Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/15 tsamba 8-9
  • Pemphero, ndi Kudalira Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pemphero, ndi Kudalira Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Ulaliki Wotchuka Woposa Wonse Umene Unaperekedwa
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Ulaliki Wotchuka wa Paphiri
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Mapemphero Anu Amagwirizana ndi Zimene Yesu Anaphunzitsa?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Khalani ndi Moyo Wolinganizika, Wopepuka
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Pemphero, ndi Kudalira Mulungu

PAMENE Yesu akupitirizabe ndi ulaliki wake, iye akutsutsa chinyengo cha anthu amene amawonetsera umulungu wawo wachiphamaso. “Paliponse upatsa mphatso zachifundo,” iye akutero, “usamawomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga.”

“Ndipo,“ Yesu akupiritiriza, “pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m’masunagoge, ndi pamphambano zamakwalala, kuti awonekere kwa anthu.” Mmalo mwake, iye akulangiza kuti: “Popemphera, Iowa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali mtseri.” Yesu mwiniyo anapereka mapemphero apoyera, chotero iye sakutsutsa amenewa. Amene iye akutsutsa ndiwo mapemphero amene amaperekedwera kuchititsa chidwi omvetsera ndi kupeza thamo lawo loyamikira.

Yesu akuwonjezera kupereka uphungu: “Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja.” Yesu sakutanthauza kuti kubwereza mwa iko kokha nkolakwa. Nthawi zina, iyemwiniyo anagwiritsira ntchito “mawu ofanana“ mobwerezabwereza popemphera. Koma chimene akutsutsa ndicho kulankhulidwa kwa mawu olowezedwa pamtima “mobwerezabwereza,“ monga momwe amachitira owerenga mikanda ndi chala pamene akubwerezabwereza mapemphero awo pamtima.

Kuti athandize omvetsera ake kupemphera, Yesu akupereka pemphero lachitsanzo limene limaphatikizapo mapempho asanu ndi awiri. Atatu oyambirira akuvomereza kufunika kwa Mulungu ndi zifuno zake. Iwo ali mapempho a dzina la Mulungu kuti liyeretsedwe, Ufumu wake kudza, ndi chifuniro chake kuchitidwa. Anayi otsala ali mapempho a munthu mwini, ndiko kuti, a chakudya cha tsiku ndi tsiku, kukhululukidwa kwa machimo, kusayesedwa koposa chipiriro cha munthuyo, ndi kusatengeredwa kwa woipayo.

Popitirizabe, Yesu akutchula msampha wa kuika chigogomezero chopambanitsa pa chuma chakuthupi. lye akulimbikitsa kuti: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba.” Sikokha kuti chuma chotero nchokhoza kuwonongeka koma sichimapangitsa unansi uliwonse ndi Mulungu.

Chifukwa chake, Yesu akuti: “Koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba.”Zimenezi zimachitidwa mwakuika utumiki wa Mulungu pachiyambi m’moyo wanu. Palibe munthu amene angakuchotsereni ubwino umene mwauwunjika motero ndi Mulungu, kapena mphotho yake yabwinoyo. Kenako Yesu akuwonjezera kuti: “Kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.”

Mowonjezera polankhula za msampha wokondetsa zinthu zakuthupi, Yesu akupereka fanizo: “Nyali yathupi ndiyo diso. Pamenepo, ngati, diso lanu liri bwino, thupi lanu lonse lidzaunikiridwa; koma ngati diso lanu liri loipa, thupi lanu lonse lidzakhala mu mdima (NW).”Diso limene limagwira ntchito bwino liri lofanana ndi nyali yoyatsidwa m’malo amdima kuthupilo. Koma kuti liwone molondola, disolo liyenera kukhala bwino, ndiko kuti, liyenera kusumikidwa pa chinthu chimodzi. Diso losasumikidwa bwino limatsogolera ku kupima zinthu molakwa, kuika kulondola zinthu zakuthupi patsogolo pa utumiki wa Mulungu, kumene kumachititsa “thupi” lonse kukhala mu mdima.

Yesu akumaliza nkhaniyi ndi fanizo lamphamvu kumati: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma.”

Atatha kupereka uphungu umenewu, Yesu akutsimikizira omvetsera ake kuti safunikira kudera nkhawa ndi zosowa zawo zakuthupi ngati iwo aika utumiki wa Mulungu pachiyambi. “Yang’anirani mbalame zakumwamba,“ iye akutero, “kuti sizimafesai, kapena sizimatemai, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wakumwamba azidyetsa.” Kenako iye akufunsa kuti: “Nanga inu mulibe kusiyana kuziposa kodi?“Kenako, Yesu akutchula maluwa akuthengo nanena kuti “angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la amenewa. Koma ngati,“ iye akupitiriza, “Mulungu aveka chotero udzu wakuthengo . . . nanga siinu kopambana ndithu inu akukhulupirira pang’ono?“

Chotero Yesu akumaliza mwakumati: “Musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena Tidzavala chiyani? . . . Pakuti Atate wanu wakumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” Mateyu 6:1-34; 26:36-45.

◆ Kodi ndimalangizo otania pemphero amene Yesu anapereka?

◆ Kodi nchifukwa ninji chuma chakumwamba chiri chopambana, ndipo chimapezedwa motani?

◆ Kodi ndimafanizo otani amene akuperekedwa kuthandiza munthuyo kupewa kukondetsa zinthu zakuthupi?

◆ Kodi nchifukwa ninji Yesu ananena kuti palibe kufunikira kudera nkhawa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena