Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 10/1 tsamba 8-9
  • Kupsyinjika Mtima m’Munda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupsyinjika Mtima m’Munda
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Ululu m’Mundamo
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Anapemphera Pamene Anali ndi Chisoni Kwambiri
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Tsiku Lomaliza la Moyo Waumunthu wa Yesu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kukonzekeretsa Atumwi Kaamba ka Kuchoka Kwake
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 10/1 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kupsyinjika Mtima m’Munda

PMENE Yesu wamaliza kupemphera, iye ndi atumwi ake okhulupirika 11 akuimba nyimbo zachitamando kwa Yehova. Kenaka akutsika pachipinda chosanja, kutulukira panja pozizira mumdima wa usiku, ndikubwerera ku Chigwa cha Kedroni kulinga ku Betaniya. Koma ali paulendowo, iwo akuima pamalo okondeka, munda wa Getsemane. Uwo uli pafupi ndi Phiri la Azitona. Yesu wakhala akukumana ndi atumwi ake pamalo ameneŵa kaŵirikaŵiri pakati pa mitengo ya azitona.

Akumasiya atumwi asanu ndi atatu​—mwinamwake pafupi ndi poloŵera pa mundawo​—iye akuwalangiza kuti: “Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere.” Pamenepo iye anatenga atatu enawo​—Petro, Yakobo, ndi Yohane​—napita mkati mwa mundawo. Yesu akhala wachisoni navutitsidwa kwakukulu. ‘Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa,’ iye akuwauza tero. ‘Khalani pano muchezere pamodzi ndi ine.’

Pamene anamuka patsogolo pang’ono, Yesu agwada pansi, ndipo ataweramitsa nkhope yake pansi ayamba kupemphera mowona mtima motere: ‘Atate, ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire ine; koma si monga ndifuna ine, koma inu.’ Kodi iye akutanthauzanji? Kodi nchifukwa ninji iye ali ‘ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa’? Kodi iye akuzemba chosankha chake cha kufa ndi kupereka dipo?

Kutalitali! Yesu sakupembedzera kuti apulumutsidwe ku imfa. Ngakhale lingaliro lopeŵa imfa yansembe, limene panthaŵi ina linaperekedwa ndi Petro, nlonyansa kwa iye. M’malo mwake, iye ngwopsyinjika mtima chifukwa akuwopa kuti njira imene adzaferamo posachedwapa​—monga mpandu woipitsitsa​—idzabweretsa chitonzo pa dzina la Atate wake. Iye akuzindikira tsopano kuti m’maola oŵerengeka adzapachikidwa pamtengo monga munthu woipitsitsa​—wochitira Mulungu mwano! Ichi ndicho chimene chikumvutitsa kwambiri.

Pambuyo popemphera kwa nthaŵi yaitali, Yesu akubwerera napeza atumwi atatuwo akugona. Akumalankhula kwa Petro, iye akuti: ‘Simukhoza kuchezera ndi ine [ola limodzi, NW]? Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m’kuyesedwa.’ Komabe, akumavomereza chitsenderezo chomwe ali nacho chifukwa chakuti ndiusiku, iye akuti: “Mzimutu uli wakufuna, koma thupi liri lolefuka.”

Pamenepo Yesu akubwererako kachiŵirinso napempha kuti Mulungu achotse ‘chikho ichi,’ uku ndiko kuti, gawo lake logaŵiridwa ndi Yehova, kapena chifuniro chake. Pamene iye akubwerera, akuwapezanso atatuwo atagona pamene akufunikira kuti adzipemphera kuti asaloŵe m’kuyesedwa. Pamene Yesu akulankhula nawo, iwo sakudziŵa zoyankha.

Pomalizira pake, nthaŵi yachitatu, Yesu akupita pamtunda woponya mwala, nagwada pansi napemphera molira ndi misozi, nati: ‘Atate, mukafuna inu, chotsani chikho ichi pa ine.’ Yesu akumva kupweteka kwakukulu chifukwa cha chitonzo chimene imfa yake monga mpandu ikabweretsa padzina la Atate wake. Eya, kupatsidwa mlandu wakuti ngwamwano​—munthu amene amatukwana Mulungu​—nkovuta kupirira nako!

Mosasamala kanthu za izo, Yesu akupitiriza kupemphera motere: ‘Si chimene ndifuna ine, koma chimene mufuna inu.’ Momvera Yesu akugonjetsera chifuniro chake kwa Mulungu. Pamphindi imeneyi, mngelo wochokera kumwamba awonekera namulimbikitsa ndi mawu olimbikitsa. Mwachiwonekere, mngeloyo akuuza Yesu kuti wavomerezedwa ndi Atate wake.

Komabe, ndi mtolo wolemetsa wotani nanga umene uli pamapeŵa a Yesu! Moyo wake weniweni wosatha ndi wa mtundu wonse wa anthu uli pamuyeso. Chitsenderezo chamaganizo nchachikulu. Chotero Yesu akupitiriza kupemphera mofunitsitsa, ndipo thukuta lake lakhala ngati madontho a mwazi pamene likugwera pansi. The Journal of the American Medical Association ikufotokoza kuti: “Ngakhale kuti ichi ndi chochitika cha kamodzikamodzi, thukuta lamwazi . . . lingawoneke mumkhalidwe wovutika maganizo kwabasi.”

Pambuyo pake, Yesu akubwerera kachitatu kwa atumwi ake, ndipo awapezanso akugona. Iwo atopa ndi chisoni. “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula?” (New Testament in Modern Chicheŵa) iye akufunsa. ‘Chakwanira; yafika nthaŵi; onani Mwana wa munthu aperekedwa m’manja a anthu ochimwa. Ukani, tizimuka; onani wakundiperekayo ali pafupi.’

Iye ali chilankhulirebe, Yudase Isikariote akudza, ali ndi khamu la anthu onyamula miuni ndi nyali ndi zida. Mateyu 26:30, 36-47; 16:21-23; Marko 14:26, 32-43; Luka 22:39-47; Yohane 18:1-3; Ahebri 5:7.

◆ Pamene achoka m’chipinda chosanja, kodi Yesu akumka nawo kuti atumwiwo, ndipo kodi iye akuchitanji kumeneko?

◆ Pamene Yesu akupemphera, kodi atumwiwo akuchitanji?

◆ Kodi nchifukwa ninji Yesu wapsyinjika mtima, ndipo kodi iye akupemphanji kwa Mulungu?

◆ Kodi nchiyani chomwe chikusonyezedwa ndi kukhala monga madontho a mwazi kwa thukuta la Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena