MUTU 3
“Kumbukirani Amene Akutsogolera Pakati Panu”
MAWU a mtumwi Paulo amenewa, olembedwa pa Aheberi 13:7, angamasuliridwenso kuti: “Kumbukirani anthu amene amakulamulirani.” Kuyambira pa Pentekosite wa mu 33 C.E., atumwi okhulupirika a Ambuye wathu Yesu Khristu ndi amene ankatumikira ngati bungwe lolamulira limene linali ndi udindo wopereka malangizo ku mpingo wachikhristu womwe unali utangokhazikitsidwa kumene. (Mac. 6:2-4) Pofika m’chaka cha 49 C.E., bungwe lolamulira linali litakula moti munalinso anthu ena omwe sanali atumwi. Ndipo bungwe lolamulira limene linagamula nkhani yokhudza mdulidwe, linali lopangidwa ndi “atumwi ndi akulu ku Yerusalemu.” (Mac. 15:1, 2) Bungweli linali ndi udindo wosamalira nkhani zokhudza Akhristu onse. Ankatumiza makalata ndi malamulo omwe ankalimbikitsa mipingo komanso omwe ankathandiza kuti ophunzira apitirize kukhala ogwirizana. Mipingo inkamvera ndi kugonjera malangizo ochokera ku bungwe lolamulira, ndipo chifukwa chochita zimenezi, Yehova ankaidalitsa komanso inkawonjezereka.—Mac. 8:1, 14, 15; 15:22-31; 16:4, 5; Aheb. 13:17.
2 Koma atumwi atamwalira, mpatuko waukulu unayamba. (2 Ates. 2:3-12) Monga mmene Yesu ananeneratu m’fanizo lake lonena za tirigu ndi namsongole, tirigu (Akhristu odzozedwa) anasakanikirana ndi namsongole (Akhristu onyenga). Kwa zaka zambiri, tirigu ndi namsongole zinaloledwa kuti zikulire limodzi mpaka nthawi yokolola, yomwe ndi “mapeto a nthawi ino.” (Mat. 13:24-30, 36-43) Pa nthawiyi Mkhristu wodzozedwa aliyense payekha ankagwiritsidwabe ntchito ndi Yesu koma panalibe bungwe lolamulira, kapena kuti njira yodziwika bwino imene Yesu ankagwiritsa ntchito popereka malangizo kwa otsatira ake. (Mat. 28:20) Komabe anali ataneneratu kuti zinthu zidzasintha m’nthawi yokolola.
3 Yesu Khristu anayamba kufotokoza fanizo lomwe ndi mbali ya “chizindikiro” cha “mapeto a nthawi ino” ndi funso lakuti: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?” (Mat. 24:3, 42-47) Yesu anasonyeza kuti kapolo wokhulupirikayu azidzapereka chakudya chauzimu kwa anthu a Mulungu “pa nthawi yoyenera.” M’nthawi ya atumwi, Yesu ankagwiritsa ntchito gulu la anthu potsogolera mpingo. Mofanana ndi zimenezi, kapolo wokhulupirika amene Yesu akugwiritsa ntchito m’nthawi ya mapeto ino si munthu mmodzi ayi.
KODI “KAPOLO WOKHULUPIRIKA NDI WANZERU” NDI NDANI?
4 Kodi Yesu anasankha ndani kuti azidyetsa otsatira ake? Anasankha Akhristu odzozedwa amene ali padziko lapansi. Baibulo limawafotokoza anthu amenewa kuti ndi “ansembe achifumu” omwe apatsidwa ntchito “‘yolengeza makhalidwe abwino kwambiri’ a amene anawaitana kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.” (1 Pet. 2:9; Mal. 2:7; Chiv. 12:17) Kodi Akhristu onse odzozedwa amene ali padziko lapansi ali m’gulu la kapolo wokhulupirika? Ayi. Pa nthawi imene ankadyetsa mozizwitsa amuna 5,000, osawerengera akazi ndi ana, Yesu anapereka chakudyacho kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawa chakudyacho kwa anthu. (Mat. 14:19) Anadyetsa anthu ambiri pogwiritsa ntchito anthu ochepa. Masiku anonso akugwiritsa ntchito njira ngati yomweyi popereka chakudya chauzimu.
5 Choncho, “mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika ndi wanzeru,” ndi kagulu kochepa ka abale odzozedwa omwe amakonza ndi kupereka chakudya chauzimu m’nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. (Luka 12:42) M’masiku otsiriza ano, abale odzozedwa amene ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” amatumikira limodzi kulikulu lathu. Abale odzozedwa amenewa ndi omwe ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.
6 Khristu amagwiritsa ntchito bungwe limeneli pofotokozera anthu mmene maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwira komanso kupereka malangizo a pa nthawi yake a mmene anthu angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo. Chakudya chauzimu chimenechi chimaperekedwa kudzera m’mipingo ya Mboni za Yehova. (Yes. 43:10; Agal. 6:16) Kale, kapolo kapena mtumiki yemwe anali wokhulupirika ankapatsidwa udindo woyang’anira zinthu zonse zapakhomo. Mofanana ndi zimenezi, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wapatsidwa udindo woyang’anira zinthu za Khristu padzikoli. Choncho, kapolo wokhulupirika amayang’aniranso chuma, ntchito yolalikira, ntchito yophunzitsa pa misonkhano ikuluikulu, ntchito yopanga mabuku komanso amaika anthu pa maudindo osiyanasiyana ndipo “antchito apakhomo” amapindula ndi zimenezi.—Mat. 24:45.
7 Ndiyeno kodi “antchito apakhomo” amenewa ndi ndani? Mwachidule, ndi onse amene amapindula ndi chakudya chauzimu. Poyamba antchito apakhomo anali Akhristu odzozedwa okhaokha. Koma patapita nthawi, khamu lalikulu la “nkhosa zina” linakhalanso m’gulu la antchito apakhomo. (Yoh. 10:16) Magulu awiri onsewa amalandira chakudya chauzimu chofanana kuchokera kwa kapolo wokhulupirika.
8 Yesu akadzabwera pa chisautso chachikulu kudzapereka chiweruzo ku dziko loipali, ndi pamene adzaike kapolo wokhulupirika pa udindo wachiwiri woti “aziyang’anira zinthu zake zonse.” (Mat. 24:46, 47) Pa nthawi imeneyi, abale amene ali m’gulu la kapolo wokhulupirika limodzi ndi Akhristu onse odzozedwa adzalandira mphoto yawo yakumwamba. Onse pamodzi alipo 144, 000 ndipo adzalamulira limodzi ndi Khristu kumwamba. Ngakhale kuti pa nthawiyi padziko lapansi padzakhala palibe kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, Yehova ndi Yesu azidzapereka malangizo kwa nzika za Ufumu wa Mesiya pogwiritsa ntchito anthu amene adzasankhidwe kukhala “akalonga.”—Sal. 45:16.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA ‘KUKUMBUKIRA AMENE AKUTSOGOLERA PAKATI PATHU’?
9 Pali zifukwa zambiri zotichititsa ‘kukumbukira amene akutsogolera pakati pathu’ ndiponso kusonyeza kuti timawakhulupirira. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kothandiza? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani.” (Aheb. 13:17) Choncho tiyenera kumvera ndi kugonjera malangizo a anthu amene akutitsogolera chifukwa amatiyang’anira kuti tikhale otetezeka komanso kuti zinthu zizitiyendera bwino mwauzimu.
10 Palemba la 1 Akorinto 16:14, Paulo anati: “Zonse zimene mukuchita, muzichite mwachikondi.” Choncho, zilizonse zimene abale amene amatitsogolera amasankha kuti tizitsatira, amazichita chifukwa cha khalidwe lapadera limeneli la chikondi. Lemba la 1 Akorinto 13:4-8 limanena kuti: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. Chikondi sichichita nsanje, sichidzitama, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha, sichikwiya. Sichisunga zifukwa. Sichikondwera ndi zosalungama, koma chimakondwera ndi choonadi. Chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha.” Popeza anthu amene amatitsogolera amatikonda ndipo amasankha zinthu zonse n’cholinga choti zitiyendere bwino, sitikayikira kuti kutsatira malangizo amene amatipatsa n’kothandiza kwambiri. Zimene abalewa amachita zimasonyezanso kuti Yehova amatikonda.
Kumvera anthu amene amatiyang’anira n’kofunika kwambiri kuti zinthu zitiyendere bwino mwauzimu
11 Mofanana ndi mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, anthu amene Yehova akuwagwiritsa ntchito potsogolera anthu ake ndi opanda ungwiro. Komabe Yehova wakhala akugwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro kuti akwaniritse cholinga chake. Mwachitsanzo, Nowa anamanga chingalawa komanso analalikira zoti Mulungu akufuna kuwononga anthu oipa. (Gen. 6:13, 14, 22; 2 Pet. 2:5) Mose anasankhidwa kuti atsogolere anthu a Mulungu kutuluka ku Iguputo. (Eks. 3:10) Ndiponso Mulungu anagwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro kuti alembe Baibulo. (2 Tim. 3:16; 2 Pet. 1:21) Choncho, timakhulupirirabe gulu la Mulungu ngakhale kuti Yehova akugwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro kuti azitsogolera ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Timachita zimenezi chifukwa timadziwa kuti gululi silingakwanitse kuchita zimene limachita popanda kuthandizidwa ndi Yehova. Kapolo wasonyeza kuti amatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu chifukwa chopirira mavuto amene wakhala akukumana nawo. Yehova wadalitsa kwambiri mbali ya padziko lapansi ya gulu lake, choncho tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi gululi komanso kulikhulupirira ndi mtima wonse.
KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI TIMAKHULUPIRIRA AMENE AKUTITSOGOLERA?
12 Abale amene ali ndi udindo mu mpingo amasonyeza kuti amakhulupirira kapolo polandira ndi mtima wonse ndi kukwaniritsa maudindo amene apatsidwa. (Mac. 20:28) Ena tonsefe timasonyeza kuti timakhulupirira kapolo tikamalalikira mwakhama za Ufumu kunyumba ndi nyumba, popanga maulendo obwereza komanso pochititsa maphunziro a Baibulo. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Kuti tipindule mokwanira ndi chakudya chauzimu chimene kapolo wokhulupirika amapereka, timakonzekera ndi kupezeka pamisonkhano yachikhristu kuphatikizapo misonkhano yadera ndi yachigawo. Timapindulanso kwambiri tikamalimbikitsana pamene tikucheza ndi abale athu pamisonkhano imeneyi.—Aheb. 10:24, 25.
13 Timasonyezanso kuti timakhulupirira kapolo tikamathandiza gulu la Mulungu ndi zopereka zathu. (Miy. 3:9, 10) Tikadziwa kuti abale athu akusowa zinazake timawathandiza mwamsanga. (Agal. 6:10; 1 Tim. 6:18) Timachita zimenezi chifukwa chowakonda ndipo nthawi zonse timafufuza njira zimene tingasonyezere kuti tikuyamikira Yehova ndi gulu lake pa zinthu zonse zabwino zimene amatichitira.—Yoh. 13:35.
14 Njira ina imene timasonyezera kuti timakhulupirira kapolo ndi kugwirizana ndi zimene wasankha. Zimenezi zikuphatikizapo kumvera modzichepetsa malangizo omwe timapatsidwa ndi abale amene ali ndi udindo woyang’anira, monga oyang’anira madera komanso akulu mumpingo. Abale amenewa ali m’gulu la anthu ‘amene amatitsogolera,’ omwe tiyenera kuwamvera ndi kuwagonjera. (Aheb. 13:7, 17) Ngakhale kuti sitingamvetse zifukwa zimene asankhira kuchita zinazake, koma tiyenera kumverabe chifukwa timadziwa kuti tikamawamvera zinthu zidzatiyendera bwino. Ndipo Yehova amatidalitsa chifukwa chomvera Mawu ake komanso gulu lake. Timasonyezanso kuti timagonjera Ambuye wathu, Yesu Khristu.
15 Choncho tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Satana, yemwe ndi mulungu wa nthawi ino, akuyesetsa mmene angathere kunyoza dzina la Yehova ndi gulu lake. (2 Akor. 4:4) Koma ifeyo tiyenera kupewa misampha yake. (2 Akor. 2:11) Iye akudziwa kuti “wangotsala ndi kanthawi kochepa” kuti aponyedwe m’phompho n’chifukwa chake akuyesetsa kuti apatutse anthu ambiri kwa Yehova. (Chiv. 12:12) Choncho pamene Satana akuchita zimenezi, tiyenera kuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Tiyeneranso kukhulupirira kwambiri njira imene Yehova akugwiritsa ntchito potsogolera anthu ake masiku ano. Kuchita zimenezi kumalimbitsa ubale wathu wa padziko lonse.