ayenera kukhala maso kuti asavutike maganizo ndi kuthekera kokha kapena mphekesera, ndipo kusachita mopambanitsa kuli kofunika ngakhale pakupenda malebulo kapena pofunsa eni mabutchala. Komabe, ngati kuli kodziŵika kuti magazi amagwiritsidwa ntchito kwambiri m’chitaganyacho​—kaya m’chakudya kapena m’mankhwala akuchipatala​—Akristu ayenera kukhala osamala kumvera lamulo la Mulungu lakusala mwazi. (Machitidwe 15:28, 29)​—10/15, tsamba 30-1.

▫ Kodi ndimotani mmene bukhu la Miyambo limagogomezera kuzama kwauzimu kwa njira zakuphunzitsa zogwiritsidwa ntchito mu Israyeli?

Bukhu la Miyambo limasonyeza kuti chifuno chake chinali kuphunzitsa “opanda chidziŵitso” zinthu zapamwamba zonga nzeru, mwambo, kuzindikira, chidziŵitso, chiweruzo, kuchenjera, kudziŵa ndi luntha​—zonsezi ziri mu “kuwopa Yehova.” (Miyambo 1:1-7; 2:1-14)​—11/1, tsamba 12.

▫ Kodi ndilingaliro losankitsa lotani lamaphunziro limene achichepere ayenera kukhala nalo lerolino?

Akristu ayenera kuwona maphunziro monga njira yogwiritsidwa ntchito kufikira chonulirapo chokhumbidwa. Chifuno chawo m’masiku ano otsiriza ndicho kutumikira Yehova kwambiri ndi mogwira mtima monga momwe kungathekere mu utumiki wanthaŵi yonse ngati angakhoze.​—11/1, tsamba 18.

▫ Kodi nchifukwa ninji Yehova anafuna kuti mtundu wa Israyeli ulipire zakhumi?

Choyamba, kuti akasonyeze mwanjira yowoneka kuyamikira kwawo ubwino wa Yehova. Chachiŵiri, kuti athandizire kuchirikizidwa kwa Alevi, amene pamenepo akakhoza kusumika maganizo pamathayo awo, kuphatikizapo kuphunzitsa Chilamulo. (Wonani 2 Mbiri 17:7-9.)​—12/1, tsamba 9.

▫ Kodi chakhumi nchiyani chimene Akristu akupemphedwa kubwera nacho? (Malaki 3:10)

Chakhumi chimaimira gawo la zinthu zathu limene timabwera nalo kwa Yehova kapena kuligwiritsira ntchito mu utumiki wake. Limeneli liri chisonyezero cha kumkonda kwathu ndi kuzindikira kwathu kuti ndife ake.​—12/1, tsamba 15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena