Kodi ndi Mulungu Uti Amene Mumamlambira?
KUZUNGULIRA padziko lonse, anthu angayankhe funso limenelo m’njira zambiri zosiyana. Mtumwi Paulo analongosola kuti: “Iriko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri,” ndipo milungu imene ikulambiridwa lerolino imafikira chiŵerengero cha mamiliyoni. (1 Akorinto 8:5) Komabe, kodi munkadziŵa kuti anthu ambiri amalambira mulungu wosiyana ndi amene amaganiza kuti akumlambira? Ndipo kodi munkazindikira kuti anthu ambiri osakhulupirira Mulungu ali opembedza kwenikweni kuposa awo amene amakhulupirira mulungu? Mwanjira yotani?
Eya, tanthauzo limodzi la kulambira ndilo “kulingalira ndi ulemu, kulemekeza, kapena kudzipereka kwakukulu, ngakhale kopambanitsa.” M’zinenero zoyambirira za Baibulo, mawu otanthauza kulambira anali ndi lingaliro la utumiki kapena kugwadira munthu wina. Pokumbukira zimenezi, tiyeni tiwone mmene anthu angalakwire ponena za amene kapena chimene iwo akulambiradi.
Kulambira Kosakaniza
Talingalirani chitsanzo cha Asamariya akale. Ambiri a iwo adali alendo amene Asuri anawabweretsa ku Palestina kudzaloŵa mmalo mafuko khumi akumpoto a Israyeli okhala m’ndende. Kalelo, iwo ankalondola milungu yachikunja, koma tsopano anapanga kuyesayesa kuphunzira za Yehova, Mulungu wa Israyeli. Kodi iwo analeka chipembedzo chawo chakale? Ayi. Baibulo likusimba kuti: ‘Koma sanamvera, nachita monga mwa mwambo wawo woyamba. Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano awo osema.’ (2 Mafumu 17:40, 41) Chotero Asamariya, ngakhale kuti anamdziŵa Yehova, iwo anatumikirabe milungu yawo yakale, mwakutero kutsatira chipembedzo chosakaniza.
Chinthu chofananacho chinachitika pamene amishonale anayambitsa Chiroma Katolika Kum’mwera kwa Amereka. Iwo anatembenuza anthu ambiri, koma mofanana ndi Asamariya akalewo, anthuwo sanaiwale milungu yawo yakale. Motero, m’Brazil miyambo yachikunja ya using’anga idakachitidwabe ndi “Akristu,” monga momwe iriri miyambo yolemekeza milungu yakale, monga ngati mulungu wachikazi Iemanjá. Zinthu zofananazo zimachitika m’maiko ena a Kum’mwera kwa Amereka.
Ndiponso, chipembedzo chimene amishonalewo anayambitsa Kum’mwera kwa Amereka mwa icho chokha chidali chipembedzo chosakaniza. Ziphunzitso zake zambiri, monga ngati Utatu, moto wa helo, ndi kusakhoza kufa kwa moyo, zinachokera ku zipembedzo zachikunja zakale ndi nthanthi. Izo sizinkapezeka m’Baibulo. Mofananamo, mapwando ake—kuphatikizapo Krisimasi ndi Isitala—sanali achiyambi Chachikristu.a Kodi nkotheka kusunga mapwando achikunja oterowo ndikukhulupirira ziphunzitso zosakhala Zachikristu zoterozo ndiyeno m’kumalambirabe Mulungu wa Baibulo, amene anati: “Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha”? (Eksodo 20:3) Ndithudi ayi!
“Dzisungireni Nokha Kupewa Mafano”
Talingalirani njira ina imene anthu amanyengedwa m’nkhani ya kulambira. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Tiana, dzisungireni nokha kupewa mafano.” (1 Yohane 5:21) Pafupifupi anthu miliyoni chikwi chimodzi andandalitsidwa kukhala a Chikristu Chadziko, ndipo iwo amanena kuti amalambira Mulungu mmodzimodziyo amene Yohane ankalambira. Komabe, mamiliyoni mazana ambiri a iwo amagwadira zifanizo za “oyera mtima,” za Yesu, ndi za namwali Mariya.
Pali mitundu ina yobisika yakulambira mafano. M’chaka cha 44 C.E., Mfumu Herode Agripa anapereka nkhani yapoyera, ndipo anthu anasangalala kwakuti anafuula kuti: ‘Ndiwo mawu a mulungu, si a munthu ayi.’ (Machitidwe 12:21, 22) Inde, iwo anampanga Herode kukhala fano, kumpanga kukhala mulungu. Zinthu zofananazo zikuchitika lerolino. M’masiku oyambirira pamene Chinazi chinkayamba kulamulira ku Ulaya, mfuu yakuti “Heil Hitler!” idalidi kufuula kolemekeza. Ambiri anali ofunitsitsa kumenya nkhondo ndikufera Führer ngati kuti iye anali mulungu, mpulumutsi wa dzikolo. Komabe, ambiri a awo amene ankapereka ulemu woterowo anali ziŵalo za matchalitchi a Chikristu Chadziko!
Patsogolo ndi pambuyo pa Hitler, atsogoleri ena andale adzikweza iwo eni kukhala apulumutsi ndipo akakamiza kuti ayenera kugonjeredwa kotheratu. Awo amene anagonjera anapanga anthuŵa kukhala milungu, mosasamala kanthu kuti “olambirawo” anali achipembedzo chiti kapena ngakhale ngati anati sakhulupirira Mulungu. Ulemu umene akatswiri azamaseŵera, akatswiri a kanema, ndi osangulutsa ena amalandira kuchokera kwa ochemerera awo ngwofanana ndi kulambira.
Kulambira Ndalama
Kuwonjezera apa, talingalirani matanthauzo a mawu a Yesu pamene anati: ‘Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.’ (Mateyu 6:24) Kodi mumadziŵa munthu aliyense amene ali ndichipembedzo chakutichakuti koma amene chikondwerero chake chachikulu m’moyo ndicho kupanga ndalama? Pamenepo, kodi munthu woteroyo akutumikiradi yani, Mulungu kapena chuma? Kodi ndi osakhulupirira angati amene mumadziŵa amene agwidwa ndi kulondola ndalama? Ndithudi, iwonso ngolambira ndalama, mwinamwake mwachangu kwambiri kuposa akhulupiriri ambiri.
Mtumwi Paulo analongosola lamulo lamakhalidwe abwino lofananalo pamene analemba kuti: ‘Chifukwa chake fetsani ziŵalozo ziri padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chiri kupembedza mafano.’ (Akolose 3:5) Ngati timasirira chinachake mwamphamvu kwakuti timapanga kuyesayesa kulikonse kuti tichipeze icho, mwinamwake kufikira pa kuswa lamulo pochita zimenezo, pamenepo kwa ife chinthucho ndifano, mulungu. (Aefeso 5:5) M’kalata ina, Paulo analemba motere ponena za ochita zolakwa ena: ‘Mulungu wawo ndiyo mimba yawo.’ (Afilipi 3:19) Ngati chifuno chathu chonse m’moyo ndicho kudzikondweretsa tokha, kudzaza mimba zathu, kunena kwake titero, pamenepo ndife mulungu wa enife. Kodi ndiangati amene mumadziŵa amene amalambira mulungu wamtundu umenewu?
Inde, monga momwe analembera mtumwi Paulo kuti: “Iriko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri.” Ndipo m’zochitika zambiri, alambiri ake ngofanana ndi Asamariya akale, otumikira mulungu mmodzi ndi mawu awo ndi wina mwa zochita zawo. Komabe, kwenikwenidi, pali Mulungu mmodzi yekha amene amafunikira kulambira kwathu. Kodi mumamdziŵa iye? Kuwonjezera apa, pali chinthu chimodzi chimene chimagwirizanitsa kulambira kwa milungu ina yonse kupatulapo iye yekha. Kodi icho nchiyani? Tidzawona m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka, onani bukhu lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, masamba 212-13, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.