Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 1/1 tsamba 8-9
  • Thayo la Kukhala Wophunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thayo la Kukhala Wophunzira
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Thayo la Kukhala Wophunzira
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kukhala Wophunzira wa Yesu Ndi Udindo Waukulu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Amene Anakhala Ophunzira a Yesu
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Ulaliki Wotchuka Woposa Wonse Umene Unaperekedwa
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 1/1 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Thayo la Kukhala Wophunzira

PAMBUYO pa kuchoka ku nyumba ya M’farisi wotchuka, yemwe mwachiwonekere ali chiwalo cha Bwalo Lalikulu la Milandu la Chiyuda, Yesu akupitiriza kulinga ku Yerusalemu. Makamu akulu akumutsatira iye. Koma nziti zomwe ziri zolinga zawo? Nchiyani kwenikweni chomwe chiri chophatikizidwa m’kukhala wotsatira wake wowona?

Pamene akuyenda, Yesu atembenukira kwa makamuwo ndipo mwinamwake kuwazizwitsa iwo pamene akunena kuti: “Munthu akadza kwa ine osada atate wake ndi amake ndi mkazi wake ndi ana ndi abale ndi alongo, inde, ndi moyo wake womwe wa iyemwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.”

Nchiyani chimene Yesu akutanthauza? Osati kuti otsatira ake ayenera m’chenicheni kudana ndi anansi awo. M’malomwake, iwo ayenera kudana nawo m’lingaliro la kukonda iwo mochepera kuposa mmene amamkondera iye. Agogo a Yesu Yakobo ananenedwa kukhala “anada” Leya ndi kukonda Rakele, chomwe chinatanthauza kuti Leya anakondedwa mochepera kuposa m’ng’ono wake Rakele.

Lingalirani, kachiŵirinso, kuti Yesu ananena kuti wophunzira ayenera kudana “ndi moyo wake wa iyemwini,” kapena moyo. Kachiŵirinso chimene Yesu akutanthauza chiri chakuti wophunzira wowona ayenera kumkonda Iye mokulirapo kuposa mmene amakondera moyo wake wa iyemwini. Yesu mwakutero akugogomezera kuti kukhala wophunzira wake kuli thayo lalikulu. Sichiri chinachake chofunikira kutengedwa popanda kulingalira kosamalitsa.

Zovuta ndi chizunzo zikuloŵetsedwamo m’kukhala wophunzira wa Yesu, monga mmene iye akupitirizira kusonyeza: “Amene aliyense sasenza [mtengo wake wozunzirapo, NW] wa mwini yekha ndi kudza pambuyo panga sakhoza kukhala wophunzira wanga.” Chotero, wophunzira wowona ayenera kukhala wofunitsitsa kupita pansi pa thayo lina la chitonzo limene Yesu anapirira nalo, ngakhale kuphatikizapo, ngati nkoyenera, kufa pa manja a adani a Mulungu, chimene Yesu posachedwapa adzachita.

Kukhala wophunzira wa Kristu, chotero, kuli nkhani imene makamu omutsatira iye afunikira kuisanthula mosamalitsa. Yesu akugogomezera nsongayi kupyolera mwa fanizo. “Pakuti,” iye akutero, “ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali sathanga wakhala pansi naŵerengera mtengo wake, awone ngati ali nazo za kuimaliza? Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya ku maziko ake osakhoza kuimaliza, anthu onse akuyang’ana adzayamba kumseka iye, ndi kunena kuti, ‘Munthu uyu anayamba kumanga koma sanathe kumaliza.’”

Chotero Yesu akuchitira fanizo kwa makamu otsatira iye kuti asanakhale ophunzira ake, iwo ayenera kukhala ogamulapo mwamphamvu kuti angakwaniritse chomwe chikulowetsedwamo, monga mmene munthu wofuna kumanga nsanja amatsimikizira asanayambe kuti ali ndi magwero a kuimaliza iyo. Akumapereka fanizo lina, Yesu akupitiriza:

“Kapena mfumu yanji, pa kupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sathanga wakhala pansi nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye uja alinkudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi aŵiri? Koma, ngati sakhoza, atumiza akazembe pokhala winayo ali kutali nafunsa za mtendere.”

Yesu kenaka akugogomezera nsonga ya mafanizo ake, mwa kunena kuti: “Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo sakhoza kukhala wophunzira wanga.” Chimenecho ndi chimene makamu omutsatira iye, ndipo, inde, wina aliyense amene aphunzira za Kristu, ayenera kukhala wofunitsitsa kuchita. Iwo ayenera kukhala okonzekera kupereka nsembe chirichonse chimene ali nacho​—zinthu zawo zonse, kuphatikizapo moyo weniweniwo​—ngati angakhale ophunzira ake. Kodi muli wofunitsitsa kuchita ichi?

“Kotero, m’chere, uli wokoma,” Yesu akupitiriza. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri iye ananena kuti ophunzira ake ali “m’chere wa pa dziko lapansi,” kutanthauza kuti iwo ali ndi chisonkhezero chosunga pa anthu, mongadi mmene m’chere weniweni uli chosungitsa. “Koma ngati m’chere utasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Suyenera kuthira pa munda kapena pa dzala,” Yesu akumaliza tero. “Autaya kunja. Amene ali nawo makutu akumva, amve.”

Chotero Yesu akusonyeza kuti ngakhale awo omwe akhala ophunzira ake kwa nthaŵi yaitali sayenera kufooka m’kugamulapo kwawo kwa kupitiriza. Ngati iwo atero, adzakhala opanda pake, chinthu choseketsa ku dziko iri ndipo osayenera pamaso pa Mulungu, m’chenicheni, chitonzo pa Mulungu. Chotero, mofanana ndi m’chere wosukuluka, woipitsidwa, iwo adzataidwa kunja, inde, kuwonongedwa. Luka 14:25-35; Genesis 29:30-33; Mateyu 5:13.

◆ Nchiyani chimene chimatanthauza “kudana” ndi anansi ake a wina ndi iyemwini?

◆ Ndi mafanizo aŵiri otani amene Yesu akupereka, ndipo kodi iwo akutanthauzanji?

◆ Ndi iti yomwe iri nsonga ya ndemanga zomalizira za Yesu ponena za m’chere?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena