Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”
    Nsanja ya Olonda—2013 | December 15
    • 9. Kodi ena amalakwitsa n’kumaganiza chiyani za mkate umene Yesu anagwiritsa ntchito?

      9 Anthu a m’matchalitchi ena amanena kuti Yesu anati: ‘Mkate uwu ndi thupi langa.’ Choncho amakhulupirira kuti mkatewo unasintha mozizwitsa n’kukhala thupi lake lenileni. Koma zimenezi si zoona.a Tikutero chifukwa chakuti pa nthawiyo thupi la Yesu linalipo ndipo mkate woti adyewo unaliponso. Choncho Yesu ankangonena zinthu mophiphiritsira ngati mmene ankachitiranso nthawi zina zambiri.—Yoh. 2:19-21; 4:13, 14; 10:7; 15:1.

      10. Kodi mkate wa pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye umaimira chiyani?

      10 Mkate umene anagwiritsa ntchito pa nthawiyo umaimira thupi la Yesu. Koma kodi thupi lake ndi liti? Poyamba atumiki a Mulungu ankaganiza kuti mkate umaimira mpingo wa odzozedwa, womwe umatchedwanso “thupi la Khristu.” Ankaganiza choncho chifukwa chakuti Yesu ananyemanyema mkate koma pamene ankaphedwa sanathyoledwe fupa lililonse. (Aef. 4:12; Aroma 12:4, 5; 1 Akor. 10:16, 17; 12:27) Koma atumiki a Mulunguwo ataganizira mozama n’kufufuza m’Malemba, anazindikira kuti mkatewo umaimira thupi la Yesu limene Mulungu anamukonzera. Yesu “anavutika m’thupi” mpaka kupachikidwa. Choncho mkate wa pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye umaimira thupi la Yesu limene ‘linanyamula machimo athu.’—1 Pet. 2:21-24; 4:1; Yoh. 19:33-36; Aheb. 10:5-7.

  • “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”
    Nsanja ya Olonda—2013 | December 15
    • 15, 16. Kodi pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, mkate amachita nawo chiyani?

      15 Ndiyeno chakumapeto, wokamba nkhaniyo adzasonyeza kuti yafika nthawi yoti tichite zimene Yesu anauza atumwi ake kuti azichita. Monga tanena kale, padzakhala mkate ndi vinyo. Mwina zidzaikidwa patebulo chapafupi ndi wokamba nkhani. Ndiyeno wokambayo adzafotokoza mavesi a m’Baibulo osonyeza zimene Yesu ananena ndiponso kuchita poyambitsa mwambowu. Mwachitsanzo, timawerenga m’buku la Mateyu kuti: “Yesu anatenga mkate, ndipo atapempha dalitso, anaunyemanyema n’kuupereka kwa ophunzira ake. Iye anati: ‘Eni, idyani. Mkate uwu ukuimira thupi langa.’” (Mat. 26:26) Yesu ananyema mkate wopanda chofufumitsa kuti apereke kwa ophunzira ake. Ndiyeno pa April 14, mikate yotereyi adzainyemanyema n’kuiika m’mbale.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena