Mutu 14
Kodi Yehova Amatsogolera Motani Gulu Lake?
KODI Mulungu ali ndi gulu? Malemba ouziridwa amatiuza kuti ali nalo. M’Mawu ake, amatipatsa chithunzi cha mbali yakumwamba ya ulemerero ya gululo. (Ezekieli 1:1, 4-14; Danieli 7:9, 10, 13, 14) Ngakhale kuti mbali ya kumwamba imeneyi sitingaione, olambira oona lerolino imawakhudza kwambiri. (2 Mafumu 6:15-17) Gulu la Yehova lilinso ndi mbali yooneka padziko lapansi. Baibulo limatithandiza kuidziŵa ndi mmenenso Yehova amaitsogolera.
Kuzindikira Mbali Yooneka
2 Kwa zaka 1,545 mtundu wa Israyeli unali mpingo wa Mulungu. (Machitidwe 7:38) Koma Aisrayeli analephera kusunga malamulo a Mulungu ndiponso anakana Mwana wake wa Mulunguyo. Choncho mpingo umenewo Yehova anaukana ndipo anasiya kuugwiritsa ntchito. Yesu anauza Ayuda kuti: “Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” (Mateyu 23:38) Ndiyeno Mulungu anakhazikitsa mpingo watsopano, umene anapanga nawo pangano latsopano. Mpingo umenewu unali kudzakhala ndi anthu okwana 144,000 osankhidwa ndi Mulungu kuti akakhale limodzi ndi Mwana wake kumwamba.—Chivumbulutso 14:1-4.
3 Anthu oyamba kukhala mu mpingo watsopano umenewo anadzozedwa ndi mzimu woyera wa Yehova pa Pentekoste mu 33 C.E. Za nkhani yosaiŵalika imeneyi, timaŵerenga kuti: “Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi. Ndipo mwadzidzidzi anamveka mawu ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene anali kukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogaŵanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera.” (Machitidwe 2:1-4) Motero mzimu wa Mulungu unapereka umboni wosatsutsika wakuti tsopano Mulungu akakwaniritsa cholinga chake mwa kugwiritsa ntchito anthu ameneŵa otsogozedwa ndi Yesu Kristu kumwamba.
4 Lerolino, otsalira ochepa chabe a 144,000 ndiwo adakali padziko lapansi. Koma pokwaniritsa ulosi wa Baibulo, anthu a “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” omwe alipo mamiliyoni, awagwirizanitsa ndi otsalira odzozedwawo. Yesu, Mbusa Wabwino, wagwirizanitsa nkhosa zina zimenezi ndi otsalirawo kuti apange gulu limodzi limene iyeyo monga Mbusa wawo mmodzi amalitsogolera. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:11, 16) Onseŵa amapanga mpingo umodzi wogwirizana, ndipo ndiwo gulu looneka la Yehova.
Lotsogozedwa ndi Mulungu
5 Mawu a m’Malemba akuti ‘mpingo wa Mulungu wamoyo’ amaonetsa bwino amene akutsogolera gulu limeneli. Gululi amalilamulira ndi Mulungu. Yehova amatsogolera anthu ake kudzera mwa Yesu, yemwe anamuika kukhala Mutu wosaoneka wa mpingo, ndiponso kudzera m’Mawu Ake ouziridwa, Baibulo.—1 Timoteo 3:14, 15, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono; Aefeso 1:22, 23; 2 Timoteo 3:16, 17.
6 Utsogoleri umenewu unaoneka bwino pa Pentekoste. (Machitidwe 2:14-18, 32, 33) Unaonekanso pamene mngelo wa Yehova anatsogolera kuti uthenga wabwino ufalikire ku Africa, pamene mawu a Yesu anapereka malangizo panthaŵi ya kutembenuka kwa Saulo wa ku Tariso, ndiponso pamene Petro anayamba ntchito yolalikira kwa Akunja. (Machitidwe 8:26, 27; 9:3-7; 10:9-16, 19-22) Komabe m’kupita kwa nthaŵi, mawu anasiya kumveka kuchokera kumwamba, angelo anasiya kuoneka, anthu anasiya kulandira mphatso za mzimu zochita zozizwitsa. Komatu Yesu analonjeza kuti: “Onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:20; 1 Akorinto 13:8) Lerolino, Mboni za Yehova zimazindikira kuti Yesu akuwatsogolera. Popanda utsogoleri wake, ntchito yolengeza uthenga wa Ufumu sikanatheka ndi chidani choopsa chimene chilipochi.
7 Atatsala pang’ono kufa, Yesu anauza ophunzira ake za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene iye monga Mbuye akamupatsa udindo wapadera. “Kapolo” ameneyo akakhala alipo pamene Ambuye akuchoka kupita kumwamba ndipo akakhala akugwirabe ntchito zolimba pamene Kristu akubweranso mosaoneka m’mphamvu ya Ufumu. Mmene akufotokozeramu, sakunena za munthu mmodzi yekha chifukwa sangazikwanitse zimenezi, koma akunena za mpingo wodzozedwa wa Kristu. Ataugula ndi mwazi wake, Yesu anati mpingowo ndi “kapolo” wake. Analamula anthu mumpingowo kupanga ophunzira ndi kuwadyetsa pang’onopang’ono, kuwapatsa “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.”—Mateyu 24:45-47; 28:19; Yesaya 43:10; Luka 12:42; 1 Petro 4:10.
8 Popeza gulu la kapolo linali kugwira ntchito ya Mbuye wawo mokhulupirika mmene Mbuyeyo anabweranso mosaoneka mu 1914, pali umboni wakuti kapoloyu anamuwonjezera udindo wake mu 1919. Kuyambira chaka chimenecho mpaka pano, umboni wa Ufumu wakhala ukuperekedwa padziko lonse, ndipo khamu lalikulu la olambira Yehova likusonkhanitsidwa kuti lidzapulumuke chisautso chachikulu. (Mateyu 24:14, 21, 22; Chivumbulutso 7:9, 10) Iwoŵanso amafunika chakudya chauzimu, ndipo amapatsidwa ndi gulu la kapolo. Kuti tikondweretse Yehova, tifunika kulandira ndi kutsatira malangizo amene amatipatsa kudzera m’njira imeneyi.
9 Nthaŵi zina pamabuka mafunso okhudza ziphunzitso ndi kayendetsedwe ka zinthu. Kodi zikatero zimatha bwanji? Machitidwe chaputala 15 amatiuza mmene anathetsera mkangano wokhudza Akunja otembenuka mtima. Nkhaniyo anapita nayo kwa atumwi ndi amuna akulu ku Yerusalemu, amene anapanga bungwe lolamulira limene onse anali kuyang’anako. Amuna amenewo anali n’zolakwa zawo, komabe Mulungu anawagwiritsa ntchito. Anafufuza zimene malemba amanena pankhaniyo ndiponso umboni wakuti mzimu wa Mulungu unagwira ntchito potsegula gawo la Akunja. Ndiyeno anagamula nkhaniyo. Mulungu anadalitsa kayendetsedwe ka zinthu kameneko. (Machitidwe 15:1-29; 16:4, 5) Bungwelo linali kutumiza anthu okathandiza ntchito yolalikira Ufumu.
10 Masiku athu ano, Bungwe Lolamulira la gulu looneka la Yehova lapangidwa ndi abale odzozedwa ndi mzimu ochokera m’mayiko osiyanasiyana ndipo lili ku likulu la dziko lonse lapansi la Mboni za Yehova. Motsogoleredwa ndi Yesu Kristu, Bungwe Lolamulira limalimbikitsa kulambira koyera m’dziko lililonse, ndipo limayang’anira ntchito yolalikira m’mipingo zikwizikwi ya Mboni za Yehova. Amene ali m’Bungwe Lolamulira ali ndi maganizo ofanana ndi a mtumwi Paulo amene analembera Akristu anzake kuti: “Sikuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.”—2 Akorinto 1:24.
11 Mboni za Yehova padziko lonse zimayembekezera Bungwe Lolamulira kusankha abale oyenerera amenenso amapatsidwa mphamvu zoika akulu ndi atumiki otumikira oti azisamalira mipingo. Ziyeneretso za amene amaikidwa pa maudindowo zili m’Baibulo ndipo sizifuna kuti munthu achite kukhala wangwiro kapena wosalakwa kuti aikidwe. Akulu amene amavomereza amuna oti aikidwe pa maudindowo ndiponso akulu amene amaika enawo ali ndi udindo waukulu kwa Mulungu. (1 Timoteo 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9) Motero iwo amapereka pemphero kuti mzimu wa Mulungu uwathandize, ndipo amalola Mawu ake ouziridwa kuwatsogolera. (Machitidwe 6:2-4, 6; 14:23) Tiyeni tiziyamikira “mphatso mwa amuna” zimenezi, chifukwa zimatithandiza tonsefe kufika pa “umodzi m’chikhulupiriro.”—Aefeso 4:8, 11-16, NW.
12 Malemba amalangiza kuti amuna ndiwo aziyang’anira mpingo. Uku si kutsitsa akazi, chifukwa ena a iwo ndi oloŵa Ufumu wakumwamba, komanso ndiwo amalalikira kwambiri. (Salmo 68:11) Ndiponso, chifukwa chosamalira mokhulupirika udindo wawo pabanja, akazi amathandiza kuti mbiri ya mpingo ikhale yabwino zedi. (Tito 2:3-5) Koma kuphunzitsa mu mpingo kumachitidwa ndi amuna amene amaikidwa kuti azichita zimenezo.—1 Timoteo 2:12, 13.
13 M’dzikoli, munthu amene ali ndi udindo waukulu ndiye amamuona kukhala wofunika, koma m’gulu la Mulungu amayendera mfundo iyi: “Iye wakukhala wamng’onong’ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.” (Luka 9:46-48; 22:24-26) Malemba amalangiza akulu kukhala osamala kuti asachite ufumu pa anthu a Mulungu koma kuti akhale zitsanzo za gulu la nkhosalo. (1 Petro 5:2, 3) Amene ali ndi mwayi woimira Wolamulira wa chilengedwe chonse, polankhula modzichepetsa m’dzina lake ndi kuuza anthu kulikonse za Ufumu wake si anthu osankhika ochepa okha, koma Mboni zonse za Yehova, amuna ndi akazi omwe.
