Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Khalani Akuchita Mawu, Osati Akumva Okha
    Nsanja ya Olonda—1990 | October 1
    • 3. Kodi ndi malangizo otani onena za kuweruza amene Yesu akupereka chotsatira mu Ulaliki wa pa Phiri?

      3 Pamene Yesu anapitiriza ndi Ulaliki wake wa pa Phiri, mawu ambiri anafotokozedwa amene Akristu ayenera kukalamira kuwatsanzira. Panopa pali ena amene amawonekera kukhala opepuka, koma amatsutsa chimodzi cha zikhoterero zovuta kwenikweni kuzichotsa: ‘Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso. Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwemwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m’diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m’diso lakoli. Wonyenga iwe! tayamba kuchotsa m’diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m’diso la mbale wako.’​—Mateyu 7:1-5.

  • Khalani Akuchita Mawu, Osati Akumva Okha
    Nsanja ya Olonda—1990 | October 1
    • 5. Kodi nchifukwa ninji kuli kopepuka kwambiri kuwona zophophonya mwa ena kuposa zomwe tiri nazo?

      5 M’zaka za zana loyamba C.E., chifukwa cha miyambo yapakamwa, Afarisi ochuluka anakhoterera kuweruza ena mwansontho. Aliyense wa amvetseri a Yesu amene anali ndi chizoloŵezi cha kuchita ichi anafunikira kuleka. Nkopepuka kuwona zitsotso m’diso la ena kuposa mitanda yokhala mwathu​—ndipo kumasangalatsa malingaliro athu! Monga mmene mwamuna wina ananenera kuti, “Ndimakonda kusuliza ena chifukwa kumandipangitsa kudzimva bwino kwambiri!” Chizoloŵezi cha kuloza chala ena chingatipatse malingaliro akudziganiza kukhala abwino kumene kungaphimbe zophophonya zathu zimene tikufuna kubisa. Koma ngati kuwongolera kuli koyenerera, kuyenera kuperekedwa mumzimu wofatsa. Wopereka chiwongoleroyo ayenera nthaŵi zonse kulingalira zophophonya zake.​—Agalatiya 6:1.

  • Khalani Akuchita Mawu, Osati Akumva Okha
    Nsanja ya Olonda—1990 | October 1
    • 6. Kodi ziweruzo zathu zitafunikira, ziyenera kuzikidwa pamaziko otani, ndipo kodi ndi thandizo lotani limene tiyenera kufunafuna kuti tisakhale osuliza mopambanitsa?

      6 Yesu sanabwere kudzaweruza dziko koma kudzalipulumutsa. Ziweruzo zonse zimene iye anapereka sizinali zake koma zinazikidwa pamawu amene Mulungu anampatsa kuti awalankhule. (Yohane 12:47-50) Ziweruzo zirizonse zimene tingapange ziyeneranso kukhala zogwirizana ndi Mawu a Yehova. Tiyenera kupeŵa chikhoterero chaumunthu cha kukhala oweruza. Pochita tero, tiyenera kupitirizabe kupempherera thandizo la Yehova: “Dzipemphanibe, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; dzifunafunanibe, ndipo mudzapeza; dzigogodanibe, ndipo kudzatsegulidwa kwa inu. Pakuti yense wopempha amalandira, ndipo yense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda kudzatsegulidwa kwa iye.” (Mateyu 7:7, 8, NW) Ngakhale Yesu anati: ‘Sindikhoza kuchita kanthu kwa ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha iye wondituma ine.’​—Yohane 5:30.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena