Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w20 March tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kutetezedwa Ndi Apolisi N’kolimbitsa Mtima Komanso N’kokayikitsa
    Galamukani!—2002
  • ‘Anasonkhanitsa a Bwalo la Akulu’
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Apolisi Ndi Ofunika Chifukwa Chiyani?
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
w20 March tsamba 31
JApolisi apakachisi amanga anthu awiri molamulidwa ndi anthu otsutsa kulambira koona.

Mafunso Ochokera Kwa Owerenga

Kodi apolisi apakachisi anali ndani, nanga ntchito yawo inali yotani?

Anthu amtundu wa Levi omwe sanali ansembe ankagwira ntchito zina zofanana ndi zimene apolisi amagwira masiku ano. Iwo ankagwira ntchito zimenezi motsogoleredwa ndi woyang’anira kachisi. Munthu wina wolemba mbiri ya Ayuda dzina lake Philo anafotokoza ntchito zina za apolisi apakachisi. Iye anati: “Ena ankakhala pageti penipeni pa kachisi. Koma ena ankakhala chakutsogolo kuti aziletsa anthu ena kupita kumalo opatulika, kaya mwadala kapena mosazindikira. Ena ankazungulira kunja kwa kachisiyo ndipo ankachita izi mosinthanasinthana masana ndi usiku womwe.”

Khoti Lalikulu la Ayuda linkatha kutuma anthu amenewa kuti awathandize pa zinthu zina. Awa anali ngati asilikali a Chiyuda okhawo amene Aroma ankawalola kuyenda ndi zida.

Katswiri wina dzina lake Joachim Jeremias ananena kuti: “Pamene anthu anapita kukagwira Yesu, iye anawafunsa kuti n’chifukwa chiyani sanamugwire pamene ankaphunzitsa m’kachisi. (Mat. 26.55) Yesu sakanafunsa funso limeneli zikanakhala kuti apolisi apakachisi sanali m’gulu la anthu odzamugwirawo.” Katswiriyu amakhulupiriranso kuti anthu amene anatumidwa kuti akagwire Yesu pa nthawi ina izi zisanachitike analinso apolisi apakachisi. (Yoh. 7:32, 45, 46) Apolisiwa limodzi ndi wowayang’anira ndi amenenso anatumidwa kuti akagwire ophunzira a Yesu n’kupita nawo ku Khoti Lalikulu la Ayuda. Ndipo ayenera kuti ndi amene anagwira Paulo n’kumukokera kunja kwa kachisi.​—Mac. 4:1-3; 5:17-27; 21:27-30.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena