Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Sonyezani Chikhulupiriro mwa Yehova—Mwa Kuchita Zinthu Zophunziridwa
    Nsanja ya Olonda—1988 | August 15
    • 11. Ndimotani mmene ena agwidwira m’kulondola zinthu zakuthupi, ndipo nchifukwa ninji ichi chiri chopanda nzeru?

      11 “Koma muthange mwafuna ufumu ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Chiri chomvetsa chisoni chotani nanga pamene ena alephera kulabadira mawu amenewo! Akumameza nthano ya chisungiko cha zachuma, iwo mopusa amalondola chuma, maphunziro a kudziko, ndi ntchito za kudziko, “akumatama kulemera kwawo.” (Masalmo 49:6) Solomo anachenjeza kuti: “Usadzitopetse kuti ulemere. . . . Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu yowuluka mlengalenga.”​—Miyambo 23:4, 5.

  • Sonyezani Chikhulupiriro mwa Yehova—Mwa Kuchita Zinthu Zophunziridwa
    Nsanja ya Olonda—1988 | August 15
    • 13. Nchifukwa ninji chiri chabwino koposa kukhala okwaniritsidwa ndi “chakudya ndi chofunda”?

      13 Awo amene amakhulupirira mwa Yehova kupereka kaamba ka iwo amadzipatula iwo eni ku zowawa ndi zodera nkhaŵa zambiri. Zowona, kukhala okhutiritsidwa ndi kokha “chakudya ndi chofunda” chingatanthauze muyezo wa makhalidwe odzichepetsa mokulira. (1 Timoteo 6:8) Koma “chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo.” (Miyambo 11:4) M’kuwonjezerapo, pamene tiwonjezera utumiki wathu kwa Yehova, timadziika ife eni pa mzera kaamba ka “madalitso a Yehova” omwe “alemeretsa, ndipo sawonjezerapo chisoni.”​—Miyambo 10:22.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena