Moyo ndi Uminisitala za Yesu
“Ali Woyenera Kumupha”
YESU, womangidwa monga mpandu wamba, akupititsidwa kwa Anasi, mwamuna wotchuka yemwe kale anali mkulu wansembe. Anasi anali mkulu wansembe pamene Yesu monga mnyamata wazaka 12 zakubadwa anazizwitsa aphunzitsi achirabi pakachisi. Ana angapo a Anasi pambuyo pake anatumikira monga mkulu wansembe, ndipo pakali pano mkamwini wake Kayafa akutumikira pamalowo.
Mwinamwake Yesu akupititsidwa kunyumba kwa Anasi choyamba chifukwa cha kutchuka kwa wansembe wamkuluyo kwanthaŵi yaitali m’moyo wopembedza Wachiyuda. Kudzera pa nyumba pa Anasi kumeneku kuti amuwone kukupatsa nthaŵi Mkulu Wansembe Kayafa kuti asonkhanitse Bungwe la Akulu, khoti lalikulu Lachiyuda laziŵalo 71, ndikutinso apeze mboni zonama.
Wansembe wamkulu Anasi tsopano akufunsa Yesu ponena za ophunzira ake ndiponena za kuphunzitsa kwake. Komabe, Yesu akuyankha kuti: ‘Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa ine nthaŵi zonse m’sunagoge ndi m’kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu. Undifunsiranji ine? Funsa iwo amene adamva chimene ndinalankhula nawo; tawona, amenewo adziŵa chimene ndinanena ine.’
Pakumva izi, mmodzi wa maofisala woimirira pafupi ndi Yesu ampanda kumaso, ndikunena kuti: ‘Kodi uyankha mkulu wa ansembe chomwecho?’
‘Ngati ndalankhula choipa,’ Yesu akuyankha motero, ‘chita umboni wa choipacho, koma ngati bwino, undipandiranji?’ Pambuyo pakuyankhana kumeneku, Anasi akutumiza Yesu womangidwa kwa Kayafa.
Tsopano akulu ansembe onse ndi amuna aakulu ndi alembi, inde, Bungwe la Akulu lonse, akuyamba kusonkhana. Mwachiwonekere malo awo okumanira ndikunyumba kwa Kayafa. Komabe, kuzenga mlandu koteroko pausiku wa Paskha nkowonekeratu kukhala kotsutsana ndi lamulo Lachiyuda. Koma ichi sichikulepheretsa atsogoleri achipembedzowo kuchita chifuniro chawo choipa.
Milungu ingapo pasadakhale, pamene Yesu anaukitsa Lazaro, Bungwe la Akulu linali litagamula kale pakati pawo kuti iye ayenera kufa. Ndipo masiku aŵiri okha pasadakhale, Lachitatu, akulu achipembedzowo anapanga upo pamodzi kuti amgwire Yesu mwamachenjera ndikumupha. Talingalirani, iye anali ataweruzidwa kale asanazengedwe mlandu!
Kuyesayesa kukuchitidwa tsopano kwakupeza mboni zimene zidzapereka umboni wonama kotero kuti amkoloŵeke mlandu Yesu. Komabe, mboni sizikupezeka zovomerezana ndi chinenezo chawo. Potsirizira pake, aŵiri akubwera kutsogolo ndikunenetsa kuti: ‘Ife tinamva iye alikunena, kuti, Ine ndidzawononga Kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.’
“Suyankha kanthu kodi?” Akufunsa motero Kayafa. ‘Nchiyani ichi chimene awa alikuchitira mboni?’ Koma Yesu akhala chete. Nzochititsa manyazi kwa Bungwe la Akulu, popeza kuti ngakhale m’chinenezo chonama ichi, mbonizo zikulephera kumvana m’zokamba zawo. Chotero mkulu wansembeyo akuyesa machenjera osiyana.
Kayafa akudziŵa mmene Ayuda amakwiira ndi aliyense wodzinenera kukhala Mwana weniweni wa Mulungu. Pa zochitika ziŵiri pasadakhale, iwo mwansontho anatcha Yesu kukhala wamwano woyenerera kuphedwa, pamene molakwa analingalira kuti iye ankadziyesa kukhala wofanana ndi Mulungu. Kayafa tsopano akupempha mwamachenjera nati: “Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.”
Mosasamala kathu ndizimene Ayudawo akulingalira, Yesu alidi Mwana wa Mulungu. Ndipo kukhala chete kukalingaliridwa kuti iye wakana kukhala kwake Kristu. Chotero Yesu akuyankha molimba mtima nati: “Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.”
Pakumva izi, Kayafa, mwaukali, anang’amba zovala zake nafuula nati: ‘Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo; muganiza bwanji?’
“Ali woyenera kumupha,” akulengeza motero a Bungwe la Akuluwo. Ndiyeno akuyamba kumchitira chipongwe, ndikunena zinthu zambiri momnyoza. Ampanda pankhope nam’lavulira. Ena aphimba pankhope pake ndikummenya khofu namnyodola nati: “Utilote ife, Kristu Iwe; wakumenya Iwe ndani?” Mkhalidwe wamwano, wopanda lamulowu ukuchitika mkati mwa kuzenga mlandu kwa usikuko. Mateyu 26:57-68; 26:3, 4; Marko 14:53-65; Luka 22:54, 63-65; Yohane 18:13-24; 11:45-53; 10:31-39; 5:16-18.
◆ Kodi Yesu akupititsidwa kuti choyamba, ndipo kodi nchiyani chimene chikumchitikira kumeneko?
◆ Kodi Yesu kenaka akupititsidwa kuti, ndipo kaamba ka chifuno chotani?
◆ Kodi Kayafa watha bwanji kuchititsa Bungwe la Akulu kulengeza kuti Yesu ayenera kuphedwa?
◆ Kodi ndi mkhalidwe wamwano, wopanda lamulo wotani umene ukukhalapo mkati mwa kuzenga mlanduko?