14 Ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimazindikira mmene Yehova akutsogolera gulu lake looneka? Kodi zoganiza zanga, zolankhula zanga ndiponso zochita zanga zimasonyeza zimenezo?’ Kusinkhasinkha mfundo zotsatirazi kungathandize tonse kudzipenda moteromo.
Ngati ndimagonjeradi Kristu monga Mutu wa mpingo, ndiye kuti, mogwirizana ndi malemba otsatiraŵa, ndiyenera kumachita chiyani? (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Yohane 13:34, 35)
Ndikamayamikira zinthu zauzimu zimene ndimalandira kuchokera kwa gulu la kapolo ndi Bungwe lake Lolamulira, kodi ndimasonyeza kuti ndikulemekeza yani? (Luka 10:16)
Kodi aliyense mu mpingo, makamaka akulu, ayenera kumachita zinthu motani ndi ena? (Aroma 12:10)
15 Yehova akutitsogolera lerolino mwa kugwiritsa ntchito gulu lake looneka lomwe Kristu akuliyang’anira. Maganizo athu pa makonzedwe ameneŵa amasonyeza mmene timaonera nkhani ya ulamuliro. (Ahebri 13:17) Satana amati anthufe tinachuluka dyera. Koma ngati titumikira m’njira iliyonse yofunika ndi kupeŵa zinthu zodzionetsera, timaonetsa kuti Mdyerekezi ndi wabodza. Tikamakonda ndi kulemekeza amene amatitsogolera, koma n’kumakana ‘kutama anthu chifukwa cha kupindula nawo,’ timasangalatsa Yehova. (Yuda 16; Ahebri 13:7) Mwa kukhala okhulupirika ku gulu la Yehova, timasonyeza kuti Yehova ndiye Mulungu wathu ndi kuti ndife ogwirizana pomulambira.—1 Akorinto 15:58.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• Kodi gulu looneka la Yehova masiku ano n’chiyani? Kodi cholinga chake n’chiyani?
• Kodi ndani anaikidwa kukhala Mutu wa mpingo, ndipo amatitsogolera mwachikondi kudzera m’makonzedwe ati ooneka?
• Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo abwino ati kwa amene ali m’gulu la Yehova?
[Mafunso]
1. Kodi Baibulo limatiuzanji za gulu la Yehova, nanga n’chifukwa chiyani tifunika kudziŵa zimenezo?
2. Kodi ndi mpingo watsopano uti umene Mulungu anakhazikitsa?
3. Kodi chinachitika n’chiyani pa Pentekoste mu 33 C.E. monga umboni wosatsutsika wakuti tsopano Mulungu anali kugwiritsa ntchito mpingo watsopano?
4. Kodi ndani lerolino amene amapanga gulu looneka la Yehova?
5. Kodi ndani amene amatsogolera gulu la Mulungu, ndipo amalitsogolera motani?
6. (a) Kodi zinaoneka motani m’zaka 100 zoyambirira kuti utsogoleri wa mpingo unali kuchokera kumwamba? (b) N’chiyani chikuonetsa kuti Yesu adakali Mutu wa mpingo?
7. (a) Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndani, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi ‘kapoloyo’ anapatsidwa ntchito yotani?
8. (a) Kodi gulu la kapolo lili ndi maudindo otani tsopano? (b) N’chifukwa chiyani tifunika kulabadira malangizo amene timalandira kudzera m’njira imene Mulungu waika?
9, 10. (a) M’zaka 100 zoyambirira, kodi panali njira yotani yothetsera mafunso okhudza ziphunzitso ndiponso kupereka malangizo polalikira uthenga wabwino? (b) Kodi pali njira yotani yoyang’anira ntchito ya anthu a Yehova masiku ano?
11. (a) Kodi akulu ndi atumiki otumikira amaikidwa motani? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kugwirizana kwambiri ndi oikidwa pa udindo?
12. Kodi akazi amawagwiritsa ntchito motani Yehova m’gulu lake?
13. (a) Kodi Baibulo limalimbikitsa akulu kukhala ndi maganizo otani pa udindo wawo? (b) Kodi tonse tingakhale ndi mwayi wotani?
14. Pogwiritsa ntchito malemba amene asonyezedwa, kambiranani mafunso amene ali kumapeto kwa ndimeyi.
15. (a) Kodi maganizo athu pa gulu looneka la Yehova amasonyeza chiyani? (b) Kodi ndi motani mmene tingaonetsere kuti Mdyerekezi ndi wabodza n’kusangalatsa mtima wa Yehova?
[Zithunzi patsamba 133]
Yehova amatitsogolera pogwiritsa ntchito gulu lake looneka limene Kristu akuliyang’anira