Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kp tsamba 24-27
  • “Kuti Mungaloŵe M’kuyesedwa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kuti Mungaloŵe M’kuyesedwa”
  • Dikirani!
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyesedwa Kuti Tichite Chiyani?
  • “Chezerani ndi Kupemphera”
  • Musayembekezere Zimene Sizingachitike
  • Kumbukirani Nkhani Zimene Zinabuka Zija
  • “Yandikirani kwa Mulungu”
  • Kugonjetsa Kufooka Kwaumunthu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Mungatani Kuti Musamagonje Mukakumana ndi Mayesero?
    Galamukani!—2014
  • “Yehova Mulungu Wako Ndi Amene Uyenera Kumulambira”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Mzimu Woyera Umatipatsa Mphamvu Yolimbana ndi Mayesero Ndiponso Zofooketsa
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Dikirani!
kp tsamba 24-27

“Kuti Mungaloŵe M’kuyesedwa”

“Chezerani ndi kupemphera, kuti mungaloŵe m’kuyesedwa.”—MATEYU 26:41.

NKHAŴA imene Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, anali nayo inali yaikulu kuposa nkhaŵa iliyonse imene anakhalapo nayo. Mapeto a moyo wake wa padziko lapansi anali pafupi. Yesu ankadziŵa kuti pakapita nthaŵi yochepa adzamangidwa, kuweruzidwa kuti aphedwe, ndi kupachikidwa pa mtengo wozunzirapo. Ankadziŵa kuti chilichonse chimene angachite chidzakhudza dzina la Atate ake. Yesu ankadziŵanso kuti, kuti anthu adzakhale ndi moyo m’tsogolo, zimadalira zimene achite. Ali ndi nkhaŵa yaikulu choncho, kodi anachita chiyani?

2 Yesu anapita ku munda wa Getsemane ndi ophunzira ake. Malo ameneŵa Yesu ankawakonda kwambiri. Ali kumeneko anayenda pang’ono kuchoka pamene panali ophunzira ake. Ali payekha, analankhula ndi Atate ake kuti amupatse mphamvu, ndipo anapemphera kuchokera pansi pa mtima, osati kamodzi kokha, koma katatu. Ngakhale kuti anali wangwiro, Yesu sanaganize kuti akanatha kulimbana ndi chiyeso chimenechi yekha.—Mateyu 26:36-44.

3 Masiku ano, nafenso tikukumana ndi zinthu zimene zimatidetsa nkhaŵa. Kumayambiriro kwa kabuku kano tinaona umboni wosonyeza kuti tikukhala m’masiku otsiriza a dongosolo loipa lino. Ziyeso ndi mavuto m’dziko la Satana lino zikuwonjezeka. Zimene ifeyo timachita monga anthu amene timanena kuti timatumikira Mulungu zimakhudza dzina lake, ndiponso kuti tidzakhale ndi moyo m’dziko lake latsopano zimadalira zimenezo. Yehova timamukonda. Tikufuna kupirira mpaka mapeto, kaya akhale mapeto a moyo wathu kapena a dongosolo lino, chilichonse chimene chingayambirire. (Mateyu 24:13) Koma kodi tingapitirize bwanji kuona kuti nthaŵi yatsala pang’ono kutha, n’kupitirizabe kudikira?

4 Podziŵa kuti ophunzira ake, oyambirirawo komanso a masiku ano, adzakumana ndi ziyeso, Yesu anawalimbikitsa kuti: “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungaloŵe m’kuyesedwa.” (Mateyu 26:41) Kodi mawu amenewo amatanthauza chiyani kwa ife masiku ano? Kodi mumakumana ndi ziyeso zotani? Ndipo kodi ‘mungachezere,’ kapena kuti kukhala maso, motani?

Kuyesedwa Kuti Tichite Chiyani?

5 Tonsefe tsiku lililonse timakumana ndi chiyeso chokodwa mu “msampha wa Mdyerekezi.” (2 Timoteo 2:26) Baibulo limatichenjeza kuti Satana akulimbana makamaka ndi anthu olambira Yehova. (1 Petro 5:8; Chivumbulutso 12:12, 17) Kodi cholinga chake n’chiyani? Osati kuti atiphe ayi. Satana sangapindule chilichonse ngati titafa tili okhulupirika kwa Mulungu. Satana akudziŵa kuti pa nthaŵi Yake, Yehova adzagonjetsa imfa mwa kuukitsa anthu akufa.—Luka 20:37, 38.

6 Satana akufuna kuwononga chinthu chamtengo wapatali kwambiri kuposa moyo umene tili nawowu. Chinthuchi ndicho kukhulupirika kwathu kwa Mulungu. Satana akuyesayesa kusonyeza kuti angathe kutileketsa kulambira Yehova. Choncho ngati titati tigonje n’kukhala osakhulupirika, mwa kusiya kulalikira uthenga wabwino kapena kusiya kutsatira mfundo zachikristu, Satana angaone kuti wapambana. (Aefeso 6:11-13) Choncho “woyesayo” amatipatsa mayeso.—Mateyu 4:3.

7 “Machenjerero a mdyerekezi” ndi osiyanasiyana. (Aefeso 6:11) Angatiyese ndi zinthu monga kukonda kwambiri chuma, mantha, kukayikira, kapena kukonda kwambiri zosangalatsa. Koma njira yake imodzi imene imagwira ntchito kwambiri ndiyo kutilefula. Pokhala katswiri wodziŵa kuchenjerera ena, amadziŵa kuti kulefuka kungatipangitse kugonja mosavuta poyesedwa. (Miyambo 24:10) Choncho, makamaka tikavutika maganizo, m’pamene amatiyesa kuti timugonjere.—Salmo 38:8.

8 Pamene tikuyandikira kwambiri mapeto a masiku otsiriza, zikuoneka kuti zinthu zolefula zikuchuluka, ndipo zimatikhudza. (Onani bokosi lakuti “Zinthu Zina Zimene Zimatilefula.”) Tikalefuka sititha kuchita zambiri, kaya kulefukako kubwere mwanjira yotani. ‘Kuchita machawi,’ kapena kuti kuwombola nthaŵi, kuti muchite zinthu zauzimu monga kuphunzira Baibulo, kupita ku misonkhano yachikristu, ndi kupita mu utumiki zingakhale zinthu zovuta kwambiri ngati mwatopa, ngati simukuganiza bwino, ndiponso ngati simukumva bwino mumtima. (Aefeso 5:15, 16) Kumbukirani kuti Woyesayo akufuna kuti mugonje. Koma nthaŵi ino si yoti munthu ayambe kubwerera m’mbuyo kapena yoti asiye kuzindikira kuti tikukhala m’nthaŵi yofunika kukhala atcheru. (Luka 21:34-36) Kodi mungalimbane bwanji ndi ziyeso n’kupitirizabe kudikira? Taganizirani mfundo zinayi zimene zingakuthandizeni.

“Chezerani ndi Kupemphera”

9 Dalirani Yehova mwa kupemphera. Kumbukirani chitsanzo cha Yesu m’munda wa Getsemane. Ali ndi nkhaŵa yaikulu m’maganizo mwake, kodi anachita chiyani? Analankhula ndi Yehova kuti amuthandize, ndipo anapemphera ndi mtima wake wonse mpaka “thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.” (Luka 22:44) Taganizirani zimenezi. Yesu ankamudziŵa bwino Satana. Yesu ali kumwamba anaona mayesero onse amene Satana amagwiritsa ntchito kuti agonjetse atumiki a Mulungu. Komabe, Yesu sanaganize kuti akanatha kuthana mosavuta ndi chilichonse chimene Woyesayo angamuyese nacho. Ngati Mwana wangwiro wa Mulungu anaona kuti anafunika kupemphera kuti Mulungu amuthandize ndi kumupatsa mphamvu, kuli bwanji ifeyo!—1 Petro 2:21.

10 Kumbukiraninso kuti atalimbikitsa ophunzira ake ‘kuchezera ndi kupemphera,’ Yesu anati: “Mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.” (Mateyu 26:41) Kodi Yesu ankanena za thupi la ndani? Mwachionekere sankanena za thupi lake, chifukwa thupi lake langwiro silinali lofooka m’njira iliyonse. (1 Petro 2:22) Koma sizinali choncho ndi ophunzira ake. Chifukwa cha kupanda ungwiro kumene anatengera kwa makolo awo ndiponso chibadwa chawo chokonda kuchita uchimo, anafunikira kwambiri kuthandizidwa kulimbana ndi ziyeso. (Aroma 7:21-24) N’chifukwa chake anawalimbikitsa ophunzirawo, komanso Akristu onse pambuyo pawo, kupempherera thandizo kuti athe kulimbana ndi ziyeso. (Mateyu 6:13) Yehova amayankha mapemphero oterowo. (Salmo 65:2) Motani? Tiyeni tionepo njira ziŵiri.

11 Yoyamba, Mulungu amatithandiza kuzindikira ziyeso. Ziyeso za Satana zili ngati misampha imene yatcheredwa paliponse m’njira yamdima. Ngati simuiona, mungathe kukodwa nayo. Mwa kugwiritsa ntchito Baibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo, Yehova amaunika misampha ya Satana, motero amatithandiza kupeŵa kugonja ndi ziyeso. Kuyambira zaka za m’mbuyomu mpaka panopa, mabuku ndi nkhani za pa misonkhano yadera ndi yachigawo mobwerezabwereza zakhala zikutichenjeza za kuopsa kwa kuopa anthu, chiwerewere, kukonda chuma, ndi ziyeso zina za Satana. (Miyambo 29:25; 1 Akorinto 10:8-11; 1 Timoteo 6:9, 10) Kodi simukuthokoza Yehova chifukwa chotichenjeza za machenjera a Satana? (2 Akorinto 2:11) Machenjezo onsewo ndi yankho la mapemphero anu opempha thandizo kuti mulimbane ndi ziyeso.

12 Yachiŵiri, Yehova amayankha mapemphero athu mwa kutipatsa mphamvu zimene timafunikira kuti tipirire ziyeso. Mawu ake amati: “Mulungu . . . sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” (1 Akorinto 10:13) Ngati tipitiriza kumudalira, Mulungu sadzalola kuti chiyeso chikhale chachikulu kwambiri mpaka chitilepheretse kukhala ndi mphamvu zauzimu zimene tingafunikire kuti tilimbane nacho. Kodi ‘amatiikira populumukirapo’ motani? Amapereka “Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye.” (Luka 11:13) Mzimu umenewo ungatithandize kukumbukira mfundo za m’Baibulo zimene zingatilimbikitse kuchita zinthu zolondola ndi kutithandiza kusankha zinthu mwanzeru. (Yohane 14:26; Yakobo 1:5, 6) Ungatithandize kusonyeza makhalidwe enieniwo amene timafunikira kuti tithane ndi zizoloŵezi zoipa. (Agalatiya 5:22, 23) Mzimu wa Mulungu ungachititsenso okhulupirira anzathu ‘kukhala otitonthoza mtima.’ (Akolose 4:11) Kodi simukuthokoza Yehova chifukwa choyankha mwachikondi choncho mapemphero anu ofuna thandizo?

Musayembekezere Zimene Sizingachitike

13 Kuti tidikire, sitiyenera kuyembekezera zinthu zimene sizingachitike. Chifukwa cha zovuta pamoyo wathu, tonsefe timatopa nthaŵi zina. Koma tiyenera kukumbukira kuti Mulungu sanalonjeze kuti tidzakhala ndi moyo wopanda mavuto m’dongosolo lakale lino. Ngakhale mu nthaŵi za m’Baibulo, atumiki a Mulungu anakumana ndi mavuto, monga kuzunzidwa, umphaŵi, kuvutika maganizo, ndi matenda.—Machitidwe 8:1; 2 Akorinto 8:1, 2; 1 Atesalonika 5:14; 1 Timoteo 5:23.

