Kukhala Olinganizidwa Kaamba ka Kupulumuka Kuloŵa m’Zaka Chikwi
“Zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.”—YOHANE 10:16.
1. Kwa Mulungu wokhalako nthaŵi zonse, kodi zaka chikwi ziri ngati chiyani?
YEHOVA ali Mlengi wa nthaŵi kaamba ka mtundu wa anthu. Ndipo kwa iye, Mulungu wosafa yemwe ali kuchokera ku nthaŵi zosayamba kufikira ku nthaŵi zosatha, zaka chikwi ziri kokha ngati tsiku lomapita mofulumira kapena kokha nyengo yochepera ya koloko mkati mwa umodzi wa usiku wathu.—Salmo 90:4; 2 Petro 3:8.
2. Kodi ndi nyengo yotani ya nthaŵi imene Yehova waika pambali kaamba ka kudalitsa mtundu wonse wa anthu?
2 Mulungu wakhazikitsa tsiku lophiphiritsira la zaka chikwi mkati mwa limene iye adzadalitsa mabanja onse a dziko lapansi. (Genesis 12:3; 22:17, 18; Machitidwe 17:31) Ichi chimaphatikiza awo omwe ali akufa tsopano ndi omwe adakali amoyo. Kodi ndimotani mmene Mulungu adzachitira chimenechi? Nkulekeranji, chidzakhala kupyolera mwa Ufumu Wake mwa Yesu Kristu, “mbewu” ya mkazi Wake wophiphiritsira!—Genesis 3:15.
3. (a) Kodi ndimotani mmene chitende cha Mbewu ya mkazi wa Mulungu chinalalidwira, koma kodi ndimotani mmene bala limenelo linapoletsedwera? (b) Pamapeto pa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu, kodi nchiyani chimene iye adzachita ku njoka yophiphiritsira?
3 Chitende chophiphiritsira cha Mbewu ya mkazi wa Mulungu (kapena gulu lakumwamba) chinalaliridwa pamene Yesu Kristu anavutika ndi imfa yophedwera chikhulupiriro ndi kukhala wakufa kwa mbali za masiku atatu m’chaka cha 33 cha Nyengo yathu Yachisawawa. Koma pa tsiku lachitatu, Mulungu Wamphamvuyonse, Mpatsi Wamkulu wa Moyo, anachiritsa bala limenelo mwa kuwukitsa Mwana wake wokhulupirira ku moyo wosafa m’mbali yamizimu. (1 Petro 3:18) Popeza kuti Yesu sadzafanso, iye ali m’malo a kulamulira monga Mfumu pa mtundu wa anthu kwa zaka chikwi ndi “kulalira” mutu wa njoka yophiphiritsira, kumuchotseratu iye pambuyo pa mapeto a Kulamulira kwa Zaka Chikwi. Limenelo lidzakhala dalitso lotani nanga kaamba ka mtundu wa anthu okhulupirika obwezeretsedwa!
4. Kodi ndi mtundu wotani wa programu imene Mulungu wakhala akuchita ndi anthu ake?
4 Kulinganiza kwakukulu kwakhala kukuchitidwa pakati pa anthu a Yehova dziko lonse lapansi mkati mwa “mapeto a dongosolo lazinthu” iri chiyambire kutha kwa Nthaŵi za Akunja mu 1914. (Mateyu 24:3, NW; Luka 21:24, King James Version) Programu ya gulu imeneyi yoyambirira ku Zaka Chikwi ikuchitidwa mogwirizana ndi chifuniro ndi pansi pa chitsogozo cha Wolinganiza Wamkulu, Yehova Mulungu. Kupyolera mwa mkazi wake, gulu lake lakumwamba longa mkazi, kubadwa kwa Ufumu wake wolonjezedwa kupyolera mwa Yesu Kristu kunachitika mu 1914, monga momwe kunatsimikiziridwa ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo.
5. Kodi ndi kubadwa kwa chiyani komwe kunanenedweratu pa Chibvumbulutso 12:5, ndipo kodi ndi liti pamene ichi chinalongosoledwa choyamba mu Nsanja ya Olonda?
5 Chotero omwe akwaniritsidwa mwaulemerero ali mawu awa a Chibvumbulutso 12:5: “Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi ku mpando wachifumu wake.” Kubadwa kwa Ufumu wa Yehova kupyolera mwa Kristu, monga momwe kwachitiridwa chithunzi ndi mwana wobadwa chatsopano wa mkazi wa Mulungu, kunalongosoledwa choyamba mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1925. Kubadwa kwa Ufumu Waumesiya umenewu m’mwamba mu 1914 kumasiyana ndi kubadwa kwa “mtundu” wa ‘ana’ a Zioni pa dziko lapansi mu 1919.—Yesaya 66:7, 8.
6. (a) Kodi kubadwa kwa Ufumu kunaitanira kaamba ka ntchito yotani yonenedweratu ndi Yesu? (b) Kodi kuchita ntchito imeneyi kunaitanira kaamba ka chiyani ku mbali ya anthu a Yehova, ndipo kodi ndi mtundu wotani wa kupita patsogolo umene iwo tsopano akuwunikira?
6 Kubadwa kwa Ufumu wa Yehova kupyolera mwa umene iye adzakweza ulamuliro wake wolondola pa chilengedwe chaponseponse—aha, pano panali chinachake chomwe chinafunikira kulengezedwa m’dziko lonse lapansi! Ndipo tsopano inali nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa mawu awa a Yesu onena za zitsimikiziro za “kukhalapo” kwake kosawoneka: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:3, 14, NW) Kulalikira kogwirizana, komvana pa mlingo wa mitundu yonse, m’dziko lonse lapansi ndithudi kukaitanira kaamba ka kulinganiza mbali yowoneka ndi maso ya gulu la Yehova la chilengedwe chaponseponse. Watch Tower Bible and Tract Society, monga momwe inaimiridwa ndi yemwe pa nthaŵiyo anali prezidenti wake, J. F. Rutherford, inayanja chimenechi. Chotero, kuyambira m’chaka cha pambuyo pa nkhondo cha 1919, kulinganiza kwa achilikizi okhulupirika a Sosaite monga mtundu wobwezeretsedwa kunapita patsogolo mogamulapo, ndi pemphero kaamba ka chitsogozo ndi dalitso la Wolinganiza Wamkulu, Yehova Mulungu. Poyang’anizana ndi Nkhondo ya Dziko ya II, mosasamala kanthu za chizunzo choipitsitsa chochitidwa ndi Magulu Ankhanza, gulu la Nazi la Hitler, ndi Kachitidwe ka Chikatolika, Mboni za Yehova dziko lonse lapansi zinawunikira kupita patsogolo kogwirizana ku dziko la mdani.
7. (a) Ndi kokha mwa kukhala mu unansi wotani ndi wina ndi mnzake mmene anthu a Yehova angayembekezere kupulumuka chisautso chachikulu? (b) Kodi ndimotani mmene opulumuka Chigumula anapyolera Chigumula cha chiwunda chonse, ndipo kodi iwo anaimira ndani?
7 Kokha Mboni za Yehova, awo a otsalira odzozedwa ndi “khamu lalikulu,” monga gulu logwirizana pansi pa chitetezero cha Wolinganiza Wamkulu, ndi amene ali ndi chiyembekezo chirichonse cha m’Malemba cha kupulumuka mapeto oyandikira a dongosolo lowukiridwa iri lolamulidwa ndi Satana Mdyerekezi. (Chibvumbulutso 7:9-17; 2 Akorinto 4:4) Iwo adzapanga gulu la “munthu” amene Yesu Kristu ananena kuti akapulumutsidwa kupyola chisautso chachikulu choipitsitsa cha mbiri yonse ya anthu. Monga momwe zinaliri m’masiku a Nowa, anatero Yesu, zidzakhalanso tero m’tsiku limene Iye adzavumbulidwa. Mkati mwa chingalawa chomwe chinatenga zaka zambiri za kuyesayesa kolinganizidwa kuchitsiriza, kokha miyoyo ya anthu isanu ndi itatu inapulumuka Chigumula cha dziko lonse. Iwo anapulumuka monga gulu la banja logwirizana. (Mateyu 24:22, 37-39, NW; Luka 17:26-30) Mkazi wa Nowa amafaniziridwa ku mkwati wa Kristu, ndipo ana ake aamuna ndi apongozi ake kwa “nkhosa zina” za Yesu zamakono, zomwe zakula kukhala khamu lalikulu lomawonjezerekawonjezereka, chiŵerengero chotsirizira tsopano sitikuchidziŵa. (Yohane 10:16) Kuti apulumuke kuloŵa m’Zaka Chikwi pansi pa Nowa Wamkulu, Yesu Kristu, iwo afunikira kukhala olinganizidwa ndi otsalira odzozedwa, “osankhidwa” kwa amene masiku a “chisautso chachikulu” adzafupikitsidwa.—Mateyu 24:21, 22.
Kupulumuka Kuloŵa m’Zaka Chikwi
8. M’kutsiriza ulosi wake wonena za kukhalapo kwake, kodi ndi fanizo lotani limene Yesu anapereka, ndipo kodi ndimotani mmene deti la June 1, 1935, linaliri lapadera ponena za kulimvetsetsa?
8 Mogwirizana ndi Uthenga Wabwino wa Mateyu, Yesu anamaliza ulosi wake ndi chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi fanizo. Lodziŵitsidwa mofala kukhala fanizo la nkhosa ndi mbuzi, ilo limagwira ntchito tsopano, mkati mwa mapeto a dongosolo la zinthu iri, lomwe linayamba pamapeto pa Nthaŵi za Akunja mu 1914. (Mateyu 25:31-46) Deti la Loŵeruka, June 1, 1935, linali lapadera ponena za kumvetsetsa kwa chizindikiritso cha nkhosa za fanizoli kukhala ziŵalo za khamu lalikulu. Pa tsiku limenelo, pa msonkhano wa Mboni za Yehova mu Washington, D.C., anthu 840 anabatizidwa m’kuchitira chithunzi kudzipereka kwawo kwa Yehova Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu. Unyinji wa amenewa unatenga kachitidwe kameneka m’kuyankha mofulumira ku nkhani ya pa Chibvumbulutso 7:9-17 yoperekedwa ndi J. F. Rutherford. Chinali chikhumbo chawo cha kukhala mbali ya khamu lalikulu la Mbusa Wabwino wa nkhosa zina, kukhala ndi mwaŵi wa kupulumuka chisautso chachikulu chikudzacho ndi kukhala ndi moyo kupyola mapeto a dongosolo iri ndi kupitirizabe kuloŵa m’Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Mbusa ndi Mfumu, Yesu Kristu. Potsirizira pake, iwo adzafikira moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi.—Mateyu 25:46; Luka 23:43.
9. Kodi nchifukwa ninji nkhosa zikuitanidwa kuloŵa “ufumu wokonzedwera kwa [iwo],” ndipo kodi ndimotani mmene iwo aliri m’malo abwino kwambiri akuchita zabwino kwa abale a Mfumuyo?
