Kuŵala kwa Kuunika—Kwakukulu ndi Kwakung’ono (Mbali 1)
“Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kumkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.”—MIYAMBO 4:18.
1. Kodi nchifukwa ninji choonadi chavumbulidwa pang’onopang’ono?
ULI umboni wa nzeru ya Mulungu kuti, malinga ndi Miyambo 4:18, kuvumbulika kwa choonadi chauzimu kwachitika pang’onopang’ono mwa kuŵala kwa kuunika. M’nkhani yapitayo, tinaona mmene lemba limeneli linakwaniritsidwira m’nthaŵi za atumwi. Ngati choonadi chonse cha Malemba chikanavumbulidwa chonse panthaŵi imodzi, chikanakhala chothobwa m’maso ndiponso chozunguza mutu—mofanana kwambiri ndi kutuluka m’phanga lamdima wa bi ndi kuima padzuŵa loŵala kwambiri. Ndiponso, choonadi chovumbulidwa pang’onopang’ono chimalimbitsa chikhulupiriro cha Akristu mosalekeza. Chimaŵalitsabe mokulirapo chiyembekezo chawo ndi kuunikira mokulirapo njira imene iwo ayenera kuyendamo.
“Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru”
2. Kodi Yesu anasonyeza kuti akagwiritsira ntchito yani kupereka kuunika kwauzimu kwa otsatira ake, ndipo kodi chiŵiya chimenecho chapangidwa ndi ayani?
2 M’nthaŵi za atumwi Yesu Kristu anakuona kukhala koyenera kugwiritsira ntchito zozizwitsa kupatsa otsatira ake kuŵala koyambirira kwa kuunika. Tili ndi zitsanzo ziŵiri za zimenezi: Pentekoste wa 33 C.E. ndi kutembenuka kwa Korneliyo mu 36 C.E. Pambuyo pake, Kristu wakuona kukhala koyenera kugwiritsira ntchito kabungwe ka anthu, monga momwedi analoserera: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya panthaŵi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika adzampeza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.” (Mateyu 24:45-47) Kapolo ameneyu sakanakhala munthu mmodzi yekha chifukwa chakuti anayenera kupereka chakudya chauzimu kuyambira pamene mpingo Wachikristu unayamba pa Pentekoste kufikira Mbuyeyo, Yesu Kristu, atadza kudzaŵerengera zinthu. Maumboni amasonyeza kuti kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kameneka kamapangidwa ndi kagulu ka Akristu odzozedwa onse okhala pa dziko lapansi panthaŵi iliyonse.
3. Kodi ena amene anali oyamba kuphatikizidwa m’kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anali ayani?
3 Kodi ena amene anali oyamba kuphatikizidwa m’kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anali ayani? Mmodzi wa iwo anali mtumwi Petro, amene analabadira lamulo la Yesu lakuti: “Dyetsa nkhosa zanga.” (Yohane 21:17) Ena oyambirira a m’kagulu ka kapoloko anaphatikizapo Mateyu, amene analemba Uthenga Wabwino wotchedwa ndi dzina lake, ndi Paulo, Yakobo, ndi Yuda, omwe analemba makalata ouziridwa. Mtumwi Yohane, amene analemba buku la Chivumbulutso, Uthenga wake Wabwino, ndi makalata ake, analinso m’kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Amunawa analemba nkhanizo mogwirizana ndi lamulo la Yesu.
4. Kodi “banja” ndani?
4 Ngati kuti odzozedwa onse monga kagulu, mosasamala kanthu za kumene akukhala pa dziko lapansi, ndiwo a kagulu ka kapolo, nangano “banja” ndayani? Ndiwo odzozedwa amodzimodziwo koma oonedwa m’lingaliro lina—monga munthu payekha. Inde, monga munthu payekha iwo akakhala a “kapolo” kapena akakhala a “banja,” malinga ngati anali kugaŵira chakudya chauzimu kapena kuchidya. Mwachitsanzo: Monga momwe kwalembedwera pa 2 Petro 3:15, 16, mtumwi Petro akutchula makalata a Paulo. Powaŵerenga, Petro akakhala ngati mmodzi wa a m’banja akudya chakudya chauzimu choperekedwa ndi Paulo monga woimira kagulu ka kapoloko.
5. (a) Kodi chinachitikira kapoloyo nchiyani m’zaka mazana ambiri pambuyo pa imfa ya atumwi? (b) Kodi panakhala zochitika zotani m’theka lomaliza la zaka za zana la 19?
5 Pankhaniyi, buku lakuti God’s Kingdom of a Thousand Years Has Approached linati: “Tilibe cholembedwa chokwanira m’mbiri chosonyeza mmene kagulu ka ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru’ kanalili ndi mmene kanatumikirira m’zaka mazana ambiri pambuyo pa imfa ya atumwi a Ambuye Yesu Kristu. Mwachionekere mbadwo umodzi wa kagulu ka ‘kapolo’ unadyetsa mbadwo wina wotsatira. (2 Timoteo 2:2) Koma m’theka lomaliza la zaka za zana la 19 panali anthu owopa Mulungu amene anakonda chakudya chauzimu cha m’Baibulo Lopatulika amenenso anafuna kuchidya . . . Timagulu tophunzira Baibulo . . . tinapangidwa ndipo tinapita patsogolo pa kumvetsetsa choonadi choyambirira cha Malemba Opatulika. Oona mtima ndi opanda dyera mwa ophunzira Baibulo ameneŵa anali ofunitsitsa kugaŵana ndi ena zidutswa zimenezi zofunika za chakudya chauzimu. Anali ndi mzimu wa kukhulupirika wa ‘kapolo’ woikidwa kupatsa ‘banja’ ‘chakudya chauzimu chofunikira panthaŵi yake.’ Anali ‘anzeru’ pozindikira kuti imeneyo inali nthaŵi yake yoyenera ndiponso njira yabwino koposa yoperekera chakudyacho. Anayesetsa kuchigaŵira.”—Masamba 344-5.a
Kuŵala Koyamba kwa Kuunika m’Nthaŵi Zamakono
6. Kodi ndi chinthu choona chiti chimene chili chapadera kwambiri ponena za kuvumbulika kwa pang’onopang’ono kwa choonadi?
6 Chinthu choona chimene chili chapadera kwambiri ponena za aja amene Yehova anagwiritsira ntchito kudzetsa kuunika kwauzimu komawonjezereka pang’onopang’ono kumeneku nchakuti iwo sanadzipezere thamo. Mkhalidwe wamaganizo wa C. T. Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, unali wakuti Ambuye anakonda kugwiritsira ntchito maluso awo osanunkha kanthu. Ponena za maina otonza amene adani ake anakonda kutchula, Mbale Russell ananenetsa kuti sanakumanepo ndi “Mrussell” ndi kuti kunalibe chinthu chonga “Chirussell.” Thamo lonse linamka kwa Mulungu.
7. Kodi ndi umboni wotani umene Mbale Russell ndi antchito anzake anapereka kusonyeza kuti analidi a kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?
7 Malinga ndi zotulukapo, sipangakhale kukayikira kulikonse kwakuti mzimu wa Yehova unali kutsogoza zoyesayesa za Mbale Russell ndi aja ogwirizana naye. Iwo anapereka umboni wakuti anali a kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Ngakhale kuti atsogoleri ambiri achipembedzo panthaŵiyo anati anakhulupirira kuti Baibulo linali Mawu ouziridwa a Mulungu ndi kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu, iwo anavomereza ziphunzitso zonyenga Zachibabulo, zonga Utatu, kusafa kwa moyo wa munthu, ndi chizunzo chosatha. Malinga ndi lonjezo la Yesu, unalidi mzimu woyera umene unachititsa kuyesayesa kodzichepetsa kwa Mbale Russell ndi anzake kuŵalitsa choonadi kuposa ndi kale lonse. (Yohane 16:13) Ophunzira Baibulo odzozedwa amenewo anapereka umboni wakuti analidi mbali ya kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, kamene ntchito yake ili yakugaŵira chakudya chauzimu ku banja la Mbuyeyo. Khama lawo linathandiza kwambiri pa kusonkhanitsa odzozedwa.
8. Kodi ndi mfundo ziti zazikulu ponena za Yehova, Baibulo, Yesu Kristu, ndi mzimu woyera zimene Ophunzira Baibulo anamvetsetsa bwino lomwe?
8 Nkosangalatsa kuona mmene Yehova, mwa mzimu woyera, anayanjira kwambiri Ophunzira Baibulo oyambirira ameneŵa ndi kuŵala kwa kuunika. Choyamba, anatsimikiza zolimba kuti Mlengi aliko ndi kuti ali ndi dzina lakelake lakuti Yehova. (Salmo 83:18; Aroma 1:20) Anaona kuti Yehova ali ndi mikhalidwe yaikulu inayi—mphamvu, chilungamo, nzeru, ndi chikondi. (Genesis 17:1; Deuteronomo 32:4; Aroma 11:33; 1 Yohane 4:8) Akristu odzozedwa ameneŵa anapereka umboni wokwana wakuti Baibulo lili Mawu ouziridwa a Mulungu ndipo ndilo choonadi. (Yohane 17:17; 2 Timoteo 3:16, 17) Ndiponso, anakhulupirira kuti Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, analengedwa ndi kuti anapereka moyo wake dipo kaamba ka anthu onse. (Mateyu 20:28; Akolose 1:15) Mzimu woyera unaonedwa kukhala mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, osati munthu wachitatu wa Utatu.—Machitidwe 2:17.
9. (a) Kodi ndi choonadi chotani chimene Ophunzira Baibulo anamvetsetsa ponena za chibadwa cha munthu ndi ziyembekezo zoperekedwa ndi Baibulo? (b) Kodi ndi choonadi china chiti chimene atumiki a Yehova anaona bwino lomwe?
9 Ophunzira Baibulo anaona bwino lomwe kuti munthu alibe moyo wosafa koma kuti iye ndiye moyo umene umafa. Anazindikira kuti “mphotho yake ya uchimo ndi imfa,” osati chizunzo chosatha, choncho kulibe malo otchedwa helo woyaka moto. (Aroma 5:12; 6:23; Genesis 2:7; Ezekieli 18:4) Ndiponso, anaona bwino lomwe kuti chiphunzitso cha chisinthiko chinali, osati chabe chosemphana ndi malemba, komanso kuti chinalibiretu umboni weniweni. (Genesis, machaputala 1 ndi 2) Anazindikiranso kuti Baibulo lili ndi ziyembekezo ziŵiri—chakumwamba kwa odzozedwa a 144,000 otsatira mapazi a Kristu ndi cha pa dziko lapansi la paradaiso kwa “khamu lalikulu” losaŵerengeka la “nkhosa zina.” (Chivumbulutso 7:9; 14:1; Yohane 10:16) Ophunzira Baibulo oyambirira amenewo anazindikira kuti dziko lapansi likhala kosatha ndi kuti silidzatenthedwa, monga momwe zimaphunzitsira zipembedzo zambiri. (Mlaliki 1:4; Luka 23:43) Anaphunziranso kuti kubweranso kwa Kristu kukakhala kosaoneka ndi kuti pambuyo pake akapereka chiweruzo pa mitundu ndi kudzetsa paradaiso wa pa dziko lapansi.—Machitidwe 10:42; Aroma 8:19-21; 1 Petro 3:18.
10. Kodi ndi zoona zotani zimene Ophunzira Baibulo anadziŵa ponena za ubatizo, kusiyanitsa atsogoleri achipembedzo ndi opembedza wamba, ndi Chikumbutso cha imfa ya Kristu?
10 Ophunzira Baibulowo anaphunzira kuti ubatizo wa m’Malemba sindiwo kuwaza madzi makanda koma kuti mogwirizana ndi lamulo la Yesu pa Mateyu 28:19, 20, ndiwo kumiza okhulupirira amene aphunzitsidwa. Anadzaona kuti palibe maziko a Malemba a kusiyanitsira kagulu ka atsogoleri achipembedzo ndi opembedza wamba. (Mateyu 23:8-10) Mosiyana ndi zimenezo, Akristu onse ayenera kukhala alaliki a uthenga wabwino. (Machitidwe 1:8) Ophunzira Baibulo anamvetsetsa kuti Chikumbutso cha imfa ya Kristu chiyenera kuchitidwa kamodzi chaka ndi chaka, pa Nisani 14. Ndiponso, anaona kuti Isitala ndi holide yachikunja. Ndiponso, odzozedwawo anali ndi chidaliro kwambiri chakuti Mulungu anali kuchirikiza ntchito yawo moti sanali kusonkhetsa ndalama. (Mateyu 10:8) Kuyambira pachiyambi, iwo anamvetsetsa kuti Akristu ayenera kutsatira malamulo a Baibulo, amene amaphatikizapo kukulitsa zipatso za mzimu woyera wa Mulungu.—Agalatiya 5:22, 23.
Kuŵala Kowonjezereka kwa Kuunika
11. Kodi ndi kuunika kotani kumene kunaŵala pa ntchito ya Mkristu ndi pa fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi?
11 Makamaka chiyambire 1919 atumiki a Yehova adalitsidwa ndi kuŵala kowonjezereka kwa kuunika. Ndi kuŵala kwambiri chotani nanga kwa kuunika kumene kunaonekera pa msonkhano ku Cedar Point mu 1922 pamene J. F. Rutherford, pulezidenti wachiŵiri wa Watch Tower Society, anamveketsa mfundo yakuti thayo lalikulu la atumiki a Yehova ndi la ‘kulengeza, kulengeza, kulengeza, Mfumu ndi ufumu wake’! Chaka chotsatira, kuunika kwakukulu kunaŵala pa fanizo la nkhosa ndi mbuzi. Kunapezeka kuti ulosi umenewu ukakwaniritsidwa m’tsiku la Ambuye lilipoli, osati mtsogolo mkati mwa Zaka Chikwi monga momwe ankalingalirira. M’Zaka Chikwizo, abale a Kristu sadzadwala, kapena kuponyedwa m’ndende. Ndipotu, pamapeto a Zaka Chikwi, Yehova Mulungu ndiye adzaweruza osati Yesu Kristu.—Mateyu 25:31-46.
12. Kodi ndi kuŵala kotani kwa kuunika kumene kunakhalako ponena za Armagedo?
12 Mu 1926 kuŵala kwina kwakukulu kwa kuunika kunavumbula kuti nkhondo ya Armagedo sinali kupandukira maboma kwa anthu, mmene analingalirira Ophunzira Baibulo panthaŵi ina. M’malo mwake, idzakhala nkhondo mwa imene Yehova adzasonyezera mphamvu yake poyera moti anthu onse adzakhulupiriradi kuti ndiye Mulungu.—Chivumbulutso 16:14-16; 19:17-21.
Krisimasi—Holide Yachikunja
13. (a) Kodi ndi kuunika kotani kumene kunaŵala pa kukondwerera Krisimasi? (b) Kodi nchifukwa ninji masiku a kubadwa sanalinso kusungidwa? (Phatikizanipo mawu amtsinde.)
13 Mwamsanga pambuyo pake, kuŵala kwa kuunika kunachititsa Ophunzira Baibulo kusiya kukondwerera Krisimasi. Nthaŵiyo isanafike Ophunzira Baibulo padziko lonse anali kukondwerera Krisimasi nthaŵi zonse, ndipo chikondwerero chake kumalikulu ku Brooklyn chinali nthaŵi ya kusekera kwadzaoneni. Komano anadzazindikira kuti kukumbukira December 25 kunalidi kwachikunja ndipo kunasankhidwa ndi Dziko Lachikristu lampatuko kuti kutembenuka kwa akunja kukhale kwapafupi. Ndiponso, anapeza kuti Yesu sakanabadwa m’chisanu, popeza kuti pa kubadwa kwake, abusa anali kudyetsa nkhosa kumabusa—zimene sakanachita usiku kumapeto kwa December. (Luka 2:8) M’malo mwake, Malemba amasonyeza kuti Yesu anabadwa cha ku ma October 1. Ophunzira Baibulo anazindikiranso kuti otchedwa amuna anzeru amene anafika kwa Yesu zaka pafupifupi ziŵiri iye atabadwa anali anzeru achikunja.b
Dzina Latsopano
14. Kodi nchifukwa ninji dzina lakuti Ophunzira Baibulo silinali kuwadziŵikitsa bwino kwambiri anthu a Yehova?
14 Mu 1931 kuŵala kwakukulu kwa kuunika kunavumbulira Ophunzira Baibulowo dzina loyenera la m’Malemba. Anthu a Yehova anadziŵa kuti sangalandire maina owajeda nawo amene anthu ena anawapatsa, onga Arussell, Amillennial Dawn, ndi “okana helo.”c Koma anayambanso kuzindikira kuti dzina limene iwo eni analitenga—Ophunzira Baibulo a pa Dziko Lonse—silinali kuwadziŵikitsa bwino kwambiri. Iwo sanali ophunzira Baibulo chabe. Ndiponso, nthaŵi zonse panakhala ena ambiri amene anali kuphunzira Baibulo koma amene anali osiyana ndi Ophunzira Baibulo.
15. Kodi ndi dzina liti limene Ophunzira Baibulo anatenga mu 1931, ndipo chifukwa ninji lili loyenera?
15 Kodi Ophunzira Baibulo anafikira motani pa kukhala ndi dzina latsopano? Kwa zaka zambiri The Watch Tower inali kumveketsa dzina la Yehova. Chotero, kunali koyenera kwambiri kwa Ophunzira Baibulo kulandira dzina lopezeka pa Yesaya 43:10: “Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziŵe, ndi kundikhulupirira ine, ndi kuzindikira, kuti ine ndine; ndisanakhale ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.”
Kutsimikiza ndi “Khamu Lalikulu”
16. Kodi nchifukwa ninji maulosi a kubwezeretsedwa sanali kunena za kubwerera kwa Ayuda enieni ku Palestina, koma kodi amanena za ayani?
16 M’voliyumu yachiŵiri ya Vindication, yofalitsidwa ndi Watch Tower Society mu 1932, kuŵala kwa kuunika kunavumbula kuti maulosi akubwezeretsedwa olembedwa ndi Yesaya, Yeremiya, Ezekieli, ndi aneneri ena sanali kunena za Ayuda akuthupi (monga momwe kunkalingaliridwira), amene anali kubwerera ku Palestina opanda chikhulupiriro ndi okhala ndi zolinga za ndale. M’malo mwake, maulosi akubwezeretsedwa ameneŵa, amene anakwaniritsidwa pang’ono pamene Ayuda anabwerako ku ukapolo ku Babulo mu 537 B.C.E., anakwaniritsidwa kwambiri mwa kulanditsidwa ndi kubwezeretsedwa kwa Israyeli wauzimu koyamba mu 1919 ndi kulemera kotsatirapo m’paradaiso wauzimu amene atumiki oona a Yehova alimo lerolino.
17, 18. (a) M’kupita kwa nthaŵi, kodi nchiyani chimene chinasonyezedwa mwa kuŵala kwa kuunika kukhala chifuno chachikulu cha Yehova? (b) Kodi ndi kuŵala kotani kwa kuunika kokhudza Chivumbulutso 7:9-17 kumene kunachitika mu 1935?
17 M’kupita kwa nthaŵi, kuŵala kwa kuunika kunavumbula kuti chifuno chachikulu cha Yehova chinali, osati chipulumutso cha anthu, koma kutsimikiza kuti ulamuliro wake ndiwo woyenera. Mutu wa nkhani wa Baibulo wofunika koposa unaonedwa kukhala, osati dipo, koma Ufumu, pakuti udzatsimikiza kuti ulamuliro wa Yehova ndiwo woyenera. Kumeneko kunali kuŵala kwa kuunika kotani nanga! Nkhaŵa yaikulu ya Akristu odzipatulira sinalinso pa kupita kwawo kumwamba.
18 Mu 1935 kuŵala kwakukulu kwa kuunika kunavumbula kuti khamu lalikulu lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9-17 silinali gulu lachiŵiri lakumwamba. Kunalingaliridwa kuti otchulidwa m’mavesiwo anali ena a odzozedwa amene sanali okhulupirika kwambiri choncho anali kuimirira ku mpando wachifumu m’malo mwa kukhala pa mipando yachifumu kuchita ufumu ndi unsembe ndi Yesu Kristu. Komatu palibiretu lingaliro la kukhala wokhulupirika pang’ono. Munthu amakhala wokhulupirika kapena wosakhulupirika. Chotero kunaonedwa kuti ulosi umenewu unanena za khamu lalikulu losaŵerengeka lochokera m’mitundu yonse amene tsopano akusonkhanitsidwa ndipo ali ndi ziyembekezo za pa dziko lapansi. Ndiwo “nkhosa” za pa Mateyu 25:31-46 ndi “nkhosa zina” za pa Yohane 10:16.
Mtanda—Suuli Chizindikiro cha Chikristu
19, 20. Kodi nchifukwa ninji mtanda sungakhale chizindikiro cha Chikristu choona?
19 Kwa zaka zambiri Ophunzira Baibulo anaona mtanda monga chizindikiro chofunika kwambiri cha Chikristu. Ndipo anali ndi naphini wa “mtanda ndi korona.” Malinga ndi kunena kwa King James Version, Yesu anauza otsatira ake kunyamula “mtanda” wawo, ndipo ambiri anafikira pa kukhulupirira kuti iye anapachikidwa pa mtanda. (Mateyu 16:24; 27:32) Kwa zaka zambiri chizindikiro chimenechi chinalinso pa chikuto cha magazini a Watch Tower.
20 Buku lakuti Chuma, lofalitsidwa ndi Sosaite mu 1936, linamveketsa bwino lomwe kuti Yesu Kristu anapachikidwa, osati pa mtanda, koma pa mlongoti, kapena pa mtengo. Malinga ndi kunena kwa buku lina, liwu la Chigiriki (stau·rosʹ) lomasuliridwa “mtanda” mu King James Version “limatanthauza, kwakukulukulu, mlongoti woimirira kapena mtengo. [Uyenera] kusiyanitsidwa ndi mtanda wachipembedzo wa mitengo iŵiri. . . . Womalizawu unayambira ku Kaldayo wakale, ndipo unali chizindikiro cha mulungu Tammuz.” M’malo mwa kuchiyesa fano, anthu ayenera kunyansidwa nacho chipangizo chimene Yesu anapachikidwapo.
21. Kodi nchiyani chimene chidzalingaliridwa m’nkhani yotsatira?
21 Palinso zitsanzo zina za zonse ziŵiri kuŵala kwakukulu kwa kuunika ndi kuja kumene kungayesedwe kwakung’ono. Chonde onani nkhani yotsatira kaamba ka malongosoledwe a zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b M’kupita kwa nthaŵi, anaona kuti ngati kuti chikondwerero cha kubadwa kofunika koposa kumene sikunachitikepo sichinachitidwe, ndiye kuti sitiyenera kukondwerera tsiku la kubadwa lililonse. Ndiponso, Aisrayeli kapena Akristu oyambirira sanakondwerere masiku a kubadwa. Baibulo limangotchula masiku aŵiri a kubadwa, lina la Farao ndi lina la Herode Antipa. Lililonse la mapwando aŵiriwo linaipitsidwa ndi kunyongedwa kwa munthu. Mboni za Yehova sizimakondwerera masiku a kubadwa chifukwa chakuti zochitika zimenezi zinayambira kuchikunja ndipo zimakweza eni tsiku la kubadwalo.—Genesis 40:20-22; Marko 6:21-28.
c Kumeneku kunali kuphonya kumene mipingo yambiri ya Dziko Lachikristu inachita. Lutheran linali dzina lowajeda nalo limene adani a Martin Luther anapatsa otsatira ake, amenenso analilandira. Mofananamo, a Baptist analandira dzina lowajeda nalo limene akunja anawapatsa chifukwa chakuti iwo ankalalikira ubatizo wa kumiza. Mofanananso ndi zimenezo, zichita ngati kuti a Methodist analandira dzina limene akunja anawapatsa. Ponena za mmene a Society of Friends anafikira pa kutchedwa Quakers, The World Book Encyclopedia imati: “Liwulo Quaker poyamba linali lotonza Fox [myambitsi wake], amene anauza woweruza Wachingelezi ‘kunthunthumira ndi Mawu a Ambuye.’ Woweruzayo anatcha Fox ‘quaker.’”
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndani, ndipo “banja” ndayani?
◻ Kodi kuŵala koyambirira kwa kuunika m’nthaŵi zamakono kunaphatikizapo chiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji dzina latsopano lakuti, Mboni za Yehova, linali loyenera?
◻ Kodi ndi zoona ziti zapadera zimene zinavumbulidwa mu 1935?
[Chithunzi patsamba 17]
C. T. Russell ndi anzake anafalitsa kuunika kwauzimu, koma thamo lonse linamka kwa Yehova