Kusunga Diso Lathu Lili “la Kumodzi” m’Ntchito Yaufumu
GERMAN Democratic Republic (G.D.R.), kapena dziko limene linadziŵika kukhala East Germany, linali litangofikitsa kumene zaka zake zapakati. Kukhalapo kwake kwazaka 41 kunatha pa October 3, 1990, pamene dera lake, pafupifupi la ukulu wofanana ndi Liberia kapena chigawo cha Tennessee mu United States, linagwirizanitsidwa ndi Federal Republic of Germany, amene anali kutchedwa West Germany.
Kugwirizanitsidwa kwa mbali ziŵirizo za Germany kwatanthauza masinthidwe ochuluka. Chimene chinalekanitsa maiko aŵiriwo chinali, osati malire okha, komanso kusiyana kwa malingaliro. Kodi zonsezi zinatanthauzanji kwa anthu a kumeneko, ndipo ndimotani mmene moyo wasinthira kwa Mboni za Yehova?
Wende, kusintha kwa zinthu m’November 1989 kumene kunapangitsa kugwirizanitsako kukhala kotheka, kunachitika zitangokwanira zaka makumi anayi za chisosholizimu champhamvu. Mkati mwa nyengo imeneyo, ntchito ya Mboni za Yehova inaletsedwa, ndipo kuzunzidwa kwawo nthaŵi zina kunali kwakukulu.a Pamene ufulu unadza m’G.D.R., chikondwerero chake chinadzadza mtunduwo. Koma pamene chikondwererocho chinazirala, anthu ambiri anakhala ozunguzika maganizo, ogwiritsidwa mwala, ngakhale opanda chimwemwe. Ntchito ya kugwirizanitsa mbali ziŵiri za Germany kuti zikhale dziko limodzi m’chitaganya, m’ndale, ndi m’chuma ikukhaladi yaikulu koposa.
Malinga ndi mpambo wa “162 Tage Deutsche Geschichte” (Masiku 162 a Mbiri ya Germany) mu Der Spiegel, pambuyo pa kugwirizanitsidwako panali mantha aakulu a ulova, kukwera mtengo kwa zinthu, ndi kuwonjezereka kwa ndalama za lendi. “Kodi ndidzalandira ndalama zokwanira nditapuma pantchito?” anthu ambiri a m’dziko limene kale linali G.D.R. anafunsa motero. Bwanji nanga za nyumba? “Mu G.D.R. yense, nyumba zakale zikugumuka, misewu yake ikuwonongeka.” Kuipitsa malo kunafika pamilingo yowopsa.
Poyang’anizana ndi mavuto akakhalidwe ndi azachuma otero, kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova m’dziko limene kale linali G.D.R. zachitira?
Kusunga Diso Lili Lopenya Bwino
Mboni za Yehova zilibe malingaliro osiyana. Chikhulupiriro chawo chozikidwa pa Baibulo nchofanana, kaya kukhale ku East kapena ku West. Limodzi ndi kusintha kwa mkhalidwe wawo m’chitaganya, Mboni zambiri zimasunga uchikatikati wauzimu mwa kusumika maso awo pachonulirapo choyamba cha kutumikira Yehova. Kodi nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika?
Chifukwa chakuti “maonekedwe a dziko ili apita.” (1 Akorinto 7:31) Mkristu wina amene ali mkulu akunena kuti kulalikira pansi pa chiletso Wende isanadze kunafunikira kulimba mtima; kunaphunzitsa Mbonizo kudalira Yehova ndipo kunawaphunzitsa kukhala aluso pogwiritsira ntchito Baibulo. Komabe, tsopano, “tiyenera kusamala kwambiri kuti tisacheukitsidwe ndi kukondetsa zinthu zakuthupi ndi nkhaŵa za moyo.”
Ufulu ndi kupita patsogolo kaŵirikaŵiri zimapimidwa ndi zinthu zakuthupi. Anthu ambiri m’chigawo chimenechi amalingalira za kupeza zimene akanachita nthaŵi imene yapita yotayikayo kapena mwinamwake zinthu zokondweretsa zimene anasoŵa. Zimenezi zimaonekera bwino pamene munthu akuyenda ndi galimoto m’misewu yokonzedwa ndi miyala m’matauni ndi midzi ya Thuringia ndi Saxony kummwera. Misewuyo ingafunikire kukonzedwa, nyumba zake zosaoneka bwino, komatu nzonchuluka chotani nanga ziwiya za masetilaiti a mawailesi a kanema zonga mbalezo! Nkosavuta kwa munthu kunyengeka ndi kukhulupirira kuti chisungiko ndi chimwemwe zimadza chifukwa cha kukhala ndi zinthu zonse zimene maso amaona. Ndimsampha wowopsa chotani nanga umenewo!
Mu Ulaliki wa pa Phiri, Yesu analankhula za ngozi ya kusamalira kosayenera zinthu zakuthupi ndi nkhaŵa za moyo. “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi,” iye anachenjeza motero. Anawonjezera kuti: “Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako lili la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala loŵalitsidwa.” (Mateyu 6:19, 22) Kodi anatanthauzanji? Diso la kumodzi ndilo limene limaona bwino ndi limene limasonyeza zithunzithunzi zozindikiridwa bwino ndi ubongo. Diso lauzimu limene lili la kumodzi limaona bwino chithunzithunzi cha Ufumu wa Mulungu. Chotero kusankha kwa Mkristu kusunga diso lake lili la kumodzi, loona bwino Ufumu wa Mulungu, ndi kunyalanyaza nkhaŵa kumamthandiza kukhala wachikatikati mwauzimu.
Zimenezi zingafotokozedwe mwafanizo ndi chokumana nacho cha mwamuna wina ndi mkazi okwatirana ku Zwickau, Saxony, amene anakondwerera Baibulo panthaŵi ya Wende. Bizinesi lawo linali lodya nthaŵi kwambiri, komabe iwo anaika zinthu zauzimu pamalo oyamba, akumafika pamisonkhano yonse Yachikristu. “Polingalira za bizinesi lathulo, sitingathe kupeza nthaŵi,” iwo anavomereza motero, “koma mwauzimu timaifuna.” Nchosankha chanzeru chotani nanga!
Lingaliraninso za banja lina ku Plauen, nalonso la ku Saxony. Mwamuna anali wokonza mawotchi, mmisiri weniweni pabizinesi lakelo. Pambuyo pa Wende, ndalama za lendi ya malowo zinawonjezeredwa kwambiri. Kodi anayenera kuchitanji? “Ikandidyera ndalama zambiri, ndipo ndinaona chowonadi kukhala chofunika.” Chotero anasamukira kumalo amtengo wotsikirapo opanda malonda kwambiri. Inde, wokonza mawotchi ameneyu anadziŵa msanga za kusunga diso lili la kumodzi.
Komabe, oŵerengeka adziŵa zimenezi mochedwa kwambiri. Mkulu wina Wachikristu, polingalira kuti kuyambitsidwa kwa mpikisano wa malonda kunali kolonjeza kwambiri, anayamba kuchita bizinesi. Woyang’anira woyendayenda anamthandiza mokoma mtima kuti asalole mathayo a bizinesilo kuphimba mkhalidwe wake wauzimu. Komabe, mwachisoni, zimenezo nzimene zinachitika. Miyezi ingapo pambuyo pake mbaleyo analeka kukhala mkulu. Pambuyo pake iye analemba kuti: “Malinga ndi chokumana nacho changa, ndingakonde kulangiza mbale aliyense amene akukalimira mwaŵi wautumiki kuti asachite bizinesi la yekha.” Zimenezi sizikutanthauza kuti kudzigwirira ntchito kwa Mkristu nkolakwa. Koma kaya tili ndi bizinesi lathu la ife eni kapena ayi, kusumika kwambiri malingaliro athu pankhaŵa zachuma kungatiloŵetse m’kukhala akapolo achuma mosafuna. Yesu anasonyeza chotulukapo chake kuti: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina.” (Mateyu 6:24) Wolemba ndakatulo wa ku Germany wotchedwa Goethe anafotokoza kuti: “Palibe anthu amene amaloŵa muukapolo woipa kwambiri koposa awo amene monama amakhulupirira kuti ngomasuka.”
Titakumana ndi kavumvulu weniweni tingafunikire kutsinzina pang’ono kapena kuphimba manja kumaso kuti tionebe. Pamene tizingidwa ndi chipwirikiti cha ndale, cha zachuma, kapena cha kakhalidwe, tifunikira kusamala kwambiri kuti tisungebe chonulirapo chathu chauzimu m’maganizo. Kodi Akristu ena akuchitanji kuti asunge diso lawo kukhala la kumodzi m’ntchito ya Ufumu?
Ntchito ya Ufumu Yowonjezereka
M’dziko limene kale linali G.D.R. yense, Mboni zikuthera nthaŵi yochuluka pantchito ya kulalikira kuposa kale lonse. M’zaka ziŵiri zapitazo, avareji ya nthaŵi yotheredwa muutumiki wakumunda inakwera ndi 21 peresenti. Chotulukapo chake ndicho chiwonjezeko chachikulu cha 34 peresenti m’maphunziro a Baibulo apanyumba. Ndiponso, chiŵerengero cha apainiya okhazikika pakali pano chakwera kuŵirikiza kanayi kuposa mmene chinaliri zaka ziŵiri zapitazo! Pamene kuli kwakuti ena amavutika maganizo ndi kudandaula, Akristu oposa 23,000 mu amene kale anali G.D.R. akulimbana bwino lomwe ndi mkhalidwewo mwa kusunga diso lili la kumodzi. Zimenezi zathandizira chiwonjezeko chodabwitsa muntchito ya Ufumu.—Yerekezerani ndi Yoswa 6:15.
Ntchito yofutukulidwa imeneyi ikutanthauza kuti gawo likusamaliridwa bwino cha kummwera, kumene kuli unyinji wa Mboni. Ambiri a maina a malo a kumeneko amakumbutsa za m’mbiri. Ngati mumakonda ziŵiya zodyera zadothi zotchedwa china, mudzazindikira tauni ya Meissen, pafupi ndi Dresden, monga kumene kunayambira zina za ziŵiya zabwino koposa za padziko lonse. Meissen tsopano ndiko kwawo kwa ofalitsa Ufumu 130. Kapena lingalirani za Weimar, “malikulu akale a Germany.” Chimango chotchedwa Goethe-Schiller Memorial pakati patauniyo chimapereka umboni wa mgwirizano wolemekezeka wa Weimar ndi olemba mabuku aŵiriwo ndipo ndicho chinthu chonyaditsa anthu ambiri kumeneko. Lerolino mzinda wa Weimar unganyadire ofalitsa ake a mbiri yabwinowo 150.
Komabe, kumpoto zinthu nzosiyana kwambiri, pokhala ndi ofalitsa oŵerengeka ndi kutalikirana kwa mipingo. Makamaka ntchito nzovuta kupeza. Ambiri amene amagwira ntchito amaumirizika kugwira ntchito maola owonjezereka kuti asatayikiridwe ndi ntchitoyo. Mbale wina wotumikira monga mlaliki wanthaŵi yonse kumpoto akufotokoza kuti: “Pamene tinali pansi pa chiletso mbale aliyense anafunikira chitetezo cha Yehova muutumiki wakumunda, koma kupeza ntchito kunali kosavuta. Koma tsopano zinthu zasintha. Tili ndi ufulu wa kulalikira, komano tikufunikira chitsogozo chake ponena za ntchito. Kusintha kotero kufunikira kukuzoloŵera.”
Kodi ofalitsa akukondwa kukhala okhoza kulalikira mowonjezereka? Lingaliro la Wolfgang nlakuti: “Nkwabwino kwambiri kuti wofalitsa mmodzimodziyo agwire ntchito m’gawo limodzimodzilo mobwerezabwereza. Anthu amakulitsa chidaliro mwa munthuyo ndipo amakhala omasuka kwambiri.” Ndiponso, eninyumba “salinso ndi manyazi kulankhula za chipembedzo pakhomo, ngakhale pamene odutsa m’njira ali pafupi moti angamve. Chipembedzo sichilinso nkhani yachinsinsi.” Ralf ndi Martina akuvomereza zimenezo. “Timasangalala kugwira ntchito kaŵirikaŵiri m’gawo lathu. Timadziŵana ndi anthu mwachindunji ndipo nawonso amakondwerera mitundu yosiyanasiyana ya mabuku amene alipo.”
Kuyamikira Mabuku Athu
Ralf ndi Martina amayamikira makamaka buku lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Kwa ambiri amene analandira lingaliro la kusakhalako kwa Mulungu mu amene kale anali G.D.R., buku limeneli likukhaladi chithandizo chabwino kwambiri cha phunziro la Baibulo. Iwo analakalakanso chofalitsidwa cholembedwa mwachidule chokhala ndi nkhani yofananayo. “Mmene tinaliri okondwera nanga pamene brosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? linatulutsidwa pa Msonkhano Wachigawo wa 1992 wa ‘Onyamula Kuunika’ m’Dresden. Linali yankho la mapemphero athu.”
Ambiri amene sali Mboni afikira pakuyamikira zofalitsidwa za Watch Tower. Mu July 1992 mphunzitsi wa maphunziro a kakhalidwe ka anthu analemba kalata yosonyeza “ulemu [wake] ndi kuyamikira kwakukulu” kaamba ka zofalitsidwazo, zimene amagwiritsira ntchito pokonzekera maphunziro okaphunzitsa. Mu January 1992 mkazi wina wa ku Rostock analandira kope la buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kwa Mboni ziŵiri zimene zinafika pakhomo pake. Iye analembera kalata ofesi ya nthambi ya Germany kuti: “Ndine wa Tchalitchi cha Lutheran. Ndimayamikira kwambiri ntchito ya gulu la Mboni za Yehova. Izo zimanena motsimikiza mtima kuti anthu sangathe kuchita zinthu popanda chitsogozo cha Mulungu.”
Kodi ndichitsogozo chochuluka motani chimene matchalitchi a Dziko Lachikristu apatsa ziŵalo zawo? Nyuzipepala yotchuka yotchedwa Die Zeit inathirira ndemanga m’December 1991 kuti pamene kuli kwakuti Tchalitchi cha Lutheran chinali “ndi ulemerero kwakanthaŵi monga amayi wa kusintha kwa zinthu mwamtendere, kutchuka kwake kukuzimiririka mofulumira.” Ndithudi, nthumwi ina ya Tchalitchi cha Lutheran inadandaula kuti: “Anthu asokoneza moyo ndi ulemerero wa dongosolo la mpikisano wa malonda ndi paradaiso.” Chiŵalo china cha tchalitchi m’Magdeburg chinalemba kalata yopempha kudziŵa zambiri. Chifukwa ninji? “Pambuyo pa zaka zambiri za kusakhulupirira,” mwamunayo analemba motero, “tsopano ndakhutiritsidwa maganizo kwambiri kuti dzikoli lafika m’masiku ake otsiriza ndi kuti tidzakumana ndi mavuto aakulu mtsogolomu posachedwa.”—2 Timoteo 3:1-5.
Kumangira Chifutukuko
Wende isanachitike, Nyumba Zaufumu sizinaloledwe m’G.D.R. Tsopano nzofunika mwamsanga; kuzimanga kukuikidwa poyamba. Imeneyi ndiyo mbali ina ya kulambira kowona imene yakhala ndi kusintha kwakukulu. Chokumana nacho cha mbale wina chikufotokoza mwafanizo mmene kusintha kumeneku kwakhalira kofulumira.
M’March 1990, patangopita maola angapo Mboni za Yehova zitalandira chilolezo cha lamulo m’G.D.R., mbale wina anapemphedwa kukalankhula ndi kagulu ka Mboni, akumagwiritsira ntchito chokuzira mawu kwanthaŵi yoyamba m’moyo wake. Zaka ziŵiri ndi theka pambuyo pake, mpingo umene iye amasonkhanako unapatulira Nyumba Yaufumu yatsopano kotheratu. Podzafika pakutha kwa 1992, Nyumba Zaufumu zisanu ndi ziŵiri zinali zitamangidwa kaamba ka mipingo 16. Zina zoposa 30, ndiponso Nyumba ya Msonkhano yokongola, zikulinganizidwa.
Diso Losumikidwa pa Ufumu wa Mulungu
“Mwamsanga Wende itachitika,” akutero mkulu wina Wachikristu, “anthu ambiri anakana Baibulo. Anaika chiyembekezo chawo pa boma latsopano, limene linawalonjeza kuti padzakhala mikhalidwe yabwino tsopano.” Kodi lonjezo lawolo linakwaniritsidwa? “Mkati mwa zaka ziŵiri iwo anasintha maganizo awo. Tsopano anthu akuvomerezana nafe kuti maboma a anthu sangadzetse mtendere ndi chilungamo.”
Makamu a anthu anasangalala pakuzimiririka kwa chisosholizimu champhamvucho m’G.D.R., kukumachititsa kuyambika kwa imene analingalira kukhala nyengo yachipambano koposa ya lingaliro la Kumadzulo. Koma anagwiritsidwa mwala. Mosasamala kanthu za mtundu wa boma limene likulamulira, Mboni za Yehova zimasunga diso lawo lili la kumodzi ndi losumikidwa kotheratu pa Ufumu wa Mulungu, umene umaŵala monga nyenyezi kuthambo. Chiyembekezo choterocho sichidzagwiritsa mwala munthu.—Aroma 5:5.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Yehova Anatisamalira Pansi pa Chiletso,” Magawo 1-3, m’makope a Nsanja ya Olonda a April 15, May 1, ndi May 15, 1992.
[Zithunzi patsamba 26]
Mboni m’Germany zikugwiritsira ntchito ufulu wawo kuchita zochuluka m’ntchito ya Ufumu