Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 9/15 tsamba 7-8
  • Mapemphero Omwe Adzayankhidwadi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapemphero Omwe Adzayankhidwadi
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Dzina Lanu Liyeretsedwe”
  • “Ufumu Wanu Udze”
  • ‘Kufuna Kwanu Kuchitidwe’
  • Pamene Ufumuwo Ulamulira
  • “Ambuye, Tiphunzitseni Ife Kupemphera”
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Ambuye—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi ndi Mapemphero Andani Amene Amayankhidwa?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Pankhani ya Mapemphero Amene Mulungu Amamva
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 9/15 tsamba 7-8

Mapemphero Omwe Adzayankhidwadi

PALI mapemphero amene mosakaikira adzayankhidwadi. Mfundo yawo yaikulu iri yophatikizidwa m’chitsanzo chimene Yesu Kristu anapatsa ophunzira ake pamene anati: ‘Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’​—Mateyu 6:9-13.

Mawu amenewo a pemphero lachitsanzo la Yesu abwerezedwa kwanthaŵi mamiliyoni ambirimbiri. Ngakhale kuti Kristu sanayembekezere otsatira ake owona kungotchula mwapamtima pemphero lotero, mapembedzero awo ofotokoza mfundo zofananazo adzayankhidwadi. (Mateyu 6:7, 8) Choncho, kodi kuyeretsa dzina la Mulungu kumatanthauzanji? Kodi nkupemphereranji kuti Ufumu wake udze? Ndipo kodi nkupempheranji kuti chifuniro cha Mulungu chichitidwe?

“Dzina Lanu Liyeretsedwe”

Yehova, “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,” ndi Amene Yesu anatchula kukhala ‘Atate wathu wa kumwamba.’ (Salmo 83:18) Mulungu ‘anabala’ Aisrayeli mwakuwamasula kuchoka muukapolo wa ku Igupto ndi mwakuloŵa nawo m’pangano. (Deuteronomo 32:6, 18; Eksodo 4:22; Yesaya 63:16) Lerolino, Akristu odzozedwa ali ndi ulemu waukulu kwa Yehova monga Atate wawo. (Aroma 8:15) Ndipo atsamwali awo, amene ali ndi chiyembekezo chapadziko lapansi, mofananamo amapemphera kwa Yehova Mulungu monga Atate wawo.​—Yohane 10:16; Chibvumbulutso 7:1-9.

Koma kodi nkupemphereranji kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe? Eya, kuyambira pachipanduko cha anthu aŵiri oyambirira m’munda wa Edene, chitonzo chaikidwa pa dzina laumulungu. Poyankha pemphero lotero, Yehova adzachotsa chitonzo chonse chomwe chaikidwa pa dzina lake lachikumbukiro. (Salmo 135:13) Adzachita zimenezi mwakuchotsa kuipa padziko lapansi. Ponena za nthaŵiyo, Mulungu kupyolera mwa mneneri Ezekieli ananena kuti: ‘Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.’​—Ezekieli 38:23.

Yehova Mulungu ndi woyera ndi waudongo. Chotero dzina lake liyenera kuyeretsedwa, kapena kupatulikitsidwa kukhala loyera. Iye adzasonyeza chiyero chake mwakuchitapo kanthu kudziyeretsa iyemwini pamaso pa chilengedwe chonse. (Ezekieli 36:23) Awo okhumba kukhala ndi chiyanjo chake ndi moyo wamuyaya ayenera kumuwopa Yehova ndi kuyeretsa dzina lake mwakuliwona kukhala losiyana ndi lokwezeka kuposa ena onse. (Levitiko 22:32; Yesaya 8:13; 29:23) Mofananamo, Yesu anauza otsatira ake kupemphera kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe” kapena, “kupatulikitsidwa; likhalitsidwe loyera.” Tiri otsimikiza kuti Mulungu adzayankha mbali imeneyi ya pemphero lachitsanzo la Yesu.

“Ufumu Wanu Udze”

Yesu anauzanso otsatira ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze.” Mosakaikira mapemphero a kudza kwa Ufumu wa Mulungu adzayankhidwa. Ufumuwo ndiwo ulamuliro wauchifumu wa Yehova wochitidwa kupyolera mwa boma lakumwamba Laumesiya lokhala m’manja mwa Mwana wake, Yesu Kristu, ndi “oyera mtima” oyanjanitsidwa. (Danieli 7:13, 14, 18, 22, 27; Yesaya 9:6, 7) Mboni za Yehova kwanthaŵi yaitali zatsimikizira kuchokera m’Malemba kuti Yesu anaikidwa pampando wachifumu kukhala Mfumu yakumwamba m’chaka cha 1914. Nangano, nchifukwa ninji aliyense ayenera kupempherera Ufumuwo kuti “udze”?

Kupempherera kudza kwa Ufumuwo kumatanthauzadi kupempha kuti udze kudzachotsa onse otsutsa ulamuliro wa Mulungu padziko lapansi. Tsopano posachedwapa ‘ufumu [wa Mulungu] . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [a padziko lapansi]. Nudzakhala chikhalire.’ (Danieli 2:44) Chochitika chimenechi chidzawonjezera kuyeretsedwa kwa dzina loyera la Yehova.

‘Kufuna Kwanu Kuchitidwe’

Yesu analangizanso ophunzira ake kuti: ‘Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’ Ili ndi pemphero lakuti Yehova achitepo kanthu mogwirizana ndi chifuniro chake kaamba ka dziko lapansi. Nlofanana ndi chilengezo cha wamasalmo chakuti: ‘Chirichonse chimkonda Yehova achichita, kumwamba ndi pa dziko lapansi, m’nyanja ndi mozama monse. Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang’animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake. Anapanda oyamba a Aigupto, kuyambira munthu kufikira zoŵeta. Anatumiza zizindikiro ndi zodabwitsa pakati pako, Aigupto iwe, pa Farao ndi pa omtumikira onse. Ndiye amene anapanda amitundu ambiri, napha mafumu amphamvu.’​—Salmo 135:6-10.

Kupemphera kuti chifuniro cha Yehova chichitidwe pa dziko lapansi kuli pempho lakuti achite zifuno zake kulinga ku mbulunga imeneyi. Zimenezi zimaphatikizapo kuchotsedwa kotheratu kwa omtsutsa, mongadi momwe anaŵachotsera kumlingo wochepera m’nthaŵi zamakedzana. (Salmo 83:9-18; Chibvumbulutso 19:19-21) Mapemphero a kuchitidwa kwa chifuniro cha Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi ndi chilengedwe chonse adzayankhidwadi.

Pamene Ufumuwo Ulamulira

Mmalo mwa kuipa kumene kumavutitsa chitaganya cha anthu, kodi nchiyani chimene chingayembekezeredwe pamene Ufumu wa Mulungu ulamulira ndipo chifuniro chaumulungu chichitidwa padziko lapansi monga kumwamba? Malinga ndi kunena kwa mtumwi Petro, ‘monga mwa lonjezano [la Mulungu] tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.’ (2 Petro 3:13) “Miyamba yatsopano” ndiyo mphamvu zolamulira zauzimu​—Yesu Kristu ndi 144,000 oloŵa naye mu Ufumu wakumwamba. (Aroma 8:16, 17; Chibvumbulutso 14:1-5; 20:4-6) “Dziko latsopano” sindilo mbulunga ina yadziko lapansi. Mmalomwake, ndilo chitaganya cha anthu olungama okhala pa dziko lapansi.​—Yerekezerani ndi Salmo 96:1.

Pansi pa ulamuliro wa Ufumuwo, dziko lapansi lidzasandulizidwa kukhala paradaiso wapadziko lonse. (Luka 23:43) Panthaŵiyo anthu onse omvera adzasangalala ndi mtendere weniweni ndi kukhupuka. (Salmo 72:1-15; Chibvumbulutso 21:1-5) Inuyo mungakhale pakati pa makamu amenewo a anthu achimwemwe ngati ndinu wochirikiza wokhulupirika wa ulamuliro Waumesiya pa nzika zomvera zapadziko lapansi. Ochirikiza ulamuliro umenewo amapempherera mowona mtima kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova, kudza kwa Ufumu wake, ndikuti chifuniro chake chichitidwe. Mapemphero awo ochokera mumtima adzayankhidwadi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena