“Uwu ndi Thupi Langa”
“TENGANI ndi kuudya; . . . uwu ndi thupi langa.” (Mateyu 26:26, The New Jerusalem Bible)
Ndi mawu ameneŵa, Yesu Kristu anapereka mkate wopanda chotupitsa kwa atumwi ake pamene ankakhazikitsa Mgonero wa Ambuye. Koma kodi iye anatanthauzanji ndi mawu akuti, “Uwu ndi thupi langa”?
YANKHO la funso limeneli nlofunika kwambiri kwa Aroma Katolika, popeza kuti mawu a Yesu amapanga maziko a chiphunzitso cha kusandulika kwenikweni. Mogwirizana ndi chiphunzitso chimenechi, pamene Akatolika akondwerera Misa ndikumeza mkatewo, umasandulika kukhala thupi lenileni, kapena mnofu wa Kristu. Chotero, iwo angatsutse mwamphamvu New World Translation of the Holy Scriptures, imene imamasulira mawu a Yesu motere: “Tengani, idyani. Uwu utanthauza thupi langa.” Kumasulira kumeneku kumapereka lingaliro lakuti mkatewo unali chiphiphiritsiro cha mnofu wa Yesu, osati mnofu weniweniwo. Kodi ndimatembenuzidwe ati amene akupereka lingaliro lolondola?
Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “ndi” kapena “utanthauza” ndilo e·stinʹ. Kwenikweni ilo limatanthauza “ndi,” koma lingatanthauzenso “kusonyeza, kuzindikiritsa.” Kodi ndikumasulira kuti kumene kuli kwabwinoko m’mawu apambuyo ndi apatsogolo a lembali?
Ofunika kudziŵidwa ndi mawu am’tsinde pa Mateyu 26:26 m’chinenero cha Chispanya La Sagrada Escritura, Texto y comentario por Profesores de la Compañía de Jesús, Nuevo Testamento I (Malemba Opatulika, Lemba ndi Ndemanga Yopangidwa ndi Aprofesa a Kampani ya Yesu, Chipangano Chatsopano). Iyo ikufotokoza kuti: ‘Kutembenuzaku, mogwirizana ndi katchulidwe ka mawu, kukanamasuliridwanso bwino monga kuzindikiritsa kapena kuphiphiritsira monga ndi—kutanthauza chizindikiritso chenicheni. Monga zitsanzo za mmene tanthauzo nla kuphiphiritsira, Genesis 41:26; Ezekieli 5:5; Danieli 7:17; Luka 8:11; Mateyu 13:38; 16:18; Agalatiya 4:24; Chibvumbulutso 1:20 angasonyezedwe. Tanthauzo la liwu lakuti ndi ([m’lingaliro lonena kuti] chofanana ndi) likusonyezedwa, monga momwe lingawonekere m’magazini a ziphunzitso zoikidwiratu, osaphatikizapo kuthekera kwa kufotokoza mwa fanizo, kapena kuphiphiritsira, ndiponso m’njira imene Tchalitchi Choyambirira chinamvetsetsera mawuwo.’
Monga momwe matembenuzidwe Aroma Katolika ameneŵa akusonyezera mosabisa, m’katchulidwe ka mawu, mawu a Yesu angamvedwe m’njira zonse ziŵirizo. Kwenikweni, liwu Lachigiriki lakuti e·stinʹ limatembenuzidwa “tanthauzo la” kwinakwake mu New Jerusalem Bible Yachikatolika. (Mateyu 12:7) Kodi ndiliwu liti limene wotembenuza ayenera kusankha pa Mateyu 26:26? Popeza kuti Yesu adali wamoyobe m’thupi langwiro pamene analankhula mawu a lemba limenelo, mkate umene anapereka kwa atsatiri ake sukanakhala mnofu wake weniweni. Kuwonjezerapo, thupi lake lonse lathunthu langwiro linaperekedwa monga nsembe yadipo. (Akolose 1:21-23) Chotero, kumasulira kwabwino koposa kwa vesili ndi uku: “Uwu utanthauza thupi langa.” Mkate wopanda chotupitsawo unaphiphiritsira thupi la Yesu, lomwe linali pafupi kuperekedwa nsembe kaamba ka anthu.
Ngakhale ngati Baibulo lanu laumwini liri ndi mawu akuti “Uwu ndi thupi langa,” simufunikira kusokonezeka. Kaŵirikaŵiri Yesu anagwiritsira ntchito chinenero chofananacho. Pamene iye anati, “Ine ndine khomo” ndi, “Ine ndine mpesa weniweni,” palibe amene anamvetsetsa kuti iye analidi khomo lenileni kapena mpesa weniweni. (Yohane 10:7; 15:1) Ndipo mogwirizana ndi The New Jerusalem Bible, pamene iye anapereka chikho kwa ophunzira ake nati: “Chikho ichi ndi pangano latsopano,” palibe amene analingalira kuti chikho chenichenicho chinali pangano latsopano. (Luka 22:20) Mofananamo, pamene iye ananena kuti mkatewo ‘unali’ thupi lake, tiyenera kumvetsetsa kuti mkatewo ‘unatanthauza,’ kapena unaphiphiritsira, thupi lake.