Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chilungamo Osati Miyambo Yapakamwa
    Nsanja ya Olonda—1990 | October 1
    • 12. (a) Kodi nkusintha kotani kuchoka pa njira yanthaŵi zonseyi ya kupereka zilozero ku Malemba Achihebri kumene Yesu anakupanga mu Ulaliki wake wa pa Phiri, ndipo kodi nchifukwa ninji? (b) Kodi tikuphunziranji m’kugwiritsira ntchito kwachisanu ndi chimodzi kwa mawu akuti “Kunanenedwa”?

      12 Pamene Yesu poyambirira anagwira mawu kuchokera m’Malemba Achihebri, iye anati: “Kwalembedwa.” (Mateyu 4:4, 7, 10) Koma nthaŵi zisanu ndi imodzi mu Ulaliki wa pa Phiri, iye anayamba yomwe inamveka ngati ndemanga yochokera m’Malemba Achihebri ndi mawu akuti: “Kunanenedwa.” (Mateyu 5:21, 27, 31, 33, 38, 43) Kodi nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti iye ankalozera ku Malemba monga momwe anamasulidwira mlingaliro la miyambo ya Afarisi imene inatsutsana ndi malamulo a Mulungu. (Deuteronomo 4:2; Mateyu 15:3) Ichi chamveketsedwa m’kulozera kwa Yesu kwa chisanu ndi chimodzi ndi komalizira uku mumpambowu: “Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako.” Koma panalibe lamulo la Mose limene linati, ‘Uzida mdani wako.’ Alembi ndi Afarisi ndiwo analinena. Uku kunali kumasulira kwawo Chilamulo kwa kukondana ndi mnansi wako​—mnansi wako Wachiyuda, osati wina aliyense.

  • Chilungamo Osati Miyambo Yapakamwa
    Nsanja ya Olonda—1990 | October 1
    • 14. Kodi ndimotani mmene Yesu akutipatsira uphungu kusalowa konse panjira yotsogolera ku chigololo?

      14 Yesu chotsatira anati: ‘Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.’ (Mateyu 5:27, 28) Kodi inuyo simudzachita chigololo? Pamenepo musalowemo konse m’njira yonkira kukachichita mwa kusunga malingaliro oganizira za icho. Chinjirizani mtima wanu, mmene mumakhala maziko a zinthu zoterezi. (Miyambo 4:23; Mateyu 15:18, 19) Yakobo 1:14, 15 akuchenjeza motere: ‘Koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iyemwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolako chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.’ Nthaŵi zina anthu amati: ‘Musayambe kuchita chinthu chomwe simungathe kuchimaliza.’ Koma pankhani ino tiyenera kunena kuti: ‘Musayambe kuchita chinthu chomwe simungathe kuchileka.’ Ena amene akhala okhulupirika ngakhale pamene awopsyezedwa ndi imfa pamaso pa asilikali okonzekera kuwombera mfuti pambuyo pake agwera m’mbuna yoipa ya chisembwere cha kugonana.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena