Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Anapemphera Pamene Anali ndi Chisoni Kwambiri
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Atafika kumundako, komwe kunali mitengo yambiri ya maolivi, Yesu anauza atumwi ake 8 kuti amudikire ndipo iye anatengana ndi atumwi atatu. N’kutheka kuti Yesu anawauza kuti adikirire pamalo olowera m’mundawo chifukwa ananena kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.” Yesu anatengana ndi Petulo, Yakobo ndi Yohane ndipo analowa m’mundamo. Iye anavutika kwambiri mumtima ndipo anauza atumwi atatuwo kuti: “Moyo wanga ukumva chisoni chofa nacho. Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”—Mateyu 26:36-38.

  • Anapemphera Pamene Anali ndi Chisoni Kwambiri
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Yesu ali kumwamba ankaona mmene Aroma ankazunzira komanso kuphera anthu. Choncho ankadziwa zimene akumane nazo chifukwa pa nthawiyi anali ndi thupi ngati lathuli ndipo ankamva kupweteka. Koma Yesu ankavutika kwambiri chifukwa ankadziwa kuti aphedwa ngati chigawenga ndipo zimenezi zikanachititsa kuti anthu anyoze dzina la Atate wake. Pa nthawiyi anali atatsala ndi maola ochepa kuti apachikidwe pamtengo ngati mmene zinkakhalira ndi munthu amene wanyoza Mulungu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena