Kodi Mumakumbukira?
Kodi mwapeza makope a Nsanja ya Olonda a posachedwa kukhala okuthandizani? Nangano bwanji osayesa kuona ngati mungakumbukire mafunso otsatirapoŵa?
▫ Ngati malingaliro achisembwere alionse abwera okha m’maganizo mwathu, kodi tiyenera kuchitanji?
Tiyenera kusintha nkhaniyo m’maganizo, kukayendayenda kunja, kuŵerenga, kapena kuchita ntchito ina ya panyumba. Nalonso pemphero lili chithandizo champhamvu m’mikhalidwe yotero. (Salmo 62:8)—4/15, tsamba 17.
▫ Kodi nchifukwa ninji achichepere ayenera kukhala osamala ndi mtundu wa nyimbo zimene amamvetsera?
Nyimbo zili ndi mphamvu yosonkhezera, kusangalatsa, ndi kukopa. Popeza kuti nyimbo zambiri zili ndi mawu obisa otanthauza zachisembwere ndi zamakhalidwe oipa, nkosavuta kuona kuti tiyenera kusamala kwambiri posankha malekodi, makaseti ndi madisc.—4/15, tsamba 20-1.
▫ Kodi mawu akuti “kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Kristu” amatanthauzanji? (1 Atesalonika 5:23)
Ameneŵa amanena za kukhalapo kosaoneka kwachifumu kwa Ambuye Yesu Kristu monga Mfumu, kuyambira mu 1914 ndi pambuyo pake, ataikidwa pampando wachifumu kumwamba. (Salmo 110:1, 2)—5/1, tsamba 11.
▫ Kodi kuyeretsa kachisi wauzimu kochitidwa ndi Yehova kunatumikira chifuno chotani? (Malaki 3:1-4)
Yehova anafuna kuti kachisi wake akhale mumkhalidwe woyera kotero kuti pamene ziŵerengero zazikulu za olambira zokhala ndi ziyembekezo za padziko lapansi ziloŵetsedwamo, zikapeze malo amene uchifumu wake wachilengedwe chonse ukulemekezedwa, kumene dzina lake laumulungu likuyeretsedwa, ndi kumene malamulo ake olungama akutsatiridwa.—5/1, tsamba 16.
▫ Kodi nchiyani chimene chili “zinthu” zimene Yesu Kristu akupereka kwa kapolo wake woikidwa? (Mateyu 24:45-47)
“Zinthu” zimenezi ndizo chuma chonse chauzimu chimene chili padziko lapansi chimene chakhala chuma cha Kristu mogwirizana ndi ulamuliro wake monga Mfumu yakumwamba. Zimenezi zikaphatikizapo ntchito ya kupanga ophunzira a Kristu mwa anthu amitundu yonse. (Mateyu 28:19, 20)—5/1, tsamba 17.
▫ Kodi ndimotani mmene akulu Achikristu amasonyezera ‘kufunitsitsa’ kuŵeta gulu la nkhosa, malinga nkunena kwa mawu osonkhezera a Petro pa 1 Petro 5:2?
Mkulu Wachikristu amene amasamalira nkhosa adzagwira ntchito yake mofunitsitsa, chifukwa cha kudzipereka kwake, pansi pa chitsogozo cha Mbusa Wabwino, Yesu Kristu. Kutumikira mofunitsitsa kumatanthauzanso kuti mbusa Wachikristu amagonjera kuulamuliro wa Yehova ndi kulemekeza makonzedwe a teokratiki.—5/15, tsamba 20.
▫ Kodi Yesu anatanthauzanji pamene ananena kuti aliyense womtsata “adzikane yekha”? (Mateyu 16:24)
‘Kudzikana’ kumatanthauza kupereka umwini wanu wonse kwa Yehova. (1 Akorinto 6:19, 20) Kumatanthauza kuti mukhale ndi moyo, osati wodzikondweretsa, koma wokondweretsa Mulungu. (Aroma 14:8)—6/1, tsamba 9.
▫ Kodi nchiyani chimene chimafunika kuti munthu akhale wachimwemwe?
Kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova ndi kukhala wotanganitsidwa muutumiki wake kumadzetsa chimwemwe chenicheni m’moyo wa munthu.—6/1, tsamba 22.
▫ Kodi nchifukwa ninji Yehova analola Abrahamu kulankhula naye momasuka ponena za chifuno Chake cha kuwononga Sodomu? (Genesis 18:22-32)
Chifukwa chimodzi chinali chakuti Abrahamu anali bwenzi la Mulungu. (Yakobo 2:23) Ndiponso, Yehova anazindikira za kuvutika mtima kwa Abrahamu. Mulungu anadziŵa kuti Loti mwana wa mbale wake wa Abrahamu anali kukhala m’Sodomu ndi kuti Abrahamuyo anada nkhaŵa kwambiri ndi moyo wa Loti. Chifukwa cha zifukwa zimenezo Yehova anali wofunitsitsa kuyankha mafunso a Abrahamu onena za chifuno Chake cha kuwononga Sodomu.—6/15, tsamba 16.
▫ Kodi Kukonzanso kwa Aprotestanti kwa m’zaka za zana la 16 kunasonyeza kutembenukira kwa anthu ku Chikristu?
Ayi, sikunatero! Mmalo mwa kutembenuzira anthu ku Chikristu chenicheni, Kukonzansoko kunadzetsa unyinji wa matchalitchi a mitundu yosiyanasiyana kapena a maiko amene ayanjana ndi maboma andale ndi kuwachilikiza mokangalika m’nkhondo zawo.—7/1, tsamba 10-11.
▫ Kodi nchiyani chimene chili “chuma m’mwamba” chimene Yesu ananena pa Mateyu 6:20?
Chimenechi ndicho chuma chimene sichimatha, kuphatikizapo kupanga dzina labwino ndi Yehova ndi mbiri yabwino yosungidwa ya utumiki Wachikristu wochitidwa mokhulupirika. Zinthu zimenezi zili pakati pa zimene Yehova samaiŵala. (Ahebri 6:10)—7/1, tsamba 32.
▫ Kodi ndimikhalidwe yotani imene Petro akutchula kukhala yofunika kwambiri kaamba ka chikhulupiriro chathu? (2 Petro 1:5-7)
Petro anati ukoma, chidziŵitso, kudziletsa, chipiriro, kudzipereka kwaumulungu, kukonda abale, ndi chikondi ziyenera kuwonjezeredwa pachikhulupiriro chathu.—7/15, tsamba 13.
▫ Kodi ndichenjezo lotani loperekedwa kwa anthu a Mulungu limene lili m’nkhani ya tchimo la Davide ndi Batiseba? (2 Samueli 11:2-4)
Ngakhale kuti iye anali waufulu kusangalala muukwati wake, Davide analola chikhumbo cha kugonana choipa kukula. Poona mmene mkazi wa Uriya analiri wokongola, sanaleke malingaliro ake—ndi zochita zake—za kupeza chisangalalo choipa cha kugonana ndi mkaziyo. Zofananazo zingachitike kwa aliyense wa atumiki a Mulungu ngati sapeŵa mtundu umenewu wa chisiriro. (Yakobo 1:14, 15)—8/1, tsamba 14.