Phunziro pa Mbalame ndi Maluŵa
KODI nchiyani lerolino chimene anthu kaŵirikaŵiri amada nacho nkhaŵa kwambiri kuposa chilichonse? Kwa ambiri, ndicho kukhala ndi ndalama zokwanira zosamalirira banja lawo kapena kukhala okhoza kutukula miyoyo yawo.
Kupeza ndalama zokwanira kunalinso nkhaŵa yaikulu pamene Yesu Kristu anali pa dziko lapansi. Koma anachenjeza kuti nkhawa yovomerezeka imeneyi ikhoza kukhala yaikulu kwambiri ndi kutsekereza zinthu zauzimu kunja. Pochitira fanizo mfundo yake, Yesu anauza ophunzira ake kupenyetsetsa mbalame ndi maluŵa.
Mbalame zimafunika kudya tsiku lililonse—kuposa mmene timadyera chifukwa kupeza mphamvu kwake kumadalira pa chakudya chambiri. Ndiponso, sizimafesa mbewu, kututa, kapena kututira chakudya chamtsogolo mu nkhokwe. Komabe, monga momwe Yesu ananenera, ‘Atate wathu wakumwamba azidyetsa.’ (Mateyu 6:26) Momwemonso, Mulungu amaveka “maluŵa a kuthengo” mokongola koposa.—Mateyu 6:28-30.
Yesu akutitsimikizira kuti ngati tiika zosoŵa zakuthupi pamalo ake ndi kuika zinthu zauzimu pamalo oyamba, Mulungu adzatipatsadi zakudya ndi zovala zofunika. Ngati Yehova Mulungu amasamalira mbalame ndi maluŵa, adzasamaliradi awo amene amamkonda ndi ‘kupitiriza kufuna ufumu wake ndi chilungamo chake choyamba.’ (Mateyu 6:33, NW) Kodi mukuika zinthu za Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba m’moyo wanu?