9 Kodi nchifukwa ninji onga nkhosa amenewa akuitanidwa “kuloŵa mu ufumu wokonzedwera kwa [iwo] pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi”? Mfumuyo ikuwawuza iwo kuti chiri chifukwa chakuti iwo anachita zabwino kwa “abale” ake, ndipo mwakutero anachita chimenecho kwa iye. Ndi mawu akuti “abale,” Mfumuyo ikutanthauza otsalira a abale ake auzimu omwe adakali pa dziko lapansi m’mapeto ano a dongosolo la zinthu. Pokhala gulu limodzi ndi abale amenewa a Mbusa ndi Mfumu, Yesu Kristu, iwo akakhala mu unansi wathithithi wothekera ndi otsalira oterowo ndipo mwakutero akakhala m’malo abwino koposa a kuchita zabwino kwa iwo. Ngakhale m’njira ya zinthu zakuthupi, iwo akathandiza abale a Yesu kulalikira uthenga wa Ufumu wokhazikitsidwa dziko lonse mapeto asanadze. M’chiyang’aniro cha ichi, nkhosa zikawona kukhala wa mtengo wapatali mwaŵi wawo wa kukhala olinganizidwa ndi otsalira monga gulu limodzi la Mbusa mmodzi.
10. Kodi chimatanthauzanji kaamba ka nkhosa “kuloŵa mu ufumu wokonzedwera kwa [iwo] pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi”?
10 Kuloŵa mu “ufumu wokonzedwera kwa [iwo]” sikukutanthauza kuti nkhosa zimenezi zidzalamulira ndi Yesu Kristu ndi abale ake m’mwamba kwa zaka chikwi. M’malomwake, kuchokera pachiyambi penipeni pa Zaka Chikwi, nkhosazo zidzaloŵa mbali ya dziko lapansi ya Ufumuwo. Popeza kuti iwo ali mbadwa za Adamu ndi Hava, mbali ya dziko lapansi imeneyi imene Ufumu wa Mulungu kupyolera mwa Kristu udzatenga inakonzekeretsedwa kaamba ka iwo kuchokera “pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi” la mtundu wa anthu owomboledwa. Kuwonjezerapo, popeza kuti nkhosa zimakhala ana a pa dziko lapansi a Mfumuyo, yemwe amakhala “Atate [wawo] Wosatha,” iwo akuloŵa m’mbali ya dziko lapansi, kapena mkhalidwe, pansi pa Ufumu wa Mulungu.—Yesaya 9:6, 7.
11. Kodi ndimotani mmene nkhosa zimasonyezera kuti zimaima kaamba ka Ufumu, ndipo chifukwa cha ichi, kodi ndi dalitso lotani limene liri lawo?
11 Mosiyana ndi mbuzi zophiphiritsira, onga nkhosawo amasonyeza mosalakwika kuti akuchirikiza Ufumuwo. Motani? Mwa makhalidwe, osati kokha mawu. Chifukwa cha kusawoneka ndi maso kwa Mfumuyo m’mwamba, iwo sangachite zabwino mwachindunji kwa iye m’kuchirikiza Ufumu wake. Chotero iwo amachita zabwino kwa abale ake auzimu omwe adakali pa dziko lapansi. Ngakhale kuti ichi chimabweretsa udani, chitsutso, ndi chizunzo kumbali ya mbuzi, kaamba ka kuchita zabwino koteroko, nkhosazo zikuwuzidwa ndi Mfumuyo kuti izo ziri ‘zodalitsidwa ndi Atate wake.’
12. Kodi ndani omwe nkhosa zopulumuka zidzakhala ndi mwaŵi wa kulonjera, ndipo m’chigwirizano ndi ichi, kodi ndi lingaliro lotani limene ziŵalo za otsalira zakhala nalo?
12 Khamu lalikulu la opindula onga nkhosa a abale auzimu a Mfumuyo adzadalitsidwa ndi mwaŵi wosangalatsa wa kupulumuka kuloŵa m’Zaka Chikwi. M’kupita kwa nthaŵi, iwo adzatenga mbali m’kulonjera anthu akufa omwe ali m’manda a chikumbukiro. (Yohane 5:28, 29; 11:23-25) Awa adzaphatikizapo makolo okhulupirika ndi aneneri omwe anavutika ndi kupirira zochuluka kaamba ka kuyeretsedwa kwa ulamuliro wa Yehova ndi cholinga chakuti iwo angakhoze “kupeza chiwukiriro chabwinopo,” mothekera choyambirira. (Ahebri 11:35) Amuna ndi akazi achikhulupiriro owukitsidwa oterowo, ondandalitsidwa mochepera mu Ahebri mutu 11, akaphatikizapo Yohane Mbatizi. (Mateyu 11:11) Ena a otsalira odzozedwa aganiza za kupulumuka ndi kukhala ndi moyo kudzalonjera owukitsidwa okhulupirika oterowo omwe anamwalira Pentekoste ya 33 C.E. isanadze. Kodi odzozedwa adzakhala ndi mwaŵi woterowo?
