-
“Kapolo Wokhulupirika” Wapambana Mayeso!Nsanja ya Olonda—2004 | March 1
-
-
2, 3. Kodi ‘kapolo woipa ameneyo’ anachokera kuti, ndipo zinakhala bwanji?
2 Yesu atangotha kufotokoza za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” anafotokoza za kapolo woipa. Anati: “Kapolo woipa [ameneyo, NW] akanena mumtima mwake, Mbuye wanga wachedwa; nadzayamba kupanda akapolo anzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera; mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekeza iye, ndi nthaŵi yosadziŵa iye, nadzam’dula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.” (Mateyu 24:48-51) Mawu akuti ‘kapolo woipa ameneyo’ akutikumbutsa mawu okhudza kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene Yesu ananena asanafike pamfundoyi. Inde, ‘kapolo woipayu’ anachokera pa kagulu ka kapolo wokhulupirika.a Motani?
-
-
“Kapolo Wokhulupirika” Wapambana Mayeso!Nsanja ya Olonda—2004 | March 1
-
-
4. Kodi Yesu anachitanji ndi “kapolo woipa” pamodzi ndi onse omwe asonyeza mtima wofanana ndi wake?
4 Anthuŵa, omwe kale anali Akristu, anayamba kudziŵika monga “kapolo woipa,” ndipo Yesu anawalanga ndi chilango ‘chowadula.’ Motani? Anawakana, ndipo sanayembekezerenso kupita kumwamba. Koma sikuti anawonongedwa nthaŵi yomweyo. Choyamba anafunika kukhala ndi nthaŵi yolira ndiponso kukukuta mano mu “mdima wakunja” kwa mpingo wachikristu. (Mateyu 8:12) Kuchokera masiku oyambirira amenewo, odzozedwa enanso ochepa asonyezanso mtima woipawu, ndi kugwirizana ndi “kapolo woipa.” Enanso a “nkhosa zina” atengera kusakhulupirika kwawo. (Yohane 10:16) Adani onse a Kristu ameneŵa alinso ‘ku mdima [wauzimu] kunja.’
-