Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuikidwa Lachisanu, Manda Opanda Kanthu pa Sande
PANTHAŴIYI Nlachisanu masana kwenikweni, ndipo Sabata la Nisani 15 lidzayamba dzuŵa litaloŵa. Mtembo wa Yesu udakali wolenjekekabe pamtengopo, koma achifwamba aŵiri okhala kumbali kwake adakali amoyo. Lachisanu masana likutchedwa Lokonzera popeza kuti mpamene anthu amakonza zakudya ndi kutsiriza ntchito ina iriyonse yamwamsanga yomwe singayembekezere kufikira pambuyo pa Sabata.
Sabata lomwe latsala pafupi kuyamba sindilo Sabata lanthaŵi zonse (tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mlungu) komanso Sabata la ubwino woŵirikiza kaŵiri, kapena ‘lalikulu.’ Likutchedwa motero chifukwa chakuti Nisani 15, lomwe liri tsiku loyamba la Phwando la Mikate Yopanda Chotupitsa la masiku asanu ndi aŵiri (ndipo nthaŵi zonse liri Sabata, mosasamala kanthu ndi pa tsiku lotani la mlungu pomwe ilo limadza), limachitika patsiku limodzimodzilo la Sabata yanthaŵi zonse.
Mogwirizana ndi lamulo la Mulungu, matupi sayenera kusiidwa olenjekeka pamtengo usiku wonse. Chotero Ayuda akupempha Pilato kuti imfa ya onyongedwawo ifulumizidwe mwa kuthyola miyendo yawo. Motero, asirikaliwo athyola miyendo ya achifwamba aŵiriwo. Koma popeza kuti Yesu akuwoneka kuti wafa, miyendo yake sikuthyoledwa. Ichi chikukwaniritsa lemba lomwe limati: ‘Fupa la iye silidzathyoledwa.’
Komabe, kuti atsimikizire kuti Yesu wafadi, mmodzi wa msirikali akumubaya ndi mkondo m’nthiti mwake. Mkondowo ukubaya dera la mtima wake, ndipo pomwepo mwazi ndi madzi zituluka. Mtumwi Yohane, yemwe ali mboni yowona ndi maso, akusimba kuti ichi chikukwaniritsa lemba lina lomwe limati: “Adzayang’ana pa Iye amene anampyoza.”
Yemwenso alipo pa kunyongedwako ndi Yosefe wochokera ku mzinda wa Arimateya, chiŵalo cholemekezeka cha Bungwe la Akulu. Iye anakana kuyanja kachitidwe kosalungama ka khoti lalikulu kotsutsana ndi Yesu. Yosefe ali kwenikweni wophunzira wa Yesu, ngakhale kuti wachita mantha kudzitchula monga mmodzi wa iwo. Komabe tsopano, akuchita molimba mtima napita kwa Pilato kukapempha thupi la Yesu. Pilato aitana mkulu wa asirikali wosamalira nkhaniyi, ndipo pamene ndunayi yapereka chitsimikiziro kuti Yesu ngwakufa, Pilato aupereka mtembowo.
Yosefe autenga mtembowo naukulunga m’bafuta woyera kukonzekera kukauika m’manda. Iye akuthandizidwa ndi Nikodemo, chiŵalo china cha Bungwe la Akulu. Nikodemo nayenso walephera kusonyeza chikhulupiriro chake mwa Yesu chifukwa cha kuwopa kutaya udindo wake. Koma tsopano iye abweretsa mpukutu wokhala ndi pafupifupi makilogramu Achiroma makumi atatu mphambu atatu a mure ndi mafuta onunkhira a aloe amtengo wapamwamba. Mtembo wa Yesu ukukulungidwa ndi nsalu zokhala ndi zonunkhira zimenezi, monga mwa mwambo wamaikidwe a maliro Achiyuda.
Ndiyeno mtembowo ugonekedwa m’manda achikumbukiro atsopano a Yosefe osemedwa m’thanthwe m’munda wapafupi. Potsirizira pake, chimwala chachikulu chikunkhunizidwa pakhomo pa mandawo. Kukonzekera mtembowo kufulumizidwa kuti atsirize kuika maliro Sabata lisanafike. Chotero, Mariya wa Magadala ndi Mariya amayi ŵake ŵa Yakobo Wamng’ono, amene mwinamwake akhala akuthandizira kukonzekerako, athamangira kunyumba kukakonzekera zonunkhira ndi mafuta owonjezereka. Pambuyo pa Sabata, iwo akonzekera kukaupakanso mtembo wa Yesu kuti usungike kwa nyengo yaitali.
Tsiku lotsatira, pa Loŵeruka (Sabata), ansembe aakulu ndi Afarisi apita kwa Pilato nati: ‘Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu. Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapena ophunzira ake angadze, nadzamuba iye, nadzanena kwa anthu, kuti iye anauka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho.’
“Tengani alonda,” akuyankha motero Pilato. “Mukani, kasungeni monga mudziwa.” Chotero iwo amuka ndi kukasungitsa manda mwa kusindikizapo chizindikiro pamwalapo ndi kuika asirikali Achiroma monga alonda.
Pa Sande m’mamawa, Mariya wa Magadala, Mariya amayi ŵake ŵa Yakobo, limodzinso ndi Salome, Yohana, ndi akazi ena, abweretsa zonunkhira kumandako kudzapaka mtembo wa Yesu. Akali m’njira iwo alankhuzana nati: “Adzatikunkhunizira ndani mwalawo, pa khomo la manda?” Koma pamene afika, iwo apeza kuti chivomezi chachitika ndipo mngelo wa Yehova wakunkhuniza mwala kuuchotsapo. Alondawo palibepo, ndipo manda ali opanda kanthu! Mateyu 27:57–28:2; Marko 15:42–16:4; Luka 23:50–24:3, 10; Yohane 19:31–20:1; 19:14; 12:42; Levitiko 23:5-7; Deuteronomo 21:22, 23; Salmo 34:20; Zekariya 12:10.
◆ Kodi nchifukwa ninji Lachisanu likutchedwa Lokonzera, ndipo kodi Sabata ‘lalikulu’ nchiyani?
◆ Kodi ndi malemba ati omwe akwaniritsidwa m’chigwirizano ndi mtembo wa Yesu?
◆ Kodi Yosefe ndi Nikodemo ali nakonji kuikidwa kwa Yesu, ndipo kodi unansi wawo ndi Yesu ngwotani?
◆ Kodi ndi pempho lotani limene ansembe akulipereka kwa Pilato, ndipo kodi iye akuliyankha motani?
◆ Kodi nchiyani chomwe chikuchitika pa Sande m’mamawa?