13. Kodi nchifukwa ninji sichikakhala choyenerera kaamba ka otsalira kukhalapo kuti alonjere ndi kusamalira awo owukitsidwa padziko lapansi?
13 Ichi sichikakhala choyenerera. Khamu lalikulu la opulumuka chisautso chachikulu lidzakhalapo m’chiŵerengero chokwanira kusamalira mkhalidwewo ndi kuzoloŵeretsa owukitsidwawo ndi “dziko latsopano” pansi pa “miyamba yatsopano.” (2 Petro 3:13) Ngakhale tsopano, khamu lalikulu likulinganizidwa kaamba ka chimenechi. Lerolino, pamene abale auzimu a Yesu pa dziko lapansi akufikira chiŵerengero chochepera pa 9,000, opulumuka pakati pawo m’lingaliro lirilonse akakhala ochepera kwenikweni kusamalira ntchito yonse ya kukonzekera yotsogolera ku kuwukitsidwa kwa chisawawa. (Ezekieli 39:8-16) Pano, kenaka, ndi pamene khamu lalikulu, limene chiŵerengero chake chiri m’mamiliyoni, lidzagwira ntchito bwino koposa. Ndipo mwaŵi woterowo mosakaikira unasungidwira iwo.
14. (a) Kodi ambiri a khamu lalikulu akulangizidwa kaamba ka chiyani, ndipo kodi nchifukwa ninji unyinji kwa iwo tsopano afunikira kutenga thayo? (b) Kodi ndi zochitika zotani zimene ziyenera kuchitika posachedwapa, ndipo kodi ndi ntchito yotani yomwe ikuyembekezera nkhosa zina?
14 Ambiri a khamu lalikulu akuphunzitsidwa kale m’mathayo a mpingo ndi kupyolera m’maprogramu omanga amene gulu la Mulungu likusamalira m’dziko lonse lapansi. Ndipo chiri cholimbikitsa kuwona amuna auzimu achikulire owonjezereka a khamu lalikulu akugawiridwa kutenga thayo lokulira m’gulu limene Yehova tsopano akugwiritsira ntchito pa dziko lapansi. Otsalira a odzozedwa akukula m’zaka ndipo ali osathekera kunyamula katunduyo. Abale amenewa a Mfumu amakondwera ndi thandizo lachikondi la gulu lomwe akulu ndi atumiki otumikira oyeneretsedwa mwauzimu a nkhosa zina ali okhoza kupereka. Posachedwapa, Babulo Wamkulu adzachotsedwa pa nkhope ya dziko lapansi. Kenaka, monga momwe Chibvumbulutso 19:1-8 chikusonyezera, ukwati wa Mwanawankhosa ndi mkwatibwi wake wa a 144,000 onse udzachitidwa kumwamba, ndipo nkhosa zina, zotumikira monga dziko lapansi latsopano pansi pa miyamba yatsopano, zidzaimira Mfumu m’kupitiriza ntchito yaikulu yobwezeretsa kufikira dziko lonse lapansi litakhala paradaiso wodzala ndi anthu ku chitamando cha Yehova.—Yesaya 65:17; yerekezani ndi Yesaya 61:4-6.
15. Kodi ndi ziyembekezo zotani zimene khamu lalikulu likuyembekezera kaamba ka Zaka Chikwi?
15 Mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu, pamene akufa owomboledwa a mtundu wa anthu adzawukitsidwa, khamu lalikulu lopulumutsidwa lidzasangalala ndi mwaŵi wokulira ndi wolemekezeka koposa. Iwo kenaka adzakhala ana aamuna ndi ana aakazi a Mfumuyo. Chidzakhala chotheka kwa ana aamuna oterowo pakati pawo kutenga malo a akalonga, mongadi mmene ana aamuna a Mfumu Davide analiri akalonga okhala ndi mathayo osiyanasiyana.a Ichi chimatikumbutsa ife za Salmo 45, lolembedwa m’kulozera kwa “mfumu” yodzozedwa ya Yehova.
16. Kodi ndi kwa ndani kumene Salmo 45 m’chenicheni linalembedwerako, ndipo kodi ndimotani mmene ichi chingatsimikizidwire?
16 Kodi Salmo 45 yalembedwera kwa mfumu iti? Nkulekeranji, kwa Yesu Kristu! Ahebri 1:9 ikupanga kugwiritsira ntchito kumeneko m’kugwira mawu Salmo 45:7, yomwe imaŵerenga kuti: “Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa: Chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.” Chotero chiridi kwa Yesu Kristu wolemekezedwa kumene Salmo 45:16 ikunena kuti: “M’malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako, udzawaika akhale [akalonga, NW] m’dziko lonse lapansi.”
17. Kodi ndi m’chiyani ndipo kodi ndi kwa ndani kumene Mfumu, Yesu Kristu, ali wokondweretsedwa mwapadera?
17 Molondola, Yesu ali wokondweretsedwa kwenikweni ndi mtsogolo mwake monga Mfumu yolamulira kuposa m’nthaŵi yake ya kumbuyo ya pa dziko lapansi. Ndithudi, iye samaiwala nthaŵi ya kumbuyo imeneyo ndipo makamaka makolo ake aumunthu ophatikizidwa m’lonjezo la Yehova la kudalitsa mabanja onse kupyolera mwa Mbewu ya Abrahamu. Koma tsopano chikondwerero chake chachikulu chiri mtsogolo mofupikira monga momwe chalinganizidwira ndi Mpangi wa Mfumuyo, Yehova Mulungu. Chotero ana a pa dziko lapansi a Yesu, makamaka ana aamuna oyeneretsedwa pakati pawo odzatumikira pansi pa iye m’ntchito za ukalonga, adzatenga malo okondweretsa—mowonjezereka tero kuposa makolo ake a pa dziko lapansi.
18. Kodi ndimotani mmene malembedwe ena a Salmo 45:16 amagogomezera chikondwerero chokulira cha Yesu mwa ana aamuna a ukalonga kuposa mwa makolo ake a padziko lapansi?
18 Chikondwerero chachikulu cha Yesu mwa ana aamuna aukalonga kuposa mwa makolo chagogomezeredwa ndi matembenuzidwe a Baibulo osiyanasiyana. Pano pali mmene ena a iwo amalembera Salmo 45:16: “Ana ako aamuna adzaloŵa malo a atate ako, ndi kukwera kukhala akalonga m’dziko lonse.” (Moffatt) “Ana ako aamuna adzatenga malo a atate ako; udzawapanga iwo kukhala akalonga m’dziko lonse.” (Vesi 17, The New American Bible) “M’malo mwa atate ako ana adzabadwira iwe: ndipo udzawapanga iwo akalonga pa dziko lonse lapansi.”—The Septuagint Version, lofalitsidwa ndi Samuel Bagster and Sons.
19. Kodi amuna ena a khamu lalikulu tsopano ali ndi thayo lotani mu mpingo, ndipo kodi ndi ku malo otani kumene Mfumu, Yesu Kristu, ingawaike iwo mkati mwa Kulamulira kwake kwa Zaka Chikwi?
19 Ku chikondwerero chathu chokulira, omwe adzakhala akalonga ali pakati pathu penipeni. Iwo akupezeka pakati pa nkhosa zina zomwe zimamvera liwu la Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. Iwo akhala akumvetsera ku ilo makamaka chiyambire 1935, pamene Chibvumbulutso 7:9-17 chinalongosoledwa pa msonkhano wa Mboni za Yehova mu Washington, D.C. Lerolino, zikwi zingapo za khamu lalikulu limeneli la nkhosa zina zikutumikira monga akulu, kapena oyang’anira, m’mipingo yoposa 57,670 ya Mboni za Yehova m’maiko 212 kuzungulira dziko. Mwa kukhala olinganizidwa ndi otsalira a abale auzimu a Yesu omwe adakali pa dziko lapansi, amuna amenewa amayembekezera kudzatengedwa mokwanira kukhala ana aamuna padziko lapansi a Mfumu, Yesu Kristu, mkati mwa Kulamulira kwake kwa Zaka Chikwi pa dziko lapansi latsopano lolonjezedwa. (2 Petro 3:13) Motero, iwo angaikidwe kukhala akalonga kutumikira m’dziko lapansi latsopano.
20. (a) Kodi Mfumu idzakhala ndi mkhalidwe wotani kulinga kwa oikidwa ake padziko lapansi? (b) Kodi khamu lalikulu lidzalonjera ndani, ndipo kodi ndi mwaŵi wotani womwe waikidwa kwa awo owukitsidwa?
20 Mfumu, Yesu Kristu, adzakhala wosangalatsidwa kuzindikira akalonga oikidwa chatsopanowa, monga mmene iye tsopano akuzindikirira uyang’aniro wa nkhosa zina zokhulupirika m’mipingo yamakono ya Mboni za Yehova. Ziŵalo zonse za khamu lalikulu la nkhosa zina—akazi limodzinso ndi amuna—adzakhala ndi mwaŵi wosangalatsa wa kulonjera anthu akufa onse omwe adzamva mawu a Yesu ndi kudzuka ku mwaŵi wa kupeza moyo wosatha mu ungwiro wa anthu pa dziko lapansi loyeretsedwa lomwe lidzasinthidwira kukhala paradaiso ya chiwunda chonse. (Yohane 5:28, 29) Awo owukitsidwa oyanjidwa mwakuya adzaphatikiza makolo a Yesu Kristu owomboledwa, amuna achikhulupiriro omwe anali ofunitsitsa kutsimikizira chikhulupiriro chawo kwa Yehova Mulungu ngakhale kufikira imfa m’chiyembekezo cha kupeza “chiwukiriro chabwinopo.” (Ahebri 11:35) Koma kuwukitsidwira ku moyo waumunthu wangwiro mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Mfumu yawo Yowombola, Yesu Kristu, kuli kokha chiyambi. Mwa kukhala olinganizidwa mosasweka pansi pa Yehova Mulungu mkati mwa chiyeso chotsirizira pa mtundu wa anthu obwezeretsedwa pamapeto pa Zaka Chikwi, iwo adzadzitsimikizira iwo eni kukhala oyenerera kukhala olungamitsidwa ku moyo wosatha m’Paradaiso monga mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova la chilengedwe chaponseponse.—Mateyu 25:31-46; Chibvumbulutso 20:1–21:1.
[Mawu a M’munsi]
a Yerekezani ndi 2 Samueli 8:18, New World Translation Reference Bible, mawu a m’munsi.
Kodi Ndimotani Mmene Mukayankhira?
◻ Kodi Yehova waika pambali nyengo yotani ya nthaŵi kaamba ka kudalitsa mtundu wonse wa anthu?
◻ Kodi ndi kokha mwa kukhala mu unansi wotani kwa wina ndi mnzake mmene wina angapulumuke chisautso chachikulu?
◻ Kodi chimatanthauzanji kaamba ka nkhosa ‘kuloŵa ufumu wokonzedwera kwa iwo pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi’?
◻ Mkati mwa Zaka Chikwi, kodi ndi mu mwaŵi wotani umene khamu lalikulu lidzagawanamo?