14 Masiku ano, nafenso timakumana ndi mavuto. Tingakumane ndi chizunzo, tingade nkhaŵa chifukwa cha mavuto a zachuma, tingavutike maganizo, tingadwale, ndipo tingavutike m’njira zina. Ngati Yehova akanati atiteteze ku zovuta zonse modabwitsa, kodi zimenezo sizikanapangitsa Satana kutonza Yehova? (Miyambo 27:11) Yehova amalola atumiki ake kuyesedwa, mpaka nthaŵi zina amalola kuti atumiki akewo afe mosayembekezereka chifukwa cha zochita za otsutsa.—Yohane 16:2.

15 Choncho, kodi Yehova walonjeza chiyani? Monga momwe taonera kale, walonjeza kuti adzatithandiza kuthana ndi chiyeso chilichonse chimene tingakumane nacho ngati timukhulupirira ndi mtima wathu wonse. (Miyambo 3:5, 6) Kudzera mwa Mawu ake, mzimu wake, ndi gulu lake, amatiteteza mwauzimu, kutithandiza kuteteza ubwenzi wathu ndi iye. Ngati ubwenzi umenewo uli bwino, ngakhale titafa, zinthu zidzatiyenderabe bwino. Palibe chimene chingalepheretse Mulungu kupatsa mphoto atumiki ake okhulupirika, ngakhale imfa imene singamulepheretse. (Ahebri 11:6) Ndipo m’dziko latsopano limene latsala pang’ono kubwera, Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake ena onse ochititsa chidwi ndi kudalitsa anthu amene amamukonda.—Salmo 145:16.

Kumbukirani Nkhani Zimene Zinabuka Zija

16 Kuti tipirire mpaka mapeto, tiyenera kukumbukira nkhani zofunika kwambiri zimene zinachititsa Mulungu kulola kuipa. Ngati nthaŵi zina mavuto athu amaoneka osatheka kuthana nawo ndipo timafuna kugonja, tiyenera kudzikumbutsa kuti Satana anatsutsa ufulu wa Yehova wolamulira. Wonyengayo anakayikiranso kudzipereka ndi kukhulupirika kwa anthu olambira Mulungu. (Yobu 1:8-11; 2:3, 4) Nkhani zimenezo, ndiponso njira imene Yehova wasankha kuti azithetsere n’zofunika kwambiri kuposa aliyense wa ife payekha. Motani?

17 Chifukwa chakuti Mulungu walola kuvutika kukhalapo kwa kanthaŵi, zapatsa anthu ena mpata wophunzira choonadi. Taganizirani izi: Yesu anazunzika n’cholinga choti tipeze moyo. (Yohane 3:16) Kodi sitiyamikira zimenezo? Koma kodi ndife okonzeka kuvutika kwa kanthaŵi kuti enanso apeze moyo? Kuti tipirire mpaka mapeto, tiyenera kukumbukira kuti nzeru za Yehova n’zapamwamba kwambiri kuposa zathu. (Yesaya 55:9) Adzathetsa kuipa pa nthaŵi imene idzakhale yabwino kuthetseratu nkhani zimene zinabuka zija komanso imene idzakhale yabwino kwa ife kuti zinthu zitiyendere bwino mpaka kalekale. Indedi, kodi pangakhalenso njira ina yabwino yothetsera nkhanizo kuposa imeneyi? Mulungu sachita chinthu chosalungama!—Aroma 9:14-24.

“Yandikirani kwa Mulungu”

18 Kuti tipitirizebe kuona kuti nthaŵi yatsala pang’ono, tiyenera kukhalabe oyandikana ndi Yehova. Musaiwale kuti Satana akuchita chilichonse chimene angathe kuti awononge ubwenzi wathu wabwino ndi Yehova. Satana angakonde titamaganiza kuti mapeto sadzafika ndipo palibe chifukwa cholalikirira uthenga wabwino kapena kutsatira mfundo za m’Baibulo pamoyo wathu. Koma “ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Tiyenera kuyesetsa ‘kukaniza Mdyerekezi.’ Sitiyenera kuona ubwenzi wathu ndi Yehova ngati chinthu chopepuka. Baibulo limatilimbikitsa mwachikondi kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:7, 8) Kodi mungayandikire bwanji kwa Yehova?

19 Kusinkhasinkha ndi kupemphera n’zofunika kwambiri. Mavuto akakula kwambiri pamoyo wanu, muuzeni Yehova zakukhosi kwanu. Mukamapempha zinthu mosapita m’mbali, m’pamenenso muzitha kuona bwino yankho la mapemphero anu. Yankho lake mwina nthaŵi zonse silingakhale limene inuyo mumayembekezera, koma ngati cholinga chanu ndi kumulemekeza ndi kukhalabe wokhulupirika, adzakupatsani thandizo limene mukufunikira kuti mupirire mpaka mapeto. (1 Yohane 5:14) Mukamaona akukutsogolerani m’moyo wanu, mudzayandikira kwambiri kwa iye. Kuŵerenga ndi kuganizira za makhalidwe a Yehova ndiponso njira zake, monga momwe zafotokozedwera m’Baibulo n’kofunikanso kwambiri. Kusinkhasinkha koteroko kumakuthandizani kumudziŵa bwino Yehova, kumakhudza mtima wanu kuti muzichita zinthu zabwino, ndipo kumakulitsa chikondi chanu pa iye. (Salmo 19:14) Ndipo chikondi chimenecho, kuposa china chilichonse, n’chimene chidzakuthandizeni kulimbana ndi ziyeso n’kupitiriza kudikira.—1 Yohane 5:3.

20 Kuti tiyandikane ndi Yehova m’pofunikanso kuti tikhale oyandikana ndi okhulupirira anzathu. Tikambirana zimenezi m’mbali yomaliza ya kabuku kano.

MAFUNSO OGWIRITSA NTCHITO POPHUNZIRA

• Kodi Yesu anachita chiyani pamene anali ndi nkhaŵa yaikulu mapeto a moyo wake wa padziko lapansi atatsala pang’ono kufika, ndipo analimbikitsa ophunzira ake kuchita chiyani? (Ndime 1-4)

• N’chifukwa chiyani Satana akulimbana makamaka ndi anthu olambira Yehova, ndipo kodi amatiyesa m’njira zotani? (Ndime 5-8)

• Kuti tilimbane ndi ziyeso, n’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera nthaŵi zonse (Ndime 9-12), kusayembekezera zinthu zimene sizingachitike (Ndime 13-15), kukumbukira nkhani zimene zinabuka (Ndime 16-17), ndi ‘kuyandikira kwa Mulungu’ (Ndime 18-20)?

[Bokosi patsamba 25]

Zinthu Zina Zimene Zimatilefula

Thanzi/zaka zathu. Ngati tikudwala matenda osachiritsika kapena ngati ukalamba ukutilepheretsa kuchita zinthu zina, tingalefuke chifukwa cholephera kuchita zambiri potumikira Mulungu.—Ahebri 6:10.

Kukhumudwa. Tingalefuke ngati tikuona kuti anthu sakumvetsera pamene tikuyesetsa kuwalalikira Mawu a Mulungu.—Miyambo 13:12.

Kudziona ngati wosafunika. Chifukwa chozunzidwa kwa nthaŵi yaitali, munthu angayambe kukhulupirira kuti palibe amene amamukonda, ngakhale Yehova amene.—1 Yohane 3:19, 20.

Kupsetsedwa mtima. Ngati munthu wapsetsedwa mtima kwambiri ndi wokhulupirira mnzake, angakhumudwe kwambiri mpaka kufika posiya kupita ku misonkhano yachikristu kapena kuchita nawo utumiki wa kumunda.—Luka 17:1.

Kuzunzidwa. Anthu ena a chikhulupiriro chosiyana ndi chanu angakutsutseni, kukuzunzani, kapena kukusekani.—2 Timoteo 3:12; 2 Petro 3:3, 4.

[Chithunzi patsamba 26]

Yesu anatilimbikitsa ‘kuchezera ndi kupemphera’ kuti tipeze thandizo polimbana ndi ziyeso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena