-
Yerusalemu—“Mzinda wa Mfumu Yaikulukulu”Nsanja ya Olonda—1998 | October 15
-
-
Yerusalemu—“Mzinda wa Mfumu Yaikulukulu”
“Musalumbire . . . kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulukulu.”—MATEYU 5:34, 35.
-
-
Yerusalemu—“Mzinda wa Mfumu Yaikulukulu”Nsanja ya Olonda—1998 | October 15
-
-
Malo a “Mpando Wachifumu wa Yehova”
4, 5. Kodi Davide anachita zotani pothandizira kuti Yerusalemu akhale wofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Mulungu?
4 M’zaka za zana la 11 B.C.E., Yerusalemu anadziŵika padziko lonse lapansi monga likulu la mtundu wosungika ndiponso wamtendere. Yehova Mulungu anadzoza mnyamatayo Davide kukhala mfumu ya mtundu wakalewo—Israyeli. Davide ndi mbadwa zake zoloŵa ufumu zinakhala pa “mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova,” kapena kuti “mpando wachifumu wa Yehova” ku Yerusalemu, likulu la bomalo.—1 Mbiri 28:5; 29:23.
5 Mwamuna woopa Mulunguyo Davide—Mwisrayeli wa fuko la Yuda—analanda Yerusalemu kwa Ayebusi olambira mafano. Panthaŵiyo, mzindawo unali kungokwanira paphiri lotchedwa Ziyoni, koma dzina limenelo linadzakhala lotanthauzanso Yerusalemu. M’kupita kwa nthaŵi, Davide analisamutsira ku Yerusalemu likasa la pangano la Mulungu ndi Israyeli, kumene analiika m’hema. Zaka zambiri kumbuyoko Mulungu anali kulankhula ndi Mose mumtambo wokhala pamwamba pa Likasa lopatulikalo. (Eksodo 25:1, 21, 22; Levitiko 16:2; 1 Mbiri 15:1-3) Likasalo linaphiphiritsira kukhalapo kwa Mulungu, popeza kuti Yehova ndiye anali Mfumu yeniyeni ya Israyeli. Chotero, mwa njira ziŵirizi ankanena kuti Yehova Mulungu akulamulira ali mumzinda wa Yerusalemu.
6. Kodi Yehova analonjezanji ponena za Davide ndi Yerusalemu?
6 Yehova analonjeza Davide kuti ufumu wa nyumba yake yachifumuyo, woimiridwa ndi Ziyoni, kapena kuti Yerusalemu, sudzatha. Zimenezi zinatanthauza kuti mbadwa ina ya Davide inali kudzaloŵa ufumuwo ndi kulamulira kosatha monga Wodzozedwa wa Mulungu—Mesiya, kapena kuti Kristu.a (Salmo 132:11-14; Luka 1:31-33) Baibulo limatchulanso kuti woloŵa “mpando wachifumu wa Yehova” ameneyu wamuyaya adzalamulira mitundu yonse, osati Yerusalemu yekha.—Salmo 2:6-8; Danieli 7:13, 14.
7. Kodi Mfumu Davide anachirikiza motani kulambira koyera?
7 Ena omwe anayesayesa kuchotsapo wodzozedwa wa Mulungu, Mfumu Davide, analephera. M’malo mwake, mitundu yodana nawo inagonjetsedwa, ndipo Dziko Lolonjezedwa linafutukulidwa mpaka kumalire ake olembedwa ndi Mulungu. Davide anapezerapo mpata wokulitsira kulambira koyera. Ndipo masalmo ambiri a Davide amatama Yehova kukhala Mfumu yeniyeni ya Ziyoni.—2 Samueli 8:1-15; Salmo 9:1, 11; 24:1, 3, 7-10; 65:1, 2; 68:1, 24, 29; 110:1, 2; 122:1-4.
8, 9. Kodi kulambira koona m’Yerusalemu kunakula motani mu ulamuliro wa Mfumu Solomo?
8 Mu ulamuliro wa mwana wa Davide Solomo, kulambira Yehova kunapita patsogolo. Solomo anafutukulira Yerusalemu chakumpoto kufika kuphiri la Moriya (pamene tsopano pali malo otchedwa Dome of the Rock). Pamalo okwezeka ameneŵa, iye anali ndi mwayi womangapo kachisi wokongola kwadzaoneni wopangitsa anthu kutamanda Yehova. Likasa la pangano linaikidwa m’Malo Opatulikitsa a kachisiyo.—1 Mafumu 6:1-38.
9 Pamene mtundu wa Israyeli unali kuchirikiza ndi mtima wonse kulambira Yehova kochitikira m’Yerusalemu, uwo unali pamtendere. Pofotokoza bwino mkhalidwe umenewu, Malemba amati: “Ayuda ndi Aisrayeli anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera. . . . Nakhala ndi mtendere [Solomo] kozungulira konseko. Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake.”—1 Mafumu 4:20, 24, 25.
10, 11. Kodi zopezedwa m’mabwinja zimachirikiza motani zonena za Baibulo zokhudza Yerusalemu pamene Solomo anali kulamulira?
10 Zimene ofukula m’mabwinja apeza zimachirikiza nkhani imeneyi yonena za ulamuliro waulemerero wa Solomo. Polofesa Yohanan Aharoni m’buku lake lakuti The Archaeology of the Land of Israel (Zopezedwa m’Mabwinja a Dziko la Israyeli) anati: “Chuma chomwe chinaloŵa m’mabwalo achifumu kuchokera kumadera onse, ndi kupita patsogolo kwa zamalonda . . . zinachititsa chitukuko chamwamsanga ndiponso choonekeratu. . . . Kupita patsogolo kwa chitukukocho . . . kukuonekera osati kokha mwa zinthu za mwana alirenji komanso makamaka mwa zoumbaumba zadothi. . . . Mtundu wa zoumbaumba zadothizo ndi kutenthedwa kwake zinakhala zaukatswiri zedi.”
11 Nayenso Jerry M. Landay analemba kuti: “Mu ulamuliro wa Solomo, chitukuko chinapita patsogolo kwambiri m’Israyeli pazaka makumi atatu kuposa mmene zinachitikira pazaka mazana aŵiri apitawo. M’mabwinja a zinthu za mu ulamuliro wa Solomo timapezamo zotsala za nyumba zazikulu kwadzaoneni, mizinda yaikulu zedi yokhala ndi malinga aakulu kwambiri, nyumba zokhalamo zowonjezereka zomangidwa bwino za anthu achuma, kupitadi patsogolo kwa luso la oumba miphika ndi kapangidwe kawo ka zinthu. Timapezamonso zotsala za katundu wopangidwa kumalo akutali, umboni wakuti kunali malonda aakulu ndi maiko ena.”—The House of David.
Kuchoka pa Mtendere Kukhala Wabwinja
12, 13. Kodi nchiyani chinachitika kuti kulambira koona kulekeke m’Yerusalemu?
12 Mtendere ndi chuma cha Yerusalemu, mzinda umene munali malo opatulika a Yehova, zinalidi nkhani zoyenera kuzipempherera. Davide analemba kuti: “Mupempherere mtendere wa Yerusalemu; akukonda inu adzaona phindu. M’linga mwako mukhale mtendere, m’nyumba za mafumu mukhale phindu. Chifukwa cha abale anga ndi mabwenzi anga, ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu.” (Salmo 122:6-8) Ngakhale kuti Solomo anali ndi mwayi womanga kachisi wokongola kwambiri mumzinda wamtendere umenewo, m’kupita kwa nthaŵi iye anakwatira akazi ambiri akunja. Atakalamba, iwo anamnyenga nampangitsa kuchirikiza kulambira milungu yonyenga ya m’tsikulo. Mpatuko umenewu unaipitsa mtundu wonsewo, kuthetsa mtendere weniweni wa mtunduwo ndi wa anthu ake.—1 Mafumu 11:1-8; 14:21-24.
13 Mwana wa Solomo Rehabiamu atangoyamba kulamulira, mafuko khumi anapanduka ndi kupanga ufumu wakumpoto wa Israyeli. Chifukwa cha kulambira kwawo mafano, Mulungu analola kuti ufumuwo ulandidwe ndi Asuri. (1 Mafumu 12:16-30) Yerusalemu anakhalabe likulu la ufumu wakummwera wa Yuda wa mafuko aŵiri. Koma m’kupita kwa nthaŵi iwonso anasiya kulambira koyera, choncho Mulungu analola mzinda wopandukawo kuwonongedwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E. Kwa zaka 70 Ayuda otengedwa undende anavutika ku Babulo monga akapolo. Ndiyeno, mwa chifundo cha Mulungu, iwo analoledwa kubwerera ku Yerusalemu ndi kuyambiranso kulambira koona.—2 Mbiri 36:15-21.
14, 15. Kodi ndi motani mmene Yerusalemu anakhaliranso wofunika kwambiri ukapolo wa ku Babulo utatha, koma kodi nchiyani chinasintha?
14 Mzindawo utakhala wabwinja kwa zaka 70, m’nyumba zowonongedwazo muyenera kuti munamera zitsamba. Linga la Yerusalemu linawonongeka, ndipo linali lotseguka pamalo pamene panali zipata zazikulu ndi nsanja zolimbitsa lingalo. Komabe, Ayuda amene anabwererawo analimbika mtima. Iwo anamanga guwa la nsembe pamalo pamene kale panali kachisi nayamba kupereka nsembe kwa Yehova tsiku ndi tsiku.
15 Chimenechi chinali chiyambi chabwino, koma Yerusalemu womangidwansoyo sanakhalenso likulu la ufumu wolamuliridwa ndi mbadwa ya Mfumu Davide. M’malo mwake, Ayuda analamuliridwa ndi kazembe woikidwa ndi ogonjetsa Babulo ndipo Ayudawo anali kukhoma msonkho kwa olamulira awo Aperisiya. (Nehemiya 9:34-37) Ngakhale kuti Yerusalemu anali ‘woponderezedwa,’ uwo unakhalabe mzinda wokhawo wokondedwa ndi Yehova Mulungu padziko lonse lapansi. (Luka 21:24) Pokhala likulu la kulambira koyera, mzindawo unaimiranso ufulu wa Mulungu wochita ulamuliro padziko lonse lapansi kudzera mwa mbadwa ya Mfumu Davide.
Atsutsidwa ndi Anansi Achipembedzo Chonyenga
16. Kodi nchifukwa ninji Ayuda amene anabwerako ku Babulo analekeza kumanganso Yerusalemu?
16 Posapita nthaŵi Ayuda amene anabwerera ku Yerusalemu kuchokera kuukapolo anapanga maziko a kachisi watsopano. Koma anansi awo achipembedzo chonyenga anatumiza kalata yowaneneza kwa Mfumu Aritasasta ya Perisiya, yonena kuti Ayuda adzapanduka. Chotero, Aritasasta anawaletsa kuti asapitirize kumanga ku Yerusalemu. Mutha kuyerekezera kuti ngati munali kukhala mumzindawo kalelo, bwenzi mukusinkhasinkha za tsogolo la Yerusalemu. Chotero, Ayuda anasiya kumanga kachisi naloŵerera pakudzikundikira chuma chawo.—Ezara 4:11-24; Hagai 1:2-6.
17, 18. Kodi Yehova anagwiritsira ntchito ndani poonetsetsa kuti Yerusalemu amangidwenso?
17 Patapita zaka 17 iwo atabwerera, Mulungu anadzutsa mneneri Hagai ndi mneneri Zekariya kuti awongolere maganizo a anthu ake. Atalapa, Ayuda anayamba kumanganso kachisi. Panthaŵiyo, Dariyo anali atakhala mfumu ya Perisiya. Iye anapeza lamulo la Mfumu Koresi lonena kuti Yerusalemu amangidwenso. Dariyo anatumiza kalata kwa anansi a Ayuda, kuwachenjeza kuti ‘azikhala kutali ndi Yerusalemu’ ndipo azipereka thandizo landalama lotengedwa pamisonkho ya mfumu kuti ntchito yomangayo imalizidwe.—Ezara 6:1-13.
18 Ayuda anamaliza kumanga kachisiyo patapita zaka 22 atabwerera. Mutha kuona kuti chinthu chachikulu chimenechi chinali choyenera kuchikondwerera kwambiri. Komabe, zinthu zina zambiri m’Yerusalemu ndiponso malinga ake zinali zidakali zabwinja. Mzindawo unakonzedwa bwino “m’masiku a Nehemiya kazembe, ndi a Ezara wansembe mlembiyo.” (Nehemiya 12:26, 27) Malinga ndi umboni umene ulipo, podzafika kumapeto kwa zaka za zana lachisanu B.C.E., Yerusalemu yense anali atamangidwanso monga mzinda waukulu koposa m’dziko lakalelo.
Mesiya Aonekera!
19. Kodi Mesiya anati bwanji povomereza mkhalidwe wapadera wa Yerusalemu?
19 Komano tiyeni tidumphe zapakatipa ndipo tipite kuzaka za mazana akutsogolo panthaŵi ya chochitika china chofunika kwambiri m’chilengedwe chonse, kubadwa kwa Yesu Kristu. Mngelo wa Yehova Mulungu anali atauza amayi wa Yesu amene anali namwali kuti: “Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake . . . ndipo ufumu wake sudzatha.” (Luka 1:32, 33) Patapita zaka zambiri, Yesu anapereka Ulaliki wake wa pa Phiri wotchukawo. Muulalikiwo, anapereka chilimbikitso ndi uphungu pankhani zambiri. Mwachitsanzo, iye analimbikitsa omvetsera ake kuti azikwaniritsa zoŵinda zawo kwa Mulungu koma kuti azisamala kuti sakulumbira paliponse mwamaseŵera. Yesu anati: “Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako: koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula Kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu; kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa lili popondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulukulu.” (Mateyu 5:33-35) Panotu Yesu anatchulapo za mkhalidwe wapadera wa Yerusalemu—mkhalidwe umene mzindawo unakhala nawo kwa zaka mazana ambiri. Inde, unali “mzinda wa Mfumu yaikulukulu,” Yehova Mulungu.
20, 21. Kodi anthu ambiri okhala m’Yerusalemu anasintha motani malingaliro awo mwamsanga?
20 Atatsala pang’ono kumaliza moyo wake wa padziko lapansi, Yesu anadzipereka kwa okhala mu Yerusalemu monga Mfumu yawo yoikidwa mwalamulo. Pachochitika chosangalatsa chimenecho, ambiri anafuula mwachimwemwe kuti: “Wolemekezeka Iye wakudza m’dzina la Ambuye: Wolemekezeka Ufumu ulinkudza, wa atate wathu Davide.”—Marko 11:1-10; Yohane 12:12-15.
21 Koma mlungu umodzi usanathe, makamuwo anagwirizana ndi atsogoleri achipembedzo a m’Yerusalemu poukira Yesu. Iye anachenjeza kuti mzinda wa Yerusalemu ndiponso mtundu wonsewo sudzakhalanso woyanjidwa ndi Mulungu. (Mateyu 21:23, 33-45; 22:1-7) Mwachitsanzo, Yesu anati: “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” (Mateyu 23:37, 38) Panthaŵi ya Paskha mu 33 C.E., otsutsa Yesu anamupha popanda mlandu kunja kwa Yerusalemu. Komabe, Yehova anaukitsa Wodzozedwa wake ndi kumpatsa ulemerero wa moyo wauzimu wosakhoza kufa ku Ziyoni wakumwamba, chinthu chimene tonsefe tingapindule nacho.—Machitidwe 2:32-36.
22. Pambuyo pa imfa ya Yesu, kodi zambiri zonena za Yerusalemu zakhala zikutanthauzanji?
22 Kuyambira panthaŵi imeneyo, maulosi ambiri amene sanakwaniritsidwe onena za Ziyoni, kapena kuti Yerusalemu, tingawatenge kuti akunena za makonzedwe akumwamba kapena za otsatira a Yesu odzozedwa. (Salmo 2:6-8; 110:1-4; Yesaya 2:2-4; 65:17, 18; Zekariya 12:3; 14:12, 16, 17) Zolembedwa zambiri zonena za “Yerusalemu” kapena “Ziyoni” zimene zinalembedwa pambuyo pa imfa ya Yesu zimaonekeratu kuti nzophiphiritsa ndipo sizikunena za mzinda weniweniwo kapena kumene kuli mzindawo. (Agalatiya 4:26; Ahebri 12:22; 1 Petro 2:6; Chivumbulutso 3:12; 14:1; 21:2, 10) Umboni womaliza wosonyeza kuti Yerusalemu sunalinso “mzinda wa Mfumu yaikulukulu” unaonekera mu 70 C.E. pamene magulu ankhondo a Roma anausakaza, monga momwe Danieli ndi Yesu Kristu analosera. (Danieli 9:26; Luka 19:41-44) Olemba Baibulo kapenanso Yesu iyemwiniyo sanaloserepo zakuti Yerusalemu wapadziko lapansi adzabwezeretsedwa panthaŵi ina nkukhalanso woyanjidwa mwapadera ndi Yehova Mulungu ngati poyamba.—Agalatiya 4:25; Ahebri 13:14.
-